Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akristu Osaloŵerera M’zinthu za Dziko M’masiku Otsiriza

Akristu Osaloŵerera M’zinthu za Dziko M’masiku Otsiriza

Akristu Osaloŵerera M’zinthu za Dziko M’masiku Otsiriza

“Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.”​—YOHANE 17:16.

1, 2. Kodi Yesu anati chiyani za ubale wa otsatira ake ndi dziko lapansi, ndipo mawu akewo akudzutsa mafunso otani?

YESU pa usiku womaliza wa moyo wake monga munthu wangwiro, anapereka pemphero lalitali ophunzira ake akumva. M’pemphero limenelo, iye anafotokoza chinthu china chimene chimasonyeza mmene moyo wa Akristu onse oona uyenera kukhalira. Polankhula za otsatira ake, iye anati: “Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.”​—Yohane 17:14-16.

2 Yesu ananena kaŵiri konse kuti otsatira ake sali a dziko lapansi. Ndiponso, kusiyana ndi dziko kumeneko kudzayambitsa udani, dziko lidzawada. Komabe, Akristu safunika kuchita mantha. Yehova adzawayang’anira. (Miyambo 18:10; Mateyu 24:9, 13) Poona zimene Yesu ananena, tingafunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani Akristu oona sali mbali ya dziko lapansi? Kodi kusakhala mbali ya dziko lapansi kumatanthauza chiyani? Ngati Akristu akudedwa ndi dziko lapansi, kodi amaliona bwanji dzikoli? Makamaka, kodi amawaona bwanji maboma a dziko lapansi?’ Mayankho a m’Malemba a mafunso ameneŵa ndi ofunika kwambiri chifukwa akutikhudza tonsefe.

“Tili Ife Ochokera mwa Mulungu”

3. (a) Kodi n’chiyani chimatichititsa kusiyana ndi dziko lapansi? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti dziko lapansi “ligona mwa woipayo”?

3 Chimodzi mwa zifukwa zimene sitili mbali ya dziko lapansi ndicho ubwenzi wathu wapamtima ndi Yehova. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mawu a Yohane onena za dziko lapansi akuonekeratu kuti ndi oona. Nkhondo, umbanda, nkhanza, kuponderezana, chinyengo, ndi chiwerewere zimene zafala masiku ano zikupereka umboni wa mphamvu za Satana osati za Mulungu. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4; Aefeso 6:12) Munthu akakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, sangachite kapena kugwirizana nazo zinthu zoipa zimenezi, ndipo zimenezo zimamuchititsa kusakhala mbali ya dziko lapansi.​—Aroma 12:2; 13:12-14; 1 Akorinto 6:9-11; 1 Yohane 3:10-12.

4. Kodi timasonyeza m’njira zotani kuti ndife a Yehova?

4 Yohane ananena kuti Akristu, ‘ali ochokera kwa Mulungu,’ mosiyana ndi dziko lapansi. Onse amene amadzipatulira kwa Yehova amakhala a iye. Mtumwi Paulo anati: “Tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.” (Aroma 14:8; Salmo 116:15) Popeza ndife a Yehova, timam’lambira iye yekha basi. (Eksodo 20:4-6) Motero, Mkristu woona sapereka moyo wake ku zinthu za dziko lapansi. Ndipo ngakhale kuti amalemekeza zizindikiro za dziko, sazilambira kaya mwa kuchitapo kanthu kapena chamumtima. Salambira akatswiri a maseŵero kapena mafano ena amakono. N’zoona kuti amalemekeza ufulu wa ena wochita zimene akufuna, koma iye amalambira Mlengi yekha basi. (Mateyu 4:10; Chivumbulutso 19:10) Zimenezinso zimam’siyanitsa ndi dziko lapansi.

“Ufumu Wanga Suli wa Dziko Lino Lapansi”

5, 6. Kodi kugonjera ku Ufumu wa Mulungu kumatisiyanitsa bwanji ndi dziko lapansi?

5 Akristu amatsatira Yesu Kristu ndipo ndi nzika za Ufumu wa Mulungu, zimenenso zimawachititsa kusakhala mbali ya dziko lapansi. Pamene Yesu anali kuimbidwa mlandu pamaso pa Pontiyo Pilato, iye anati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:36) Kudzera mu Ufumu umenewu, dzina la Yehova lidzayeretsedwa, adzatsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira, ndiponso chifuniro chake chidzachitika padziko lapansi monga kumwamba. (Mateyu 6:9, 10) Muutumiki wake wonse, Yesu analalikira uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo ananena kuti udzalalikidwa ndi otsatira ake mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Mateyu 4:23; 24:14) Mu 1914, mawu aulosi a pa Chivumbulutso 11:15 anakwaniritsidwa. Mawuwo amati: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” Tsiku lina posachedwapa, Ufumu wakumwamba umenewo udzakhala wokhawo umene udzalamulira anthu. (Danieli 2:44) Panthaŵi ina yake, ngakhale olamulira a dziko lapansi adzakakamizika kuvomereza ulamuliro wake.​—Salmo 2:6-12.

6 Poganizira zimenezi, Akristu oona masiku ano ali nzika za Ufumu wa Mulungu, ndipo amatsatira malangizo a Yesu oti apitirize ‘kuthanga afuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Zimenezo sizimawachititsa kusagonjera ku dziko limene akukhalamo koma zimawasiyanitsa mwauzimu ndi dzikoli. Ntchito yaikulu ya Akristu masiku ano, monga mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, ndiyo “kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu.” (Machitidwe 28:23) Palibe boma la anthu lililonse limene lili ndi ufulu wolepheretsa ntchito yoperekedwa ndi Mulungu imeneyi.

7. N’chifukwa chiyani Akristu oona saloŵerera m’zinthu za dziko, ndipo asonyeza bwanji zimenezi?

7 Mogwirizana ndi kukhala kwawo a Yehova ndi kutsatira kwawo Yesu ndiponso kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova sizinaloŵerere m’nkhondo zapachiweniweni ndi nkhondo za mayiko za m’zaka za m’ma 1900 ndi m’ma 2000. Izo sizinathandizire mbali iliyonse, sizinatenge zida zankhondo kumenyana ndi wina aliyense, ndipo sizinadziloŵetse m’manenanena okhudza nkhani za dzikoli. Posonyeza mwapadera chikhulupiriro chawo ngakhale zikumane ndi udani wooneka ngati wosapiririka, izo zatsatira mfundo zimene zinafotokoza kwa olamulira a chipani cha Nazi ku Germany mu 1934 kuti: “Ife sitiloŵerera mu nkhani za ndale, koma tadzipatulira ndi mtima wonse ku ufumu wa Mulungu umene Kristu ndiye Mfumu yake. Sitidzavulaza wina aliyense. Tingakonde kukhala mumtendere ndi kuchitira anthu onse zabwino tikakhala ndi mpata wotero.”

Akazembe ndi Nthumwi za Kristu

8, 9. Kodi ndi m’njira ziti zimene Mboni za Yehova masiku ano zilili akazembe ndi nthumwi, ndipo kodi zimenezi zimakhudza bwanji mmene zimachitira ndi mayiko?

8 Paulo anafotokoza kuti iye pamodzi ndi Akristu anzake odzozedwa anali “atumiki [“akazembe,” NW] m’malo mwa Kristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife.” (2 Akorinto 5:20; Aefeso 6:20) Kuyambira mu 1914, Akristu odzozedwa ndi mzimu moyenera angatchedwe akazembe a Ufumu wa Mulungu, umene iwo ndiwo “ana” ake. (Mateyu 13:38; Afilipi 3:20; Chivumbulutso 5:9, 10) Ndiponso, Yehova wasonkhanitsa mwa amitundu “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” Akristu amene akuyembekezera kudzakhala pa dziko lapansi, kuti athandize ana odzozedwa m’ntchito yawo yaukazembe. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) “Nkhosa zina” zimenezi zingatchedwe “nthumwi” za Ufumu wa Mulungu.

9 Kazembe ndi ogwira ntchito mu ofesi yake saloŵerera nkhani za m’dziko limene akugwira ntchito. Mofananamo, Akristu saloŵerera m’nkhani za ndale za mayiko. Iwo sakhalira mbali kapena kutsutsana ndi dziko lililonse, fuko lililonse, chikhalidwe chilichonse, kapena gulu lililonse la zachuma. (Machitidwe 10:34, 35) M’malo mwake, iwo ‘amachitira onse chokoma.’ (Agalatiya 6:10) Popeza Mboni za Yehova siziloŵerera m’zinthu za dzikoli, palibe amene angakane uthenga wawo n’kumati akutero chifukwa chakuti izo zikugwirizana ndi fuko, dziko, kapena mtundu umene ukutsutsana ndi unzake.

Amadziŵika ndi Chikondi

10. Kodi chikondi n’chofunika bwanji kwa Mkristu?

10 Kuwonjezera pa zimene takambiranazi, Akristu saloŵerera m’zinthu za dzikoli chifukwa cha ubale wawo ndi Akristu ena. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chikondi cha pa abale ndicho mbali yofunika kwambiri yokhalira Mkristu. (1 Yohane 3:14) Ubale wa Mkristu ndi Akristu ena ndi wapamtima monga mmene ulili ubale wake ndi Yehova ndi Yesu. Sangokonda anthu a mumpingo wake wokha ayi. Amakondanso “abale [ake onse] ali m’dziko.”​—1 Petro 5:9.

11. Kodi kukondana kwa Mboni za Yehova kwakhudza bwanji khalidwe lawo?

11 Masiku ano, Mboni za Yehova zimasonyeza kukonda abale mwa kukwaniritsa mawu a pa Yesaya 2:4 akuti: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Molangizidwa ndi Yehova, Akristu oona ali pamtendere ndi Mulungu ndiponso wina ndi mnzake. (Yesaya 54:13) Popeza amakonda Mulungu ndi abale awo, sanganyamule zida za nkhondo kumenyana ndi Akristu anzawo, kapena wina aliyense, m’mayiko ena. Mtendere pamodzi ndi mgwirizano wawo ndi mbali yofunika kwambiri ya kulambira kwawo, zimene zimasonyeza kuti alidi ndi mzimu wa Mulungu. (Salmo 133:1; Mika 2:12; Mateyu 22:37-39; Akolose 3:14) Iwo ‘amafuna mtendere ndi kuulondola,’ podziŵa kuti “maso a Yehova ali pa olungama mtima.”​—Salmo 34:14, 15.

M’mene Akristu Amaonera Dzikoli

12. Kodi Yehova amawasonyeza chiyani anthu m’dzikoli zimene Mboni za Yehova zimatsanzira, ndipo zimachita bwanji zimenezo?

12 Yehova wanena kuti adzaweruza dziko lapansili, koma sanaweruzebe munthu aliyense payekha m’dzikoli. Adzachita zimenezo kudzera mwa Yesu pa nthaŵi Yake yoikika. (Salmo 67:3, 4; Mateyu 25:31-46; 2 Petro 3:10) Panopo, iye amasonyeza chikondi chachikulu kwa anthu. Iye anapereka ngakhale Mwana wake wobadwa yekha kuti aliyense akhale ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16) Ife monga Akristu, timatsanzira chikondi cha Mulungu mwa kuuza ena za makonzedwe a Mulungu a chipulumutso, ngakhale kuti anthu ambiri samvera zimene timawauza.

13. Kodi tiziwaona bwanji olamulira a dzikoli?

13 Kodi olamulira a dzikoli tiziwaona bwanji? Paulo anayankha funso limenelo pamene analemba kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.” (Aroma 13:1, 2) Anthu ali ndi ulamuliro (wokulirapo kapena wocheperapo kwa wina ndi mnzake, koma nthaŵi zonse wochepa kwambiri kwa Yehova), chifukwa Wamphamvuyonse wawalola kuti akhale nawo. Mkristu amagonjera maulamuliro a dziko chifukwa imeneyo ndi mbali ina ya kumvera kwake Yehova. Koma bwanji ngati pakhala kusagwirizana pakati pa zimene Mulungu amafuna ndi zimene boma la anthu likufuna?

Lamulo la Mulungu Ndiponso la Kaisara

14, 15. (a) Kodi Danieli anatani kuti apeŵe kusagwirizana pankhani ya kumvera? (b) Kodi Ahebri atatu anachita chiyani pamene kusagwirizana pankhani ya kumvera sikukanapeŵeka?

14 Danieli ndi anzake atatu anapereka chitsanzo chabwino cha mmene tingagwirizanitsire kugonjera maboma a anthu ndi kugonjera Mulungu. Pamene Ahebri achinyamata amenewo anali ku ukapolo ku Babulo, anali kumvera malamulo a m’dzikolo ndipo posakhalitsa anawasankha kuti awaphunzitse mwapadera. Danieli atazindikira kuti maphunzirowo mwachionekere akanatsutsana ndi Lamulo la Yehova, anakambirana nkhaniyo ndi mkulu amene anali kuwayang’anira. Zotsatira zake zinali zakuti anapanga makonzedwe apadera pofuna kulemekeza zikumbumtima za Ahebri anayiwo. (Danieli 1:8-17) Mboni za Yehova zimatsanzira chitsanzo cha Danieli pamene zimafotokoza mosamala maganizo awo kwa akuluakulu a boma pofuna kupeŵa mavuto.

15 Komabe ulendo wina, kusagwirizana pankhani ya kugonjera sikukanapeŵeka. Mfumu ya ku Babulo inaimika fano lalikulu m’chigwa cha Dura ndipo inalamula akuluakulu a boma, kuphatikizapo olamulira a madera, kudzasonkhana popatulira fanolo. Panthaŵi imeneyi, anzake atatu a Danieli anali ataikidwa kukhala olamulira a madera ku Babulo, motero lamuloli linawakhudza. Panthaŵi ina mwambowo uli m’kati, onse osonkhanawo anafunika kugwadira fanolo. Koma Ahebriwo anadziŵa kuti kuchita zimenezo kudzakhala kuswa lamulo la Mulungu. (Deuteronomo 5:8-10) Motero pamene onse anagwada, iwo anangoima. Mwa kusamvera lamulo la mfumu, iwo analolera kufa mochititsa mantha, ndipo anangopulumuka mozizwitsa; komabe anasankha kufa m’malo mwa kusamvera Yehova.​—Danieli 2:49–3:29.

16, 17. Kodi atumwi anati chiyani atalamulidwa kuti asiye kulalikira, ndipo n’chifukwa chiyani anatero?

16 M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, atumwi a Yesu Kristu anawaitana kukaonekera pamaso pa atsogoleri achiyuda ku Yerusalemu ndipo anawalamula kuti asiye kulalikira m’dzina la Yesu. Kodi atamva zimenezo anatani? Yesu anali atawalamula kuti apange ophunzira m’mitundu yonse, zimene zinaphatikizaponso ku Yudeya. Anawauzanso kuti akhale mboni zake mu Yerusalemu ndi padziko lonse lapansi. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Atumwiwo ankadziŵa kuti zimene Yesu anawalamula zinaimira zimene Mulungu ankafuna kwa iwo. (Yohane 5:30; 8:28) Motero, iwo anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 4:19, 20; 5:29.

17 Atumwiwo sanali kuukira. (Miyambo 24:21) Komabe, pamene olamulira a anthu anawaletsa kuchita chifuniro cha Mulungu, iwo anayenera kunena kuti, ‘Tiyenera kumvera Mulungu osati munthu.’ Yesu ananena kuti tiyenera ‘kupereka zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.’ (Marko 12:17) Ngati sitimvera lamulo la Mulungu chifukwa chakuti munthu wina watiuza kuti tisamvere, ndiye kuti tikupereka kwa munthu zimene tinayenera kupereka kwa Mulungu. M’malo mwake, timapereka kwa Kaisara zonse zimene tikufunikira kupereka kwa iye, koma timazindikira kuti Yehova ndiye ali ndi ulamuliro waukulu. Iye ndi wolamulira wa chilengedwe chonse, Mlengi, kumene kumachokera ulamuliro wonse.​—Chivumbulutso 4:11.

Tidzachirimikabe

18, 19. Kodi abale athu ambiri achirimika motani, ndipo tingatsanzire bwanji chitsanzo chawo?

18 Pakalipano, maboma ambiri amadziŵa kuti Mboni za Yehova siziloŵerera m’zochitika za dziko, ndipo timayamikira chifukwa cha zimenezo. Komabe, m’mayiko ena, Mboni zatsutsidwa kwadzaoneni. M’zaka zonse za m’ma 1900 mpaka kudzafika pakalipano, abale ndi alongo athu ena alimbika mwamphamvu, kumenya mwauzimu “nkhondo yabwino yachikhulupiriro.”​—1 Timoteo 6:12.

19 Kodi tingachirimike bwanji monga mmene iwo achitira? Choyamba timakumbukira kuti tiyenera kuyembekezera kuti ena adzatitsutsa. Tisachite mantha kapena ngakhale kudabwa ngati titsutsidwa. Paulo anachenjeza Timoteo kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12; 1 Petro 4:12) M’dziko lino limene Satana akulamulira, zingatheke bwanji kusakumana ndi chitsutso? (Chivumbulutso 12:17) Ngati tili okhulupirika, nthaŵi zonse padzakhala ena amene ‘adzayesa chachilendo, natichitira mwano.’​—1 Petro 4:4.

20. Kodi tikukumbutsidwa mfundo zolimbikitsa ziti?

20 Chachiŵiri, tikukhulupirira kuti Yehova ndi angelo ake adzatithandiza. Monga mmene Elisa wakale ananenera, “okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” (2 Mafumu 6:16; Salmo 34:7) Zingakhale kuti Yehova, pa zifukwa zake zabwino, akulola adani kutivutitsa kwa kanthaŵi. Komabe, iye nthaŵi zonse adzatipatsa mphamvu zimene tikufunikira kuti tipirire. (Yesaya 41:9, 10) Ena aphedwa, koma zimenezo sizikutichititsa mantha. Yesu anati: “Musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.” (Mateyu 10:16-23, 28) Ndife “ogonera” chabe m’dongosolo lino la zinthu. Timagwiritsira ntchito nthaŵi yathu kuti ‘tigwire moyo weniweniwo,’ moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Petro 2:11; 1 Timoteo 6:19) Palibe munthu amene angatilande mphoto imeneyo ngati tikhalabe okhulupirika kwa Mulungu.

21. Kodi nthaŵi zonse tizikumbukira chiyani?

21 Motero, tiyeni tikumbukire ubale wamtengo wapatali umene tili nawo ndi Yehova Mulungu. Tiyeni nthaŵi zonse tiyamikire phindu lokhala otsatira a Kristu ndi nzika za Ufumu. Tiyeni ndi mtima wonse tikonde abale athu, ndipo nthaŵi zonse tikondwere ndi kutikonda kwawo. Koposa zonse, tiyeni timvere mawu a wamasalmo akuti: “Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.” (Salmo 27:14; Yesaya 54:17) Tikatero, monga mmene anachitira Akristu ambirimbiri ife tisanakhaleko, tidzachirimikabe tikutsimikizira zimene tikuyembekezera. Tidzakhalabe Akristu okhulupirika osaloŵerera m’zinthu za dziko, amene sitili mbali ya dziko lapansi.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi ubale wathu ndi Yehova umatisiyanitsa bwanji ndi dzikoli?

• Monga nzika za Ufumu wa Mulungu, kodi timatani kuti tisaloŵerere m’zinthu za dzikoli?

• Kodi ndi m’njira zotani zimene kukonda abale athu kumatichititsa kusaloŵerera m’zinthu za dzikoli, kukhala osiyana ndi dziko?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi kugonjera kwathu Ufumu wa Mulungu kumakhudza bwanji mmene timachitira ndi dzikoli?

[Chithunzi patsamba 16]

Mhutu ndi Mtutsi akugwirira ntchito limodzi mosangalala

[Chithunzi patsamba 17]

Myuda ndi Mwarabu omwe ndi abale achikristu

[Chithunzi patsamba 17]

Akristu a ku Serbia, Bosnia, ndi ku Croatia ali limodzi

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati olamulira atiuza kuti tiswe lamulo la Mulungu?