Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulera Ana M’dziko Lachilendo—Mavuto ndi Mphoto Zake

Kulera Ana M’dziko Lachilendo—Mavuto ndi Mphoto Zake

Kulera Ana M’dziko Lachilendo​—Mavuto ndi Mphoto Zake

ANTHU ambiri pofuna kuyamba moyo watsopano amasamukira m’dziko lina. Pakalipano ku Ulaya kuli anthu oposa 20,000,000 ochokera m’mayiko ena. Ku United States kuli anthu oposa 26,000,000 obadwira m’mayiko ena ndipo ku Australia anthu 21 mwa anthu 100 alionse ndi obadwira m’mayiko ena. Nthaŵi zambiri, mabanja amene amasamukira m’mayiko ena amavutika kuphunzira chinenero chatsopano ndiponso kuti azoloŵere chikhalidwe chatsopano.

Nthaŵi zambiri, ana sachedwa kuphunzira chinenero cha dziko lawo latsopano ndipo amayamba kuganiza momwe anthu achinenero chimenecho amaganizira. Makolo awo zingawatengere nthaŵi. Pamene ana akukula m’dziko lomwe n’lachilendo kwa makolo awo, kusiyana chinenero kungabweretse vuto la kulankhulana, lomwe n’lovuta kulithetsa.

Chinenero chatsopano chimakhudza momwe ana amaganizira komanso chikhalidwe cha dziko latsopanolo chingakhudzenso momwe amaonera zinthu. Makolo angaone kuti zochita za ana awo n’zosamvetsetseka. Choncho, makolo amene asamukira dziko lina ndipo akuyesetsa kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye” amakumana ndi mavuto apadera.​—Aefeso 6:4.

Vuto la Kuwakhudza Maganizo ndi Kuwafika Pamtima

Makolo achikristu amafuna kuphunzitsa ana awo “chinenero choyera” cha choonadi cha m’Baibulo ndipo umenewu ndi udindo wawo. (Zefaniya 3:9, NW) Komabe, ngati ana amangodziŵa pang’ono chinenero cha makolo awo ndiponso ngati makolo sachidziŵa bwino chinenero chimene ana awo azoloŵera, kodi makolo angakhomereze bwanji chilamulo cha Yehova m’mitima ya ana awo? (Deuteronomo 6:7) Anawo angamve zimene makolo awo akunena, koma ngati siziwafika pamtima, anawo angakhale alendo m’nyumba mwawo momwe.

Pedro ndi Sandra anasamuka ku South America kupita ku Australia, ndipo amapeza vuto limeneli polera anyamata awo aŵiri. * Pedro akuti: “Pokambirana nkhani zauzimu pamafunika kukhudzika mtima ndi maganizo. Mufunika kufotokoza mfundo zakuya ndi zatanthauzo, choncho n’kofunika kuchidziŵa bwino chinenerocho.” Sandra anawonjezera kuti: “Ngati ana athu sachidziŵa bwino chinenero chathu, ndiye kuti moyo wawo wauzimu ungawonongeke kwambiri. Angasiye kuchimvetsa choonadi, sangamvetse mfundo ya zimene akuphunzira. Kuzindikira kwawo kwauzimu kungaloŵe pansi, ndipo ubale wawo ndi Yehova ungawonongeke.”

Gnanapirakasam ndi Helen anasamuka ku Sri Lanka kupita ku Germany ndipo tsopano ali ndi ana aŵiri. Iwo akuvomereza kuti: “Timaona kuti n’kofunika kwambiri kuti ana athu azilankhula chinenero cha makolo athu komanso aziphunzira Chijeremani. N’kofunika kuti azitha kutiuza maganizo awo moona mtima ndiponso momasuka.”

Miguel ndi Carmen, amene anasamuka ku Uruguay kupita ku Australia, akuti: “Makolo amene ali ngati ife ayenera kulimbikira. Ayenera kuphunzira chinenero chatsopano bwinobwino moti akhoza kumva ndi kufotokoza nkhani zauzimu m’chinenero chimenecho, apo ayi aphunzitse ana awo kuchidziŵa kwambiri chinenero cha makolo awowo.”

Chosankha cha Banja

Kuti banja limene lasamukira m’dziko lina likhale lauzimu, chofunika kwambiri ndicho kusankha chinenero chimene banjalo lizilankhula ‘pophunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yesaya 54:13) Ngati banjalo layandikana ndi mpingo wachinenero cha kwawo, lingasankhe zosonkhana ndi mpingo umenewu. Komanso, lingasankhe kumasonkhana ndi mpingo umene umalankhula chinenero chofala kwambiri m’dziko limene asamukiralo. Kodi ndi mfundo ziti zimene zidzapangitsa kusankha zimenezi?

Demetrios ndi Patroulla, amene anasamuka ku Cyprus kupita ku England ndipo ankalera ana awo asanu kumeneko, akufotokoza zimene zinapangitsa kuti asankhe zimene anachita. Akuti: “Poyamba, banja lathu linkasonkhana ndi mpingo wa Chigiriki. Ngakhale kuti zimenezi zinathandiza kwambiri makolofe, zinalepheretsa ana athu kukula mwauzimu. Ngakhale kuti Chigiriki ankachidziŵa pang’ono, ankavutika kumva mfundo zabwino zauzimu. Tinkaona zimenezi chifukwa ankachedwa kukula mwauzimu. Monga banja, tinasamukira ku mpingo wa Chingelezi, ndipo sipanatenge nthaŵi kuti zionekere kuti ana athu akuchita bwino. Alimbikitsidwa mwauzimu. Kunali kovuta kusamuka, koma tinachita zanzeru.”

Banjali linapitirizabe kulankhula chinenero cha makolo awo ndipo linapeza mphoto zambiri. Ana awo akuti: “Kudziŵa zinenero zingapo n’chinthu chabwino zedi. Ngakhale kuti Chingelezi ndiye chinenero chathu, taona kuti kudziŵa Chigiriki kwatithandiza kukhala ogwirizana kwambiri pabanja, makamaka ndi agogo athu. Ndipo kwatithandizanso kuchitira chifundo anthu osamukira m’dziko lina, ndipo zinatilimbitsa mtima kuti tingathe kuphunzira chinenero china. Choncho titakula, banja lathu linasamuka kukathandiza mpingo wa Chialubaniya.”

Christopher ndi Margarita nawonso anasamuka ku Cyprus kupita ku England ndipo ankalera ana atatu kumeneko. Anasankha kumasonkhana ku mpingo wa Chigiriki. Mwana wawo wamwamuna, Nikos, amene tsopano ndi mkulu ku mpingo wa Chigiriki akuti: “Tinapemphedwa kupita ku mpingo watsopano wa Chigiriki. Banja lathu linaona zimenezi ngati ntchito imene Mulungu watipatsa.”

Margarita akuti: “Ana anga aamuna aŵiri atakwanitsa wina zaka seveni pamene winayo zaka eiti, analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Teokalase. Monga makolo, tinkadera nkhaŵa chifukwa sankachidziŵa kwenikweni Chigiriki. Komabe, akapatsidwa nkhani m’sukuluyi inali ntchito yabanja lonse, ndipo tinkatha nthaŵi yaitali kuwathandiza kukonzekera.”

Mwana wawo wamkazi Joanna akuti: “Ndimakumbukira kuti kunyumba Bambo ankatiphunzitsa Chigiriki, ankalemba zilembo pabolodi ndipo tinkaziphunzira zonse mwachifatse. Anthu ambiri amatha zaka zambiri akuphunzira chinenero, koma ife chifukwa chakuti Mayi ndi Bambo ankatithandiza, tinaphunzira Chigiriki kwanthaŵi yochepa.”

Mabanja ena amasonkhana ndi mpingo wa chinenero cha kwawo chifukwa chakuti makolo amaona kuti n’kofunika kuphunzira m’chinenero cha makolo awo kuti akulitse “chidziŵitso cha mzimu” komanso kuti apite patsogolo. (Akolose 1:9, 10; 1 Timoteo 4:13, 15) Mwina banja lingaone kuti chinenero chawo chingathandize anthu ena achinenero chimenecho amene ali m’dzikolo kuphunzira choonadi.

Komanso, banja lingaone kuti zingawathandize kwambiri kumasonkhana ndi mpingo wachinenero chofala kwambiri m’dziko limene asamukiralo. (Afilipi 2:4; 1 Timoteo 3:5) Akakambirana nkhaniyi pabanjapo, mutu wabanja uyenera kusankha chochita utapempha malangizo kwa Mulungu. (Aroma 14:4; 1 Akorinto 11:3; Afilipi 4:6, 7) Kodi ndi mfundo ziti zimene zingathandize mabanja ameneŵa?

Mfundo Zina Zothandiza

Pedro ndi Sandra, amene tawatchula kale aja, akuti: “Tili ndi lamulo lakuti panyumba tizilankhula Chisipanya chokha basi, kuti tisaiŵale chinenero cha makolo athu. N’kovuta kutsatira lamuloli, popeza ana athu amadziŵa kuti timamva Chingelezi. Koma popanda lamulo limeneli, sangachedwe kuiŵala Chisipanya.”

Miguel ndi Carmen, amenenso tawagwira mawu koyamba kuja, akuti: “Ngati makolo amachititsa phunziro la banja mokhazikika ndiponso ngati tsiku lililonse amakambirana lemba latsiku m’chinenero cha makolo awo, ndiye kuti ana adzachidziŵa mokulirapo chinenerocho ndiponso adzaphunzira kufotokoza nkhani zauzimu m’chinenerocho.”

Miguel akutinso: “Yesetsani kuti ulaliki uzikhala wosangalatsa. Mbali yaikulu ya gawo lathu ili mu mzinda waukulu, ndipo nthaŵi yambiri timathera tikuyenda pagalimoto kuti tipeze anthu amene amalankhula chinenero chathu. Nthaŵi imene timakhala tikuyenda timaigwiritsa ntchito kuchita maseŵera a nkhani za m’Baibulo ndiponso kukambirana nkhani zofunika. Ndimayesetsa kukonza maulendo okalalikira kuti tikhale ndi maulendo obwereza angapo abwino kwambiri. Ndiyeno pomaliza paulendowo, ana amakhala atalankhula zogwira mtima ndi munthu mmodzi kapena kuposerapo.”

Kuthana ndi Vuto la Kusiyana Chikhalidwe

Mawu a Mulungu amalimbikitsa achinyamata kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” (Miyambo 1:8) Komabe mwambo wa atate ndi “chilangizo” cha amayi zikakhala zosiyana ndi zimene ana amaona m’deralo, pangakhale mavuto.

N’zoona kuti ndi ntchito ya mutu wa banja lililonse kusankha momwe aziŵeruzira banja lake, ndipo sayenera kutengera kwambiri mabanja ena. (Agalatiya 6:4, 5) Komabe, makolo savutika kutengera chikhalidwe chatsopanocho ngati alankhulana bwino ndi ana awo.

Komabe, zikhalidwe kapena zochitika zambiri zofala m’mayiko olemera n’zowononga moyo wauzimu wa Akristu. Nthaŵi zambiri nyimbo ndi zosangalatsa zotchuka zimalimbikitsa chisembwere, umbombo, ndi kupanduka. (Aroma 1:26-32) Makolo achikristu sayenera kunyalanyaza udindo wawo wolamulira ana awo pankhani ya nyimbo ndi zosangalatsa zimene amakonda kokha chifukwa chakuti sachidziŵa bwino chinenerocho. Ayenera kuika malamulo okhwima. Komabe zimenezi zingabweretse mavuto.

Carmen akuti: “Nthaŵi zambiri sitimva mawu a nyimbo zimene ana anthu amamvetsera. Kaimbidwe kangakhale kabwino ndithu, koma sitingadziŵe ngati mawu a nyimbozo ali ndi mbali yabwino ndi yoipa kapena ngati muli mawu osonyeza makhalidwe oipa.” Kodi athana nalo bwanji vuto limeneli? Miguel akuti: “Nthaŵi yambiri timakhala tikuphunzitsa ana athu kuopsa kwa nyimbo zoipa, ndipo timawathandiza kusankha nyimbo zimene Yehova angazivomereze.” Inde, mpofunika khama ndi kulolera kuti muthane ndi kusiyana chikhalidwe.​—Deuteronomo 11:18, 19; Afilipi 4:5.

Kupeza Mphoto

Kulera ana m’dziko lachilendo kumafuna nthaŵi yambiri ndi khama. Ndipotu zimenezi n’zoona. Koma makolo ndi ana omwe, angapeze mphoto zambiri chifukwa cha khama lawo.

Azzam ndi mkazi wake Sara, anasamuka ku Turkey kupita ku Germany kumene analelera ana awo atatu. Panopa mwana wawo wamkulu wamwamuna akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Selters, Germany. Azzam akuti: “Phindu lalikulu limene ana athu apeza n’lakuti aphunzira makhalidwe ofunika kwambiri m’zikhalidwe zonse ziŵiri.”

Antonio ndi Lutonadio anasamuka ku Angola kupita ku Germany ndipo akulera ana asanu ndi anayi kumeneko. Banjali limalankhula Chilingala, Chifalansa ndi Chijeremani. Antonio akuti: “Kulankhula zinenero zosiyanasiyana kumathandiza banja lathu kulalikira kwa anthu a m’mayiko ambiri. Izi zimatisangalatsa kwambiri.”

Ana aŵiri a banja lina la ku Japan limene linasamukira ku England amaona kuti kudziŵa Chijapani ndiponso Chingelezi kwawathandiza kwambiri. Ana awo akuti: “Kudziŵa zinenero ziŵiri kunatithandiza kupeza ntchito. Tapindula zedi ndi misonkhano ikuluikulu ya Chingelezi. Komanso, tili ndi mwayi wapadera wotumikira ku mpingo wa Chijapani, komwe n’kosoŵa kwambiri anthu olalikira.”

Zingakuyendereni Bwino

Kuyambira m’nthaŵi za m’Baibulo, atumiki a Mulungu avutika kulera ana pakati pa anthu osiyana nawo chikhalidwe. Makolo a Mose zinawayendera bwino ngakhale kuti ankakhala ku Igupto. (Eksodo 2:9, 10) Ayuda ambiri amene anali ku ukapolo ku Babulo analera ana amene anali ofunitsitsa kubwerera ku Yerusalemu kukakhazikitsanso kulambira koona.​—Ezara 2:1, 2, 64-70.

Chimodzimodzinso masiku ano, makolo achikristu zingawayendere bwino. Angapindule kumva ana awo akunena zimene banja lina linamva ana awo akunena kuti: “Ndife banja logwirizana kwambiri chifukwa chakuti Bambo ndi Mayi timalankhulana nawo bwino nthaŵi zonse, amatikonda ndiponso amatisamalira. Ndife osangalala kukhala m’gulu labanja lapadziko lonse limene likutumikira Yehova.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Tasintha mayina ena.

[Chithunzi patsamba 24]

Kulankhula chinenero cha makolo anu chokha kunyumba kumathandiza ana anu kuchidziŵa pang’ono chinenerocho

[Chithunzi patsamba 24]

Kulankhula chinenero chimene nonse mumachidziŵa kumathandiza kuti agogo ndi zidzukulu azigwirizana

[Chithunzi patsamba 25]

Kuphunzira Baibulo ndi ana anu kumakulitsa “chidziŵitso [chawo] cha mzimu”