‘Khalani Wanzeru pa Chimaliziro Chanu’
‘Khalani Wanzeru pa Chimaliziro Chanu’
Jean de La Bruyère, wolemba nkhani wa ku France wa m’zaka za m’ma 1600 anati: “Anthu ambiri pazaka zoyambirira za moyo wawo, amachita zinthu zimene zimapangitsa mapeto a moyo wawo kukhala omvetsa chisoni.” Zoonadi, wachinyamata wosadziŵa chochita angamakaikekaike kuti achita chiyani, zimene zingam’pangitse kusakhutira ndi moyo wake ndiponso kunong’oneza bondo. Komanso, wachinyamata waliuma angakakamire mtunda wopanda madzi, zimene zingapangitse kuti m’tsogolo asadzasangalale. Mbali zonsezi, kusachita zabwino kapena kuchita zolakwika kungabweretse mavuto aakulu.
Kodi tingapeŵe bwanji zimenezi? Mawu a Mulungu amalangiza achinyamata amene amasoŵa chochita paunyamata wawo kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.” (Mlaliki 12:1) Ngati ndinu wachinyamata, tsatirani njira zabwino kuti muphunzire za ‘Mlengi wanu’ mudakali wamg’ono.
Nanga, kodi Baibulo limathandiza bwanji achinyamata kupeŵa kuchita zinthu zolakwika paunyamata wawo? Limati: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.” (Miyambo 19:20) Baibulo limasonyezanso momveka bwino kuti kukana nzeru ya Mulungu mwa kunyalanyaza kapena kupanduka paunyamata, kapena pa msinkhu wina uliwonse, kumakhala ndi zotsatira zopweteka. (Miyambo 13:18) Koma, kutsatira malangizo a Mulungu zotsatira zake n’zakuti munthu amakhala ndi “masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere,” womwe ndi moyo wosangalala ndi wopindulitsa.—Miyambo 3:2.