Chilimbikitso Panthaŵi ya Mavuto
Chilimbikitso Panthaŵi ya Mavuto
NKHANI zomwe zikuulutsidwa masiku ano n’zoopsa kwambiri. Munthu wina analemba kuti: “Zomwe zikuchitika masiku ano n’zoopsa zedi moti nthaŵi zambiri timachita mantha kuonera nkhani za madzulo.” Dziko ladzala ndi nkhondo, uchigaŵenga, kuvutika, upandu, ndiponso matenda, zomwe ndi zinthu zoipa kwambiri zimene zingatichitikire posachedwapa ngati sizinatichitikirepo kale.
Baibulo linaneneratu molondola za zinthu zimenezi. Yesu pofotokoza za nthaŵi yathu ino, ananena kuti kudzakhala nkhondo zikuluzikulu, miliri, njala, ndiponso zivomezi. (Luka 21:10, 11) Mofanana ndi zimenezi, mtumwi Paulo nayenso analemba za “nthaŵi zoŵaŵitsa” pamene anthu adzakhala aukali, okonda ndalama, ndiponso osakonda zabwino. Iye anatcha nthaŵi imeneyi kuti “masiku otsiriza.”—2 Timoteo 3:1-5.
Chotero, mavuto omwe nkhani zimasonyeza okhudza mmene zinthu zilili padziko lonse, akufananako ndi zomwe Baibulo linaneneratu. Koma zinthu ziŵirizi zimangofanana pokhapa basi. Baibulo limatchula mfundo zomwe nkhani sizitchula. M’Mawu ouziridwa a Mulungu tikhoza kupeza chifukwa chomwe kuipa kwafikira pamenepa komanso mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolo.
Mmene Mulungu Amaonera Kuipa
Baibulo limafotokoza mmene Mulungu amaonera mavuto a masiku athu ano. Ngakhale kuti anadziŵiratu za mavutoŵa, iye sakukondwera 1 Yohane 4:8) Yehova amawaganizira kwambiri anthu ndipo amadana ndi kuipa. M’pake kuti Mulungu akhoza kutilimbikitsa chifukwa chakuti ndi wabwino ndiponso wachifundo ndipo ali ndi mphamvu zothetseratu kuipa padziko lapansi pano ndipo akufunadi kutero. Wamasalmo analemba kuti: ‘[Mfumu yakumwamba yomwe Mulungu wasankha] idzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Idzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nidzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Idzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.’—Salmo 72:12-14.
nawo ndiponso sakufuna kuti apitirire mpaka kalekale. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (Kodi mumawamvera chisoni anthu ovutika? Ndithudi m’matero. Kumva chisoni ndi khalidwe lachibadwa chifukwa chakuti Yehova anatilenga m’chifanizo chake. (Genesis 1:26, 27) Choncho, tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova amamva chisoni ndi mavuto a anthu. Yesu yemwe ankamudziŵa bwino kwambiri Yehova kuposa wina aliyense, anaphunzitsa kuti Yehova amatiganizira kwambiri ndiponso ndi wachifundo zedi.—Mateyu 10:29, 31.
Chilengedwe chimasonyeza kuti Mulungu amasamalira anthu. Yesu ananena kuti Mulungu “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Mtumwi Paulo anauza anthu a mumzinda wa Lustra kuti: “[Mulungu] sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”—Machitidwe 14:17.
Kodi Ali ndi Mlandu Ndani?
N’zochititsa chidwi kuti Paulo anauzanso anthu a ku Lustra kuti: “M’mibadwo yakale [Mulungu] adaleka mitundu yonse iyende m’njira mwawo.” Choncho, mitundu kapena kuti anthu ndiwo kwenikweni amadziputira okha mavuto ambiri omwe akukumana nawo leroŵa. Mulungu sitingamuimbe mlandu.—Machitidwe 14:16.
N’chifukwa chiyani Yehova amalolera zinthu zoipa kuchitika? Kodi adzachitapo kalikonse pa kuipa kumeneku? Yankho la mafunso ameneŵa lingapezeke m’Mawu a Mulungu basi. Izi zili choncho chifukwa chakuti yankholo limakhudza kwambiri mzimu winawake ndiponso nkhani yomwe mzimuwo unayambitsa kumalo a mizimu.
[Zithunzi patsamba 4]
Anthu amamverana chisoni. Kodi Mulungu saganizira kuvutika kwa anthu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
PACHIKUTO: Kasinja: UN PHOTO 158181/J. Isaac; chivomezi: San Hong R-C Picture Company
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Pamwamba kumanzere, Croatia: UN PHOTO 159208/S. Whitehouse; mwana wovutika: UN PHOTO 146150 BY O. MONSEN