Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kanizani Mdyerekezi”

“Kanizani Mdyerekezi”

Kanizani Mdyerekezi”

“Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.”​—YAKOBO 4:7.

1. Kodi tingafotokoze bwanji mmene dziko lilili pakalipano, ndipo n’chifukwa chiyani odzozedwa pamodzi ndi anzawo afunika kukhala tcheru?

“MULUNGU wasoŵa koma Mdyerekezi alipobe.” Mawu ameneŵa a wolemba mabuku wina wachifalansa dzina lake André Malraux angafotokoze bwino mmene dziko lapansi tikukhala lino lilili. Zimene anthu akuchita zikuonekadi kuti zikusonyeza machenjera a Mdyerekezi kuposa zimene Mulungu amafuna. Satana akusocheretsa anthu “mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka.” (2 Atesalonika 2:9, 10) Komabe ‘m’masiku otsiriza’ ano, Satana wafiirira maso kwambiri atumiki a Mulungu odzipatulira, kumenya nkhondo ndi Akristu odzozedwa, “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 12:9, 17) Atumiki odzozedwa a Mulungu ameneŵa pamodzi ndi anzawo amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi afunika kukhala tcheru.

2. Kodi Satana ananyenga bwanji Hava, ndipo mtumwi Paulo anali ndi nkhaŵa yotani?

2 Satana amanyenga m’njira zosiyanasiyana. Pogwiritsa ntchito njoka monga pobisalira, iye ananyenga Hava kuti aganize kuti angasangalale kwambiri ngati atamachita zinthu mosadalira Mulungu. (Genesis 3:1-6) Patapita zaka pafupifupi 4,000, mtumwi Paulo anada nkhaŵa kuti Satana akanachenjerera Akristu odzozedwa a ku Korinto. Iye analemba kuti: “Ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:3) Satana amaipitsa ndi kupotoza maganizo a anthu. Monga mmene ananyengera Hava, iye angachititse Akristu kuganiza molakwika ndi kuona ngati angasangalale atamachita zinthu zimene Yehova ndi Mwana wake amazitsutsa.

3. Kodi Yehova wapereka chiyani kuti zititeteze kwa Mdyerekezi?

3 Satana tingamuyerekezere ndi mlenje amene amatchera misampha kuti akole mbalame zimene zikungodziyendera. Kuti tipeŵe misampha ya Satana tifunika ‘kukhala m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba,’ malo ophiphiritsira a chitetezo amene Yehova amapereka kwa anthu amene mwa zochita zawo amasonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wake wachilengedwe chonse. (Salmo 91:1-3) Timafunikira chitetezo chonse chimene Mulungu amapereka kudzera m’Mawu ake, mzimu wake, ndiponso gulu lake kuti ‘tikhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.’ (Aefeso 6:11) Mosakayika, Mdyerekezi amagwiritsa ntchito machenjera ambirimbiri pofuna kukola atumiki a Yehova.

Misampha Imene Satana Anatchera Akristu Oyambirira

4. Kodi Akristu oyambirira ankakhala m’dziko lotani?

4 Akristu amene anakhalako m’zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri C.E. anali kukhala m’nthaŵi imene Ufumu wa Aroma unafika pachimake. Umene ankati Mtendere wa Aroma unachititsa malonda kupita patsogolo. Chitukuko chimenechi chinachititsa anthu olamulira kukhala ndi nthaŵi yochuluka yopuma, ndipo anakonza zoti anthu wamba akhale ndi zosangalatsa zambiri kuti asaukire boma. Nthaŵi zina, masiku a tchuti anali kufanana ndi masiku ogwira ntchito. Atsogoleriwo anali kugwiritsa ntchito ndalama za boma kuti apatse anthu zinthu zofunika pamoyo wawo pamodzi ndi zosangalatsa, kuwadyetsa bwino ndi cholinga chowasintha maganizo.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani sikunali koyenera kuti Akristu akapezeke ku mabwalo a zisudzo ndi mabwalo aakulu a maseŵera a Aroma? (b) Kodi Satana anagwiritsa ntchito msampha wotani, ndipo Akristu akanaupeŵa bwanji?

5 Kodi m’dziko lotereli munali ngozi iliyonse kwa Akristu oyambirira? Poona machenjezo a olemba ena omwe anakhalako atumwi atatha, monga Tertullian, zochitika za panthaŵi yopuma m’masiku amenewo zinadzala ndi ngozi zauzimu ndiponso zamakhalidwe kwa Akristu. Imodzi mwa ngozizo inali yakuti mapwando ambiri a anthu onse ndiponso maseŵero ankachitika pofuna kulemekeza milungu yachikunja. (2 Akorinto 6:14-18) Kumabwalo a zisudzo, ngakhale maseŵero a chikhalidwe cha nthaŵi imeneyo ankadzala ndi zachiwerewere kapena chiwawa chokhetsa mwazi. Pamene nthaŵi inali kupita, anthu sanalinso kukonda maseŵeroŵa, ndipo analoŵedwa m’malo ndi zisudzo zolaula zimene wochitayo ankalankhula ndi thupi osatulutsa mawu. Wolemba mbiri wina, Jérôme Carcopino, m’buku lake lakuti Daily Life in Ancient Rome, anati: “M’zisudzo zimenezi akazi ankaloledwa kuvula n’kungokhala mbulanda . . . Pankakhala kukhetsa mwazi kwadzaoneni. . . . [Wochita chisudzoyo] ankasonyeza monkitsa makhalidwe oipa a zakugonana amene anali kulamulira anthu mumzindamo. Anthu sanali kuipidwa ndi zisudzo zoterozo chifukwa anali atazoloŵera kale chiwawa chokhetsa mwazi chimene chinkachitika ku mabwalo aakulu a maseŵera ndipo maganizo awo anapotoka.”​—Mateyu 5:27, 28.

6 M’mabwalo aakulu a maseŵera, anthu ankamenyana mpaka wina kufa kapena ankamenyana ndi nyama zakuthengo, kaya kuzipha kapena nyamazo kupha anthuwo. Zigaŵenga, ndiponso kenako Akristu ambiri, anali kuwaponya ku zilombo zolusa. Ngakhale panthaŵi zakalezo, msampha umene Satana anagwiritsa ntchito unali wowachititsa anthu kusaipidwa ndi zachiwerewere ndiponso chiwawa mpaka zimenezi zinali ponseponse ndipo anthu anali kuzifuna kwambiri. Njira yokha imene munthu akanapeŵera msampha umenewo inali kusapita kumabwalo a zisudzowo ndi kumabwalo aakulu a maseŵera.​—1 Akorinto 15:32, 33.

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani sikunali kwanzeru kuti Mkristu apite ku mipikisano ya magaleta? (b) Kodi Satana ayenera kuti anagwiritsa ntchito bwanji malo osambira a Aroma kuti akole Akristu?

7 Mipikisano ya magaleta imene inali kuchitikira m’mabwalo aakulu a maseŵera mosakayika inali yosangalatsa kwambiri, koma inali yosavomerezeka kwa Akristu chifukwa anthu oonerera nthaŵi zambiri anali kuchita chiwawa. Wolemba wina wa m’zaka za m’ma 200 C.E. ananena kuti oonerera ena anali kumenyana, ndipo Carcopino anati “openda nyenyezi ndi mahule analinso ndi malo awo amalonda” kuseri kwa chinyumba cha bwalo la maseŵeralo. Inde, mabwalo a maseŵera a Aroma ochitirako mipikisanoyi sanali malo oti Akristu angapiteko.​—1 Akorinto 6:9, 10.

8 Nanga bwanji za malo osambirako otchuka a Aroma? N’zoona kuti panalibe cholakwika kuti munthu asambe ndi kukhala waukhondo. Koma malo ambiri osambira a Aroma anali aakulu ndipo anali ndi zipinda zimene anali kutikitirako thupi, zipinda zochitirako maseŵero, zipinda zotchoverako njuga, ndi malo ena odyerako ndi kumwa. Ngakhale kuti mwapakamwa chabe ankaika nthaŵi ya amuna ndi nthaŵi ya akazi, nthaŵi zambiri onse anali kuloledwa kusambira limodzi. Clement wa ku Alesandriya analemba kuti: “Malo osambira amatsekulidwa mwachisawawa kwa amuna ndi akazi; ndipo kumeneko onse amavula mbulanda kuti achite zachiwerewere.” Motero, Satana anagwiritsa ntchito mosavuta malo abwinobwino ogwiritsidwa ntchito ndi anthu onse kuti akole Akristu. Anthu anzeru sanali kupita kumalo oterowo.

9. Kodi ndi misampha iti imene Akristu oyambirira anafunika kuipeŵa?

9 Nthaŵi imene Ufumu wa Aroma unafika pachimake, anthu panthaŵi yopuma ankakonda kwambiri kutchova njuga. Akristu oyambirira akanapeŵa kubetcherana kumene kunkachitika pa mipikisano ya magaleta mwa kusapita ku mabwalo a maseŵeroŵa. Njuga zina zing’onozing’ono zinkachitikanso mosavomerezeka m’zipinda zamkati mwa nyumba za alendo ndi malo omwerako moŵa. Anthu anali kubetcherana pa manambala osiyanasiyana a timiyala tosalala tobulungika kapena timafupa timene woseŵera winayo anali kutisunga m’manja. Kutchova njuga kunkasangalatsa anthu chifukwa anali kuyembekezera kupeza ndalama mosavuta. (Aefeso 5:5) Ndiponso, akazi ogulitsa moŵa m’malo ameneŵa nthaŵi zambiri anali mahule, zimenenso zinkachititsa kuti pakhale ngozi yochita chisembwere. Imeneyi ndi ina mwa misampha imene Satana anatchera Akristu omwe ankakhala m’mizinda ya mu Ufumu wa Aroma. Kodi masiku ano zinthu zikusiyana kwambiri ndi mmene zinalili panthaŵiyo?

Misampha Imene Satana Amagwiritsa Ntchito Masiku Ano

10. Kodi mmene zinthu zilili masiku ano zikufanana bwanji ndi zimene zinkachitika mu Ufumu wa Aroma?

10 Kwenikweni, misampha ya Satana sinasinthe ngakhale kuti papita zaka zambiri. Mtumwi Paulo analangiza mwamphamvu Akristu amene anali kukhala mumzinda woipa wa Korinto kuti ‘asawachenjerere Satana.’ Iye anati: “Sitikhala osadziŵa machenjerero [a Satana].” (2 Akorinto 2:11) M’mayiko ambiri olemera zinthu masiku ano zili mmene zinalili m’nthaŵi imene Ufumu wa Aroma unafika pachimake. Anthu ali ndi nthaŵi yambiri yopuma kuposa kale. Malotale a boma amachititsa ngakhale anthu osauka kuyembekezera kuti adzakhala opeza bwino. Pali zosangalatsa zambiri zotchipa zimene zatenga anthu maganizo. Mabwalo a maseŵera amadzaza ndi anthu, pamakhala kutchova njuga, oonerera nthaŵi zina amachita chiwawa, ndipo nthaŵi zambiri oseŵerawo amachitanso chimodzimodzi. Anthu amamvetsera nyimbo zoipa. Maseŵero olaula amaonetsedwa m’mabwalo a zisudzo ndiponso m’mavidiyo ndi pa TV. M’mayiko ena, nthaŵi zambiri amuna ndi akazi amasambira limodzi m’malo osambira ndi m’malo otuluka madzi otentha achilengedwe. Ndiponso m’malo ena osambira a kunyanja amuna ndi akazi amasambira limodzi ali maliseche. Monga mmene zinalili kwa Akristu oyambirira, Satana akuyesetsa kukopa atumiki a Mulungu pogwiritsa ntchito zochita za panthaŵi yopuma za m’dzikoli.

11. Kodi pamakhala misampha yotani pamene munthu akufuna kupumula ndi kuchitako zinthu zina zosangalatsa?

11 M’dziko lino lodzala ndi kuvutika maganizo, munthu angafunedi kupumula kapena kuchitako zinthu zina zosangalatsa. Komabe, monga mmene malo osambira a Aroma analili ndi zinthu zimene zikanavulaza Akristu oyambirira, malo ena ochitirako tchuti ndi malo osangalalira akhala msampha umene Satana wagwiritsa ntchito kuwapangitsa Akristu a masiku ano kuchita chiwerewere kapena kuledzera. Paulo analembera Akristu a ku Korinto kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma. Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziŵitso cha Mulungu.”​—1 Akorinto 15:33, 34.

12. Kodi ndi misampha ina iti imene Satana akugwiritsa ntchito kuti akole atumiki a Yehova masiku ano?

12 Taona pankhani ya Hava mmene Satana anagwiritsira ntchito machenjera ake kuti aipitse maganizo a Havayo. (2 Akorinto 11:3) Masiku ano, msampha wina umene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito ndiwo kuwachititsa Akristu kuganiza kuti ngati atengera zochita za zadziko zochulukirapo pofuna kusonyeza kuti Mboni za Yehova n’zofanana ndi anthu ena onse, adzatha kukopa ena kuti aphunzire choonadi chachikristu. Nthaŵi zina amapitirira malire, ndiye m’malo mwake zimene zimachitika n’zosiyana ndi zimenezo. (Hagai 2:12-14) Msampha wina umene Satana amagwiritsa ntchito ndiwo kuchititsa Akristu odzipatulira, achinyamata ndi achikulire omwe, kukhala Akristu nthaŵi zina pamene nthaŵi zina n’kumakhala ngati si Akristu ndipo motero ‘amamvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu.’ (Aefeso 4:30) Ena akodwa mumsampha umenewu pogwiritsa ntchito molakwika Intaneti.

13. Kodi ndi msampha wobisika uti womwe ndi machenjera ena a Mdyerekezi, ndipo ndi malangizo ati a m’buku la Miyambo omwe angathandize pamenepa?

13 Msampha wina wa Satana ndiwo zinthu zobisika zokhudza mizimu. Palibe Mkristu woona amene angamaseŵere dala ndi zinthu zausatana kapena zamizimu. Komabe, ena mosadziŵa sasamala poonerera mafilimu, maseŵero a pa TV, maseŵera a pa vidiyo, ndiponso ngakhale mabuku ndi timabuku ta zinthuzi ndi nkhani zoseketsa za ana zimene zimasonyeza chiwawa ndi zinthu zina zauchiŵanda. Tifunika kupeŵa chilichonse chimene chikukhudzana ndi zamizimu. Mwambi wanzeru umati: “Minga ndi misampha ili m’njira ya wokhota; koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.” (Miyambo 22:5) Popeza Satana ndi “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” chilichonse chotchuka kwambiri chingathe kubisa msampha wake wina.​—2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 2:15, 16.

Yesu Anakaniza Mdyerekezi

14. Kodi Yesu anakaniza bwanji mayesero oyamba a Mdyerekezi?

14 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pokaniza Mdyerekezi ndi kum’pangitsa kuti athaŵe. Yesu atabatizidwa ndi kusala kudya kwa masiku 40, Satana anamuyesa. (Mateyu 4:1-11) Mayesero ake oyamba anagwiritsa ntchito njala imene Yesu anali nayo atatha kusala kudya. Satana anauza Yesu kuti achite chozizwitsa chake choyamba kuti athetse njala yake. Yesu anagwira mawu pa Deuteronomo 8:3 ndipo anakana kugwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika ndipo ananena kuti chakudya chauzimu chinali chofunika kwambiri kuposa chakudya chenicheni.

15. (a) Kodi ndi chilakolako chachibadwa chiti chimene Satana anagwiritsa ntchito poyesa Yesu? (b) Kodi ndi machenjera aakulu ati amene Mdyerekezi akugwiritsa ntchito kuti agonjetse anthu a Mulungu masiku ano, koma kodi tingam’kanize bwanji?

15 Chochititsa chidwi pa mayesero ameneŵa n’chakuti Mdyerekezi sanafune kuti Yesu achite tchimo la chiwerewere. Njala yomwe mwachibadwa imachititsa munthu kufuna chakudya anaiona kuti ndi chilakolako chathupi champhamvu kwambiri chimene akanagwiritsa ntchito poyesa Yesu panthaŵi imeneyi. Kodi ndi ziyeso zotani zimene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito kuti akope anthu a Mulungu masiku ano? Pali zambiri ndiponso zosiyanasiyana, koma akugwiritsa ntchito ziyeso za chiwerewere monga machenjera ake aakulu pofuna kuswa kukhulupirika kwa anthu a Yehova. Mwa kutsanzira Yesu, tingakanize Mdyerekezi ndi ziyeso. Monga mmene Yesu anagonjetsera zolinga za Satana mwa kukumbukira malemba oyenerera, tikayesedwa pankhani imeneyi tingakumbukire malemba monga Genesis 39:9 ndi 1 Akorinto 6:18.

16. (a) Kodi Satana anayesa bwanji Yesu ulendo wotsatira? (b) Kodi ndi njira ziti zimene Satana angatikope kuti tiyese Yehova?

16 Kenako, Mdyerekezi anauza Yesu kuti adumphe kuchokera pamwamba pa kachisi ndi kuyesa Mulungu kuti amuteteze pogwiritsa ntchito angelo Ake. Yesu anagwira mawu Deuteronomo 6:16, ndipo anakana kuyesa Atate wake. Satana sangatiyese kuti tidumphe kuchokera pamwamba pa chimbudzi cha kachisi, koma angatikope kuti tiyese Yehova. Kodi timafuna kuona kuti tingatsanzire mpaka pati masitayelo a dzikoli pankhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu asanatipatse uphungu? Kodi timakonda zosangalatsa zoipa? Ngati tikutero ndiye kuti tikuyesa Yehova. Ngati timakonda kuchita zimenezi, ndiye kuti m’malo moti Satana atithaŵe, adzakhala nafebe, kutikopa mosalekeza kuti tikhale kumbali yake.

17. (a) Kodi Mdyerekezi anayesa bwanji Yesu ulendo wachitatu? (b) Kodi zimene zili pa Yakobo 4:7 zingatichitikire bwanji ife?

17 Satana atauza Yesu kuti am’patsa maufumu onse a dziko lapansi ngati atangom’gwadira chabe posonyeza kum’lambira, Yesu anamukanizanso mwa kugwira mawu m’Malemba, kutsimikiza mtima kulambira Atate wake yekha basi. (Deuteronomo 5:9; 6:13; 10:20) Satana sangatipatse maufumu a dziko lapansi, koma nthaŵi zonse amatiyesa ndi chisangalalo chimene chimaoneka kuti tingakhale nacho ngati titakhala ndi chuma chambiri, ngakhale kuona ngati tikhala ndi kaufumu ndithu. Kodi timachita monga mmene Yesu anachitira, kulambira Yehova yekha basi? Ngati ndi choncho, zimene zinachitikira Yesu zidzatichitikira ifenso. Nkhani ya Mateyu imati: “Pomwepo Mdyerekezi anamsiya iye.” (Mateyu 4:11) Satana adzatisiya ngati tim’kaniza zolimba mwa kukumbukira mfundo za m’Baibulo zoyenerera ndi kuzitsatira. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Yakobo 4:7) Mkristu wina analembera ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku France kuti: “Satana ndi wochenjeradi. Ngakhale kuti ndimafunitsitsa kuchita zabwino, zimandivuta kulamulira mtima wanga ndi zilakolako zanga. Komabe, mwa kulimba mtima, kuleza mtima, ndipo koposa zonse, mothandizidwa ndi Yehova, ndakwanitsa kukhalabe wokhulupirika ndi kugwiritsitsa choonadi.”

Okonzeka Bwino Kukaniza Mdyerekezi

18. Kodi ndi zida zauzimu ziti zimene zimatikonzekeretsa kuti tikanize Mdyerekezi?

18 Yehova watipatsa zida zonse zankhondo yauzimu kuti tithe “kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11-18) Kukonda kwathu choonadi kudzamanga m’chiuno chathu, kapena kutikonzekeretsa, kuti tichite ntchito zachikristu. Kutsimikiza mtima kwathu kutsatira miyezo ya Yehova ya chilungamo kudzakhala ngati chapachifukwa choteteza mtima wathu. Ngati mapazi athu avala uthenga wabwino, nthaŵi zonse tidzagwira ntchito yolalikira, ndipo zimenezi zidzatilimbikitsa ndi kutiteteza mwauzimu. Chikhulupiriro chathu cholimba chidzakhala ngati chikopa chachikulu, chimene chidzatiteteza ku “mivi yonse yoyaka moto ya woipayo,” kuukira kwake kochenjera ndi mayesero ake. Kuyembekeza kwathu ndi chikhulupiro chonse kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake kudzakhala ngati chisoti chimene chidzateteza luso lathu la kulingalira ndi kutipatsa mtendere wamaganizo. (Afilipi 4:7) Ngati tigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu, adzakhala ngati lupanga limene tingagwiritse ntchito kumasula anthu ku ukapolo wauzimu wa Satana. Tingawagwiritsenso ntchito kudzitetezera, monga mmene Yesu anachitira pamene anayesedwa.

19. Kodi n’chiyaninso chikufunika kuphatikiza pa ‘kukaniza Mdyerekezi’?

19 Mwa kuvalabe “zida zonse za Mulungu” zimenezi ndi kupitiriza kupemphera nthaŵi zonse, tingakhulupirire kuti Yehova adzatiteteza Satana akatiukira. (Yohane 17:15; 1 Akorinto 10:13) Koma Yakobo anasonyeza kuti sikokwanira ‘kungokaniza Mdyerekezi.’ Koposa zonse, tiyeneranso ‘kumvera Mulungu,’ amene amatisamalira. (Yakobo 4:7, 8) Nkhani yotsatirayi idzafotokoza mmene tingachitire zimenezi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi misampha iti ya Satana imene Akristu oyambirira anafunika kuipeŵa?

• Kodi ndi machenjera otani amene Satana amagwiritsa ntchito masiku ano kuti akole atumiki a Yehova?

• Kodi Yesu anakaniza bwanji mayesero a Mdyerekezi?

• Kodi ndi zida za nkhondo yauzimu ziti zimene zimatithandiza kukaniza Mdyerekezi?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Yesu anakaniza Mdyerekezi molimbika

[Zithunzi patsamba 10]

Akristu oyambirira anapeŵa zosangalatsa zachiwawa ndi zoipa

[Mawu a Chithunzi]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck