Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amadalitsa ndi Kuteteza Anthu Omvera

Yehova Amadalitsa ndi Kuteteza Anthu Omvera

Yehova Amadalitsa ndi Kuteteza Anthu Omvera

“Wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”​—MIYAMBO 1:33.

1, 2. N’chifukwa chiyani kumvera Mulungu n’kofunika? Perekani chitsanzo.

ANAPIYE achikasu osalimba atanganidwa kutolatola zakudya mu udzu waufupi, osadziŵa kuti kabawi ali mumlengalenga kufuna kuti awagwire. Mwadzidzidzi, mayi wa anapiyewo akulira kwambiri kuchenjeza ana akewo kuti athaŵire kwa iye ndipo akutambasula mapiko ake. Anapiyewo akuthamangira kuli mayi wawoyo, ndipo posakhalitsa atetezeka kunsi kwa mapiko ake. Kabawi walephera kugwira anapiyewo. * Tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti kumvera kumapulumutsa miyoyo.

2 Zimene tikuphunzira pamenepa n’zofunika kwambiri makamaka kwa Akristu masiku ano, chifukwa Satana akuchita zonse zimene angathe kuti agwire anthu a Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 12, 17) Cholinga chake n’chakuti awononge moyo wathu wauzimu kuti Yehova asatiyanje ndiponso kuti tisadzakhale ndi moyo wosatha. (1 Petro 5:8) Komabe, ngati tiyandikira kwa Mulungu ndi kutsatira mwamsanga malangizo amene timalandira kudzera m’Mawu ake ndi m’gulu lake, iye adzatiteteza. Wamasalmo analemba kuti: “Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathaŵira kunsi kwa mapiko ake.”​—Salmo 91:4.

Mtundu Wosamvera Ugwidwa

3. N’chiyani chinachitika chifukwa cha kusamvera kobwerezabwereza kwa Aisrayeli?

3 Pamene mtundu wa Israyeli unali kumvera Yehova, iye anausamalira bwino kwambiri nthaŵi zonse. Koma nthaŵi zambiri, anthuwo anamusiya amene anawapanga n’kumalambira milungu ya mitengo ndi miyala, “zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa.” (1 Samueli 12:21) Patapita zaka zambiri utapanduka choncho, mtunduwo unadzala ndi mipatuko moti sukanatheka kuukonzanso. N’chifukwa chake Yesu anaulilira kuti: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”​—Mateyu 23:37, 38.

4. Kodi zinaonekera bwanji mu 70 C.E. kuti Yehova anausiya mzinda wa Yerusalemu?

4 Yehova anausiya mtundu wa Israyeli wopandukawo ndipo zimenezi zinaonekera momvetsa chisoni mu 70 C.E. M’chaka chimenecho, asilikali achiroma, omwe ananyamula mbendera zawo zimene zinali ndi chithunzi cha chiwombankhanga, anatera ngati kabawi ku Yerusalemu kudzapha modetsa nkhaŵa. Panthaŵiyo, mumzindamo munadzala anthu okondwerera Paskha. Kupereka kwawo nsembe zambiri sikunapangitse Mulungu kuwayanja. Zimenezo zinawakumbutsa mawu a Samueli kwa Mfumu yosamvera Sauli. Iye anati: “Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mawu a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.”​—1 Samueli 15:22.

5. Kodi Yehova amafuna kumvera kotani, ndipo tikudziŵa bwanji kuti kumvera koteroko n’kotheka?

5 Ngakhale kuti Yehova amatsindika kufunika komvera, amadziŵa kuti pali zina zimene anthu opanda ungwiro sangathe kuchita. (Salmo 130:3, 4) Zimene iye amafuna ndizo kuona mtima ndi kumvera chifukwa cha chikhulupiriro, chikondi, ndi kuopa kum’khumudwitsa. (Deuteronomo 10:12, 13; Miyambo 16:6; Yesaya 43:10; Mika 6:8; Aroma 6:17) ‘Mtambo waukulu wa mboni zimene zinakhalako Chikristu chisanayambe,’ zimene zinakhulupirika m’mayesero aakulu, ngakhale kufa kumene, zinasonyeza kuti kumvera koteroko n’kotheka. (Ahebri 11:36, 37; 12:1) Anthu otereŵatu anasangalatsa mtima wa Yehova! (Miyambo 27:11) Komabe, ena anakhulupirika poyamba koma analephera kukhalabe omvera. Mmodzi mwa iwo anali Mfumu Yoasi ya Yuda wakale.

Mfumu Imene Inawonongedwa ndi Mayanjano Oipa

6, 7. Kodi Yoasi anali mfumu yotani Yehoyada ali moyo?

6 Mfumu Yoasi ikanaphedwa ili mwana koma inangopulumuka mwamwayi. Pamene Yoasi anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, Mkulu wa Ansembe Yehoyada anam’tenga molimba mtima kumene anabisala ndi kumuika kukhala mfumu. Popeza kuti Yehoyada amene anali kuopa Mulungu anali ngati bambo ndiponso mlangizi wa Yoasi, mfumu yaing’onoyi “[i]nachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.”​—2 Mbiri 22:10–23:1, 11; 24:1, 2.

7 Imodzi mwa ntchito zabwino zimene Yoasi anachita ndiyo kukonzanso kachisi wa Yehova, ntchito imene inali “mumtima mwa Yoasi.” Anakumbutsa Yehoyada Mkulu wa Ansembe kuti anafunika kukhometsa msonkho wa pakachisi kuchokera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, monga “msonkho wa Mose,” kuti alipirire ntchito imeneyi. Mwachionekere, Yehoyada anakwanitsa kuilimbikitsa mfumu yaing’onoyo kuphunzira ndi kumvera Chilamulo cha Mulungu. Zotsatira zake zinali zakuti ntchito ya pa kachisi ndi zipangizo za m’kachisi zinakonzedwa mofulumira kwambiri.​—2 Mbiri 24:4, 6, 13, 14; Deuteronomo 17:18.

8. (a) Kodi n’chiyani kwenikweni chinachititsa Yoasi kugwa mwauzimu? (b) Kodi kusamvera kwa mfumu mapeto ake kunam’pangitsa kuchita chiyani?

8 N’zomvetsa chisoni kuti Yoasi sanamvere Yehova mpaka kale. Chifukwa chiyani sanatero? Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera. Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo awo, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwawo kumene.” Mayanjano oipa a akalonga a Yuda anachititsanso mfumu kusamvera aneneri a Mulungu. Mmodzi mwa iwo anali Zekariya mwana wa Yehoyada amene molimba mtima anadzudzula Yoasi ndi anthu onse chifukwa cha kusamvera kwawo. M’malo molapa, Yoasi analamula kuti Zekariya aphedwe mwa kum’ponya miyala. Ee, Yoasi anakhaladi wankhanza ndiponso wosamvera, ndipo zonsezi zinachitika chifukwa chakuti anagonjera mayanjano oipa.​—2 Mbiri 24:17-22; 1 Akorinto 15:33.

9. Kodi zimene zinachitikira Yoasi ndi akalonga zikusonyeza bwanji kuipa kwa kusamvera?

9 Atasiya Yehova, kodi n’chiyani chinachitikira Yoasi ndi anzake aja, akalonga oipa? Gulu la nkhondo la Asuri, “anthu oŵerengeka” chabe, anaukira Yuda “nawononga mwa anthu akalonga onse a anthu.” Oukiraŵa analamulanso mfumuyo kuti ipereke chuma chake pamodzi ndi golidi ndi siliva wa m’kachisi. Ngakhale kuti Yoasi sanaphedwe, anamusiya ali wofooka ndiponso wodwala. Zitangochitika kumene zimenezi, ena mwa atumiki ake anamugalukira n’kumupha. (2 Mbiri 24:23-25; 2 Mafumu 12:17, 18) Mawu amene Yehova anauza Aisrayeli analidi oona. Anati: “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake . . . matemberero . . . adzakugwerani ndi kukupezani.”​—Deuteronomo 28:15.

Mlembi Anapulumuka Chifukwa Chomvera

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kusinkhasinkha zimene Yehova analangiza Baruki? (b) Kodi Yehova anapatsa Baruki uphungu wotani?

10 Kodi nthaŵi zina mumagwa ulesi chifukwa chakuti si ambiri amene mumawapeza muutumiki wachikristu omwe amachita chidwi ndi uthenga wabwino? Kodi nthaŵi zina mumasirira anthu opeza bwino ndi moyo wawo wochita zimene angafune? Ngati ndi choncho, ganizirani za Baruki, mlembi wa Yeremiya, ndi malangizo amene Yehova anamuuza chifukwa chomukonda.

11 Pamene Baruki ankalemba ulosi wina, Yehova analankhula za iye amene. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Baruki anayamba kusasangalala ndi moyo wake, ndipo anafuna zinthu zina zabwinopo kusiyana ndi mwayi wake wapadera wotumikira Mulungu. Yehova ataona kuti Baruki wayamba kuganiza motero, anam’patsa uphungu mosapita m’mbali koma mwachifundo, kuti: “Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, . . . koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m’malo monse m’mene mupitamo.”​—Yeremiya 36:4; 45:5.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kudzifunira “zinthu zazikulu” m’dongosolo lino la zinthu?

12 Kodi m’mawu amene Yehova anauza Baruki, mukuona kuti anali kumuganizira kwambiri munthu wabwino ameneyu, amene anatumikira mokhulupirika ndiponso molimba mtima pamodzi ndi Yeremiya? N’chimodzimodzinso masiku ano, Yehova amawaganizira kwambiri anthu amene amakopeka kuti afunefune umene akuona kuti ndiwo moyo wabwinopo m’dziko lino. N’zosangalatsa kuti, mofanana ndi Baruki, ambiri mwa anthu amenewo amvera malangizo achikondi a abale okhwima mwauzimu oti asinthe. (Luka 15:4-7) Inde, tiyeni tonsefe tizindikire kuti anthu amene akudzifunira “zinthu zazikulu” m’dongosolo lino alibe tsogolo. Anthu oterowo sapeza chimwemwe chenicheni, ndipo choipa kuposa pamenepa n’chakuti posachedwapa adzapita ndi dzikoli ndi zikhumbo zake zonse zadyera.​—Mateyu 6:19, 20; 1 Yohane 2:15-17.

13. Kodi nkhani ya Baruki ikutiphunzitsa chiyani pankhani ya kudzichepetsa?

13 Nkhani ya Baruki ikutiphunzitsanso phunziro labwino pankhani ya kudzichepetsa. Onani kuti Yehova sanam’patse uphungu Baruki mwachindunji koma analankhula kudzera mwa Yeremiya, amene mwina Baruki anali kudziŵa bwinobwino kupanda ungwiro kwake ndi makhalidwe ake. (Yeremiya 45:1, 2) Komabe, Baruki sanadzikuze; anazindikira modzichepetsa kuti uphunguwo unachokera kwa Yehova. (2 Mbiri 26:3, 4, 16; Miyambo 18:12; 19:20) Motero, ngati ‘tigwidwa nako kulakwa kwakuti’ ndi kulandira uphungu umene tikufunikira kuchokera m’Mawu a Mulungu, tiyeni titsanzire kukhwima maganizo kwa Baruki, kuzindikira kwake kwauzimu, ndiponso kudzichepetsa kwake.​—Agalatiya 6:1.

14. N’chifukwa chiyani n’koyenera kumvera amene akutitsogolera?

14 Kudzichepetsa kwathu koteroko kumathandizanso amene akutipatsa uphunguwo. Ahebri 13:17 amati “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” Akulu amapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova nthaŵi zambiri, kupempherera kulimba mtima, nzeru, ndiponso luso lofunika kuti akwanitse mbali yovuta kwambiri imeneyi ya ntchito yawo yoweta. Tiyeni ‘tizindikire oterewo.’​—1 Akorinto 16:18.

15. (a) Kodi Yeremiya anasonyeza bwanji kuti anam’khulupirira Baruki? (b) Kodi Baruki anafupidwa chiyani chifukwa cha kumvera kwake kodzichepetsa?

15 Umboni ulipo woti Baruki anasintha maganizo ake, chifukwa patapita nthaŵi Yeremiya anam’patsa ntchito yovuta kwambiri, yoti apite ku kachisi kukaŵerenga mokweza uthenga wachiweruzo womwewo umene Yeremiya anali kumuuza kuti alembe. Kodi Baruki anamvera? Inde, anachita “monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri.” Ndipotu, anaŵerenga uthenga umenewo ngakhale kwa akulu a Yerusalemu, zimene n’zosachita kufunsa kuti anafunika kulimba mtima. (Yeremiya 36:1-6, 8, 14, 15) Pamene Ababulo anagonjetsa mzindawo patapita zaka 18, taganizani mmene Baruki ayenera kuti anayamikirira populumuka chifukwa chakuti anamvera chenjezo la Yehova ndi kusiya kudzifunira “zinthu zazikulu!”​—Yeremiya 39:1, 2, 11, 12; 43:6.

Kumvera Pamene Mzinda Unazingidwa Kunapulumutsa Miyoyo

16. Kodi Yehova anachitira bwanji chifundo Ayuda a mu Yerusalemu pamene Ababulo anazinga mzindawo mu 607 B.C.E.?

16 Pamene mapeto a Yerusalemu anafika mu 607 B.C.E., Mulungu anachitiranso chifundo anthu omvera. Kuzinga mzindawo kutafika pachimake, Yehova anauza Ayuda kuti: “Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa. Iye amene akhala m’mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Akasidi akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.” (Yeremiya 21:8, 9) Ngakhale kuti anthu a mu Yerusalemu anayenerera kuwonongedwa, Yehova anachitira chifundo amene anamumvera, ngakhale panthaŵi yomaliza yovuta kwambiri imeneyo. *

17. (a) Kodi ndi njira ziŵiri ziti zimene kumvera kwa Yeremiya kunayesedwa pamene Yehova anam’langiza kuuza Ayuda amene anazingidwa kuti ‘apandukire kwa Akasidi’? (b) Kodi tingapindule chiyani ndi chitsanzo cha Yeremiya cha kumvera molimba mtima?

17 Mosakayika, kuuza Ayuda kuti adzipereke kwa Akasidi kunayesa kumvera kwa Yeremiya. Chifukwa chimodzi n’chakuti iye anali kuchitira nsanje dzina la Mulungu. Sankafuna kuti adani alinyoze, amene akananena kuti apambana chifukwa cha mafano awo opanda moyo. (Yeremiya 50:2, 11; Maliro 2:16) Ndiponso, Yeremiya anadziŵa kuti pouza anthu kuti adzipereke, anali kuika moyo wake pachiswe, chifukwa ena akanaona ngati iye ndi woukira chifukwa cha mawu akewa. Komabe, iye sanachite mantha, m’malo mwake momvera analengeza zimene Yehova anamuuza. (Yeremiya 38:4, 17, 18) Monga Yeremiya, ifenso timalengeza uthenga umene anthu ambiri saukonda. Uthenga wake ndi womwewo umene anthu ananyozera Yesu. (Yesaya 53:3; Mateyu 24:9) Choncho, tiyeni ‘tisaope anthu,’ koma monga anachitira Yeremiya, timvere Yehova molimba mtima, kumukhulupirira ndi mtima wonse.​—Miyambo 29:25.

Kumvera Pamene Gogi Akuukira

18. Kodi kumvera kwa atumiki a Yehova kudzayesedwa bwanji m’tsogolomu?

18 Posachedwapa, dziko lonse la Satana loipali lidzawonongedwa mu ‘chisautso chachikulu’ chimene sichinachitikepo n’kale lonse. (Mateyu 24:21) Mosakayika, nthaŵiyo isanafike ndiponso panthaŵi imeneyo, chikhulupiriro ndi kumvera kwa anthu a Mulungu kudzayesedwa kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza kuti Satana pantchito yake monga “Gogi, wa kudziko la Magogi” adzaukira kotheratu atumiki a Yehova, kukonzekeretsa magulu a nkhondo amene awafotokoza kuti “nkhondo yaikulu [“ankhondo ambiri,” NW] . . . ngati mtambo wakuphimba dziko.” (Ezekieli 38:2, 14-16) Anthu a Mulungu omwe adzakhala ochepa poyerekeza ndi magulu ankhondowo ndiponso adzakhala opanda chida chilichonse, adzathaŵira ‘m’mapiko’ a Yehova amene akuwatambasula kuti ateteze anthu omvera.

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani kumvera kunali kofunika kwambiri kwa Aisrayeli pamene anali pa Nyanja Yofiira? (b) Kodi kusinkhasinkha mwapemphero nkhani ya ku Nyanja Yofiira kungatipindulitse bwanji masiku ano?

19 Zimenezi zikutikumbutsa ulendo wa Aisrayeli wochokera ku Igupto. Yehova atakhaulitsa Aigupto ndi milili khumi yowononga, anatsogolera anthu ake kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Sanawadzeretse njira yachidule, m’malo mwake anawadzeretsa ku Nyanja Yofiira kumene akanatha kugwidwa mosavuta ndi kuukiridwa. Kwa anthu odziŵa za nkhondo, kuchita zimenezi kunaoneka ngati kuika moyo pachiswe. Ngati mukanakhalapo, kodi mukanamvera mawu a Yehova kudzera mwa Mose ndi kuyenda nawo kupita ku Nyanja Yofiira ndi chikhulupiriro chonse, mukudziŵa kuti Dziko Lolonjezedwa silinali kumene munali kupitako?​—Eksodo 14:1-4.

20 Tikamaŵerenga Eksodo chaputala 14, timaona mmene Yehova anapulumutsira anthu ake posonyeza mphamvu zochititsa mantha. Nkhani zimenezo zingalimbitse chikhulupiriro chathu tikapatula nthaŵi kuziŵerenga ndi kuzisinkhasinkha. (2 Petro 2:9) Ndiyeno chikhulupiriro cholimba chidzatithandiza kumvera Yehova ngakhale zimene iye amafuna zitaoneka ngati zikusemphana ndi maganizo a anthu. (Miyambo 3:5, 6) Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro changa mwa kuphunzira Baibulo mwakhama, kupemphera, ndi kusinkhasinkha, pamodzi ndi kusonkhana nthaŵi zonse ndi anthu a Mulungu?’​—Ahebri 10:24, 25; 12:1-3.

Kumvera Kumapatsa Chiyembekezo

21. Kodi ndi madalitso otani amene anthu omvera Yehova angapeze pakalipano komanso amene adzapeza m’tsogolo?

21 Amene amakonda kumvera Yehova amaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Miyambo 1:33 ngakhale pakalipano. Pamenepo pamati: “Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” Mawu olimbikitsa ameneŵa adzagwiratu ntchito kwambiri m’tsiku la Yehova lobwezera chilango limene likubwera. Ndipotu, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.” (Luka 21:28) Mwachionekere, anthu omvera Mulungu okha ndi amene adzakhala ndi chikhulupiriro chomvera mawu ameneŵa.​—Mateyu 7:21.

22. (a) Kodi anthu a Yehova ali ndi chifukwa chotani chokhulupirira? (b) Kodi tidzakambirana zotani m’nkhani yotsatirayi?

22 Chifukwa chinanso chokhulupirira n’chakuti “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Masiku ano, Yehova sauzira aneneri monga ankachitira kale. M’malo mwake, walamula gulu la kapolo wokhulupirika kuti lizipereka chakudya chauzimu cha panthaŵi yake ku nyumba yake. (Mateyu 24:45-47) Ndiyetu n’kofunika kwambiri kuti tikhale ndi mtima womvera “kapolo” ameneyo. Monga mmene nkhani yotsatirayi isonyezere, kumvera kwathu kumavumbulanso mmene timamuonera Yesu, mbuye wa ‘kapoloyo.’ Iye ndi Amene ‘anthu akumumvera.’​—Genesis 49:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ngakhale kuti nthaŵi zambiri anthu amati thadzi la nkhuku ndi lamantha, buku la bungwe lina loteteza nyama limati: “Thadzi la nkhuku limamenyera nkhondo ngakhale kulolera kufa poteteza anapiye ake kuti asagwidwe.”

^ ndime 16 Yeremiya 38:19 amavumbula kuti Ayuda ambiri ‘ananka’ kwa Akasidi ndipo sanaphedwe koma anawatengera ku ukapolo. Sitikudziwa ngati anadzipereka potsatira mawu a Yeremiya. Komabe, kupulumuka kwawo kunatsimikizira mawu a mneneriyo.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi n’chiyani chinachitika chifukwa cha kusamvera kobwerezabwereza kwa Aisrayeli?

• Kodi mayanjano anamukhudza bwanji Mfumu Yoasi, kuchiyambi kwa moyo wake ndiponso patapita nthaŵi?

• Kodi tingaphunzire chiyani kwa Baruki?

• N’chifukwa chiyani palibe chifukwa choti anthu omvera a Yehova achite mantha pamene dziko limene lilipoli likuyandikira kutha?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Pamene anali kutsogoleredwa ndi Yehoyada, Yoasi yemwe anali wamng’ono anali kumvera Yehova

[Chithunzi patsamba 15]

Mayanjano oipa anapangitsa Yoasi kulamula kuti mneneri wa Mulungu aphedwe

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi mukanamvera Yehova ndi kudzionera nokha mphamvu zake zopulumutsa zochititsa mantha?