Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Okonda Choonadi

Achinyamata Okonda Choonadi

Achinyamata Okonda Choonadi

“MNYAMATA adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?” anafunsa motero wamasalmo wachihebri zaka zikwi zambiri zapitazo. (Salmo 119:9) Funsoli lidakali loyenera lerolino chifukwa chakuti achinyamata akukumana ndi mavuto ochuluka m’dzikoli. Achinyamata ambiri atenga matenda a Edzi chifukwa cha chiwerewere, ndipo pafupifupi theka la anthu omwe ali ndi matenda osautsaŵa ndi a zaka zapakati pa 15 ndi 24. Mankhwala osokoneza bongo nawonso adzetsa mavuto ochuluka kwambiri, adula miyoyo ya achinyamata. Achinyamata akuwonongeka ndi nyimbo zosalimbikitsa makhalidwe abwino; mafilimu osonyeza ziwawa ndiponso zachiwerewere, mapulogalamu a pa TV, ndi mavidiyo; ndiponso zinthu zolaula za pa Intaneti. Chotero funso la wamasalmo lidakali lofunika kwambiri kwa makolo ndiponso achinyamata ambiri lerolino.

Pa funso lakelo, wamasalmoyu anayankha kuti: “Akawasamalira monga mwa mawu anu.” Kunena zoona, Mawu a Mulungu, Baibulo, ali ndi malangizo abwino kwa achinyamata, ndipo achinyamata ambiri akusimba lokoma chifukwa chotsatira malangizo ake. (Salmo 119:105) Tiyeni tione zitsanzo zina za achinyamata okonda Mulungu ndiponso omwe akuyesetsa kukhalabe olimba mwauzimu m’dziko lokonda zosangalatsa ndi chumali.

Amayamikira Malangizo a Makolo

Jacob Emmanuel anali mpainiya wa nthaŵi zonse kwa zaka zingapo asanakatumikire pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Mexico. Amakumbukira ndipo amayamikira mmene anayambira kukonda kutumikira Mulungu. Iye akuti: “Makolo anga ndiwo anandilimbikitsa kwambiri, ngakhale kuti abale ena odziŵa zambiri mwauzimu omwe ndinkagwirizana nawo anathandizanso kwambiri. Anandilimbikitsa kuti ndizikonda ntchito yolalikira. Pang’ono ndi pang’ono ananditsogolera m’njira yoyenera; sindiona kuti anandiumiriza.”

David, amene watha zaka zingapo akuchita utumiki wa nthaŵi zonse, amakumbukira mmene zinam’limbikitsira kuona kuti makolo ake anayamba kutumikira monga apainiya apadera iye ndi mbale wake ali ang’onoang’ono. Bambo wake atamwalira, amayi wake anapitiriza upainiya wapadera. Amayi awowo ankawasamalira kuwonjezera pa kulalikira uthenga wabwino. David akuti: “Sanandiumirizepo kuti ndikhale mpainiya, koma kuti tinkakonda upainiya kwambiri monga banja moti kugwirizana kwathu ndiponso mmene tinkakhalira zinandilimbikitsa kuchita chimodzimodzi.” Ponenapo za kufunika kolangizidwa ndi kusamalidwa bwino ndi makolo, David akuti: “Usiku uliwonse, amayi ankatiŵerengera nkhani za m’buku la Kucokera ku Paradaiso Wotaika Kumka ku Paradaiso Wopezedwanso. * Mmene ankatiuzira nkhanizo zinatithandiza kuti tizikonda chakudya chauzimu.”

Kukonda Misonkhano

Achinyamata ena amavutika kuti azikonda misonkhano yachikristu. Amakasonkhana chifukwa choti makolo awo amawatenga kupita nawo ku misonkhano. Komabe, ngati apitiriza kusonkhana, m’kupita kwa nthaŵi amayamba kukonda misonkhano. Taganizani za Alfredo, amene anayamba utumiki wa nthaŵi zonse ali ndi zaka 11. Iye akuvomereza kuti pamene anali ndi zaka pafupifupi zisanu, ankazemba misonkhano chifukwa chakuti ankaodzera nayo koma makolo ake sankamulola kugona nthaŵi ya misonkhano. Iye akuti: “Pamene ndimakula, pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kusangalala kwambiri ndi misonkhano, makamaka nditaphunzira kulemba ndi kuŵerenga chifukwa chakuti ndinayambano kuyankha m’mawu angaanga.”

Cintia, mtsikana wa zaka 17 amene akutumikira monga mpainiya wokhazikika, akufotokoza mmene mayanjano abwino am’thandizira kwambiri kuti azikonda kutumikira Mulungu. Akuti: “Kugwirizana ndi abale ndiponso kufika pamisonkhano nthaŵi zonse zandithandiza kuti ndisamasoŵe anzake omwe si Mboni ndiponso ndisamasirire zochitikachitika zomwe achinyamata amakonda, monga kupita ku madansi. Kumvetsera ndemanga ndi zokumana nazo pamisonkhano zinandilimbikitsa kuti ndipatse Yehova zonse zomwe ndili nazo, ndipo ndikuona kuti chinthu chabwino kwambiri chomwe ndili nacho ndi chitsikana changa. Choncho ndinaganiza zochigwiritsira ntchito mu utumiki wake.”

Komabe, iye akuti: “Panali nthaŵi ina, ndisanabatizidwe, pamene sindinkaona vuto lililonse kuphonya misonkhano, n’kumanamizira homuweki kapena zochita zina za kusukulu. Ndinkaphonya misonkhano yambiri, ndipo izi zinayamba kundiwononga mwauzimu. Ndinayamba kugwirizana ndi mnyamata wina wosaphunzira Baibulo. Ndi thandizo la Yehova, ndinakonza zinthu m’kupita kwa nthaŵi.”

Anasankha Okha

Pablo, mnyamata winanso amene akutumikira Yehova nthaŵi zonse, akafunsidwa za chimene chimapangitsa kukonda choonadi cha m’Mawu a Mulungu, iye amati: “Ndikuganiza kuti pali zinthu ziŵiri: phunziro laumwini la nthaŵi zonse ndi kulimbikira ntchito yolalikira. Ndimayamikira makolo anga chifukwa choti anandiphunzitsa choonadi ponena za Yehova, ndipo ndimaona kuti palibenso chinthu china chabwino koposa chimenechi chomwe iwo akanandipatsa. Komabe, ndimafuna kukhala wokhutira ndi chifukwa chomwe ndimakondera Yehova. Kuti nditero, m’pofunika kudziŵa ‘kupingasa ndi kukwera’ kwa choonadi cha m’Baibulo. Ndi njira yokhayi imene imatithandiza kulakalaka Mawu a Yehova, amene amasonkha ‘moto wotentha’ m’kati mwathu kuti tiuze ena za mawuwo. Kulimbikira ntchito yolalikira kumeneko kudzapangitsa kuti tizikondabe choonadi.”​—Aefeso 3:18; Yeremiya 20:9.

Jacob Emmanuel, amene tam’tchula koyamba uja, amakumbukiranso kufunika kodzisankhira wekha kuti utumikire Yehova. Iye akuti makolo ake sanamuumirizepo kuti abatizidwe. “Ndikhulupirira kuti anachita bwino kwambiri chifukwa chakuti ndikuona ubwino wake. Mwachitsanzo, anyamata ena omwe ndinkagwirizana nawo kwambiri anapanga zoti abatizidwe. Ngakhale kuti zinali zabwino kutero, ndinkadziŵa kuti ena angoonera anzawo, ndipo patapita nthaŵi pang’ono anasiya kulimbikira ntchito za Ufumu. Koma ine makolo anga sanandiumirize kuti ndidzipatulire kwa Yehova. Ndinachita kusankha ndekha.”

Ntchito ya Mpingo

Achinyamata ena aphunzira okha choonadi cha m’Mawu a Mulungu, popanda thandizo la makolo awo. Kwa oterowo, ndi zovuta kwambiri kuphunzira kuchita chabwino ndi kupitiriza kuchita chimenecho.

Noé amakumbukira mmene wapindulira ndi choonadi. Kuyambira ali wamng’ono kwambiri, iye anali waukali ndiponso wachiwawa. Atayamba kuphunzira Baibulo pamsinkhu wa zaka 14, khalidwe lake linayamba kusintha ndipo zimenezi zinasangalatsa kwambiri makolo ake amene panthaŵiyo analibe chidwi ndi Baibulo. Pamene Noé ankapita patsogolo mwauzimu, iye ankafuna kugwiritsa ntchito kwambiri moyo wake potumikira Mulungu. Panopo akuchita utumiki wa nthaŵi zonse.

Alejandro nayenso anayamba kukonda choonadi chachikristu ali wamng’ono kwambiri, ngakhale kuti makolo ake analibe nacho chidwi. Poyamikira choonadi, iye akuti: “Ndinakulira m’banja lachikatolika. Koma malingaliro anga oti kulibe Mulungu anayamba kukula popeza tchalitchi sinkayankha mafunso omwe ndinali n’tavutika nawo kuyambira ndili wamng’ono kwambiri. Gulu la Yehova linandithandiza kudziŵa Mulungu. Linapulumutsadi moyo wanga chifukwa chakuti n’kanapanda kuphunzira Baibulo, mwina bwenzi n’taloŵerera m’zachiwerewere, uchidakwa, kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Mwinanso n’kanaloŵa kagulu kena koukira, zomwe zikanadzetsa mavuto oopsa.”

Kodi wachinyamata angapitirize motani kufufuza choonadi ndi kukhalabe m’choonadi popanda makolo ake kum’limbikitsa? N’zoonekeratu kuti akulu ndiponso anthu ena mumpingo amathandiza kwambiri. Noé akuti: “Sindinayambe ndadziona kuti ndili ndekha, chifukwa chakuti Yehova wakhala woyandikana nane kwambiri nthaŵi zonse. Komanso ndinalimbikitsidwa ndi abale ndi alongo ambiri achikondi omwe akhala atate, amayi, ndi abale anga mwauzimu.” Panopo akutumikira pa Beteli ndipo akugwiritsa ntchito nthaŵi yake kutumikira Mulungu. N’chimodzimodzinso ndi Alejandro. Iye akuti: “Chinthu chimene nthaŵi zonse ndimayamikira kwambiri n’chakuti ndinapindula kukhala mumpingo wokhala ndi akulu omwe ankaonetsa kuti amandikonda. Ndimayamikira kwambiri chifukwa chakuti nditayamba kuphunzira Baibulo, pamene ndinali ndi zaka 16, malingaliro a chinyamata anandisokoneza. Mabanja a mumpingo sanandisiye. Nthaŵi zonse pankapezeka wina wondilandira ku nyumba kwake, n’kundisunga ndi kundipatsa chakudya komanso kumvetsera zonena zanga.” Tsopano Alejandro wachita utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 13.

Anthu ena amaganiza kuti chipembedzo n’cha anthu achikulire okha basi. Komabe, achinyamata ambiri aphunzira choonadi cha m’Baibulo akali ang’onoang’ono ndipo afika pokonda Yehova ndi kukhala okhulupirika kwa iye. Mawu a Davide opezeka pa Salmo 110:3 tingawagwiritsire ntchito pa achinyamata ameneŵa. Mawuwo amati: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M’moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nawo mame a ubwana wanu.”

N’kovuta kuti achinyamata aphunzire choonadi ndi kukhalabe m’choonadi. N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti ambiri akuyandikira kwambiri ku gulu la Yehova, akusonkhana nthaŵi zonse, ndiponso akuphunzira Baibulo mwakhama. Pochita zimenezi, iwo atha kukhala ndi chikondi chenicheni pa Mawu a Mulungu ndiponso utumiki wake!​—Salmo 119:15, 16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1958; panopo silikusindikizidwanso.