Pitirizani Kuchita Zimene Mwaphunzira
Pitirizani Kuchita Zimene Mwaphunzira
“Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.”—AFILIPI 4:9.
1, 2. Kodi Baibulo lili ndi mphamvu pa moyo wa anthu ambiri amene amati ndi opembedza? Fotokozani.
“MPHAMVU ya Chipembedzo Ikukula Koma Makhalidwe Abwino Akuchepa Mphamvu.” Mutu wa nkhani umenewu m’nyuzipepala ya Emerging Trends unafotokoza mwachidule zotsatira za kafukufuku amene anachitika ku United States. Zikuoneka kuti, m’dziko limenelo anthu opita kutchalitchi awonjezeka ndipo amati chipembedzo n’chofunika kwambiri pa moyo wawo. Komabe, lipotilo linati: “Ngakhale kuti chiŵerengerochi n’chokwera kwambiri, anthu a ku America ambiri amakayikira phindu la chipembedzo pa moyo wa munthu aliyense payekha ndiponso kwa anthu onse.”
2 Zimenezi sikuti zili choncho m’dziko limodzi lokha. Padziko lonse lapansi, anthu ambiri amene amati amavomereza Baibulo ndiponso amapembedza salola kuti Malemba akhale ndi mphamvu kwenikweni pa moyo wawo. (2 Timoteo 3:5) Mkulu wa gulu lina lofufuza ananena kuti: “Timalilemekezabe kwambiri Baibulo, koma zoti n’kupatula nthaŵi kuliŵerenga, kuliphunzira, ndi kutsatira zimene taphunzirazo n’zachikale.”
3. (a) Kodi Baibulo lili ndi mphamvu yanji kwa Akristu enieni? (b) Kodi otsatira a Yesu amatsatira bwanji malangizo a Paulo amene ali pa Afilipi 4:9?
Akolose 3:5-10) Kwa otsatira Yesu, Baibulo silili buku lakutha ntchito limene limangotuŵa ndi fumbi pa shelefu. Mosiyana ndi zimenezo, mtumwi Paulo anauza Akristu a ku Filipi kuti: ‘Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.’ (Afilipi 4:9) Akristu amachita zambiri osati kungovomereza chabe choonadi cha Mawu a Mulungu. Amachita zimene aphunzira, amatsatira nthaŵi zonse malangizo a Baibulo kaya ndi pabanja, kuntchito, mumpingo, ndiponso m’mbali zina zonse za moyo wawo.
3 Koma zimenezi sizili choncho kwa Akristu enieni. Kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu kwasintha maganizo ndiponso makhalidwe awo. Ndipo anthu ena amaona mosavuta umunthu wawo watsopano umene amasonyeza. (4. N’chifukwa chiyani n’kovuta kutsatira malamulo a Mulungu?
4 N’kovuta kutsatira malamulo ndi mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Tikukhala m’dziko limene likulamulidwa ndi Satana Mdyerekezi, amene Baibulo limamutcha “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Motero, n’kofunika kwambiri kukhala tcheru kuti tipeŵe chilichonse chimene chingatilepheretse kukhala wokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Kodi tingatani kuti tikhale okhulupirika?
Tsatirani “Chitsanzo cha Mawu a Moyo”
5. Kodi mawu a Yesu akuti, ‘anditsate Ine tsiku ndi tsiku’ akusonyeza chiyani?
5 Mbali ina yochita zimene taphunzira ndiyo kutsatirabe mokhulupirika kulambira koona ngakhale osakhulupirira akutitsutsa. Kupirira kumafuna kuvala zilimbe. Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.” (Luka 9:23) Yesu sananene kuti timutsatire kwa mlungu umodzi wokha, mwezi umodzi wokha, kapena chaka chimodzi chokha ayi. M’malo mwake anati tiyenera kuchita zimenezo “tsiku ndi tsiku.” Mawu akeŵa akusonyeza kuti kukhala kwathu ophunzira si kwa nthaŵi inayake chabe pamoyo wathu kapena kudzipereka kwa nthaŵi yochepa chabe. Kukhulupirikabe pa kulambira koona kumafuna kuti tipirizebe kuyenda m’njira imene tasankha, zivute zitani. Kodi tingatani kuti tichite zimenezo?
6. Kodi chitsanzo cha mawu a moyo chimene Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anaphunzira kwa Paulo chinali chiyani?
6 Paulo analangiza wantchito mnzake Timoteo kuti: “Gwira chitsanzo cha mawu a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 1:13) Kodi Paulo anatanthauza chiyani? Liwu la Chigiriki limene pano analitembenuza kuti “chitsanzo” kwenikweni limatanthauza chithunzi cha chinthu chimene m’misiri akufuna kupanga. Ngakhale kuti chithunzicho sichingafotokoze zonse, chimasonyeza mmene chinthucho chikhalire, moti munthu wozindikira amene akuona chithunzicho angadziŵe mmene chinthucho chidzaonekera. N’chimodzimodzinso ndi chitsanzo cha choonadi chimene Paulo anaphunzitsa Timoteo ndi ena, sichikanayankha mwachindunji mafunso onse amene akanakhalapo. Komabe, zimene anaphunzitsazo zinali ndi malangizo okwanira, tingati zinali chithunzi, kuti anthu oona mtima adziŵe zimene Yehova amafuna kwa iwo. Koma kuti asangalatse Mulungu, iwo anafunika kutsatirabe chitsanzo cha choonadi chimenecho mwa kuchita zimene anaphunzirazo.
7. Kodi Akristu angatani kuti apitirizebe kutsatira chitsanzo cha mawu a moyo?
7 M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, anthu monga Humenayo, Alesandro, ndi Fileto anali kulimbikitsa zikhulupiriro zosagwirizana ndi “chitsanzo cha mawu a moyo.” (1 Timoteo 1:18-20; 2 Timoteo 2:16, 17) Kodi Akristu oyambirirawo akanapeŵa bwanji kusocheretsedwa ndi ampatuko? Akanapeŵa mwa kuphunzira mosamala malemba ouziridwa ndi kuwagwiritsa ntchito pa moyo wawo. Amene anatsatira chitsanzo cha Paulo ndi cha anthu ena okhulupirika anazindikira ndi kupeŵa chilichonse chimene sichinagwirizane ndi chitsanzo cha choonadi chimene anawaphunzitsa. (Afilipi 3:17; ) M’malo ‘moyaluka pa mafunso ndi makani a mawu,’ iwo anapitabe patsogolo m’njira yawo yolondola yodzipereka kwa Mulungu. ( Ahebri 5:141 Timoteo 6:3-6) Timachitanso chimodzimodzi tikamatsatirabe choonadi chimene taphunzira. Zimalimbikitsa kwambiri chikhulupiriro kuona kuti anthu miyandamiyanda amene akutumikira Yehova padziko lonse akutsatirabe molimbika chitsanzo cha choonadi cha Baibulo chimene aphunzira.—1 Atesalonika 1:2-5.
Peŵani “Nthano Zachabe”
8. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito chiyani pofuna kuwononga chikhulupiriro chathu masiku ano? (b) Kodi ndi langizo la Paulo lotani limene lili pa 2 Timoteo 4:3, 4?
8 Satana amayesa kuswa kukhulupirika kwathu mwa kutichititsa kukayikira zimene taphunzira. Masiku ano monganso mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, ampatuko ndi ena amafuna kuwononga chikhulupiriro cha anthu osalakwa. (Agalatiya 2:4; 5:7, 8) Nthaŵi zina amagwiritsa ntchito manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV pofalitsa nkhani zolakwika kapena bodza lam’kunkhuniza lonena za mmene anthu a Yehova amachitira zinthu ndiponso zolinga zawo. Paulo anachenjeza kuti ena adzapatutsidwa pa choonadi. Iye analemba kuti: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu [“malinga ndi zilakolako zawo,” NW] adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.”—2 Timoteo 4:3, 4.
9. Kodi Paulo ayenera kuti anali kunena za chiyani pamene anatchula “nthano zachabe”?
9 M’malo motsatira chitsanzo cha mawu a moyo, ena anakopeka ndi “nthano zachabe.” Kodi nthano zachabe zimenezo zinali ziti? Mwina Paulo anali kunena za nthano zabodza, monga zimene zimapezeka m’buku losavomerezeka la Tobit. * Zinanso mwa nthano zachabezo ziyenera kuti zinali mphekesera zokopa ndiponso zongoganizira. Ndiyenonso, ena “malinga ndi zilakolako zawo,” ayenera kuti ananyengedwa ndi nzeru za anthu amene anali kulimbikitsa kuona miyezo ya Mulungu motayirira kapena amene anali kulimbana ndi anthu omwe anali kutsogolera mumpingo. (3 Yohane 9, 10; Yuda 4) Kaya zokhumudwitsa zake zinali zotani, zikuoneka kuti ena anakonda bodza m’malo mwa choonadi cha Mawu a Mulungu. Posakhalitsa anasiya kuchita zimene anaphunzira ndipo zimenezi zinawavulaza mwauzimu.—2 Petro 3:15, 16.
10. Kodi zina za nthano zachabe masiku ano n’zotani, ndipo Yohane anasonyeza bwanji kufunika kosamala?
10 Tingapeŵe kupatutsidwa ndi nthano zachabe masiku ano ngati tipenda ndi kusankha zimene timamvetsera kapena kuŵerenga. Mwachitsanzo, nthaŵi zambiri manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV amalimbikitsa chiwerewere. 1 Yohane 4:1) Motero tifunika kusamala.
Anthu ambiri amalimbikitsa chikhulupiriro chakuti n’zosatheka kum’dziŵa Mlengi kapena kukana kumene kuti kuli Mulungu. Anthu a maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo amatsutsa zimene Baibulo limanena zoti n’louziridwa ndi Mulungu. Ndipo ampatuko a masiku ano akupitirizabe kufesa mbewu za chikayikiro kuti awononge chikhulupiriro cha Akristu. Mtumwi Yohane ponena za ngozi ngati imeneyi imene aneneri onyenga a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anabweretsa, anachenjeza kuti: “Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m’dziko lapansi.” (11. Kodi ndi njira ina iti imene tingadziyesere ndi kuona ngati tili m’chikhulupiriro?
11 Pankhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro.” (2 Akorinto 13:5) Mtumwiyo anatilimbikitsa kuti tizidziyesa tokha kuti tione ngati tikutsatira zikhulupiriro zonse zachikristu. Ngati timakonda kumvetsera anthu osakhutira, tifunika kudzipenda mwapemphero. (Salmo 139:23, 24) Kodi timakonda kupezera zolakwa anthu a Yehova? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani timatero? Kodi zimene wina anachita kapena kulankhula zatikhumudwitsa? Ngati ndi choncho, kodi tikuona zinthu moyenera? Mavuto amene timakumana nawo m’dongosolo la zinthu lino ndi osakhalitsa. (2 Akorinto 4:17) Ngakhale titakumana ndi mayesero ena ake mumpingo, n’kusiiranji kutumikira Mulungu? Ngati takhumudwa pa nkhani inayake, kodi sizingakhale bwino kuchita zimene tingathe kuti tithetse nkhaniyo ndiyeno n’kuisiya m’manja mwa Yehova?—Salmo 4:4; Miyambo 3:5, 6; Aefeso 4:26.
12. Kodi Abereya anatipatsa chitsanzo chabwino chiti?
12 M’malo modzudzula, tiyeni tizionabe bwino mwauzimu zimene timaphunzira pa phunziro laumwini ndi pa misonkhano ya mpingo. (1 Akorinto 2:14, 15) Ndipo m’malo mokayikira Mawu a Mulungu, kungakhale kwanzeru zedi kukhala ndi mtima wa Abereya a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino amene anapenda Malemba mosamala. (Machitidwe 17:10, 11) Ndiyetu tiyeni tichite zimene timaphunzira, tipeŵe nthano zachabe ndipo tigwiritsitse choonadi.
13. Kodi tingakhale tikufalitsa nkhani zabodza mosadziŵa ngati tichita chiyani?
13 Palinso nthano ina yachabe imene tifunika kupeŵa. Nkhani zambiri zokopa zimafala, nthaŵi zambiri kudzera m’mauthenga a pa kompyuta. Tifunika kusamala ndi nkhani zoterozo, makamaka ngati sitidziŵa kumene zachokera. Ngakhale kuti zochitikazo kapena nkhaniyo watumiza ndi Mkristu wa mbiri yabwino, iye akhoza kusadziŵa nkhani yonse bwinobwino. N’chifukwa chake n’kofunika kwambiri kusamala pobwereza kapena kutumiza kwa ena nkhani yopanda umboni. Mosakayika, sitingafune kubwereza “nthano zotsutsana ndi Mulungu,” kapena “nkhani zachabe zimene ziipsa chimene 1 Timoteo 4:7 New International Version; NW) Popeza tiyeneranso kulankhula zoona kwa wina ndi mnzake, ndi nzeru kupeŵa chilichonse chimene chingatipangitse kufalitsa nkhani zabodza mosadziŵa.—Aefeso 4:25.
chili choyera.” (Phindu Lotsatira Choonadi
14. Kodi timapindula chiyani tikamachita zimene taphunzira m’Mawu a Mulungu?
14 Kuchita zimene timaphunzira paphunziro la Baibulo laumwini ndi pamisokhano yachikristu kudzatipindulitsa kwambiri. Mwachitsanzo, tingaone kuti kucheza kwathu ndi okhulupirira anzathu kudzakhala kwabwino zedi. (Agalatiya 6:10) Maganizo athunso adzakhala abwinopo tikamatsatira mfundo za m’Baibulo. (Salmo 19:8) Ndiponso, mwa kuchita zimene timaphunzira, ‘timakometsera chiphunzitso cha Mulungu’ ndipo tingakopere ena ku kulambira koona.—Tito 2:6-10.
15. (a) Kodi mtsikana wina analimba mtima bwanji kulalikira kusukulu? (b) Mwaphunzirapo chiyani pankhani ya mtsikana ameneyu?
15 M’gulu la Mboni za Yehova muli achinyamata ambiri amene amachita zimene aphunzira paphunziro la Baibulo laumwini ndi m’zofalitsa zachikristu pamodzi ndi kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano ya mpingo. Khalidwe lawo labwino limakhala umboni wamphamvu kwa aphunzitsi ndi ophunzira anzawo. (1 Petro 2:12) Tamvani za Leslie, mtsikana wa zaka 13 wa ku United States. Iye anavomereza kuti zimam’vuta kuwauza ophunzira anzake chikhulupiriro chake, koma zimenezo zinasintha tsiku lina. “Ophunzira m’kalasilo ankafotokoza mmene anthu amachitira pofuna kukugulitsa zinthu. Mtsikana wina anakweza dzanja ndi kutchula kuti mwachitsanzo monga momwe zimachitira Mboni za Yehova.” Monga Mboni kodi Leslie anatani? Iye anati: “Ndinakhalira kumbuyo chikhulupiriro changa zimene mosakayika zinadabwitsa aliyense popeza kusukuluko sindikonda kulankhulalankhula.” N’chiyani chinachitika chifukwa cha kulimba mtima kwa Leslie? Iye anati: “Ndinamugaŵira wophunzirayo bulosha ndi thirakiti, popeza anali ndi mafunso ena.” Yehova amakondwera kwambiri achinyamata omwe amachita zimene amaphunzira akamalimba mtima kulalikira kusukulu.—Miyambo 27:11; Ahebri 6:10.
16. Kodi Sukulu ya Utumiki wa Teokalase yapindulitsa bwanji mtsikana wina wa Mboni?
16 Chitsanzo china n’cha Elizabeti. Kuyambira ali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri ndiponso zaka zonse zimene anali ku pulayimale, mtsikana ameneyu anali kuwaitanira aphunzitsi ake ku Nyumba ya Ufumu akakhala ndi nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Teokalase. Aphunzitsiwo akakhala kuti sanapite ku Nyumba ya Ufumuyo, Elizabeti anali kutsalira kusukulu akaŵeruka kuti awakambire aphunzitsi ake nkhaniyo. M’chaka chake chomaliza ku sekondale, Elizabeti analemba lipoti la masamba khumi lofotokoza phindu la Sukulu ya Utumiki wa Teokalase ndipo anafotokoza lipoti lakelo kwa aphunzitsi anayi. Anamupemphanso kupereka chitsanzo cha nkhani ya m’Sukulu ya Utumiki wa Teokalase, ndipo anasankha mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuipa?” Elizabeti wapindula ndi maphunziro amene Mboni za Yehova zimaphunzitsa m’Sukulu ya Utumiki wa Teokalase. Iye ndi mmodzi chabe mwa achinyamata achikristu ambirimbiri amene amatamanda Yehova mwa kuchita zimene aphunzira m’Mawu ake.
17, 18. (a) Kodi Baibulo limapereka malangizo otani pankhani ya kuona mtima? (b) Kodi kuona mtima kwa Mboni ya Yehova ina kunakhudza bwanji mwamuna wina?
17 Baibulo limalangiza Akristu kukhala oona Ahebri 13:18) Chinyengo chingawononge ubale wathu ndi anthu ena, ndipo koposa pamenepa, chingawononge ubale wathu ndi Yehova. (Miyambo 12:22) Kukhulupirika kwathu kumasonyeza kuti timachita zimene timaphunzira, ndipo kwachititsa anthu ochuluka kulemekeza kwambiri Mboni za Yehova.
mtima m’zinthu zonse. (18 Taonani zimene zinachitikira msilikali wina dzina lake Phillip. Iye anataya cheke chosainasaina koma chosalemba ndalama zake kuti n’zingati ndipo sanadziŵe kuti wachitaya mpaka pamene anam’bwezera. Wa Mboni za Yehova wina ndi amene anatola chekecho, ndipo pom’bwezera mwiniyo analemba kakalata n’kutumizira limodzi kamene analembapo kuti zikhulupiriro zake zachipembedzo n’zimene zinamulimbikitsa kum’bwezera. Phillip anadabwa kwambiri. Iye anati: “Akanatha kundibera ndalama zanga zonse zokwana $9,000!” Iye anakhumudwa nthaŵi inayake pamene chipeŵa chake chinabedwa m’tchalitchi. Mwachionekere, amene anam’bera anali wodziŵana naye, koma munthu wosam’dziŵa anabweza cheke cha ndalama zambirimbiri! Inde, Akristu oona mtima amalemekeza Yehova Mulungu.
Pitirizani Kuchita Zimene Mwaphunzira
19, 20. Kodi tidzapindula bwanji ngati titsatira zimene tikuphunzira m’Malemba?
19 Amene amachita zimene aphunzira m’Mawu a Mulungu amapindula zedi. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:25) Inde, ngati titsatira zimene timaphunzira m’Malemba, tidzapeza chimwemwe chenicheni ndipo tidzatha kulimbana bwino ndi mavuto a pamoyo wathu. Ndipo kuposa zonsezi, Yehova adzatidalitsa ndipo tidzapeza moyo wosatha.—Miyambo 10:22; 1 Timoteo 6:6.
20 Ndiyetu, pitirizani kuchita khama kuphunzira Mawu a Mulungu. Sonkhanani ndi olambira Yehova nthaŵi zonse, ndipo ikani maganizo pa nkhani imene ikukambidwa pa msonkhano wachikristu. Tsatirani zimene mukuphunzira, pitirizani kuzichita, ndipo “Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.”—Afilipi 4:9.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Buku la Tobit, limene liyenera kuti analilemba m’zaka za m’ma 200 B.C.E., muli nkhani yodzala ndi kukhulupirira malodza ya Myuda wina dzina lake Tobias. Iye anam’nena kuti ankatha kupeza mphamvu zochiritsa ndi kutulutsa ziŵanda pogwiritsa ntchito mtima, ndulu, ndi chiwindi cha chinsomba chachikulu kwambiri.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi “chitsanzo cha mawu a moyo” n’chiyani, ndipo tingatani kuti tipitirize kuchitsatira?
• Kodi ndi “nthano zachabe” ziti zimene tifunika kupeŵa?
• Kodi amene amachita zimene amaphunzira m’Mawu a Mulungu amapindula chiyani?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi Akristu oyambirira akanapeŵa bwanji kusocheretsedwa ndi ampatuko?
[Zithunzi patsamba 18]
Mbewu za chikayikiro zingafesedwe kudzera m’manyuzipepala, ma TV, pa intaneti, ndiponso ampatuko a masiku ano
[Chithunzi patsamba 19]
Sikwanzeru kufalitsa nkhani yopanda umboni
[Zithunzi patsamba 20]
Mboni za Yehova zimatsatira zimene zimaŵerenga m’Mawu a Mulungu kaya kuntchito, kusukulu, ndi kwina kulikonse