Kodi Muyenera Kukhala Waphee Kapena Wamphwayi?
Kodi Muyenera Kukhala Waphee Kapena Wamphwayi?
ANTHU ambiri angaone ngati n’zonyaditsa kuti ena aziwaona kukhala osajijirika, abata, ololera. Komabe, nthaŵi zambiri khalidwe limeneli lingayambitse mphwayi. Baibulo limati: “Mphwayi za opusa zidzawaononga.” (Miyambo 1:32) Kodi zimenezi zikutanthauzanji?
Mabaibulo ena amamasulira mawu a Chihebri ameneŵa ndi mawu monga akuti “woganiza kuti zonse zili bwino” (American Standard Version), “wokhutira ndi zake” (The New American Bible), ndi “wonyalanyaza.” (The New English Bible) Motero kukhala waphee n’kogwirizana ndi ulesi ndi kusasamala ndiponso uchitsiru kapena kupusa.
M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Akristu a ku mpingo wa Laodikaya ankanyalanyaza mwadala zosoŵa zawo zauzimu. Iwo ankadzitama kuti ‘sasoŵa kanthu.’ Yesu Kristu anawawongolera maganizo, n’kuwapempha kuti akhalenso achangu pantchito zachikristu.—Chivumbulutso 3:14-19.
Anthunso a m’tsiku la Nowa anali onyalanyaza zinthu. Anatanganidwa ndi zinthu zopanda phindu m’moyo, “analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, . . . , ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” Kenako Yesu anawonjezera kuti: “Kotero kudzakhala kufika [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.
Maulosi a Baibulo amene akwaniritsidwa akusonyeza kuti tili m’nthaŵi ya “kukhalapo kwake kwa Mwana wa munthu,” Yesu Kristu. Tiyeni tisakhale onyalanyaza zinthu, osasamala, okhutira ndi zathu zokha, amphwayi.—Luka 21:29-36.