“Anditsogolera ku Madzi Odikha”
“Anditsogolera ku Madzi Odikha”
NTHAŴI yotentha ku Palesitina, nkhosa zimafunika kumwa madzi tsiku lililonse. Choncho, ntchito yofunika kwambiri ya mbusa ndiyo kumwetsa madzi nkhosa zake. Nthaŵi zina abusa amamwetsa madzi nkhosa zawo ku chitsime, mwa kutungira madzi m’zomwera n’kuzipatsa kuti zimwe. (Genesis 29:1-3) Komabe, makamaka nthaŵi ya mvula, madera a m’mbali mwa mitsinje yaing’ono ndi yaikulu amakhala ‘abusa lamsipu.’—Salmo 23:2.
Mbusa wabwino amayenera kudziŵa kumene angapeze madzi ndi msipu wabwino wa nkhosa zake. Kuti nkhosa zake zikhalebe moyo, ayenera kuwadziŵa bwino malo otereŵa. Davide, amene anaŵeta nkhosa kwa zaka zambiri ku mapiri a ku Yudeya, anayerekezera malangizo auzimu amene Mulungu amapereka ndi mbusa amene amatsogolera nkhosa zake ku msipu wabwino ndi ku madzi opatsa moyo. Davide anati: “Anditsogolera ku madzi odikha.”—Salmo 23:1-3.
Patapita zaka zambiri, Yehova mwa mneneri wake Ezekieli anagwiritsa ntchito fanizo lofanana ndi limeneli. Analonjeza kuti adzasonkhanitsa anthu ake m’madera onse m’mene anabalalikira, monga momwe mbusa amasonkhanitsira nkhosa zake. Anawatsimikizira kuti: ‘Ndidzawatulutsa . . . kuloŵa nawo m’dziko lawo; ndipo ndidzawadyetsa pa mapiri a Israyeli, patimitsinje.’—Ezekieli 34:13.
Yehova Mulungu amakondanso kwambiri kupereka madzi auzimu. Buku la Chivumbulutso limafotokoza za “mtsinje wa madzi a moyo” wochokera ku mpando wa Mulungu. (Chivumbulutso 22:1) Anthu onse akuitanidwa kudzamwa madzi ku mtsinje umenewu. “Iye wofuna, a[nga]tenge madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17.
Madzi amoyo ophiphiritsira ameneŵa akuimira dongosolo limene Mulungu wakonza la moyo wosatha. Aliyense angayambe kumwa madzi ameneŵa mwa ‘kudziŵa Mulungu woona yekha ndi Yesu Kristu amene anam’tuma.’—Yohane 17:3.