Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Samaliranidi’

‘Samaliranidi’

‘Samaliranidi’

“Tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.”​—AHEBRI 2:1.

1. Sonyezani mmene kudodometsedwa kungapangitsire ngozi.

NGOZI za galimoto zimapha anthu pafupifupi 37,000 chaka chilichonse ku United States kokha. Akatswiri amati ambiri mwa anthu ameneŵa sakanafa ngati madalaivala akanasamala kwambiri pamsewu. Madalaivala ena amadodometsedwa ndi zizindikiro ndiponso zikwangwani kapena kugwiritsa ntchito kwawo telefoni ya m’manja. Palinso ena amene amadya akuyendetsa. M’zochitika zonsezi, kudodometsedwa kungapangitse ngozi.

2, 3. Kodi Paulo anawalangiza chiyani Akristu achihebri, ndipo n’chifukwa chiyani malangizo ake anali oyenerera?

2 Zaka pafupifupi 2,000 anthu asanayambe kupanga magalimoto, mtumwi Paulo anatchula chododometsa china chimene chinkavulaza kwambiri Akristu achihebri. Paulo anatsindika kuti Yesu Kristu woukitsidwa anapatsidwa udindo woposa wa angelo onse, chifukwa anamukhazika pa dzanja lamanja la Mulungu. Ndiyeno mtumwiyo anati: “Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.”​—Ahebri 2:1.

3 N’chifukwa chiyani Akristu achihebri anafunika ‘kusamaliradi zimene anazimva’ zokhudza Yesu? Chifukwa chakuti panali patapita zaka 30 kuchokera pamene Yesu anachoka pa dziko lapansi. Popeza Mbuye wawo panalibe, Akristu ena achihebri anayamba kutengeka ndi kusiyana nacho chikhulupiriro choona. Anali kudodometsedwa ndi Chiyuda, chipembedzo chawo chakale.

Anafunika Kusamalira Kwambiri

4. Kodi n’chiyani chingakhale chifukwa chimene Akristu ena achihebri anakopeka kuti abwerere ku Chiyuda?

4 N’chifukwa chiyani Mkristu akanakopeka kuti abwerere ku Chiyuda? Chifukwa chakuti m’nthaŵi ya Chilamulo, polambira anali kugwiritsa ntchito zinthu zooneka. Anthu ankatha kuona ansembe ndi kumva fungo la nsembe yopsereza. Koma m’mbali zina, chikristu chinali chosiyana ndi zimenezo. Akristu anali ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu Kristu, koma anali asanamuone padziko lapansi kwa zaka 30. (Ahebri 4:14) Anali ndi kachisi koma malo ake opatulika anali kumwamba. (Ahebri 9:24) Mosiyana ndi mdulidwe weniweni wa m’Chilamulo, mdulidwe wa Akristu unali “wa mtima, mumzimu.” (Aroma 2:29) Choncho, kwa Akristu achihebri, Chikristu chiyenera kuti chinayamba kuoneka ngati chosamvetsetseka.

5. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti kulambira kumene Yesu anakhazikitsa kunaposa kulambira kwa m’nthaŵi ya Chilamulo?

5 Akristu achihebri anafunika kudziŵa chinthu chofunika kwambiri pa kulambira kumene Kristu anakhazikitsa. Kulambira kumeneku kunafuna kwambiri chikhulupiriro osati kuona, komabe kunaposa Chilamulo chimene chinaperekedwa kudzera mwa mneneri Mose. Paulo analemba kuti: “Ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala a ng’ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?” (Ahebri 9:13, 14) Inde, kukhululukidwa chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu kumaposa m’njira zambiri kukhululukidwa kumene kunkachitika chifukwa cha nsembe zoperekedwa m’nthaŵi ya Chilamulo.​—Ahebri 7:26-28.

6, 7. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Akristu achihebri anafunikira kwambiri ‘kusamaliradi zimene anamva’? (b) Kodi panthaŵi imene Paulo analemba kalata yake kwa Ahebri, panatsala nthaŵi yaitali bwanji kuti Yerusalemu awonongedwe? (Onani mawu am’munsi.)

6 Panalinso chifukwa china chimene Akristu achihebri anafunikira kusamaliradi zimene anamva za Yesu. Iye analosera kuti Yerusalemu adzawonongedwa. Yesu anati: “Masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang’aniridwe ako.”​—Luka 19:43, 44.

7 Kodi zimenezi zinali kudzachitika liti? Yesu sananene tsiku ndi nthaŵi yake. M’malo mwake, anapereka malangizo aŵa: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) M’kati mwa zaka 30 Yesu atanena mawu ameneŵa, Akristu ena ku Yerusalemu analeka kukhala tcheru ndipo anapatutsidwa. Tinganene kuti anasiya kuyang’ana mumsewu. Ngati sakanasintha maganizo awo, akanasimba tsoka. Kuwonongedwa kwa Yerusalemu kunali pafupi, kaya ankaganiza choncho kapena ayi. * Langizo la Paulo liyenera kuti linawadzutsa Akristu ogona mwauzimu ku Yerusalemu.

‘Kusamaliradi’ Masiku Ano

8. N’chifukwa chiyani tifunika ‘kusamaliradi’ choonadi cha Mawu a Mulungu?

8 Mofanana ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, tifunika ‘kusamaliradi’ choonadi cha Mawu a Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ifenso tikuyembekezera chiwonongeko chimene chayandikira, osati cha dziko limodzi lokha, koma cha dziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 11:18; 16:14, 16) N’zoona kuti sitikudziŵa tsiku lenileni ndi nthaŵi yake pamene Yehova adzachita zimenezi. (Mateyu 24:36) Komabe, tikuona tokha maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa zimene zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5) Motero, tiyenera kupeŵa chilichonse chimene chingatidodometse. Tifunika kumvera Mawu a Mulungu ndi kukhalabe tcheru. Ngati tichita zimenezi, ‘tidzalimbika kupulumuka zonse zimene zidzachitika.’​—Luka 21:36.

9, 10. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikusamalira zinthu zauzimu? (b) N’chifukwa chiyani mawu a Mulungu ali ngati ‘nyali kumapazi athu’ ndi ‘kuunika kwa panjira pathu’?

9 Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tikusamaliradi’ zinthu zauzimu m’nthaŵi yofunika kwambiri ino? Njira imodzi ndiyo kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano yachikristu ya mpingo ndiponso pa misonkhano yaikulu. Tifunikanso kuphunzira mwakhama Baibulo kuti tiyandikire kwambiri kwa Mwini Baibulolo, Yehova. (Yakobo 4:8) Ngati tidziŵa za Yehova mwa phunziro laumwini ndi misonkhano, tidzafanana ndi wamasalmo amene anauza Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”​—Salmo 119:105.

10 Baibulo limakhala ‘kuunika kwa panjira pathu’ pamene litiuza zolinga za Mulungu za m’tsogolo. Ndiponso ndi ‘nyali ya kumapazi athu.’ M’mawu ena, lingatithandize kuona zimene tingachite tikakumana ndi vuto lalikulu pamoyo. N’chifukwa chake n’kofunika kwambiri kuti ‘tisamaliredi’ posonkhana pamodzi ndi okhulupirira anzathu kuti timve malangizo ndiponso poŵerenga patokha Mawu a Mulungu. Zimene timaphunzira zidzatithandiza kusankha mwanzeru zochita ndiponso zopindulitsa zimene zimasangalatsa Yehova ndi kukondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11; Yesaya 48:17) Kodi tingawonjezere bwanji nthaŵi imene timatha kuika maganizo pa misonkhano ndiponso pochita phunziro laumwini kuti tipindule kwambiri ndi zinthu zauzimu zimene Mulungu amatigaŵira?

Kuwongolera Kuika Kwathu Maganizo pa Misonkhano

11. N’chifukwa chiyani kuika maganizo pa misonkhano yachikristu n’kovuta nthaŵi zina?

11 Nthaŵi zina kuika maganizo pa misonkhano yachikristu n’kovuta. Maganizo angadodometsedwe, kaya mwana akamalira kapena munthu wochedwa akamafunafuna pokhala. Kapenanso tingakhale titatopa chifukwa cha ntchito imene tagwira tsiku lonse. Amene akukamba nkhani pa pulatifomu mwina sangakhale wokamba nkhani wosangalatsa kwambiri, ndipo posakhalitsa tingayambe kuganiza zina, mwinanso kuodzera kumene. Popeza nkhani zimene zimakambidwa n’zofunika kwambiri, tiyenera kuyesetsa kuwongolera mphamvu zathu zoika maganizo pa misonkhano yampingo. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

12. N’chiyani chingatithandize kuti tisavutike kuika maganizo athu pa misonkhano?

12 Nthaŵi zambiri sizivuta kuika maganizo athu pa misonkhano ngati takonzekera bwino. Motero, bwanji osapatula nthaŵi yokonzekera nkhani imene mukaphunzire? Zimangotenga mphindi zochepa chabe tsiku lililonse kuŵerenga ndi kusinkhasinkha kachigawo ka machaputala a kuŵerenga Baibulo kwa mlunguwo. Mwa kulinganiza zinthu, tingapezenso nthaŵi yokonzekera Phunziro la Buku la Mpingo ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kaya tisankha ndandanda yotani, choonadi n’chakuti: Kukonzekera kudzatithandiza kuika maganizo pa nkhani imene ikukambidwa pa misonkhano ya mpingo.

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiikebe maganizo athu pa nkhani imene ikukambidwa pa misonkhano?

13 Kuwonjezera pa kukonzekera bwino, ena aona kuti amaika kwambiri maganizo awo pa misonkhano akakhala kutsogolo m’Nyumba ya Ufumu. Njira zinanso zimene zingathandize kuti tisamaganize zina ndizo kuyang’ana wokamba nkhaniyo, kutsegula Baibulo n’kumatsagana naye pamene akuŵerenga lemba, ndiponso kulemba notsi. Komabe, kukonzekeretsa mtima n’kofunika kwambiri kuposa njira ina iliyonse yothandiza kuti tiike maganizo pa zimene tikuphunzira. Tifunika kudziŵa cholinga cha kusonkhana kwathu pamodzi. Cholinga chachikulu chimene timasonkhanira ndi okhulupirira anzathu ndicho kulambira Yehova. (Salmo 26:12; Luka 2:36, 37) Misonkhano ndi njira yofunika kwambiri imene amatidyetsera mwauzimu. (Mateyu 24:45-47) Ndiponso, misonkhano imatipatsa mwayi ‘wofulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.’​—Ahebri 10:24, 25.

14. Kodi n’chiyani kwenikweni chimene chimachititsa misonkhano kukhala yabwino?

14 Enafe timakonda kusiyanitsa kuti msonkhano unali wabwino kapena ayi malinga ndi luso lophunzitsa la amene anakamba nkhani. Okamba nkhaniwo akakhala aluso kwambiri, tinganene kuti unali msonkhano wabwino. Koma akaoneka ngati sanaphunzitse mwaluso, tinganene kuti sunali msonkhano wabwino. N’zoona kuti amene ali pa pulogalamu ayenera kuyesetsa kuphunzitsa mwaluso ndipo makamaka kuwafika anthu pamtima. (1 Timoteo 4:16) Komabe, ife amene tikumvetsera sitiyenera kuweruza mosayenera. Ngakhale kuti luso lophunzitsa la okamba nkhaniwo n’lofunika, si chokhachi chimene chimachititsa msonkhano kukhala wabwino. Kodi simukuvomereza kuti chimene tifunika kusamalitsa kwambiri ndi mmene ifeyo tikutcherera khutu osati mmene wokamba nkhani akukambira nkhani yake? Tikakhala pa misonkhano ndi kuika maganizo athu pa zimene zikukambidwa, timalambira Mulungu mogwirizana ndi chifuniro chake. Zimenezi n’zimene zimachititsa misonkhano kukhala yabwino. Ngati tikufunitsitsa kum’dziŵa Mulungu, tidzapindula ndi misonkhano mosaganizira luso la wokamba nkhani. (Miyambo 2:1-5) Ndiyetu, tiyeni tionetsetse kuti ‘tikusamaliradi’ kumvetsera pa misonkhano.

Pindulani Kwambiri ndi Phunziro Laumwini

15. Kodi kuphunzira ndi kusinkhasinkha kungatipindulitse bwanji?

15 Timapindula kwambiri ngati ‘tisamaliradi’ kuika maganizo pa phunziro laumwini ndiponso posinkhasinkha. Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha Baibulo ndi zofalitsa zachikristu zidzatithandiza kukhala ndi mwayi wamtengo wapatali wokhomereza choonadi cha Mawu a Mulungu mumtima mwathu. Zimenezi zidzakhudza kwambiri zimene timaganiza ndi kuchita. Inde, zidzatithandiza kukondwera pochita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 1:2; 40:8) Motero tifunika kukulitsa mphamvu zathu zoikabe maganizo pophunzira kuti tipindule ndi phunzirolo. N’kwapafupi zedi kudodometsedwa. Zododometsa zazing’ono monga kulira kwa telefoni kapena phokoso zingatisokoneze. Kapena nthaŵi imene tingathe kuika maganizo pa zimene tikuphunzira ingakhale yochepa. Tingakhale pansi tikufunitsitsadi kuti tidye mwauzimu, koma posakhalitsa tingayambe kumaganizira zinthu zina. Kodi tingatani kuti ‘tisamaliredi’ pochita phunziro laumwini la Mawu a Mulungu?

16. (a) N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kupeza nthaŵi yochita phunziro laumwini? (b) Kodi mwapeza bwanji nthaŵi yophunzira Mawu a Mulungu?

16 Kukonza ndandanda ndi kusankha malo abwino oti muziphunzirirapo zimathandiza kwambiri. Ambirife n’kovuta kupeza nthaŵi ndi malo oduka mphepo. Tingaone ngati kuti zochitika zotangwanitsa za tsiku ndi tsiku zikutikokolola ngati kanthambi ka mtengo kamene katengedwa ndi madzi a mumtsinje othamanga kwambiri. Inde, tifunika kulimbana ndi zinthu zotangwanitsa zimenezi ndi kupeza nthaŵi yoti tiziphunzira mofatsa. Tisadikire kuti mpata wophunzira ubwere wokha. Mtumwi Paulo ananena kuti tiyenera “kuwombola nthaŵi.” Chotero, tikufunika kulamulira zinthu mwa kupeza nthaŵi yophunzira. (Aefeso 5:15, 16, NW) Ena amapatula nthaŵi yochepa m’maŵa pamene sipangakhale zododometsa zambiri. Ena amaona kuti angaphunzire bwino madzulo. Mfundo ndi yakuti sitiyenera kunyalanyaza kufunika kodziŵa zolondola za Mulungu ndi Mwana wake. (Yohane 17:3) Motero, tiyeni tikonze ndandanda yochita phunziro laumwini ndiyeno tizitsatira kwambiri ndandandayo.

17. Kodi kusinkhasinkha n’kutani, nanga tingapindule nako bwanji?

17 Kusinkhasinkha, komwe kumatanthauza kuganizira mozama zimene taphunzira poŵerenga, n’kofunika kwambiri. Kumatithandiza kuchotsa maganizo a Mulungu pa masamba amene asindikizidwa ndi kuwaika mumtima mwathu. Kusinkhasinkha kumatithandiza kuona mmene tingagwiritsire ntchito malangizo a m’Baibulo kuti tikhale “akuchita mawu, osati akumva okha.” (Yakobo 1:22-25) Ndiponso, kusinkhasinkha kumatithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova, chifukwa kumatithandiza kuganizira makhalidwe ake ndi mmene awasonyezera m’nkhani imene tikuphunzira pa phunzirolo.

18. N’zinthu ziti zimene zimafunika kuti kusinkhasinkha kwathu kukhale kwaphindu?

18 Kuti tipindule kwambiri pophunzira ndi posinkhasinkha, tiyenera kupeŵa zina zilizonse zimene zingadodometse maganizo athu. Kuti tiphunzire zinthu zina zatsopano posinkhasinkha, tifunika kuletsa zododometsa za moyo wa tsiku ndi tsiku. Kuchita zimenezi kumatenga nthaŵi ndipo kumafuna kuti munthu ukhale pawekha. Komatu, n’zotsitsimula kwambiri kudya chakudya chauzimu ndi kumwa madzi a choonadi a m’Mawu a Mulungu.

19. (a) Pankhani ya phunziro laumwini, kodi n’chiyani chathandiza ena kuwonjezera nthaŵi imene amatha kuika maganizo awo pa zimene akuphunzira? (b) Kodi phunziro tiziliona bwanji, ndipo tingapindulenji ndi chinthu chofunika kwambiri chimenechi?

19 Bwanji ngati nthaŵi imene timatha kuika maganizo pa zimene tikuphunzirazo ndi yochepa ndipo timayamba kuganiza zina tikangophunzira pang’ono? Ena aona kuti angawonjezere mphamvu zawo zoika maganizo pa zimene akuphunzira mwa kuyamba ndi kuphunzira kwa nthaŵi yochepa ndiyeno kumawonjezera nthaŵiyo pang’onopang’ono. Cholinga chathu chizikhala chothera nthaŵi yokwanira pophunzira osati chophunzira mothamanga. Tiyenera kukhala ndi chidwi chachikulu ndi nkhani imene tikuphunzirayo. Ndipo tingafufuzenso zowonjezereka pogwiritsa ntchito mabuku ambirimbiri amene gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru latipatsa. Tingapindule kwambiri ngati tifufuza “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Kuchita zimenezo kudzatithandiza kum’dziŵa kwambiri Mulungu ndi kukulitsa luso lathu la kuzindikira. (Ahebri 5:14) Ngati timaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, tidzakhalanso ‘odziŵa kuphunzitsa ena.’​—2 Timoteo 2:2.

20. Kodi tingatani kuti tikhale ndi ubwenzi wapamtima ndi Yehova Mulungu ndi kuusungabe?

20 Kupezeka pa misonkhano yachikristu ndi kuchita phunziro laumwini zidzatithandiza kwambiri kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndi Yehova ndi kuusungabe. Mwachionekere, zimenezi n’zomwe anachita wamasalmo amene anauza Mulungu kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Ndiyetu, tiyeni tizipezeka nthaŵi zonse pa misonkhano ya mpingo ndi misonkhano yaikulu. Ndiponso tiyeni tiziombola nthaŵi yophunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha. Tidzapindula kwambiri chifukwa potero ‘tidzasamaliradi’ Mawu a Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Paulo ayenera kuti analemba kalata kwa Ahebri mu 61 C.E. Ngatidi ndi choncho, panangopita zaka zisanu zokha ndipo Yerusalemu anazingidwa ndi magulu ankhondo a Seshasi Galasi. Posakhalitsa, magulu ankhondo amenewo anachoka, zimene zinapatsa mpata Akristu atcheru kuti athaŵe. Patapita zaka zinayi kuchokera pamenepa, mzindawo unawonongedwa ndi magulu ankhondo achiroma otsogozedwa ndi Kazembe Tito.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Akristu ena achihebri anatengeka ndi kusiyana nacho chikhulupiriro choona?

• Kodi tingatani kuti tiziikabe maganizo athu pa misonkhano yachikristu?

• N’chiyani chingatithandize kupindula ndi phunziro la Baibulo laumwini ndi kusinkhasinkha?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Akristu achihebri anafunika kukhala tcheru ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu kumene kunatsala pang’ono kuchitika

[Chithunzi patsamba 13]

Makolo angathandize ana awo kupindula ndi misonkhano yachikristu