Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu
Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu
“Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—MATEYU 28:19, 20.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti tonsefe ndife aphunzitsi? (b) Pankhani yophunzitsa, kodi Akristu oona ali ndi udindo wapadera wotani?
KODI ndinu mphunzitsi? Tinganene kuti tonsefe ndife aphunzitsi m’njira ina yake. Mukamalondolera njira munthu amene wasokera, kusonyeza mnzanu amene mukugwira naye ntchito mmene angagwirire ntchito inayake, kapena kuuza mwana mmene angamangire nsapato zake, mumakhala mukuphunzitsa. Kodi simungavomereze kuti kuthandiza anthu powachitira zimenezi kumasangalatsa?
2 Pankhani yophunzitsa, Akristu oona ali ndi udindo wapadera. Talamulidwa ‘kuphunzitsa anthu.’ (Mateyu 28:19, 20) Mu mpingonso, pali nthaŵi zina zimene timaphunzitsa. Amuna oyenerera amaikidwa kukhala ‘abusa ndi aphunzitsi,’ n’cholinga choti amangilire mpingo. (Aefeso 4:11-13) Pa ntchito zawo zachikristu za tsiku ndi tsiku, akazi okhwima mwauzimu amayenera ‘kuphunzitsa zokoma’ akazi aang’ono. (Tito 2:3-5) Tonsefe timauzidwa kulimbikitsa okhulupirira anzathu, ndipo tingamvere langizo limenelo pogwiritsa ntchito Baibulo kulimbikitsa ena. (1 Atesalonika 5:11) Ndi mwayi waukulu kukhala mphunzitsi wa Mawu a Mulungu ndi kuuza ena zinthu zauzimu zimene zingawapindulitse mpaka kalekale.
3. Kodi tingatani kuti tiziphunzitsa mogwira mtima kwambiri?
3 Koma kodi tingatani kuti tiziphunzitsa mogwira mtima kwambiri? Chinthu chachikulu chimene tingachite ndicho kutsanzira Mphunzitsi Wamkulu, Yesu. Ena angafunse kuti, ‘Koma tingamutsanzire bwanji Yesu? Iye anali wangwiro.’ N’zoona kuti sitingakhale aphunzitsi angwiro. Komabe, mosasamala kanthu za luso lathu, tingayesetse kutsanzira mmene Yesu ankaphunzitsira. Tiyeni tikambirane mmene tingagwiritsire ntchito njira zinayi mwa njira zake zophunzitsira. Zimenezi ndizo kufotokoza mosavuta kumva, mafunso ogwira mtima, mfundo zomveka, ndi mafanizo oyenerera.
Kufotokoza Mosavuta Kumva
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani kufotokoza mosavuta kumva kuli mbali yaikulu ya choonadi cha Baibulo? (b) N’chifukwa chiyani n’kofunika kusamala mawu amene tikugwiritsa ntchito kuti tiphunzitse mosavuta kumva?
4 Mfundo za choonadi zofunika kwambiri za m’Mawu a Mulungu n’zosavuta kumva. Yesu popemphera anati: “Ndivomerezana ndi Inu, Atate, . . . kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziŵitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda.” (Mateyu 11:25) Yehova wavumbula zolinga zake kwa anthu oona mtima ndi odzichepetsa. (1 Akorinto 1:26-28) Motero, kufotokoza mosavuta kumva kuli mbali yaikulu ya choonadi cha Baibulo.
5 Mukamaphunzitsa munthu Baibulo panyumba pake kapena kupita ku ulendo wobwereza kwa anthu achidwi, kodi mungaphunzitse bwanji mosavuta kumva? Eya, kodi tinaphunzira chiyani kwa Mphunzitsi Wamkulu? Pofuna kuti omvetsera ake amve, omwe ambiri anali “osaphunzira ndi opulukira [“anthu wamba,” NW], Yesu anagwiritsa ntchito mawu osavuta omwe anthuwo anatha kumva. (Machitidwe 4:13) Motero, kuti tiphunzitse moti anthuwo asavutike kumva, choyamba tifunika kusamala mawu amene tikugwiritsa ntchito. Sitifunika kugwiritsa ntchito mawu ovuta kuwamvetsa kuti ena akhulupirire kwambiri choonadi cha m’Mawu a Mulungu. ‘Mawu oposa’ amenewo angachititse mantha makamaka anthu amene sanaphunzire kwambiri kapena amene amangodziŵa mawu ochepa chabe. (1 Akorinto 2:1, 2) Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza kuti mawu osavuta osankhidwa bwino angaphunzitse choonadi mwamphamvu kwambiri.
6. Kodi tingapeŵe bwanji kulemetsa wophunzira Baibulo mwa kumuuza zinthu zambirimbiri?
6 Kuti tiphunzitse mosavuta kumva, tiyeneranso kusamala kuti tipeŵe kulemetsa wophunzira Baibuloyo mwa kumuuza zinthu zambirimbiri. Yesu ankawaganizira ophunzira ake kuti panali zina zimene sakanatha kuzimvetsa. (Yohane 16:12) Ifenso tiyenera kumuganizira wophunzirayo. Mwachitsanzo, pophunzira naye m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, sitifunika kufotokoza chilichonse mwatsatanetsatane. * Ndiponso sitifunika kuthamanga kwambiri pophunzira, ngati kuti kuphunzira zochuluka ndiye chinthu chofunika kwambiri. M’malo mwake, n’kwanzeru kuti liŵiro la phunzirolo lizidalira zimene wophunzirayo akufunikira ndiponso luso lake. Cholinga chathu ndicho kuthandiza wophunzirayo kuti akhale wophunzira wa Kristu ndiponso wolambira Yehova. Tifunika kuthera nthaŵi iliyonse yoyenerera kuti tithandize wophunzira wachidwiyo kumvetsa zimene akuphunzira. Motero choonadi chingamukhudze mtima ndi kumulimbikitsa kuchitapo kanthu.—Aroma 12:2.
7. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuphunzitsa mosavuta kumva pokamba nkhani mumpingo?
7 Kodi tingatani kuti tilankhule mawu “omveka bwino” pokamba nkhani mumpingo, makamaka ngati ena mwa omverawo ndi atsopano? (1 Akorinto 14:9) Taonani mfundo zitatu zotsatirazi zimene zingakuthandizeni. Choyamba, fotokozani mawu achilendo onse amene mugwiritse ntchito. Kumvetsa kwathu Mawu a Mulungu kwatipangitsa kudziŵa mawu amene anthu ena sawadziŵa. Ngati tigwiritsa ntchito mawu monga akuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” “nkhosa zina,” ndi “Babulo Wamkulu,” tingafunike kuwafotokoza ndi mawu aafupi osavuta amene angamveketse tanthauzo lake. Chachiŵiri, peŵani kuchulutsa mawu. Mawu ochuluka kwambiri, ofotokozedwa mopambanitsa angapangitse omvera kusiya kumvetsera. Kusiya mawu osafunika kumathandiza kuti zinthu zikhale zosavuta kumva. Chachitatu, musachulutse mfundo. Pofufuza tingapeze mfundo zambiri zosangalatsa. Koma ndi bwino kukonza nkhaniyo kuti ikhale ndi mfundo zazikulu zochepa chabe, n’kukamba zinthu zokhazo zimene zikumveketsa bwino mfundozo ndiponso zimene mungazifotokoze bwino m’nthaŵi imene mwapatsidwa.
Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mogwira Mtima
8, 9. Kodi tingasankhe bwanji funso limene lingagwirizane ndi zimene mwini nyumba angasangalale nazo? Perekani zitsanzo.
8 Kumbukirani kuti Yesu anali katswiri pogwiritsa ntchito mafunso kuthandiza ophunzira ake kuti afotokoze maganizo awo ndiponso kuwalimbikitsa ndi kuwaphunzitsa kuti aziganiza. Mwa kugwiritsa ntchito mafunso, Yesu anawafika pamtima. (Mateyu 16:13, 15; Yohane 11:26) Kodi, tingagwiritse ntchito bwanji mafunso mogwira mtima monga ankachitira Yesu?
9 Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, tingafunse mafunso kuti tidzutse chidwi, komanso kuti tipeze mpata woti tilankhule za Ufumu wa Mulungu. Kodi tingasankhe bwanji funso limene lingagwirizane ndi zimene mwini nyumbayo angasangalale nazo? Khalani maso. Mukamayandikira panyumbapo, mwazamwazani maso. Kodi pali zidole pabwalopo, zimene zikusonyeza kuti panyumbapo pali ana? Ngati ndi choncho, tingam’funse kuti, ‘Kodi munadzifunsapo kuti zinthu zidzakhala bwanji ana anu akadzakula?’ (Salmo 37:10, 11) Kodi pali maloko angapo pachitseko cha kumaso kwa nyumbayo, kapena zipangizo zotetezera? Tingam’funse kuti: ‘Kodi mukuganiza kuti idzafika nthaŵi imene anthu ngati inu ndi ine tidzakhala otetezeka panyumba pathu ndiponso munsewu?’ (Mika 4:3, 4) Kodi pali chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti pali munthu amene akudwala panyumbapo? Tingam’funse kuti: ‘Kodi idzafika nthaŵi imene aliyense sadzadwala? (Yesaya 33:24) Mungapeze mfundo zina m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. *
10. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso kuti tidziŵe maganizo a wophunzira Baibulo ndi mmene akumvera mumtima mwake, koma tizikumbukira chiyani?
10 Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito bwino mafunso, pophunzitsa Baibulo? Ife sitingadziŵe zimene zili mumtima mwa munthu monga mmene ankachitira Yesu. Komabe, kufunsa mosamala ndi mwanzeru kungatithandize kudziŵa maganizo a wophunzirayo ndi mmene akumvera mumtima mwake. (Miyambo 20:5) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikuphunzira naye mutu wakuti “Chifukwa Chake Kukhala ndi Moyo Waumulungu Kumapatsa Chimwemwe,” m’buku la Chidziŵitso. Mutu umenewu umafotokoza mmene Mulungu amaonera chinyengo, chiwerewere, ndi nkhani zina. Wophunzirayo angayankhe bwino mafunso osindikizidwawo, koma kodi akugwirizana nazo zimene akuphunzirazo? Tingam’funse kuti: ‘Kodi mukuona kuti n’kwabwino kuchita zimene Yehova amafuna pankhani zimenezi?’ ‘Kodi mungatsatire bwanji mfundo za m’Baibulo zimenezi pamoyo wanu?’ Komabe, kumbukirani kuti n’kofunika kukhala waulemu, muzilemekeza wophunzirayo. Sitifunika kufunsa mafunso amene angamuumitse pakamwa kapena kum’chititsa manyazi wophunzira Baibuloyo.—Miyambo 12:18.
11. Kodi ndi njira ziti zimene okamba nkhani za anthu onse angagwiritsire ntchito bwino mafunso?
11 Okamba nkhani za onse angagwiritsenso ntchito bwino mafunso. Mafunso omwe sitiyembekeza kuti omvera ayankhe mokweza, angathandize omverawo kuganiza ndi kusinkhasinkha. Yesu nthaŵi zina anali kufunsa mafunso oterowo. (Mateyu 11:7-9) Ndiponso, wokamba nkhaniyo akanena mawu oyamba, angafunse mafunso osonyeza mfundo zazikulu zimene nkhaniyo ifotokoze. Anganene kuti: “M’nkhani yathu lero, tikambirana mayankho a mafunso aŵa . . . ” Ndiyeno pomaliza, angabwereze mfundo zazikulu mogwiritsa ntchito mafunso aja.
12. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene akulu achikristu angagwiritsire ntchito mafunso kuti athandize wokhulupirira mnzawo kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu.
12 Pochita ubusa, akulu achikristu angafunse mafunso pothandiza ‘wamantha mtima [“wovutika maganizo,” NW] kupeza chilimbikitso m’Mawu a Yehova. (1 Atesalonika 5:14) Mwachitsanzo, pothandiza munthu amene akuvutika maganizo, mkulu angagwiritse ntchito Salmo 34:18. Lembali limati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi [“osweka mumzimu,” NW].” Pofuna kuonetsetsa kuti munthu wotaya mtimayo akuona kuti zimenezi zikugwira ntchito kwa iye, mkuluyo angam’funse kuti: ‘Kodi Yehova ali pafupi ndi yani? Kodi nthaŵi zina ‘mumasweka mtima’ ndiponso ‘kusweka mumzimu’? Popeza Yehova ali pafupi ndi anthu oterowo monga momwe Baibulo likunenera, kodi sizikutanthauza kuti ali pafupi ndi inu?’ Kumutsimikizira mokoma mtima chonchi kungalimbikitse munthu amene akuvutika maganizo.—Yesaya 57:15.
Mfundo Zomveka
13, 14. (a) Kodi tingakambirane bwanji ndi munthu amene akuti sakhulupirira Mulungu amene samuona? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyembekezera kuti onse adzakhulupirira?
13 Muutumiki wathu, timafuna kuwafika anthu pamtima ndi mfundo zomveka, zowathandiza kuti Machitidwe 19:8; 28:23, 24) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mfundo zovuta kuzimvetsa n’cholinga choti tiwathandize ena kukhulupirira kuti Mawu a Mulungu ndi oona? Ayi. Mfundo zomveka sizifunika kukhala zovuta. Nthaŵi zambiri, mfundo zomveka zomwe zafotokozedwa mosavuta n’zimene zimagwira mtima kwambiri. Taonani chitsanzo chotsatirachi.
akhulupirire. (14 Kodi tingayankhe bwanji ngati munthu wanena kuti sakhulupirira Mulungu yemwe sakumuona? Tingakambirane naye lamulo lachilengedwe lakuti pakachitika chinachake ndiye kuti chilipo chachititsa. Tikaona chinachake chimene chachitika, timavomereza kuti chilipo chachititsa. Tinganene kuti: ‘Ngati mutakhala kuti munali m’dera la kutchire ndiyeno n’kupeza nyumba yomangidwa bwino muli zakudya (chochitika), simungavutike kuvomereza kuti winawake (wochititsa) anamanga nyumbayo ndi kudzazamo zakudya m’makabati ake. Moteronso, tikamaona zinthu za luso m’chilengedwe ndiponso chakudya chambiri chimene chili “m’kabati” ya dziko lapansi (chochitika), kodi sizomveka kuvomereza kuti Winawake (wochititsa) anapanga zimenezi?’ Baibulo limafotokoza mosavuta mfundo imeneyi kuti: “Nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Komabe, ngakhale mfundo zathu zitakhala zomveka motani, si onse amene adzakhulupirira. Baibulo limatikumbutsa kuti amene angakhulupirire ndi “ofuna moyo wosatha” okha.—Machitidwe 13:48, NW; 2 Atesalonika 3:2.
15. Kodi ndi mfundo iti imene tingagwiritse ntchito posonyeza makhalidwe a Yehova ndi mmene amachitira zinthu, ndipo ndi zitsanzo ziŵiri ziti zimene zikusonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imeneyi?
15 Tikamaphunzitsa, kaya ndi muutumiki wakumunda kapena mumpingo, tingagwiritse ntchito mfundo zomveka posonyeza makhalidwe a Yehova ndi mmene amachitira zinthu. Mfundo yogwira mtima kwambiri ndi yoti “koposa kotani nanga” imene Yesu nthaŵi zina anaigwiritsa ntchito. (Luka 11:13; 12:24) Popeza mfundo imeneyi imasonyeza kusiyana kwa zinthu, ingakhudze mtima kwambiri. Pofuna kuvumbula kuti chiphunzitso cha moto wa helo n’chabodza, tinganene kuti: ‘Palibe atate wachikondi amene angalange mwana wake mwa kum’gwira dzanja m’kumamuotcha pamoto. Koposa kotani nanga mmene nkhani ya moto wa helo imamunyansira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi!’ (Yeremiya 7:31) Pophunzitsa kuti Yehova amasamalira mtumiki wake wina aliyense, tinganene kuti: ‘Ngati Yehova amadziŵa dzina la nyenyezi iliyonse mwa nyenyezi miyandamiyanda zimene zilipo, koposa kotani nanga mmene angasamalirire anthu amene amamukonda ndipo anagulidwa ndi mwazi wamtengo wapatali wa Mwana wake!’ (Yesaya 40:26; Machitidwe 20:28) Mfundo zamphamvu zimenezo zingatithandize kuwafika ena pamtima.
Mafanizo Oyenerera
16. N’chifukwa chiyani mafanizo ali ofunika kwambiri pophunzitsa?
16 Mafanizo ogwira mtima ndi zokometsera zimene zingachititse ena kulakalaka zimene tikuphunzitsa. N’chifukwa chiyani mafanizo ali ofunika kwambiri pophunzitsa? Katswiri wina wophunzitsa anati: “Anthu amavutika kwambiri kuganiza popanda zithunzi.” Mafanizo amathandiza kuti tikhale ndi zithunzi zatanthauzo m’maganizo mwathu, kutithandiza kumvetsa bwino mfundo zatsopano. Yesu anali katswiri pogwiritsa ntchito mafanizo. (Marko 4:33, 34) Tiyeni tione mmene tingagwiritsire ntchito njira yophunzitsira imeneyi.
17. Kodi ndi zinthu zinayi ziti zimene zimapangitsa fanizo kukhala logwira mtima?
17 N’chiyani chimapangitsa fanizo kukhala logwira mtima? Choyamba, liyenera kugwirizana ndi omvera athuwo, likhale la zinthu zimene omverawo angathe kuzimva mosavuta. Tikukumbukira kuti mafanizo ambiri amene Yesu anagwiritsa ntchito anali okhudza zinthu zimene omvera ake ankazidziŵa. Chachiŵiri, fanizo liyenera kugwirizana ndi mfundo imene mukufuna kunena. Ngati sizikugwirizana, fanizolo lingangowasokoneza omvera athu. Chachitatu, fanizo siliyenera kukhala ndi mfundo zambirimbiri zosafunika. Kumbukirani kuti Yesu anafotokoza mfundo zimene zinali zofunika kwambiri koma anasiya zimene zinali zosafunika. Chachinayi, tikamapereka fanizo tiyenera kuonetsetsa kuti anthu asavutike kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo yake. Kupanda kutero, ena sangatolepo kanthu.
18. Kodi tingatani kuti tipeze mafanizo oyenerera?
Machitidwe 3:19, pamene pamati Ambuye ‘amafafaniza’ kapena kuti kufufuta machimo athu. Limeneli palokha ndi fanizo lomveka, koma kodi tingagwiritse ntchito chitsanzo chenicheni chiti kuti tisonyeze mfundoyo, mwina pogwiritsa ntchito chofufutira kapena chinkhupule? Tinganene kuti: ‘Yehova akakhululuka machimo athu, amawafufuta ngati kuti wagwiritsa ntchito chinkhupule (kapena chofufutira).’ Munthu sangavutike kumva mfundo ya fanizo losavuta limeneli.
18 Kodi tingatani kuti tipeze mafanizo oyenerera? Palibe chifukwa choganizira nkhani zazitali, za mfundo zambirimbiri. Mafanizo aafupi angakhale ogwira mtima kwambiri. Mungoganizira zitsanzo za mfundo imene mukambiraneyo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikukambirana nkhani ya kukhululuka kwa Mulungu, ndipo tikufuna kusonyeza mfundo imene ili pa19, 20. (a) Kodi tingapeze kuti mafanizo abwino? (b) Perekani zitsanzo za mafanizo ogwira mtima amene afalitsidwa m’mabuku athu. (Onaninso bokosi.)
19 Kodi mungapeze kuti mafanizo oyenerera, monga zitsanzo zosonyeza zochitika zenizeni pamoyo? Fufuzani zitsanzo pamoyo wanu kapena wa okhulupirira anzanu osiyanasiyana ndiponso zimene anakumana nazo. Mungapezenso mafanizo m’zinthu zina zambiri, monga zinthu zamoyo ndi zopanda moyo, ziwiya za panyumba, kapena nkhani imene yangochitika kumene imene anthu m’deralo akuidziŵa. Chofunika kwambiri kuti mupeze mafanizo abwino ndicho kukhala maso, “kuona” zochitika za tsiku ndi tsiku zimene timakumana nazo. (Machitidwe 17:22, 23) Buku lina lofotokoza za kulankhula pagulu linati: “Wokamba nkhani amene amaonetsetsa anthu ndi ntchito zosiyanasiyana zimene amagwira, amalankhula ndi anthu a mtundu uliwonse, amaonetsetsa zinthu ndiponso kufunsa mafunso mpaka atawamvetsetsa, amapeza zinthu zofanizira zambiri zimene zingamuthandize kwambiri zikafunika.”
20 Mungapezenso mafanizo ambiri ogwira mtima mu Nsanja ya Olonda, Galamukani! ndi m’mabuku ena a Mboni za Yehova. Mungaphunzire zambiri poona mmene zofalitsa zimenezi zimagwiritsira ntchito mafanizo. * Mwachitsanzo, onani fanizo limene lili m’buku la Chidziŵitso, mutu 17 pandime 11. Ilo lafanizira kusiyanasiyana kwa anthu mumpingo ndi kusiyanasiyana kwa magalimoto amene akuyenda mumsewu pamodzi ndi lanu. N’chifukwa chiyani fanizoli n’logwira mtima? Onani kuti n’la zinthu zochitika tsiku ndi tsiku, likugwirizana kwambiri ndi mfundo imene akunena, ndiponso n’zosavuta kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundoyo. Pophunzitsa tingagwiritse ntchito mafanizo omwe anafalitsidwa kale, mwina kuwasintha kuti agwirizane ndi zofunika za wophunzira Baibulo kapena kuti tiwagwiritse ntchito m’nkhani yathu.
21. Ndi phindu lotani limene timapeza chifukwa chokhala mphunzitsi wogwira mtima wa Mawu a Mulungu?
21 Phindu lokhala mphunzitsi wogwira mtima n’lalikulu. Tikamaphunzitsa, timapatsa kwa ena; timagwiritsa ntchito zinthu zathu kuwathandiza. Kupatsa kumeneko kumabweretsa chimwemwe, chifukwa Baibulo limati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kwa aphunzitsi a Mawu a Mulungu, madalitso amenewo ndiwo chisangalalo chimene timakhala nacho chifukwa chodziŵa kuti tikuuza ena choonadi cha Yehova cha phindu lenileni ndiponso lokhalitsa. Tingapezenso chimwemwe chifukwa chodziŵa kuti tikutsanzira Mphunzitsi Wamkulu, Yesu Kristu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 9 Onani chigawo chakuti “Mawu Oyambirira Ogwiritsira Ntchito mu Uminisitala Wakumunda,” masamba 9-15.—Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 20 Kuti mupeze zitsanzo, onani buku lakuti Watch Tower Publications Index 1986-2000, pamutu wakuti “Illustrations.”—Lofalitsidwa m’zinenero zambiri ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tingaphunzitse bwanji mosavuta kumva pochititsa phunziro la Baibulo panyumba ndiponso pokamba nkhani mumpingo?
• Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito bwino mafunso polalikira kunyumba ndi nyumba?
• Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zomveka posonyeza makhalidwe a Yehova ndi mmene amachitira zinthu?
• Kodi tingapeze kuti mafanizo oyenerera?
[Mafunso]
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
Kodi Mukuwakumbukira Mafanizo Aŵa?
Ali m’munsiŵa ndi mafanizo ogwira mtima ochepa chabe. Bwanji osayang’ana m’buku kapena magazini amene tasonyezawa kuti muone mmene mafanizowo anathandizira kutsindika mfundo imene nkhaniyo inafotokoza?
• Mofanana ndi oimba ng’oma pamodzi ndi ovomerezera pakamwa, kapena amuna aŵiri otsitsa makatoni olemera m’lole yaikulu, amene akufuna kukhala ndi banja labwino zingadalire kwambiri kupeza mnzawo wodalirika.—Nsanja ya Olonda, May 15, 2001, tsamba 16.
• Kufotokoza malingaliro anu kuli ngati kuponya mpira kuti wina auŵakhe. Mungauponye bwino kuti winayo auŵakhe mosavuta kapena mungauponye mwamphamvu kwambiri n’kupweteka nawo mnzanuyo.—Galamukani!, January 8, 2001, tsamba 10.
• Kuphunzira kusonyeza chikondi kuli ngati kuphunzira chinenero chatsopano.—Nsanja ya Olonda, February 15, 1999, masamba 18, 22-23.
• Ziwanda zimagwiritsira ntchito kukhulupirira mizimu monga momwe wosaka nyama amagwiritsira ntchito nyambo. Kukhulupirira mizimu kumakopa anthu.—Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, tsamba 111.
• Tingayerekezere mmene Yesu wawombolera ana a Adamu ndi munthu wachuma wowombola amene wapereka ngongole ya kampani (yomwe anachititsa manijala wina wosaona mtima) ndi kutsegulanso fakitaleyo, n’kupindulitsa antchito ambirimbiri a pakampaniyo.—Nsanja ya Olonda, February 15, 1991, tsamba 13.
• Monga mmene anthu okonda kujambula zithunzi angachitire zonse zimene angathe kuti akonzenso chithunzi chimene chawonongeka kwambiri, Yehova angatikhululukire zolakwa zathu, kuona mbali zimene tikuchita bwino, ndipo kenako kutipatsanso ungwiro umene Adamu anataya.—Nsanja ya Olonda, February 15, 1990, tsamba 22.
[Zithunzi patsamba 20]
Akristu oona ndi aphunzitsi a Mawu a Mulungu
[Chithunzi patsamba 21]
Akulu angagwiritse ntchito mafunso pothandiza wokhulupirira mnzawo kuti apeze chilimbikitso m’Mawu a Mulungu