“Nthaŵi Yonse Palibe Munthu Analankhula Chotero”
“Nthaŵi Yonse Palibe Munthu Analankhula Chotero”
“Onse anam’chitira Iye umboni nazizwa ndi mawu a chisomo akutuluka mkamwa mwake.”—LUKA 4:22.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anyamata amene anawatuma kukagwira Yesu anabwerera chimanjamanja? (b) N’chiyani chikuonetsa kuti sanali anyamata okhawo amene anazizwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu?
ANYAMATA analephera ntchito yawo. Anawatuma kuti akagwire Yesu Kristu, koma anabwerako chimanjamanja. Ansembe aakulu ndi Afarisi anafunsa anyamatawo kuti: “Simunam’tenga Iye bwanji?” Ndipodi, n’chifukwa chiyani anyamatawo sanamugwire munthu woti sakanagwiritsa ntchito mphamvu kuti alimbane nawo? Anyamatawo anayankha kuti: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” Iwo anagoma kwambiri ndi kaphunzitsidwe ka Yesu moti sanaone chifukwa chom’mangira munthu wokonda mtendere ameneyo. *—Yohane 7:32, 45, 46.
2 Amene anazizwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu sanali anyamata okhawo. Baibulo limatiuza kuti anthu ambirimbiri anabwera kwa iye kuti adzangomumvetsera akamalankhula. Anthu a m’mudzi wa kwawo anadabwa “ndi mawu a chisomo akutuluka mkamwa mwake.” (Luka 4:22) Analankhula kangapo ali m’ngalawa kwa makamu a anthu amene anasonkhana m’mbali mwa Nyanja ya Galileya. (Marko 3:9; 4:1; Luka 5:1-3) Nthaŵi ina, “khamu lalikulu la anthu” linali naye pamodzi kwa masiku angapo ngakhale kuti silinadye kalikonse.—Marko 8:1, 2.
3. Kodi chifukwa chachikulu chimene chinapangitsa Yesu kukhala mphunzitsi wamkulu n’chiti?
3 N’chifukwa chiyani Yesu anali mphunzitsi wamkulu? Chifukwa chachikulu chinali chikondi. * Yesu anakonda choonadi chimene anali kuphunzitsa ndiponso anakonda anthu amene anali kuwaphunzitsa. Koma Yesu analinso ndi luso lapadera logwiritsa ntchito njira zophunzitsira zogwira mtima. M’nkhani zophunzira zimene zili m’magazini ino, tikambirana njira zina zogwira mtima zimene anagwiritsa ntchito ndiponso mmene tingazitsanzirire.
Kufotokoza Mwachidule Ndiponso Mosavuta Kumva
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva pophunzitsa, ndipo n’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti anatero? (b) N’chifukwa chiyani Ulaliki wa pa Phiri ndi chitsanzo cha kufotokoza zinthu mwachidule kumene Yesu anagwiritsa ntchito pophunzitsa?
4 Nthaŵi zambiri, anthu ophunzira kwambiri amagwiritsa ntchito mawu amene omvera awo sangadziŵe kuti akutanthauza chiyani. Koma ngati ena sangamve zimene tikunena, kodi angapindule bwanji ndi zimene tikuwauza? Yesu monga mphunzitsi, sanalankhule zinthu zimene ena sanathe kumva. Tangoganizani kuchuluka kwa mawu omwe iye ayenera kuti anali kudziŵa, amene akanatha kuwagwiritsa ntchito. Komabe, ngakhale kuti ankadziŵa zambiri, iye anaganizira omvera ake, osati kudziganizira yekha. Anadziŵa kuti Machitidwe 4:13) Kuti awafike pamtima, iye anagwiritsa ntchito mawu amene anthu oterowo akanatha kumvetsa. Mawuwo ayenera kuti anali osavuta, koma anali ndi mfundo za choonadi zakuya.
ambiri mwa iwo anali “osaphunzira ndi opulukira [“anthu wamba,” NW].” (5 Mwachitsanzo, taganizani za Ulaliki wa pa Phiri, umene uli pa Mateyu 5:3–7:27. Mwina Yesu analalikira ulalikiwu kwa mphindi 20 zokha basi. koma unali ndi ziphunzitso zakuya, mfundo zofunika kwambiri pankhani monga zokhudza chigololo, chisudzulo, ndi kukondetsa chuma. (Mateyu 5:27-32; 6:19-34) Komabe izo sizili mfundo zovuta kuzimva kapena zoimitsa mutu. Inde, mawu onse amene anawagwiritsa ntchito anali osavuta, ngakhale mwana anatha kumva. N’zosadabwitsa kuti atamaliza, anthuwo, amene ena mwa iwo anali alimi, abusa, ndi asodzi, “anazizwa ndi chiphunzitso chake.”—Mateyu 7:28.
6. Perekani chitsanzo cha mmene Yesu anafotokozera zinthu zosavuta kumva koma za tanthauzo lalikulu.
6 Nthaŵi zambiri Yesu anali kufotokoza zinthu zosavuta kumva koma za tanthauzo lalikulu pogwiritsa ntchito mawu afupiafupi, omveka bwino. Nthaŵi imeneyo mabuku anali asanayambe kusindikizidwa, koma mwa kugwiritsa ntchito mawu osavuta, iye anasindikiza uthenga wake m’maganizo ndi m’mitima ya omvera ake moti sakanaiwala. Taonani zitsanzo izi: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: . . . simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.” “Pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” “Olimba safuna sing’anga ayi, koma odwala.” “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” * (Mateyu 6:24; 7:1, 20; 9:12; 26:52; Marko 12:17; Machitidwe 20:35) Mpaka pano, mawu amphamvu amenewo savuta kuwakumbukira ngakhale kuti papita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene Yesu anawalankhula.
Kugwiritsa Ntchito Mafunso
7. N’chifukwa chiyani Yesu anali kufunsa mafunso?
7 Yesu anagwiritsa ntchito mafunso mochititsa chidwi. Iye nthaŵi zambiri anatero ngakhale kuti chidule chinali kungowafotokozera omverawo mfundo yake basi. Nanga n’chifukwa chiyani anali kufunsa mafunso? Nthaŵi zina, iye anagwiritsa Mateyu 12:24-30; 21:23-27; 22:41-46) Komabe, nthaŵi zambiri Yesu anali kufunsa mafunso n’cholinga choti amveketse choonadi, kuwachititsa omvera ake kufotokoza zimene zinali m’mitima yawo, ndiponso kulimbikitsa ndi kuphunzitsa ophunzira ake kuti aziganiza. Tiyeni tione zitsanzo ziŵiri, zonsezo zokhudza mtumwi Petro.
ntchito mafunso ogometsa kuti avumbule zolinga za adani ake, ndipo zimenezi zinachititsa adaniwo kusoŵa chonena. (8, 9. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mafunso kuti athandize Petro kupeza yankho lolondola pa nkhani yopereka ndalama za pakachisi?
8 Choyamba, takumbukirani nthaŵi imene olandira ndalama za ku kachisi anafunsa Petro ngati Yesu anapereka ndalama za pakachisi. * Petro, yemwe nthaŵi zina anali wopupuluma, anayankha kuti, “Apereka.” Koma, patapita nthaŵi yochepa, Yesu analankhula naye kuti: “Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja? Ndipo mmene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.” (Mateyu 17:24-27) Petro ayenera kuti anazindikira mosavuta mfundo ya mafunso a Yesu. N’chifukwa chiyani tikutero?
9 M’nthaŵi ya Yesu, anthu a m’banja lachifumu sanali kukhoma msonkho. Motero, Yesu monga Mwana wobadwa yekha wa Mfumu yakumwamba imene anali kuilambira pakachisipo, sanayenera kupereka msonkho. Onani kuti m’malo mongomuuza Petro yankho lolondola, Yesu anagwiritsa ntchito mafunso mogwira mtima koma moleza kuti amuthandize Petro kupeza yankholo, ndiponso mwina kuti amuonetse kufunika koyamba waganiza kaye asanalankhule.
10, 11. Kodi Yesu anatani pamene Petro anadula khutu la mwamuna wina usiku wa pa Paskha mu 33 C.E., ndipo zimenezi zikusonyeza bwanji kuti Yesu anadziŵa kuti mafunso ndi othandiza kwambiri?
10 Chitsanzo chachiŵiri ndi zimene zinachitika usiku wa pa Paskha mu 33 C.E. pamene khamu la anthu linabwera kudzam’gwira Yesu. Ophunzira anafunsa Yesu ngati iwo anafunika kumenyana nawo anthuwo kuti amuteteze. (Luka 22:49) M’malo modikira yankho, Petro anadula khutu la mwamuna wina ndi lupanga (ngakhale kuti mwina Petro anali n’cholinga chomuvulaza munthuyo kuposa pamenepo). Petro anachita zinthu zosemphana ndi zimene mbuye wakeyo ankafuna, chifukwa Yesu anali wokonzeka kwambiri kugwidwa. Kodi Yesu anatani? Iye moleza mtima monga mmene ankachitira nthaŵi zonse, anafunsa Petro mafunso atatu kuti: “Chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?” “Uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri? Koma pakutero, malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?”—Yohane 18:11; Mateyu 26:52-54.
11 Taimani kaye pang’ono musinkhesinkhe nkhani imeneyo. Yesu, yemwe anazunguliridwa ndi khamu la anthu okwiya, anadziŵa kuti anatsala pang’ono kumwalira ndiponso kuti kuchotsa chitonzo pa dzina la Atate wake ndi kupulumuka kwa anthu kunadalira iyeyo. Komabe, anapeza nthaŵi pomwepo yomuuzira Petro mfundo za choonadi zofunika kwambiri pogwiritsa ntchito mafunso. Kodi si zoonekeratu pamenepa kuti Yesu anadziŵa kuti mafunso ndi othandiza kwambiri?
Mafanizo Okokomeza Omveka Bwino
12, 13. (a) Kodi fanizo lokokomeza n’chiyani? (b) Kodi Yesu anagwiritsa bwanji ntchito mafanizo okokomeza pogogomezera kuti n’kupanda nzeru kumanenanena zolakwa zazing’ono za abale athu?
12 Yesu nthaŵi zambiri muutumiki wake anagwiritsa ntchito njira ina yophunzitsira yogwira mtima. Imeneyi inali njira yogwiritsa ntchito mafanizo okokomeza. Kumeneku n’kukokomeza zinthu mwadala n’cholinga chofuna kutsindika mfundo. Mwa kugwiritsa ntchito mafanizo okokomeza, Yesu ankapangitsa anthu kukhala ndi chithunzi m’maganizo cha zimene anali kunenazo zomwe zinawathandiza kuti asamaziiwale. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.
13 Potsindika kufunika kwa ‘kusaweruza’ ena, Yesu pa Ulaliki wa pa Phiri, anati: “Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwe mwini suuganizira?” (Mateyu 7:1-3) Kodi mungaone m’maganizo zimene akunenazo? Munthu wokonda kunenanena zolakwa za ena akufuna kuchotsa kachitsotso chabe “m’diso” la mbale wake. Iye anganene kuti mbale wakeyo sangathe kuona bwino zinthu kuti aweruze moyenera. Koma luso loona zinthu moyenera la munthu wokonda kunenanena zolakwa za enayo laphimbika ndi “mtanda,” mtengo umene anthu angagwiritse ntchito pomanga denga. Imeneyotu ndi njira yosaiŵalika yogogomezera kuti n’kupanda nzeru kumanenanena zolakwa zazing’ono za abale athu pomwe ifeyo mwina tili ndi zolakwa zazikulu.
14. N’chifukwa chiyani mawu a Yesu onena za kukuntha udzudzu ndi kumeza ngamila anali fanizo lokokomeza lamphamvu kwambiri?
14 Nthaŵi ina, Yesu anawanena Afarisi kuti anali ‘atsogoleri akhungu, akukuntha udzudzu, koma ngamila ameza.’ (Mateyu 23:24) Kumeneku kunali kugwiritsa ntchito fanizo lokokomeza mwamphamvu kwambiri. Chifukwa chiyani? Panali kusiyana kwakukulu pakati pa udzudzu womwe ndi waung’ono ndi ngamila, yomwe inali imodzi mwa nyama zazikulu kwambiri zimene omvera a Yesu anali kuzidziŵa. Ena ayerekezera kuti pangafunike udzudzu wokwana 70 miliyoni kuti kulemera kwake kufanane ndi kwa ngamira imodzi yaikulu bwino. Ndiponso, Yesu anadziŵa kuti Afarisi anali kukuntha vinyo pa nsalu yosefera. Anthu oumirira malamulo amenewo ankachita zimenezo n’cholinga choti apeŵe kumeza udzudzu kuti asakhale odetsedwa malinga ndi mwambo wawo. Komabe, iwo mophiphiritsira anali kumeza ngamira, yomwenso inali yodetsedwa. (Levitiko 11:4, 21-24) Mfundo ya Yesu pamenepa inali yoonekeratu. Afarisi anali kutsatira mopambanitsa tinthu ting’onoting’ono timene Chilamulo chinkafuna, koma anali kunyalanyaza zinthu zimene zinali zofunika kwambiri monga “kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro.” (Mateyu 23:23) Yesu anavumbula bwino mmene iwo analili.
15. Kodi ndi maphunziro ena ati amene Yesu anaphunzitsa pogwiritsa ntchito mafanizo okokomeza?
15 Muutumiki wake wonse, Yesu nthaŵi zambiri anagwiritsa ntchito mafanizo okokomeza. Taonani zitsanzo zina zotsatirazi. “Chikhulupiriro monga kambewu kampiru” chimene chingasunthe phiri—Yesu anagwiritsa ntchito fanizo logwira mtima limeneli potsindika kuti chikhulupiriro, ngakhale chitakhala chaching’ono, chingachite zazikulu. (Mateyu 17:20) Ngamira, yomwe ndi yaikulu ikuyesetsa kupyola pa diso la singano—fanizo limeneli likusonyeza bwino mmene zimakhalira zovuta kwa munthu wachuma kutumikira Mulungu pamenenso akuumirira moyo wokondetsa chuma. (Mateyu 19:24) Kodi simukuchita chidwi ndi mafanizo a Yesu omveka bwino ndiponso luso lake lophunzitsa anthu zinthu zakuya pogwiritsa ntchito mawu osavuta?
Mfundo Zosatsutsika
16. Kodi Yesu nthaŵi zonse anagwiritsa ntchito bwanji nzeru zake zapamwamba?
16 Popeza Yesu anali ndi maganizo angwiro, anali katswiri pogwiritsa ntchito mfundo zomveka polankhula ndi anthu. Komabe, iye sanagwiritse ntchito molakwika luso limeneli. Pophunzitsa, iye nthaŵi zonse anali kugwiritsa ntchito nzeru zake zapamwamba kuti apititse patsogolo choonadi. Nthaŵi zina, iye anali kugwiritsa ntchito mfundo zomveka ndi zamphamvu potsutsa kuneneza kwabodza kwa adani ake achipembedzo. Nthaŵi zambiri, anagwiritsa ntchito mfundo zomveka kuti aphunzitse ophunzira ake maphunziro ofunika kwambiri. Tiyeni tione luso lapamwamba la Yesu logwiritsa ntchito mfundo zomveka.
17, 18. Kodi ndi mfundo yomveka ndi yamphamvu iti imene Yesu anagwiritsa ntchito potsutsa kuneneza kwabodza kwa Afarisi?
17 Taganizirani nthaŵi imene Yesu anachiritsa Mateyu 12:22-26) Kwenikweni, Yesu anali kunena kuti: ‘Ngati ndatumidwa ndi Satana, monga mmene inu mukunenera, kupasula zimene Satana anamanga, ndiye kuti Satana akuchita zinthu zotsutsana ndi chifuniro chake chomwe ndipo sangachedwe kugwa.’ Kodi siinali mfundo yomveka ndi yamphamvu imeneyi?
mwamuna wogwidwa ndi chiŵanda amene anali wakhungu ndiponso wosalankhula. Afarisi atamva zimenezo, anati: “Uyu samatulutsa ziŵanda koma ndi mphamvu yake ya Beelzebule [Satana], mkulu wa ziŵanda.” Onani kuti Afarisi anavomereza kuti panafunika mphamvu zoposa za munthu kuti atulutse ziŵanda za Satana. Komabe, pofuna kuti anthu asakhulupirire Yesu, iwo anati mphamvu zimene iye anagwiritsa ntchito zinali za Satana. Yesu, powasonyeza kuti mfundo yawoyo inali yopanda nzeru, anawayankha kuti: “Ufumu uliwonse wogaŵanika pawokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logaŵanika palokha silidzakhala; ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agaŵanika payekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?” (18 Ndiyeno Yesu anapitiriza kufotokoza mfundo zina pa nkhani imeneyi. Iye anali kudziŵa kuti ena mwa ophunzira a Afarisiwo anatulutsapo ziŵanda. Motero, iye anafunsa funso losavuta koma logometsa lakuti: “Ngati Ine ndimatulutsa ziŵanda ndi mphamvu yake ya Beelzebule, ana [kapena kuti ophunzira] anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani?” (Mateyu 12:27) M’mawu ena, mfundo ya Yesu inali yakuti: ‘Ngati ine ndimatulutsa ziŵanda mwa mphamvu ya Satana, ndiye kuti ophunzira anunso amagwiritsa ntchito mphamvu ya Satana yomweyo.’ Kodi Afarisi akanati chiyani? Sakanavomereza kuti ophunzira awo anali kugwiritsa ntchito mphamvu ya Satana. Mwakugwiritsa ntchito mfundo yosatsutsika, Yesu anaonetsa kuti kum’neneza kwawoko kunali kopanda nzeru.
19, 20. (a) Kodi ndi njira yolimbikitsa iti imene Yesu anagwiritsira ntchito mfundo zomveka? (b) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mfundo yakuti ‘koposa kotani nanga’ poyankha pempho la ophunzira ake lakuti awaphunzitse kupemphera?
19 Kuwonjezera pa kugwiritsa ntchito mfundo zomveka pofuna kuti adani ake asoŵe chonena, Yesu anagwiritsanso ntchito mfundo zomveka, zokhudza mtima pophunzitsa choonadi cholimbikitsa ndiponso chosangalatsa cha Yehova. Nthaŵi zambiri, iye anagwiritsa ntchito mfundo imene tingaitche kuti ‘koposa kotani nanga.’ Anagwiritsa ntchito mfundo imeneyi pofuna kuthandiza omvera ake kuti zoona zimene anazidziŵa kale azitsimikizire kuposa mmene anazidziŵiramo. Tiyeni tione zitsanzo ziŵiri zokha.
20 Poyankha funso la ophunzira ake lakuti awaphunzitse kupemphera, Yesu anasimba fanizo la munthu amene “liuma” lake linachititsa bwenzi lake kum’patsa zimene anapempha ngakhale kuti bwenzilo silinkafuna. Yesu anafotokozanso kuti makolo amafuna kupatsa ana awo “mphatso zabwino.” Ndiyeno anamaliza kuti: ‘Ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?’ (Luka 11:1-13) Mfundo imene Yesu anafotokoza apa si yokhudza kufanana, koma kusiyana. Ngati bwenzi lomwe silinkafuna, pamapeto pake linakakamizika kupatsa mnzake zimene ankafuna, ndiponso ngati makolo opanda ungwiro amapereka zimene ana awo akufuna, koposa kotani nanga mmene Atate wathu wachikondi wakumwamba adzaperekera mzimu woyera kwa atumiki ake okhulupirika amene amamupempha modzichepetsa!
21, 22. (a) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mfundo zomveka ziti popereka malangizo othandiza kuthana ndi nkhaŵa ya zinthu zakuthupi? (b) Pamene tapenda njira zophunzitsira zingapo za Yesu, kodi tikufika ponena kuti chiyani?
21 Yesu anagwiritsanso ntchito mfundo yofanana Luka 12:24, 27, 28) Inde, ngati Yehova amasamalira mbalame ndi maluŵa, koposa kotani nanga mmene adzasamalirira atumiki ake! Mosakayika, mfundo zosonyeza chikondi koma zamphamvu zimenezi zinakhudza mitima ya omvera a Yesu.
ndi imeneyi popereka malangizo othandiza kuthana ndi nkhaŵa ya zinthu zakuthupi. Anati: ‘Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa: Nanga inu simuziposa mbalame kwambiri! Lingalirani maluwa, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito ndi kusapota. Koma ngati Mulungu aveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang’ono?’ (22 Pamene tapenda njira zophunzitsira zingapo za Yesu, tingaone mosavuta kuti anyamata amene analephera kum’gwira aja sikuti anakokomeza pamene anati: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” Koma njira yophunzitsira yotchuka ya Yesu inali yogwiritsa ntchito mafanizo. N’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito njira imeneyi? Ndipo n’chiyani chinachititsa mafanizo ake kukhala ogwira mtima kwambiri? Tikambirana mafunso ameneŵa m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 1 Anyamatawo ayenera kuti anali nthumwi za bwalo la milandu la Sanihedirini ndipo anali kulamulidwa ndi akulu a nsembe.
^ ndime 3 Onani nkhani yakuti “Ndakupatsani Inu Chitsanzo” ndiponso yakuti “Nditsatireni Ine Nthaŵi Zonse,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002.
^ ndime 6 Mawu omalizaŵa amene ali pa Machitidwe 20:35, anawagwira mawu ndi mtumwi Paulo yekha, ngakhale kuti mfundo ya mawuwo imapezeka m’Mauthenga Abwino. Mwina Paulo anamva mawu ameneŵa kwa munthu wina (mwina wophunzira amene anamva Yesu akunena zimenezi kapena anamva kwa Yesu woukitsidwa) kapena Mulungu anam’vumbulutsira.—Machitidwe 22:6-15; 1 Akorinto 15:6, 8.
^ ndime 8 Ayuda chaka chilichonse ankafunika kupereka ndalama ya msonkho wa pakachisi yokwana rupiya (ndalama yokwanira kulipira munthu masiku aŵiri). Ndalama ya msonkhoyi ankaigwiritsa ntchito kukonzetsera kachisi, kulipirira ntchito imene inali kuchitika pakachisipo ndiponso nsembe zimene anali kupereka kumeneko m’malo mwa mtundu wonsewo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu anaphunzitsa mwa kufotokoza zinthu mwachidule ndiponso mosavuta kumva?
• N’chifukwa chiyani Yesu anagwiritsa ntchito mafunso pophunzitsa?
• Kodi fanizo lokokomeza n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Yesu anagwiritsa ntchito njira yophunzitsira imeneyi?
• Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mfundo zomveka pophunzitsa ophunzira ake choonadi chosangalatsa cha Yehova?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 9]
Yesu anagwiritsa ntchito mawu osavuta omwe anthu wamba anatha kumva
[Chithunzi patsamba 10]
Afarisi ‘anakuntha udzudzu koma anameza ngamira’