Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Othandiza Kulambira Koona Akale ndi Amasiku Ano

Anthu Othandiza Kulambira Koona Akale ndi Amasiku Ano

Anthu Othandiza Kulambira Koona Akale ndi Amasiku Ano

KODI mukukumbukira dzina la munthu amene analilira mzinda wakale wa Yerusalemu? Mwina munganene kuti ‘Yesu,’ ndipotu n’zoona, Yesu anachitadi zimenezo. (Luka 19:28, 41) Komabe, zaka zambirimbiri Yesu asanabwere padziko lapansi, mtumiki wina wokhulupirika wa Mulungu anauliliranso chimodzimodzi mzinda wa Yerusalemu. Dzina lake anali Nehemiya.​—Nehemiya 1:3, 4.

Kodi n’chiyani chinachititsa Nehemiya kumva chisoni motero mpaka kufika polilira Yerusalemu? Kodi anachita chiyani chimene chinapindulitsa mzindawo ndi anthu amene anali m’menemo? Ndipo tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyeni tione zina mwa zinthu zimene zinachitika m’nthaŵi yake.

Munthu Wokhudzidwa Mtima Kwambiri Ndiponso Wochitapo Kanthu Mofulumira

Nehemiya anaikidwa kukhala kazembe wa Yerusalemu, koma zimenezi zisanachitike, iye anali ndi udindo waukulu m’nyumba ya mfumu ya ku Perisiya mumzinda wa Susani. Komabe, moyo wake wapamwamba sunamulepheretse kuganizira moyo wa abale ake achiyuda amene anali kutali ku Yerusalemu. Ndipotu, chinthu choyamba chimene anachita pamene Ayuda ena anabwera ku Susani kuchokera ku Yerusalemu chinali ‘kuwafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu.’ (Nehemiya 1:2) Pamene alendowo ananena kuti anthu ku Yerusalemu “akulukutika kwakukulu” ndi kuti linga la mzinda “lapasuka,” Nehemiya ‘anakhala pansi ndi kulira misozi ndi kuchita maliro masiku ena.’ Atatero anafotokoza chisoni chake m’pemphero lochokera pansi pa mtima kwa Yehova. (Nehemiya 1:3-11) N’chifukwa chiyani Nehemiya anali ndi chisoni chotero? Chifukwa chakuti mzinda wa Yerusalemu unali likulu la kulambira Yehova padziko lapansi, ndipo unali utanyalanyazidwa. (1 Mafumu 11:36) Ndiponso, kupasuka kwa mzindawo kunasonyeza kuti moyo wauzimu wa anthu okhala mmenemo unali wofooka.​—Nehemiya 1:6, 7.

Nehemiya anadera nkhaŵa kwambiri Yerusalemu ndi kuchitira chifundo Ayuda amene anali kukhala mmenemo ndipo zimenezi zinamuchititsa kudzipereka kuti awatumikire. Mfumu ya ku Perisiya itangomulola kusiya ntchito yake kwakanthaŵi kuti apite, Nehemiya anayamba kukonzekera ulendo wautali wa ku Yerusalemu. (Nehemiya 2:5, 6) Anafuna kugwiritsira ntchito mphamvu zake, nthaŵi yake, ndi luso lake pofuna kuthandiza ntchito yokonza imene inafunikira. M’masiku ochepa chabe atafika, anakonzeratu mapulani okonza linga lonse la Yerusalemu.​—Nehemiya 2:11-18.

Nehemiya anagaŵa ntchito yaikulu yokonza lingalo kwa mabanja ambiri, omwe onse anali kugwirira ntchito limodzi. * Magulu oposa 40 anapatsidwa kukonza “gawo” limodzi gulu lililonse. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Popeza panali antchito ambiri, kuphatikizapo makolo amene anali kugwirira ntchito limodzi ndi ana awo, pogwiritsira ntchito nthaŵi ndi mphamvu zawo, ntchito imene inaoneka ngati yosatheka, inatheka. (Nehemiya 3:11, 12, 19, 20) M’miyezi iŵiri imene anagwira ntchito yadzaoneni, linga lonse linakonzedwa. Nehemiya analemba kuti ngakhale anthu amene ankadana ndi ntchito yokonzayo anakakamizika kuvomereza kuti “ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.”​—Nehemiya 6:15, 16.

Chitsanzo Chofunika Kuchikumbukira

Nehemiya anathandizira m’zinthu zambiri kuwonjezera pa kugwiritsira ntchito nthaŵi yake ndi luso lake lolinganiza zinthu. Anagwiritsiranso ntchito chuma chake pothandizira kulambira koona. Anagwiritsira ntchito ndalama zake kugula abale ake achiyuda kuukapolo. Anakongoletsa ndalama zake popanda chiwongola dzanja. Iye ‘sanalemetsa’ Ayuda mwa kuwauza kuti azimulipira monga kazembe, zomwe anayenerera kuchita. M’malo mwake, iye kunyumba kwake ankalandira ndi kudyetsa “amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.” Tsiku lililonse ankapereka “ng’ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi . . . [ndi] nkhuku” kwa alendo ake. Kuwonjezera pamenepo, kamodzi pa masiku khumi alionse, iye ankawapatsa “vinyo wambiri wamitundumitundu,” zonsezi ankatero pogwiritsira ntchito ndalama za m’thumba mwake.​—Nehemiya 5:8, 10, 14-18.

Ndi chitsanzo chabwinotu kwambiri cha kuwoloŵa manja chimene Nehemiya anapereka kwa atumiki onse a Mulungu a nthaŵi imeneyo ndiponso a masiku ano! Mtumiki wa Mulungu wolimba mtima ameneyu anagwiritsira ntchito chuma chake mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse pothandiza antchitowo kuti apititse patsogolo kulambira koona. Iye moyenerera anapempha Yehova kuti: ‘Mukumbukire Mulungu, zokoma zonse ndinachitira anthu awa.’ (Nehemiya 5:19) Inde Yehova adzachitadi zimenezo.​—Ahebri 6:10.

Chitsanzo cha Nehemiya Chikutsatiridwa Masiku Ano

N’zosangalatsa kuona kuti anthu a Yehova masiku ano akusonyeza chikondi chimodzimodzicho, kufuna ndi mtima wonse kuchitapo kanthu, ndi kusonyeza mtima wodzipereka pofuna kuthandizira kulambira koona. Tikamva kuti okhulupirira anzathu akuvutika, timakhudzidwa kwambiri ndi za umoyo wawo. (Aroma 12:15) Monga anachitira Nehemiya, timapemphera kwa Yehova pothandiza abale athu ovutikawo, kumupempha kuti: “Mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu.”​—Nehemiya 1:11; Akolose 4:2.

Komabe, kudera nkhaŵa kwathu moyo wauzimu ndi wakuthupi wa abale athu achikristu ndiponso kupititsa patsogolo kulambira koona sikumangotikhudza malingaliro okha. Kumatichititsanso kuchitapo kanthu. Amene angathe kutero, chikondi chimawalimbikitsa kusiya moyo wapamwamba wa kwawo ndipo, monga anachitira Nehemiya, amapita ku madera ena kukathandiza amene akufunikira thandizo. Anthu odzipereka oterowo amathandiza kupititsa patsogolo kulambira koona, kutumikira limodzi ndi abale awo achikristu mosadodometsedwa ndi moyo wovutirapo wa m’madera amenewo. Mtima wodzipereka umene amasonyeza umayamikiridwa kwambiri.

Kuchita Mbali Yathu M’dera Lathu

N’zomveka kuti ambirife sitingathe kupita ku dera lina. Timathandizira kulambira koona m’dera lathu. Zimenezo tikuzionanso m’buku la Nehemiya. Taonani mfundo zatsatanetsatane zimene Nehemiya akuwonjezera za mabanja ena okhulupirika amene anagwira nawo ntchito yokonza. Analemba kuti: ‘Yedaya mwana wa Harumafi, anakonza pandunji pa nyumba yake. Benjamini ndi Hasubi anakonza pandunji pa nyumba pawo. Potsatizana nawo anakonza Azariya mwana wa Maseya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake.’ (Nehemiya 3:10, 23, 28-30) Amuna amenewo ndi mabanja awo anathandiza kwambiri kupititsa patsogolo kulambira koona mwa kuchita mbali yawo pantchito yokonza pafupi ndi nyumba zawo.

Masiku ano, ambirife timathandizira kulambira koona m’dera lathu m’njira zosiyanasiyana. Timagwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, kuthandiza nawo pakagwa masoka, ndipo koposa zonse, timagwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu. Ndiponso, kaya timagwira nawo ntchito yomanga kapena yothandiza pamasoka ife eni kapena ayi, tonsefe timafuna ndi mtima wonse kuthandiza kulambira koona ndi chuma chathu, monga mmene Nehemiya anachitira mooloŵa manja m’nthaŵi yake.​—Onani bokosi lakuti “Kaperekedwe Kaufulu.”

Kupeza ndalama zofunika kulipirira ntchito yathu yosindikiza mabuku imene ikukulirakulira, kuthandiza pa masoka, ndi ntchito zina zambirimbiri zimene zikuchitika padziko lonse, nthaŵi zina kungaoneke ngati n’kosatheka. Komabe kumbukirani kuti ntchito yokonza linga lalikulu la Yerusalemu inaonekanso ngati yosatheka. (Nehemiya 4:10) Koma popeza ntchitoyo anaigaŵa kwa mabanja odzipereka ambiri, inatheka ndithu. N’chimodzimodzinso masiku ano, kupeza zimene zimafunikira kuti tipitirize kugwira ntchito ya padziko lonse kudzathekabe ngati tonsefe aliyense payekha tipitiriza kuchita mbali yathu pa ntchitoyo.

Bokosi lakuti “Njira Zimene Ena Amasankha Popereka” likusonyeza njira zingapo zimene anthu angathandizire ntchito ya Ufumu popereka ndalama. Chaka chatha, ambiri mwa anthu a Mulungu anathandizira mwa njira imeneyi, ndipo Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likupezerapo mwayi kuyamikira ndi mtima wonse onse amene mtima wawo unawafulumiza kupereka nawo zopereka zaufulu. Koposa zonse, tikuyamika Yehova chifukwa chodalitsa khama lochokera pansi pa mtima la anthu ake popititsa patsogolo kulambira koona padziko lonse. Inde, tikamasinkhasinkha mmene dzanja la Yehova latitsogolerera m’zaka zonsezi, timalimbikitsidwa kuvomereza mawu a Nehemiya, amene moyamikira anati: ‘Dzanja la Mulungu wanga landikhalira mokoma.’​—Nehemiya 2:18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Nehemiya 3:5 akufotokoza kuti Ayuda ena otchuka, anthu “omveka,” anakana kugwira nawo ntchitoyo, koma ndi okhawo amene anatero. Anthu osiyanasiyana, kaya ansembe, osula golidi, osanganiza zonunkhira, akulu a madera, ndiponso amalonda, anathandiza nawo ntchitoyi.​—Mavesi 1, 8, 9, 32.

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 28, 29]

Njira Zimene Ena Amasankha Popereka

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi ya nthambi yakwawo. Mungatumizenso mwachindunji ndalama zopereka modzifunira ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu. Mungaperekenso majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani pamodzi ndi kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo mwapereka monga mphatso yeniyeni.

MAKONZEDWE APADERA A ZOPEREKA

Ndalama zingaperekedwe pa makonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso chifukwa cha vuto linalake, adzam’bwezera zoperekazo. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani ku Accounting Office pa adiresi imene tasonyeza pamwambapa.

KUPATSA KOLINGANIZA

Kuwonjezera pa mphatso zenizeni ndi ndalama zoperekedwa pa makonzedwe apadera, palinso njira zina zoperekera zinthu zopititsa patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zina mwa izo ndi izi:

Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena penshoni.

Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’malonda ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni.

Malo: Malo oti angagulitsidwe angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo amene mwiniwake angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Lankhulani ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu musanakonze pangano la malo alionse.

Chuma Chamasiye: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera m’pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lochitidwa mwalamulo.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri za alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza ameneŵa, lankhulani ndi a Accounting Office patelefoni kapena lemberani ku adiresi imene ili pansipa kapena ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749 Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01762111

[Bokosi patsamba 30]

Kaperekedwe Kaufulu

M’makalata ake kwa Akorinto, mtumwi Paulo anatchula mbali zitatu zofunika kwambiri za kaperekedwe kaufulu. (1) Polemba za kusonkhetsa ndalama, Paulo analangiza kuti: “Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.” (1 Akorinto 16:2a) Motero, kupereka n’kofunika kukonzekera pasadakhale, ndipo kumafunika kuchitika nthaŵi zonse. (2) Paulo analembanso kuti munthu aliyense ayenera kupereka “monga momwe anapindula.” (1 Akorinto 16:2b) M’mawu ena, munthu amene akufuna kupereka nawo mwaufulu angatero mogwirizana ndi m’thumba mwake. Ngakhale Mkristu atamapeza zochepa chabe, ndalama yochepa imene angapereke, Yehova amaiona kukhala yamtengo wapatali. (Luka 21:1-4) (3) Paulo anapitiriza kulemba kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Akristu oona mtima amapereka ndi mtima wonse​—mokondwera.

[Zithunzi patsamba 26]

Nehemiya anali munthu wokhudzidwa mtima ndiponso wochitapo kanthu mofulumira

[Zithunzi patsamba 30]

Zopereka zaufulu zimathandizira pa ntchito yosindikiza mabuku, kuthandiza pa masoka, kumanga Nyumba za Ufumu, ndiponso pa ntchito zina zopindulitsa padziko lonse