Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziŵa Zolondola Zokhudza Mulungu Kumatilimbikitsa

Kudziŵa Zolondola Zokhudza Mulungu Kumatilimbikitsa

Kudziŵa Zolondola Zokhudza Mulungu Kumatilimbikitsa

KWA anthu ena, zomwe Baibulo limanena kuti Mulungu ndi wachikondi ndiponso wachifundo zimabutsa mafunso othetsa nzeru. Amafunsa kuti: Ngati Mulungu amafunadi kuthetsa kuipa, ndipo kuti amadziŵa mmene angakuthetsere komanso kuti ali ndi mphamvu zochitira zimenezi, n’chifukwa chiyani kuipa kukuchulukirachulukira? Iwo amavutika kumvetsa mfundo zitatu izi: (1) Mulungu ndi wamphamvuyonse; (2) Mulungu ndi wachikondi ndiponso wabwino; ndipo (3) zinthu zoipa zikupitirizabe kuchitika. Amaganiza kuti popeza mfundo yachitatuyi ndi yoona ndipo palibe amene angatsutse, ndiye kuti imodzi mwa mfundo zina ziŵirizo singakhale yoona. Iwo amaona kuti Mulungu sangathetse kuipaku kapena kuti sizim’khudza.

Patapita masiku angapo zigaŵenga zitaphwasula Likulu la Zamalonda la Padziko Lonse ku New York, m’tsogoleri wina wotchuka wachipembedzo ku United States anati: “Ndakhala ndikufunsidwa kambirimbiri chifukwa chomwe Mulungu amalolera masoka ndiponso kuvutika kwa anthu. Kunena zoona, sindikudziŵa n’komwe yankho lake ndipo ndimalephera ngakhale kudziyankha ndekha mokhutiritsa.”

Pothirirapo ndemanga pa mawu ameneŵa, pulofesa wina wamaphunziro apamwamba a zaumulungu analemba kuti, anachita chidwi kwambiri ndi “mfundo zogwira mtima” zomwe m’tsogoleri wachipembedzoyu ananena. Iye anagwirizananso ndi zomwe katswiri wina wamaphunziro analemba. Anati: “Kusamvetsetseka kwa mavuto a anthu n’kumenenso kumachititsa Mulungu kukhalanso wosamvetsetseka.” Koma kodi n’kosathekadi kumvetsa chifukwa chomwe Mulungu amalolera kuipa?

Chiyambi cha Kuipa

Mosiyana ndi zomwe atsogoleri achipembedzo anganene, Baibulo silinena kuti n’kosatheka kumvetsa chifukwa chomwe Mulungu walolera kuipa. Mfundo yofunika kwambiri yomwe ingatithandize kumvetsa nkhani yokhudza kuipa ndiyo kuzindikira kuti Yehova sanalenge dziko loipa. Analenga mwamuna ndi mkazi oyambirira angwiro, opanda tchimo. Yehova anaona zonse zomwe analenga kuti “zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:26, 31) Cholinga cha Mulungu chinali chakuti Adamu ndi Hava afutukule munda wa Edene wa Paradaiso padziko lonse, n’kulidzaza ndi anthu achimwemwe otetezedwa ndi ulamuliro wachikondi wa Mulungu.​—Yesaya 45:18.

Kuipa kunayamba chifukwa cha mzimu winawake umene ngakhale kuti poyamba unali wokhulupirika kwa Mulungu, unayamba kufuna kulambiridwa. (Yakobo 1:14, 15) Kupanduka kwakeko kunaonekera padziko lapansi pamene mzimuwo, Satana, unanyengerera anthu aŵiri oyambirira kuti nawonso apandukire Mulungu. M’malo momvera malangizo osapita m’mbali a Mulungu oti asadye kapena kukhudza chipatso cha mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, Adamu ndi Hava anatengako chipatso cha mtengowo nadya. (Genesis 3:1-6) Mwa kuchita zimenezi, iwo sanamvere Mulungu ndipo anasonyezanso kuti akufuna kudzilamulira okha.

Zinayambitsa Nkhani Yokhudza Ulamuliro

Kupanduka komwe kunachitika mu Edene kunayambitsa nkhani yokhudza ulamuliro yofunika kwambiri kwa zolengedwa zonse. Anthu opandukawo anakayikira ngati Yehova amalamulira moyenera zinthu zomwe analenga. Kodi Mlengi anali ndi ufulu woti anthu azimumvera pa chilichonse? Kodi anthu zingawayendere bwinopo ngati atamachita zinthu modzilamulira okha?

Yehova anafuna kuthetsa nkhani yokhudza ulamuliro wake imeneyi m’njira yomwe inasonyeza kuti amagwiritsa ntchito bwino chikondi chake, chilungamo chake, nzeru zake, ndiponso mphamvu zake. Akanatha kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuwononga opandukawo nthaŵi yomweyo. Zimenezo zikanakhala chilungamo chokhachokha chifukwa iye anali ndi ufulu wochita zimenezo. Koma kutero sikukanathetsa nkhani yokhudza ulamuliro yomwe inabukayo. Komanso, Mulungu akanatha kungonyalanyaza tchimolo. Ena lerolino angaganize kuti kuteroko ndiko kukanakhala kusonyeza chikondi. Komabe, kuchita zimenezo nakonso sikukanathetsa zomwe Satana ananena kuti zinthu zitha kumawayendera bwinopo anthu ngati akudzilamulira okha. Ndiponso, kodi zimenezo sizikanangolimbikitsa ena kupatuka pa njira ya Yehova? Mapeto ake mavuto akanakhala osatha.

Yehova mwa nzeru zake, walola kuti anthu adzilamulire kwa kanthaŵi. Ngakhale kuti zimenezi zamuchititsa kulola kuipa kwa kanthaŵi, izi zapatsa anthu mwayi kuona ngatidi angadzilamulire okha bwinobwino popanda kudalira Mulungu, koma kutsatira miyezo yawoyawo ya chabwino ndi choipa. Kodi zotsatira zake n’zotani? Moyo wa anthu wakhala wa nkhondo, kupanda chilungamo, kuponderezana, ndiponso mavuto. Kulephera kochititsa manyazi kwa anthu opandukira Yehova kudzathetseratu nkhani yomwe inabuka m’munda wa Edene.

Pakalipano, Mulungu wasonyeza chikondi chake mwa kupereka Mwana wake, Yesu Kristu, amene anapereka moyo wake nsembe ya dipo. Izi zimatheketsa anthu omvera kumasulidwa ku chilango cha uchimo ndi imfa chomwe chinabwera chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Dipo linatsegula njira yopita ku moyo wosatha kwa anthu onse amene amakhulupirira Yesu.​—Yohane 3:16.

Yehova akutitsimikizira kuti kuvutika kwa anthu n’kwakanthaŵi. Wamasalmo analemba kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:10, 11.

Moyo Wopanda Mavuto Ndiponso Wachimwemwe M’tsogolo

Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kukusonyeza kuti nthaŵi yoti Mulungu athetse matenda, chisoni ndiponso imfa yayandikira. Tamvani zinthu zabwino kwambiri za m’tsogolo zomwe mtumwi Yohane anamuonetsa m’masomphenya. Iye analemba kuti: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. . . . Ndi Mulungu yekha adzakhala [ndi anthu] . . . ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Pofuna kutsimikiza kuti malonjezoŵa adzachitikadi, Yohane anauzidwa kuti: “Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”​—Chivumbulutso 21:1-5.

Nanga bwanji za anthu miyandamiyanda osalakwa amene anafa kuchokera panthaŵi yomwe anthu anapanduka mu Edene? Yehova analonjeza kuti adzaukitsa anthu amene akugona mu imfa. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Anthu oukitsidwawa adzayembekezera kukhala ndi moyo m’dziko lomwe ‘mudzakhalitsa chilungamo.’​—2 Petro 3:13.

Monga momwe tate wachikondi amalolera mwana wake kuchitidwa opaleshoni yopweteka kwambiri ngati akudziŵa kuti opaleshoniyo idzamupindulira mwanayo kwa nthaŵi yaitali, Yehova nayenso walola anthu kuvutika padziko lapansi kwa kanthaŵi. Ngakhale zili choncho, zinthu zabwino zosatha zikuyembekezera anthu onse amene amafuna kuchita zomwe Mulungu amafuna. Paulo anati: “Cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:20, 21.

Iyitu ndiyo nkhani yabwino, osati nkhani zomwe timaona pawailesi yakanema, kapena kuŵerenga m’nyuzipepala. Iyi ndi nkhani yabwino kuposa ina iliyonse. Nkhani yochokera kwa “Mulungu wotilimbikitsa” amene amatiganiziradi.​—2 Akorinto 1:3, NW.

[Zithunzi patsamba 6]

Zomwe zachitika nthaŵi yonseyi zasonyeza kuti anthu sangadzilamulire okha bwinobwino popanda kudalira Mulungu

[Mawu a Chithunzi]

Banja la ku Somalia: UN PHOTO 159849/​M. GRANT; bomba la atomu: USAF photo; msasa wa ukaidi: U.S. National Archives photo