Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi sikulakwa kutchova njuga ngati ndalama zobetcherana n’zochepa chabe?

Mawu a Mulungu safotokoza za kutchova njuga mwatsatanetsatane, koma amafotokoza mfundo zokwanira zosonyeza kuti kutchova njuga kwa mtundu uliwonse n’kosagwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. * Mwachitsanzo, n’zodziŵika kuti kutchova njuga kumayambitsa dyera. Mfundo imeneyi payokha ndi yofunika kwambiri kuti Akristu aiganizire, chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti “osirira [“adyera,” NW]” sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu ndiponso limaika chisiriro m’gulu limodzi ndi kupembedza mafano.​—1 Akorinto 6:9, 10; Akolose 3:5.

Kutchova njuga kumayambitsanso kudzikuza ndiponso mtima woipa, wampikisano, mtima wofunitsitsa kuwina. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti tipeŵe zoterezi pamene analemba kuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” (Agalatiya 5:26) Ndiponso, kutchova njuga kumalimbikitsa ena kukhulupirira malodza kuti akhale ndi mwayi. Otchova njuga amakhala ndi zikhulupiriro za malodza zosiyanasiyana, pofuna kuti achite mwayi. Anthu otereŵa akutikumbutsa za Aisrayeli osakhulupirika amene anali “kukonzera mulungu wamwayi gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza.”​—Yesaya 65:11.

Ena angaganize kuti kubetcherana ndalama zochepa poseŵera makadi kapena maseŵera ena monga bawo ndi achibale kapena anzawo apamtima sikulakwa. N’zoona kuti munthu amene akubetcha ndalama zochepa sangadzione ngati wadyera, wodzikuza, wampikisano, kapena wokhulupirira malodza. Komabe, kodi kutchova kwake njuga kungakhudze bwanji anthu amene akutchova nawo njugawo? Anthu ambiri oloŵerera ndi kutchova njuga anayamba mwa kubetcherana ndalama zochepa zedi ‘pongofuna kusangalala basi.’ (Luka 16:10) Kwa anthu ameneŵa, maseŵera amene ankaoneka ngati opanda cholakwika anasintha n’kukhala oipa kwambiri.

Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati amene akuchitawo ndi ana. Ana ambiri asangalala kwambiri kuwina pobetcherana ndalama zochepa ndipo zimenezi zawachititsa kufika pobetcherana ndalama zambiri. (1 Timoteo 6:10) Kafukufuku amene anachitika kwa nthaŵi yaitali amene bungwe la Arizona Council on Compulsive Gambling ku United States linafalitsa anatsimikizira kuti anthu ambiri oloŵerera ndi kutchova njuga anayamba ali aang’ono. Ankatero “mwa kubetcherana ndalama zochepa pakamachitika maseŵera kapena poseŵera makadi ndi anzawo kapena achibale awo.” Lipoti lina linati “ana amayambira kunyumba kutchova njuga, nthaŵi zambiri poseŵera makadi ndi a m’banja lawo kapena anzawo.” Lipotilo linawonjezera kuti “ana 30 mwa ana 100 alionse amene anali kutchova njuga anayamba kuchita zimenezo asanakwanitse zaka 11.” Achinyamata ambiri amapeza ndalama zotchovera njuga mwa kuchita umbanda kapena chiwerewere, malinga ndi kafukufuku wina amene anamutcha Why Do People Gamble Too Much​—Pathological and Problem Gambling. N’zomvetsatu chisoni zimenezi zomwe zimachitika chifukwa cha chinthu chimene poyamba chinkaoneka ngati chabwinobwino!

Popeza tikukhala m’dziko limene lili kale ndi misampha ndi zokopa zambirimbiri, n’kuputiranji daladala msampha wina? (Miyambo 27:12) Kutchova njuga, kaya ana alipo kapena palibe, kaya kubetcherana ndalama zambiri kapena zochepa, kumawononga moyo wauzimu ndipo n’kofunika kupeŵedwa. Akristu amene amaseŵera maseŵera onga bawo kapena makadi pocheza angachite bwino kumangolemba zotsatira za maseŵerawo kapena kumangoseŵera mongofuna kusangalala chabe osalemba zotsatira zake. Akristu anzeru amene amaganizira moyo wawo wauzimu ndiponso wa anzawo ndi a m’banja lawo amapeŵa kutchova njuga, ngakhale ndalama zobetcherana zikhale zochepa chabe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku lakuti World Book Encyclopedia limati kutchova njuga ndiko “kubetcherana pa zotsatira za maseŵero, zochitika, kapena zinthu zomwe zingachitike mwamwayi.” Limafotokozanso kuti “otchova njuga nthaŵi zambiri amabetcherana ndalama pa . . . maseŵero oyendera mwayi monga malotale, maseŵero a makadi, ndi mayere.”