Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthaŵi Yosangalala ku Mayiko a ku Balkan

Nthaŵi Yosangalala ku Mayiko a ku Balkan

Nthaŵi Yosangalala ku Mayiko a ku Balkan

Munali mu 1922. Msonkhano wa Ophunzira Baibulo Akhama, dzina la Mboni za Yehova nthaŵi imeneyo, unachitikira mu mzinda wa Innsbruck, ku Austria. Pamsonkhanowo panali Franz Brand, mnyamata wa m’tauni ya Apatin, m’chigawo cha Vojvodina, ku Serbia. Wokamba nkhani atangotchula dzina la Mulungu lakuti Yehova, gulu la anthu achiwawa linayamba kukuwa, zimene zinam’lepheretsa kupitiriza, ndipo msonkhano unathera pomwepo. Komabe, zimene Franz anamva zinam’fika pamtima kwambiri, ndipo anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Ichi chinali chiyambi chochepa cha kuwonjezeka kwauzimu kosangalatsa ku dziko lina la ku mayiko a ku Balkan.

KWA anthu ambiri masiku ano, dzina lakuti Yugoslavia limawapatsa chithunzi cha nkhondo ndi kupha anthu mwankhanza. Zimene zimabwera m’maganizo mwawo ndi chithunzi chomvetsa chisoni cha kupulula anthu, anthu othaŵa kwawo othedwa nzeru, nyumba zowonongedwa, ndiponso ana amasiye ovutika. Sitingathe kufotokoza mmene anthu anamvera kupweteka ndi mmene anavutikira chifukwa cha nkhondo imene inawononga Chilumba cha ku Balkan kuyambira mu 1991 mpaka 1995. Izi zinachotseratu chiyembekezo chakuti anthu angabweretse moyo wabwino ndi wopanda mavuto. Chifukwa cha nkhondo, anthu a m’dziko limene kale linali Yugoslavia ali pamavuto a zachuma ndiponso paumphaŵi wadzaoneni. *

Chifukwa chakuti kuli mavuto otereŵa, munthu sangayembekezere kupezako anthu achimwemwe. Koma ngakhale kuti zingaoneke zodabwitsa, anthu otereŵa aliko. Ndipo chakumapeto kwa m’ma 1900 anali ndi tsiku losangalala mwapadera. Kodi kusangalala kumeneku kunam’khudza bwanji Franz Brand, mnyamata amene tam’tchula kumayambiriro kwa nkhani ino uja?

Kuwonjezereka Kwauzimu ku Mayiko a ku Balkan

Franz Brand anasangalala ndi choonadi chatsopano chimene anamva ndipo anaganiza zofalitsa uthenga wabwino. Anapeza ntchito yometa anthu tsitsi ku Maribor, tauni ya ku Slovenia pafupi ndi malire a Austria, ndipo anayamba kulalikira kwa makasitomala ake, amene nthaŵi zambiri ankangokhala duu kumamvetsera uku akuwameta. Chifukwa cha kulimbikira kwake, kumapeto kwa m’ma 1920, ku Maribor kunali kagulu ka olengeza Ufumu. Nkhani za Baibulo ankakambira mu resitilanti, imene nthaŵi ina moyenerera inatchedwa kuti Lesitilanti ya Dziko Latsopano Yodyeramo Nsomba.

Patapita nthaŵi, uthenga wabwino unafalikira m’dera lonselo. “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe” (la maola asanu ndi atatu la mafilimu, zinthunzi zoyendayenda ndi nyimbo) linali lothandiza kwambiri pa kuwonjezeka kumeneku. Ndiyeno cha m’ma 1930, Mboni za Yehova zili pachizunzo chachikulu ku Germany, apainiya a ku Germany othaŵa kwawo analimbikitsa Mboni za ku Kingdom of Yugoslavia. Anasiya zinthu zabwino kapena zapamwamba, n’kupita kukalalikira ku madera akutali kwambiri a dziko la mapiri limeneli. Poyamba zinkaoneka ngati anthu kumeneko sakulabadira kwenikweni uthenga wawo. Kuchiyambi kwa m’ma 1940, ofalitsa 150 okha ndi amene anapereka malipoti a muutumiki wakumunda.

Mu 1941, panabuka chizunzo choopsa, chimene chinafika mpaka mu 1952. Zinali zosangalatsa kwambiri pamene Mboni za Yehova zinalembetsa mwalamulo mu ulamuliro Wachikomyunizimu wa Kazembe Tito, pa September 9, 1953. Chaka chimenecho, panali ofalitsa uthenga wabwino okwana 914, ndipo chiŵerengerocho chinkakulirakulira. Podzafika mu 1991, chiŵerengero cha ofalitsa chinakula kufika 7,420, ndipo chaka chimenecho pa Chikumbutso panali anthu 16,072.

Kuyambira pa August 16 mpaka pa August 18, 1991, msonkhano woyamba wa mayiko wa Mboni za Yehova m’dziko limeneli unachitikira mu mzinda wa Zagreb, ku Croatia. Panali anthu 14,684 a m’dziko limeneli ndi a m’mayiko ena. Msonkhano wosaiwalika umenewu unathandiza anthu a Yehova kukonzekera ziyeso zimene zinali kudza. Mabasi amene ananyamula nthumwi za ku Serbia pobwerera kwawo anali m’gulu la mabasi ndi magalimoto amene anali omalizira kudutsa malo ofufuzira katundu m’malire a dziko la Croatia ndi Serbia. Basi yomaliza itadutsa pamaloŵa, anatseka njirayo ndipo nkhondo inayambika.

Mpake Anthu a Yehova Kusangalala

Panthaŵi ya nkhondo, Mboni za Yehova za ku mayiko a ku Balkan zinali pachiyeso kwabasi. Komabe, anafunika kusangalala chifukwa Yehova anadalitsa anthu ake kumeneko ndi kuwonjezeka kwambiri. Kuyambira mu 1991, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu m’dera limene kale linali Yugoslavia chawonjezeka ndi anthu oposa 80 peresenti. Chaka chautumiki cha 2001 chinali ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa okwana 13,472.

Maofesi a mumzinda wa Zagreb ndi Belgrade (Serbia) ankayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova m’dziko lonse limene kale linali Yugoslavia. Chifukwa cha kuwonjezeka kwa anthu ndiponso kusintha kwa ndale, kunali kofunika kutsegula maofesi atsopano mu mzinda wa Ljubljana (Slovenia), ndi Skopje (Macedonia), komanso kupeza ena mu mzinda wa Belgrade ndi Zagreb. Pafupifupi anthu 140 amagwira ntchito m’maofesi ameneŵa. Ambiri mwa anthu ameneŵa ndi achinyamata achangu zedi komanso okonda Yehova. Chiŵerengero chabwino ndithu pa anthu ameneŵa, amagwira ntchito yomasulira mabuku othandizira kuphunzira Baibulo mu Chikroati, Chimakedoniya, Chisebiya, ndi Chisiloveniya. Chosangalatsa n’chakuti magazini ndi mabuku ambiri a Mboni za Yehova a m’zinenero zimenezi amatulukira limodzi ndi a Chingelezi. Zofalitsa zimenezi zimathandiza anthu ambiri kupeza chilimbikitso ndi kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo.

Chifukwa chinanso chosangalalira chinali thandizo losaumira limene atumiki ambiri anthaŵi zonse a m’mayiko ena anapereka. M’zaka zaposachedwapa amanga Nyumba za Ufumu zingapo zokongola, zimene zawonjezeranso chisangalalo cha anthu m’mipingo. Komabe, panali china chosangalatsa kwambiri chimene chinali kubwera. Kodi zikanatheka bwanji?

Ntchito Yapadera

Kaŵirikaŵiri ofalitsa ambiri ankafunsa kuti, ‘Kodi tidzakhala ndi Baibulo la New World Translation m’chinenero chathu?’ Chaka chilichonse pamsonkhano wachigawo ankadikira mwachidwi kumva chilengezo chimenechi. Komabe, kodi chintchito chimenechi chikanatheka bwanji, popeza anthu omasulira a zinenero zimenezi anali atangotha zaka zochepa akugwira ntchitoyi ndiponso anali ochepa chabe?

Bungwe Lolamulira litaona mmene zinthu zinalili, linavomereza kuti anthu omasulira m’Chikroati, Chimakedoniya ndi Chisebiya agwirire ntchitoyi pamodzi kuti apindule ndi maganizo a anzawo. Anthu omasulira m’Chikroati ndi amene anatsogolera ntchitoyi.

Tsiku Losangalala

Pa July 23, 1999 ndi tsiku losaiwalika kwa Mboni za Yehova za ku mayiko a ku Balkan. Misonkhano Yachigawo yakuti “Mawu a Ulosi a Mulungu” inachitika nthaŵi imodzi ku Belgrade, Sarajevo (Bosnia-Herzegovina), Skopje ndi Zagreb. Kwa kanthaŵi ndithu zinkakayikitsa ngati msonkhano wa ku Belgrade unali kudzachitika chifukwa pamene a bungwe la NATO anali kuphulitsa mabomba, sankaloleza kuchita msonkhano uliwonse. Abale anasangalala kwambiri kuyembekezera kudzasonkhana pamodzi patatha miyezi ingapo zikukayikitsa kuti zimenezi zingachitike. Komabe, zimene zinachitika zinaposa zimene ankayembekezera.

Lachisanu masana pa malo anayi onsewa panali chilengezo chapadera. Nthumwi zonse 13,497 zinangoti zii kudikira kuti kubwera zotani. Wokamba nkhani atalengeza kuti kwatuluka Baibulo la New World Translation la Malemba Achigiriki Achikristu la Chikroati ndi Chisebiya, komanso atanena kuti ntchito yomasulira Baibulo la Chimakedoniya ikuyenda bwino, nthumwizo zinalephera kungokhala chete. Anthu anaomba m’manja kwambiri moti wokamba nkhani analephera kumaliza chilengezocho. Pamsonkhano wa ku Sarajevo, atalengeza kuti atulutsa mabaibuloŵa anthu anangoti zii, chifukwa anali odabwa zedi. Kenako anawomba m’manja kwanthaŵi yaitali. M’masaya a anthu ambiri ku Belgrade munali kuyenderera misozi chifukwa chachimwemwe, ndipo kuwomba m’manja mosaleka kunadodometsa wokamba nkhaniyo kumaliza chilengezocho. Aliyense analitu wosangalala.

Mphatso imeneyi anaiyamikira kwambiri chifukwa chakuti Mboni za Yehova zinapeza chilolezo chosindikiza mabaibulo a Chikroati komanso a Chisebiya. Choncho, Baibulo lililonse la New World Translation la Malemba Achigiriki Achikristu m’zinenero ziŵirizi, analiphatikiza ndi Malemba Achihebri a chinenero chomwecho kukhala buku limodzi. Komanso, Baibulo la Chisebiya analisindikiza m’zilembo za Chiromani ndi Chisililiki.

Anthu a Yehova ku mayiko a ku Balkan poyamikira madalitso ndi malangizo onse amene analandira, akugwirizana kwambiri ndi mawu a Davide akuti: “Ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa; pakuti Inu [Yehova] muli ndi ine.” Ngakhale akupitiriza kukumana ndi mavuto, atsimikiza mtima kupanga ‘Yehova mphamvu yawo.’​—Salmo 23:4; Nehemiya 8:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dziko limene kale linali Yugoslavia linali ndi mayiko aŵa: Bosnia-Herzegovina, Croatia, Macedonia, Montenegro, Serbia ndi Slovenia.

[Chithunzi patsamba 20]

Gulu loyamba la ofalitsa lochokera ku Maribor, ku Slovenia, kulalikira ku gawo lakutali