Kodi Pali Mphamvu Zoipa Zimene Zikugwira Ntchito?
Kodi Pali Mphamvu Zoipa Zimene Zikugwira Ntchito?
“Dzikoli lapenga kwabasi, zikungokhala ngati mphamvu zodabwitsa zatseka njira zonse zimene anthu angatulukire pangozi.”—Anatero mtolankhani wina Jean-Claude Souléry.
‘Chifukwa chosoŵa mtengo wogwira, anthu amaona kuti mphamvu zoipa zikugwira ntchito.’—Anatero wolemba mbiri wina Josef Barton.
ZINTHU zoopsa kwambiri zimene zigaŵenga zinachita pa September 11, 2001, zinapangitsa anthu kuganizira zinthu mofatsa. Michael Prowse m’nkhani imene analemba mu nyuzipepala ya ku England yotchedwa Financial Times, anati: “Palibe nyama ingachite nkhanza ngati zimenezi.” Mkozi wa nyuzipepala ya New York Times ananena kuti, poganizira ntchito imene inalipo pokonzekera chiwembu chimenechi, “n’kofunikanso kwambiri kuganizira chidani chimene chinalipo kuti afike pochita chiwembu chimenechi. N’chidani choposa cha pankhondo, chosaona malire, chosatsatira mapangano.”
Anthu a zikhulupiriro zosiyanasiyana amaganiza kuti payenera kukhala mphamvu zina zoipa zimene zikugwira ntchito. Mwamuna wina wamalonda ku Sarajevo amene anaona zinthu zoopsa zimene zinkachitika ku Bosnia chifukwa cha kudana kwa mafuko anati: “Patatha chaka ku Bosnia kuli nkhondo, ndakhulupirira kuti Satana ndiye akuchititsa zonsezi. Imeneyi ndi misala yeniyeni.”
Wolemba mbiri Jean Delumeau atafunsidwa ngati ankakhulupirira zoti kuli Mdyerekezi, anati: “Ndingakane bwanji kuti kulibe mphamvu yoipa, ndikuona zimene zikuchitikazi ndiponso zimene zakhala zikuchitika chibadwireni: Zinthu monga, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse imene inapha anthu oposa 40,000,000; msasa wa Auschwitz ndiponso misasa ina yophera anthu; kuthetseratu fuko lina ku Cambodia; ulamuliro wankhanza wopha anthu wa Ceauşescu ndiponso kuzunza anthu kokhazikitsidwa ndi boma m’mayiko ambiri padziko lonse lapansi. Palinso zinthu zoopsa zambiri. . . . Choncho ndikukhulupirira kuti sikulakwa kunena kuti zimenezi ndi ntchito za ‘mdyerekezi,’ osati chifukwa chakuti amachititsa ndi Mdyerekezi wa nyanga ndi zala za mphandamphanda, koma amene ndi mzimu ndiponso mphamvu yoipa imene ikugwira ntchito padziko lapansi.”
Mofanana ndi Jean Delumeau, anthu ambiri amaona kuti zinthu zoopsa zimene zikuchitikira anthu masiku ano, kungoyambira m’banja mpaka padziko lonse ndi ntchito za “mdyerekezi.” Koma kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi zinthu zoopsa zimenezi, zikuchitika chifukwa cha mphamvu zoipa zomwe si zenizeni, kapena pali mphamvu zoipa zenizeni zimene zikulimbikitsa anthu kuchita zinthu zoopsa kuposa zinthu zoipa zimene anthu amachita masiku onse? Kodi mphamvu zimenezi zimakonzedwa ndiponso kutsogoleredwa ndi kalonga wa oipa—Satana Mdyerekezi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Ana: Chithunzi cha U.S. Coast Guard