Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwayi Wapadera Wogwira Nawo Ntchito Yofutukula Nkhondo Itatha

Mwayi Wapadera Wogwira Nawo Ntchito Yofutukula Nkhondo Itatha

Mbiri ya Moyo Wanga

Mwayi Wapadera Wogwira Nawo Ntchito Yofutukula Nkhondo Itatha

YOSIMBIDWA NDI FILIP S. HOFFMANN

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali itangotha kumene mu May 1945. Mu December chaka chomwecho, Nathan H. Knorr, amene ankayang’anira ntchito yolalikira ya padziko lonse ya Mboni za Yehova, anabwera ku Denmark ndi mlembi wake wa zaka 25, Milton G. Henschel. Tinabwereka holo yaikulu kaamba ka msonkhano umene anachititsa, womwe tinkauyembekezera kwambiri. Achinyamatafe, nkhani yomwe Mbale Henschel anakamba inali yosangalatsa kwambiri chifukwa chakuti anali wamsinkhu wathu ndiponso mutu wa nkhaniyo anasankha wakuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 12:1.

PAULENDOWO, tinauzidwa kuti pakuchitika zinthu zabwino kwambiri pofuna kupititsa patsogolo ntchito ya padziko lonse yolalikira ndiponso kuti tingaloŵetsedwe nawo m’zinthu zimenezo. (Mateyu 24:14) Mwachitsanzo, ku United States anali atatsegula sukulu yatsopano yophunzitsa amuna ndi akazi achinyamata ntchito yaumishonale. Mbale Knorr ananena motsindika kuti ngati atatiitana ku sukuluyi, tidzangogula “tikiti yopitira yokha” ndi kutinso sitidzadziŵa komwe akatitumize. Ngakhale zinali choncho, ena tinalemberako makalata ofunsira malo pa sukuluyi.

Ndisanafotokoze zomwe ndinachita nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha, ndiyambire pa kubadwa kwanga mu 1919. Panali zambiri zomwe zinachitika nkhondo isanayambe ndiponso ili m’kati zimene zinakhudza kwambiri moyo wanga.

Kuphunzira Choonadi cha m’Baibulo kwa Mwana Amene Ankati Woipa

Pamene Amayi ankayembekezera kubadwa kwanga​—mwana wawo wachisamba​—iwo anapemphera kuti ngati ndine wamphongo, ndidzakhale mmishonale. Mlongo wawo anali Wophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo, koma azibale awo ankawaona ngati mwana woipa. Nyumba yathu inali kufupi ndi mzinda wa Copenhagen. Ophunzira Baibulo akamachita misonkhano yawo yapachaka kumeneko, Amayi ankaitana alongo awowo, a Thomas, omwe ankakhala kutaliko ndi mzindawo, kuti adzakhale nafe. Pofika mu 1930 zinthu zosangalatsa kwambiri za m’Baibulo zomwe amalumewo ankazidziŵa ndiponso mfundo zawo zogwira mtima zinapangitsa Amayi kukhala Wophunzira Baibulo.

Amayi ankakonda Baibulo. Potsatira lamulo la pa Deuteronomo 6:7, iwo ankatiphunzitsa ndi mlongo wanga ‘pokhala pansi m’nyumba mwawo, poyenda panjira, pogona pansi, kapena pouka.’ M’kupita kwa nthaŵi, ndinayamba kugwira nawo ntchito yolalikira nyumba ndi nyumba. Ndinkakonda kukambirana ndi anthu nkhani monga zakuti mzimu sufa komanso moto wa helo, zimene matchalitchi ankaphunzitsa. Ndinkawasonyeza bwino kwambiri anthu m’Baibulo kuti ziphunzitso zoterozo zinali zolakwika.​—Salmo 146:3, 4; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4.

Banja Lathu Ligwirizana

Utatha msonkhano wa ku Copenhagen wa mu 1937, pa nyumba yofikira mabuku ya ofesi ya Mboni za Yehova mu Denmark pankafunika thandizo kwa nthaŵi yochepa. Ndinali nditangotsiriza maphunziro anga pa sukulu ya zamalonda ndipo ndinalibe udindo wina uliwonse, motero ndinadzipereka kukathandiza. Ntchito itatha panyumba yofikira mabukuyo, anandipempha kukathandiza pa ofesi ya nthambi. Posakhalitsa, ndinachoka kwathu n’kukakhala ku nthambi ku Copenhagen, ngakhale kuti panthaŵiyo n’kuti ndisanabatizidwe. Kukhala ndi Akristu okhwima mwauzimu tsiku ndi tsiku kunandithandiza kupita patsogolo mwauzimu. Chaka chotsatira, pa January 1, 1938, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi.

Mu September 1939, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inayambika. Kenako, pa April 9, 1940, asilikali a dziko la Germany analanda dziko la Denmark. Popeza kuti nzika za dziko la Denmark zinali ndi ufulu wochita zinthu zina, tinapitiriza ntchito yathu yolalikira.

Ndiyeno panachitika zosangalatsa kwambiri. Atate anakhala Mboni yolimbikira ndiponso yokhulupirika, zomwe zinapatsa banja lathu chimwemwe chodzala tsaya. Motero, ine ndi nzika zina zinayi za dziko la Denmark, atatiitana kuti tikaphunzire nawo m’kalasi lachisanu ndi chitatu la Sukulu ya Gileadi, banja lathu lonse linandilimbikitsa. Maphunziro a miyezi isanu, omwe anayamba mu September 1946, anachitikira pamalo okongola kwambiri kufupi ndi mzinda wa South Lansing ku New York.

Maphunziro a Gileadi ndi Ena Otsatira

Sukulu ya Gileadi inandipatsa mwayi wopeza anzanga atsopano abwino kwambiri. Tsiku lina madzulo tikuwongola miyendo pasukulupo ndi Harold King wa ku England, tinakambirana za komwe angatitumize tikatsiriza maphunziro athu. Harold anati, “Sindinaone komaliza therezi loyera la Dover, [lomwe lili Kum’mwera kwa England].” Zinali zoona, komatu panatha zaka 17 asanaonenso therezi limenelo, ndipo zaka zinayi ndi theka mwa zaka 17 zimenezo anakhala m’ndende yayekha ku China! *

Titamaliza maphunziro athu, ananditumiza ku Texas, m’dziko la U.S.A., kuti ndikatumikire monga woyang’anira woyendayenda, ndizikachezera mipingo ya Mboni za Yehova ndi kuilimbikitsa mwauzimu. Anandilandira ndi manja aŵiri. Kwa abale a ku Texas, zinali zosangalatsa kukhala ndi mnyamata wa ku Ulaya, wongotsiriza kumene maphunziro a Gileadi. Koma nditatha miyezi isanu ndi iŵiri yokha ku Texas, ndinaitanidwa ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mu New York. Kumeneko, Mbale Knorr anandipatsa ntchito ya mu ofesi, n’kundilangiza kuti ndiphunzire mmene amagwirira ntchito m’madipatimenti onse. Ndiyeno, nditabwerera ku Denmark, ndinafunika kugwiritsa ntchito zomwe ndinaphunzirazo, ndi kuonetsetsa kuti zonse zikuchitika monga momwe zikuchitikira ku Brooklyn. Cholinga chake chinali choti ntchito zochitika m’nthambi zonse padziko lapansi zikhale zolongosoka kwambiri. Kenako, Mbale Knorr ananditumizanso ku Germany.

Kugwiritsa Ntchito Malangizo pa Nthambi Zosiyanasiyana

Pamene ndinkafika ku Wiesbaden, m’dziko la Germany, mu July 1949, mizinda yambiri ya dzikolo n’kuti idakali mabwinja. Anthu amene ankatsogolera ntchito yolalikira anali amuna omwe anazunzidwa kuyambira pamene Hitler anayamba kulamulira mu 1933. Ena anali atakhala m’ndende ndi m’misasa ya ukaidi zaka zisanu ndi zitatu kapena khumi kapenanso kuposerapo! Ndinagwira ntchito ndi atumiki a Yehova ameneŵa kwa zaka zitatu ndi theka. Chitsanzo chawo chapadera chimandikumbutsa zimene wolemba mbiri wina wa ku Germany, Gabriele Yonan, analemba. Iye analemba kuti: “Pakanapanda chitsanzo cha gulu la Akristu limeneli lomwe silinasunthike ndi ulamuliro wankhanza wa chipani cha National Socialist, bwenzi tikukayika zoti munthu angakwanitse kuchita ziphunzitso za Chikristu za Yesu, pambuyo poikidwa m’ndende ya Auschwitz ndiponso kupululutsidwa ndi Anazi.”

Ntchito yanga panthambi inali yofanana ndi yomwe ndinkagwira ku Denmark: kuphunzitsa njira yatsopano, yofanana ndi mmene gulu likuyendetsedwera m’mayiko ena. Abale a ku Germany atazindikira kuti kusinthaku sikuti kunali kosuliza ntchito yawo, koma kuti nthaŵi yakwana yoti nthambi zosiyanasiyana limodzi ndi likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova zigwirire ntchito pamodzi, anayamba kunyadira kwambiri ndiponso anagwirizana nazo kwambiri.

Mu 1952 ndinalandira kalata yochokera ku ofesi ya Mbale Knorr yondilangiza kuti ndipite ku nthambi ya mu mzinda wa Bern, ku Switzerland. Anandiuza kuti kumeneko ndikatumikire monga woyang’anira nthambi, kuyambira pa January 1, 1953.

Zosangalatsa Zinanso ku Switzerland

Patapita nthaŵi pang’ono ndili ku Switzerland ndinakumana ndi Esther pa msonkhano, ndipo tinachita chinkhoswe patangopita nthaŵi pang’ono. Mu August 1954, Mbale Knorr anandiitanitsa ku Brooklyn, komwe anandiphunzitsa ntchito ina yatsopano, komanso yosangalatsa. Chifukwa cha kuchuluka ndiponso kukula kwa maofesi a nthambi padziko lonse, anakhazikitsa dongosolo latsopano. Dziko analigaŵa m’zigawo, ndipo chigawo chilichonse chinali ndi woyang’anira woyendera nthambi amene amakatumikira kumeneko. Anandipatsa zigawo ziŵiri zoti ndikatumikire: Ulaya ndi mayiko a m’dera lozungulira nyanja ya Mediterranean.

Nditakhala nthaŵi yochepa ku Brooklyn, ndinabwerera ku Switzerland ndi kukonzekera ntchito yoyendera nthambi. Tinakwatirana ndi Esther ndipo anabwera kudzatumikira nane panthambi ya ku Switzerland. Ulendo wanga woyamba ndinapita ku nyumba za amishonale ndi nthambi za ku Italy, Greece, Cyprus, m’mayiko a ku Middle East ndiponso a m’mbali mwa nyanja Kumpoto kwa Africa, Spain ndi Portugal​—onse pamodzi anali mayiko okwana 13. Nditakakhala pang’ono ku Bern, ndinapitiriza ulendo wanga m’mayiko ena onse a ku Ulaya kumadzulo kwa Soviet Union. Chaka choyamba cha ukwati wathu, ndinakhala moyenda miyezi isanu ndi umodzi, ndikutumikira abale athu achikristu.

Kusintha kwa Zinthu

Mu 1957, Esther anadziŵa kuti anali woyembekezera, ndiye popeza kuti panthambi sipakhala makolo omwe ali ndi ana, tinakonza zokakhala ku Denmark, komwe atate wanga anatilola kuti tizikhala nawo. Esther ankasamalira mwana wathu wamkazi, Rakel, ndiponso atate wanga, pomwe ine ndimathandiza nawo ntchito zina ndi zina pa ofesi ya nthambi yomangidwa kumene. Ndinatumikiranso monga mlangizi wa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya oyang’anira m’mipingo ndiponso ndinapitiriza kutumikira monga woyang’anira woyendera nthambi.

Ntchito yoyendera nthambi inapangitsa kuti ndizikhalitsa moyenda, zimene mwatsoka zinapangitsa kuti ndisamakhalitse ndi mwana wathu. Izi zinalinso ndi zotsatira zake. Panthaŵi ina ndinakakhala kanthaŵi ndithu mu mzinda wa Paris, komwe tinakhazikitsa nyumba yaing’ono yosindikizira. Esther ndi Rakel anabwera pasitima kuti adzandione ndipo anatsikira pa siteshoni ya Gare du Nord. Ine ndi Léopold Jontès wochokera ku nthambi tinapita kukawachingamira. Rakel anaima pa masitepe a sitima, n’kuyang’ana Léopold, n’kudzayang’ana ine, n’kudzayang’ananso Léopold, kenako n’kukakumbatira Léopold!

Kusintha kwinanso kwakukulu kunachitika ndili ndi zaka 45, pamene ndinasiya utumiki wa nthaŵi zonse n’cholinga chokafuna ntchito kuti ndisamalire banja langa. Popeza ndinkadziŵa zambiri chifukwa chokhala mtumiki wa Mboni za Yehova, ndinapeza ntchito monga woyang’anira zotumiza katundu kumayiko ena. Nditagwira ntchito pakampaniyo kwa zaka pafupifupi zisanu ndi zinayi ndiponso Rakel atatsiriza sukulu, tinaganiza zotsatira pempho loti tikakhale komwe kunali anthu ochepa olalikira za Ufumu.

Nditakaona mmene zinthu zilili ku Norway, ndinafunsa bungwe lina lothandiza anthu kupeza ntchito ngati panali mwayi woti ndingapeze ntchito. Sanandiyankhe zolimbikitsa. Zinali zokayikitsa kuti munthu wazaka 55 angapeze ntchito. Komabe, ndinakambirana ndi ofesi ya nthambi ku Oslo ndiyeno ndinachita lendi nyumba ina kufupi ndi mzinda wa Drøbak, ndili ndi chiyembekezo choti mwayi wa ntchito upezeka wokha. Zinaterodi, ndipo kenako ndinasangalala kwambiri ndi ntchito ya Ufumu ku Norway.

Nthaŵi yosangalatsa inali imene ambiri mu mpingo wathu ankapita kumpoto kukalalikira m’gawo losagaŵiridwa. Tinachita lendi nyumba zing’onozing’ono pa kampu ina, ndipo tsiku ndi tsiku tinkakalalikira m’mafamu a apo ndi apo m’mapiri okongola kwambiri. Zinali zosangalatsa kwambiri kuuza anthu aubwenzi ameneŵa za Ufumu wa Mulungu. Tinagaŵira mabuku ambiri, koma tinali kudzachita maulendo obwereza pakatha chaka. Komabe, anthu sanatiiŵale! Esther ndi Rakel akukumbukirabe nthaŵi yomwe tinapitakonso ndipo anatikumbatira ngati ndife achibale awo omwe anasiyana nawo kalekale. Titakhala zaka zitatu ku Norway, tinabwerera ku Denmark.

Zosangalatsa pa Moyo Wabanja

Titangobwerera, Rakel anachita chinkhoswe ndi Niels Højer, mpainiya wa nthaŵi zonse wolimbikira kwambiri. Atakwatirana, Niels ndi Rakel anapitiriza upainiya mpaka pamene anakhala ndi ana. Niels ndi mwamuna komanso tate wabwino kwambiri, wokondadi banja lake. Tsiku lina m’maŵa kwambiri anatenga mwana wake wamwamuna panjinga yake n’kupita naye kugombe la nyanja kukaona dzuŵa likutuluka. Munthu wina woyandikana nawo nyumba anafunsa mwanayo zomwe anakachita ku gombeko. Anayankha kuti: “Tinakapemphera kwa Yehova.”

Patapita zaka zingapo, ine ndi Esther tinaonerera ubatizo wa zidzukulu zathu zikuluzikulu ziŵiri, Benjamin, ndi Nadja. Niels anali nawo pa anthu oonerera ubatizowo, ndipo mwadzidzidzi anayang’anizana nane maso ndi maso. Anandiyang’ana, n’kunena kuti, “Amuna enieni salira.” Koma patangotha kanthaŵi tonsefe tinalira titakumbatirana. N’zosangalatsa kukhala ndi mkamwini yemwe ungaseke ndiponso kulira naye pamodzi!

Kupitirizabe Kusintha Mogwirizana ndi Mmene Zinthu Zilili

Dalitso lina linafika pamene ine ndi Esther anatiitana kukatumikiranso panthambi ya Denmark. Koma panthaŵiyi n’kuti zokonzekera kumanga nthambi yokulirapo kwambiri ku Holbæk zili m’kati. Ndinali ndi mwayi woyang’anira nawo ntchito yomanga nthambiyo. Ntchito yonseyo inagwiridwa ndi antchito odzifunira osalandira malipiro. Ngakhale kuti kunazizira kwambiri, pofika kumapeto kwa 1982, ntchito zikuluzikulu zomanga nthambiyo n’kuti zitatha, ndipo tonse tinasangalala kukaloŵa m’nyumba zikuluzikulu ndiponso zabwino!

Patapita nthaŵi pang’ono ndinayamba kugwira ntchito ya mu ofesi, yomwe ndinasangalala nayo kwambiri, pamene Esther ankagwira ntchito yolandira matelefoni. Koma m’kupita kwa nthaŵi anakamuchita opaleshoni m’chiuno, ndiponso patatha chaka chimodzi ndi theka anakamuchita opaleshoni ndulu. Ngakhale kuti anthu a pa nthambi ankatisamalira, tinaona kuti ndi bwino kusamuka panthambipo kuti tipepuze abale athu. Tinasamukira ku mpingo womwe munali mwana wathu wamkazi ndi banja lake.

Masiku ano Esther sali bwino kwenikweni. Komabe, ndinganene mochokera pansi pa mtima kuti pa zaka zonse zomwe takhala tikutumikirira pamodzi, pamene zinthu zambiri zimasinthasintha, iye wakhala bwenzi komanso mthandizi wabwino kwambiri. Ngakhale kuti akumadwaladwala, tonse tikupitirizabe kuchita nawo pang’onopang’ono ntchito yolalikira. Ndikalingalira za moyo wanga, ndimanena mawu a wamasalmo moyamikira, kuti: “Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga.”​—Salmo 71:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Onani Nsanja ya Olonda (ya Chingelezi) ya July 15, 1963, masamba 437-42.

[Chithunzi patsamba 24]

Tikutsitsa mabuku panthambi ya Germany pamene inkamangidwa mu 1949

[Chithunzi patsamba 25]

Ena mwa anthu omwe ndinkagwira nawo ntchito anali Mboni monga izi zochokera ku misasa ya ukaidi

[Zithunzi patsamba 26]

Ndili ndi Esther lerolino ndi patsiku la ukwati wathu pa Beteli ya ku Bern, mu October 1955