Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sitinasiye Ntchito Yomwe Tinapatsidwa

Sitinasiye Ntchito Yomwe Tinapatsidwa

Mbiri ya Moyo Wanga

Sitinasiye Ntchito Yomwe Tinapatsidwa

YOSIMBIDWA NDI HERMANN BRUDER

Zinali zosavuta kuti ndisankhe: kutumikira zaka zisanu m’gulu la ankhondo a dziko la France a kumayiko ena kapena kutsekeredwa m’ndende m’dziko la Morocco. Tandilolani ndifotokoze mmene ndinapezekera m’mavuto ameneŵa.

NDINABADWIRA ku Oppenau m’dziko la Germany, mu 1911, patangotsala zaka zitatu kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse ibuke. Makolo anga, a Joseph ndi a Frida Bruder, anali ndi ana aamuna ndi aakazi okwana 17. Ine ndinali wa nambala 13.

Zimene ndikukumbukira pa zomwe zinkachitika ndili wamng’ono kwambiri ndizo kuonerera asilikali akuguba kudutsa mu msewu waukulu m’tauni yomwe tinkakhala. Nditachita chidwi ndi nyimbo zokoma zimene amaguba, ndinatsatira omwe amaimba nyimbozo kupita ku siteshoni padakali nthaŵi kuti ndikaonerere Atate limodzi ndi amuna ena ovala zachisilikali akukwera sitima. Pamene sitimayo imanyamuka, azimayi ena pasiteshonipo anayamba kulira. Patapita nthaŵi pang’ono, wansembe wathu anakapereka ulaliki wautali kutchalitchi ndipo analengeza mayina a amuna anayi omwe anafa poteteza dziko lawo. Iye anafotokoza kuti: “Ameneŵa ali kumwamba tsopano.” Mzimayi wina amene anaima nane pafupi anakomoka.

Atate anatenga matenda a typhoid akumenyana ndi asilikali a ku Russia. Anafika kunyumba atafooka kwambiri ndipo atangofika anakawagoneka m’chipatala cha m’tauni yomwe tinkakhalayo. Wansembe anandiuza kuti: “Pita ku nyumba yopemphereramo imene ili kufupi ndi kumanda ndipo ukanene maulendo 50 pemphero la Atate Wathu ndiponso maulendo 50 pemphero la Tikuoneni Mariya. Ukakatero, bambo ako achira.” Ndinachita zimene anandiuzazo, koma Atate anamwalira tsiku lotsatira. Ngakhale kuti ndinali mnyamata wamng’ono, nkhondoyo inandipweteketsa mtima kwambiri.

Mmene Ndinapezera Choonadi

M’kati mwa zaka za 1919 mpaka 1939 kunali kovuta kuti munthu apeze ntchito m’dziko la Germany. Komabe, nditasiya sukulu mu 1928, ndinapeza ntchito yosamalira ku munda ku Basel, m’dziko la Switzerland.

Mofanana ndi Atate, ine ndinali Mkatolika wolimbikira kwambiri. Cholinga changa chinali chokatumikira monga mmishonale wachimonke ku India. Mchimwene wanga, Richard, yemwe panthaŵiyo anali wa Mboni za Yehova, atamva za malingaliro amenewo, anakonza ulendo wapadera wopita ku Switzerland n’cholinga chokayesa kundiuza kuti ndisachite zimenezo. Anandichenjeza za kuopsa kodalira anthu, makamaka atsogoleri achipembedzo, ndipo anandilimbikitsa kuti ndiziŵerenga Baibulo ndi kudalira Baibulo lokhalo basi. Ngakhale kuti sindinakhulupirire zimene iye anandiuza, ndinapeza Baibulo la Chipangano Chatsopano ndi kuyamba kuliŵerenga. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuzindikira kuti zinthu zambiri zimene ndinkakhulupirira zinali zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Tsiku lina Lamlungu, mu 1933, ndili kunyumba kwa Richard ku Germany, iye anandisonyeza kwa mwamuna wina ndi mkazi wake amene anali a Mboni za Yehova. Atazindikira kuti ndinali kuŵerenga Baibulo, iwo anandipatsa kabuku kakuti The Crisis. * Ndinakaŵerenga kabukuko mpaka pafupifupi pakati pausiku. Ndinatsimikiza kuti ndapeza choonadi!

Mboni za Yehova ku Basel zinandipatsa mavoliyumu aŵiri a buku lakuti Studies in the Scriptures * pamodzi ndi magazini ndiponso mabuku ena. Nditachita chidwi ndi zimene ndinali kuŵerenga, ndinapita kwa wansembe m’dera lathulo ndi kumuuza kuti afafanize dzina langa m’kaundula wa tchalitchi. Wansembeyo anakalipa kwambiri ndi kundichenjeza kuti ndinali pa ngozi yotaya chikhulupiriro changa. Komatu, linali bodza. Kwanthaŵi yoyamba pamoyo wanga, ndinali ndikuyamba kukhala ndi chikhulupiriro choona.

Abale mu Basel anali kukonza zoti kumapeto a sabata imeneyo apite kukalalikira kumalire ndi dziko la France. Mmodzi wa abalewo anandifotokozera bwinobwino kuti sanandiuze kuti ndipite nawo chifukwa chakuti ndinali nditangoyamba kumene kusonkhana ndi mpingo. Poona kuti zimenezi sizingandilepheretse ndinam’fotokozera cholinga changa choti ndiyambe kulalikira. Atakambirana ndi mkulu wina, mbaleyo anandipatsa gawo mu Switzerland. Lamlungu m’maŵa kwambiri, ndinanyamuka panjinga kupita ku mudzi wina waung’ono kufupi ndi Basel, nditanyamula mabuku anayi, magazini 28, ndi mabulosha 20 m’chikwama changa cha muutumiki. Pamene ndimafika n’kuti anthu ambiri m’mudziwo ali kutchalitchi. Ngakhale kuti zinali choncho, pamene nthaŵi imakwana 11 koloko, m’chikwama changa munalibiretu kanthu.

Nditawauza abale kuti ndikufuna kubatizidwa, anakambirana nane mfundo zofunika kwambiri ndi kundifunsa mafunso akuya okhudza choonadi. Ndinachita chidwi ndi changu komanso kukhala kwawo okhulupirika kwa Yehova ndiponso m’gulu lake. Popeza kuti inali nyengo ya chisanu, mbale wina anandibatizira m’bafa panyumba ya mkulu wina. Ndikukumbukira kuti ndinali ndi chimwemwe chodzala tsaya komanso wanyonga kwambiri. M’menemo munali mu 1934.

Kugwira Ntchito ku Kingdom Farm

Mu 1936, ndinamva kuti Mboni za Yehova zagula malo mu Switzerland. Ndinadzipereka kuti ndizikagwira ntchito yosamalira ku munda. Ndinasangalala pamene anandiitana kuti ndikagwire ntchito ku Kingdom Farm, m’tauni ya Steffisburg, yomwe ili pamtunda wa makilomita pafupifupi 30 kuchokera mu mzinda wa Bern. Nthaŵi zina, zikakhala zotheka, ndinkathandizanso ena ntchito zawo pa famuyo. Beteli inandiphunzitsa kufunika kokhala ogwirizana.

Chosangalatsa kwambiri pa zaka zomwe ndinakhala pa Beteli chinali ulendo wa Mbale Rutherford wodzaona famuyo mu 1936. Ataona kukula kwa tomato wathu ndiponso mmene mbewu zinalili zamphamvu, anamwetulira n’kunena kuti iye wasangalala nazo kwambiri. Anali mbale wabwino kwambiri!

Nditatumikira pa famupo kwa zaka zopitirira zitatu zokha, pa chakudya cha m’maŵa anaŵerenga kalata yochoka ku likulu la Mboni za Yehova ku United States. Kalatayo inatsindika za kufunika kwa ntchito yolalikira ndipo inalimbikitsa anthu kuti apite kukatumikira ku mayiko ena monga apainiya. Sindinazengereze, ndinadzipereka kuchita zimenezo. Anandiuza kopita mu May 1939; anandiuza kuti ndipite ku Brazil!

Panthaŵiyi, ndinkasonkhana mu mpingo wa Thun, kufupi ndi Kingdom Farm. Pa Lamlungu, gulu la alongo ndi abalefe tinkapita kukalalikira ku Alps, mtunda wa maola aŵiri kuyenda panjinga kuchoka ku Thun. Margaritha Steiner anali m’gululo. Mwadzidzidzi ndinayamba kuganiza kuti: Kodi Yesu sanatume ophunzira ake aŵiriaŵiri? Nditam’fotokozera Margaritha zoti andiuza kuti ndipite ku Brazil, iye anafotokoza kuti nayenso amafuna kutumikira kumene kukufunika olalikira ambiri. Tinakwatirana pa July 31, 1939.

Kuima Pamalo Ena Mwadzidzidzi

Kumapeto kwa August 1939, tinayamba ulendo wapamadzi wochoka ku Le Havre, ku France kupita ku Santos, ku Brazil. M’sitima yomwe tinakwera mabedi onse ogona anthu aŵiri anali atatha, motero tinafunika kuyenda ulendowo m’chipinda chakechake. Ulendo uli m’kati, panamveka kuti mayiko a Britain ndi France ayamba kumenyana ndi dziko la Germany. Nzika za dziko la Germany zokwana 30 zomwe zinali nawo paulendowo zinasonyeza kukhalira mbali dziko lawo mwa kuimba nyimbo ya fuko lawo. Izi zinakhumudwitsa mkulu woyendetsa sitimayo moti anasintha kopita ndi kukakocheza pa Safi, m’dziko la Morocco. Apaulendo omwe anali ndi zitupa zoyendera za dziko la Germany anapatsidwa mphindi zisanu kuti atsike. Zimenezi zinaphatikizapo ifeyo.

Anatisunga kupolisi kwa tsiku limodzi ndipo kenako tinakwera m’chibasi chakale momwe tinathithikana kwambiri, ndipo anapita nafe ku ndende ya ku Marrakech, mtunda wa makilomita pafupifupi 140 kuchoka ku Safi. Ndiye kunali mavuto. M’zipinda zathu kundendeko munali modzaza kwambiri ndiponso mwamdima. Chimbudzi chomwe tonse tinkagwiritsira ntchito, kadzenje komwe kanali m’chipinda chandendeyo, chinkakhala chotsekera nthaŵi zambiri. Aliyense ankam’patsa saka la bii kuti agonepo, ndipo usiku makoswe ankatiluma akatumba. Tinkalandira chakudya kaŵiri patsiku ndipo tinkalandirira m’kachitini kadzimbiri.

Msilikali wina anandifotokozera kuti angathe kundimasula ngati nditavomera kutumikira zaka zisanu m’gulu la ankhondo a dziko la France a kumayiko ena. Kukana kuchita zimenezo kunapangitsa kuti ndivutike modetsa nkhaŵa kwa maola 24. Nthaŵi yaikulu ya maola ameneŵa inatha ndikupemphera.

Patatha masiku asanu ndi atatu, akuluakulu a ndendeyo anandilola kuti ndionanenso ndi Margaritha. Anali ataonda kwambiri, ndipo analira mosatonthozeka. Ndinayesetsa kumulimbikitsa. Anatipanikiza ndi mafunso ndi kutitumiza ku Casablanca pa sitima yapamtunda, komwe Margaritha anakam’masula. Ananditumiza ku msasa wa akaidi ku Port Lyautey (komwe masiku ano ndi ku Kenitra), mtunda wa makilomita pafupifupi 180 kuchoka ku Casablanca. Kazembe wa dziko la Switzerland analangiza Margaritha kuti abwerere ku Switzerland, koma iye anakanitsitsa kuchoka popanda ine. Kwa miyezi iŵiri yomwe ndinakhala ku Port Lyautey, iye ankayenda tsiku ndi tsiku kuchoka ku Casablanca kuti adzandione ndi kudzandipatsa chakudya.

Chaka chimodzi zimenezi zisanachitike, Mboni za Yehova zinali zitafalitsa buku lakuti Kreuzzug gegen das Christentum (Crusade Against Christianity) pofuna kudziŵitsa anthu kuti Mboni sizikukhudzidwa ndi ulamuliro wa chipani cha Nazi. Pamene ndinali ku msasa wa akaidiwo, nthambi ya Mboni za Yehova ku Bern inalembera kalata akuluakulu a dziko la France, momwe anaikamo bukulo n’cholinga chofuna kuwatsimikizira kuti ife sitinali a chipani cha Nazi. Nayenso Margaritha anayesetsa kukumana ndi akuluakulu a boma ndi kuyesa kuwasonyeza kuti tinali osalakwa. Pomalizira pake, kumapeto kwa 1939, anatilola kutuluka m’dziko la Morocco.

Tinali titangouyambanso kumene ulendo wa ku Brazil pamene tinamva kuti sitima za nkhondo zoyenda pansi pa madzi za dziko la Germany zikuwombera sitima zodutsa pa nyanja ya Atlantic ndipo sitima yathu ndi yomwe ankaifuna kwambiri. Ngakhale kuti sitima yathuyo, yomwe ankaitcha kuti Jamaique, inali ya amalonda, inali ndi mfuti kutsogolo ndi kumbuyo kwake. Masana, ankaiyendetsa mokhotakhota ndipo ankaponya mabomba tsiku lonse. Usiku tinkakhala mumdima kuopa kuti Ajeremani angadziŵe komwe tili. Mitima inakhala m’malo titakocheza pa doko la Santos, ku Brazil, pa February 6, 1940, patatha miyezi yoposa isanu chichokereni ku Ulaya!

Kubwereranso Kundende

Dera lathu loyamba lomwe tinapatsidwa kuti tizilalikiramo linali Montenegro, tauni ya m’chigawo cha kum’mwera kwa dziko la Brazil cha Rio Grande do Sul. Sindikukayika kuti atsogoleri a matchalitchi anali atauzidwa za kufika kwathu. Titalalikira kwa maola aŵiri okha, apolisi anatimanga ndi kutilanda malekodi a galamafoni omwe anali ndi maulaliki a Baibulo, mabuku onse, ngakhalenso zikwama za chikopa cha ngamila zimene tinagula ku Morocco kuti tiziloŵera muutumiki. Wansembe pamodzi ndi mtumiki wina wolankhula Chijeremani anali kutiyembekezera kupolisiko. Anamvetsera, pamene mkulu wa apolisi anaika pa galamafoni yomwenso anatilanda, lekodi ya nkhani za Mbale Rutherford. Mbale Rutherford ankalankhula mosapita m’mbali. Lekodiyo itafika pamene inatchula za Vatican, wansembeyo anakwiya kwambiri, n’kutulukamo.

Apolisi anatitumiza ku Pôrto Alegre, likulu la chigawo cha Rio Grande do Sul, bishopu wa ku Santa Maria atawapempha kutero. Sipanapite nthaŵi yaitali, Margaritha anam’masula ndipo anakapempha thandizo ku ofesi ya kazembe wa dziko la Switzerland. Kazembeyo anauza Margaritha kuti abwerere ku Switzerland ndipo anakananso kundisiya. Nthaŵi yonseyi Margaritha wakhala mnzanga wokhulupirika kwambiri. Patatha masiku 30 anandipanikiza nawo mafunso ndi kundimasula. Apolisi anatiuza kuti tisankhe: kuchoka m’chigawocho pasanathe masiku khumi kapena “kuona chinameta nkhanga mpala.” Potsatira malingaliro a kulikulu ku Brooklyn, tinasamukira ku Rio de Janeiro.

“Ŵerengani Khadi Ili”

Ngakhale kuti titangofika ku Brazil zinthu sizinatiyendere bwino chonchi, tinali osangalala kwambiri kukhala m’dzikoli! Ndiponsotu, tinali amoyo, zikwama zathu zinadzazanso ndi mabuku, ndipo tinafunika kulalikira mu mzinda wonse wa Rio de Janeiro. Koma tikanalalikira motani popeza sitinkadziŵa kwenikweni Chipwitikizi? Tinatero mwa kugwiritsira ntchito khadi lolalikirira. Mawu oyambirira a Chipwitikizi omwe tinaphunzira kuti tizigwiritsira ntchito polalikira anali akuti, “Por favor, leia este cartão” (“Ŵerengani khadi ili”). Ndipo khadi limeneli linathandiza kwambiri! M’mwezi umodzi wokha, tinagaŵira mabuku oposa 1,000. Ambiri mwa anthu omwe analandira mabuku athu ofotokoza Baibulo anaphunzira choonadi pambuyo pake. Kunena zoona, mabuku athu analalikira mogwira mtima kuposa momwe ifeyo tikanachitira. Zimenezi zinandithandiza kuona kufunika kopereka mabuku athu kwa anthu omwe ali ndi chidwi.

Nthaŵi imeneyo mzinda wa Rio de Janeiro unali likulu la dziko la Brazil, ndipo anthu m’maofesi a boma ankasangalala nawo kwambiri uthenga wathu. Ndinali ndi mwayi wapadera wolalikira kwa nduna ya zachuma ndiponso kwa nduna ya zachitetezo. Panthaŵi zimenezi, ndinkaona umboni wakuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito.

Nthaŵi ina, ndikulalikira pamalo ena apakati pa mzinda wa Rio, ndinaloŵa mu ofesi ya zachilungamo. Mosadziŵika bwino, ndinaloŵa m’chipinda china momwe ndinapita pakati pa anthu ovala zakuda, mwambo winawake womwe ndinaona ngati wa maliro uli m’kati. Ndinapita kwa munthu yemwe ankaoneka wolemekezeka kwambiri ndi kum’patsa khadi langa lolalikirira. Sunali mwambo wa maliro. Ndinali nditasokoneza ntchito yozenga mlandu, ndipo ndimalankhula ndi woweruza milandu. Kwinaku akuseka, iye anauza alonda kuti asachite kalikonse. Mwaulemu ndiponso mosangalala analandira buku lakuti Children * ndipo anapereka ndalama. Pamene ndimatuluka, mlonda wina anandilozera chikwangwani chachikulu pachitseko. Chinali ndi mawu akuti: Proibida a entrada de pessoas estranhas (Anthu Opanda Chilolezo Sakuloledwa Kuloŵa).

Gawo lina lomwe zinthu zinkatiyendera bwino kwambiri kunali kudoko. Nthaŵi inayake, ndinakumana ndi munthu wina wogwira ntchito m’sitima yemwe analandira mabuku asanabwerere kunyanja. Pambuyo pake, tinakakumana naye pa msonkhano. Banja lake lonse linali litaphunzira choonadi, ndipo iyenso anali kupita patsogolo kwambiri. Izi zinatisangalatsa kwambiri.

Komatu sikuti zonse zinkayenda bwino. Makalata athu oti tikhale m’dzikomo miyezi isanu ndi umodzi anatha ntchito, ndipo tinkayembekezera kuthamangitsidwa. Titawalembera kalata a kulikulu ku Brooklyn yowadziŵitsa za vuto lathu, tinalandira kalata yosangalatsa yochoka kwa Mbale Rutherford, yotilimbikitsa kuti tipirire ndiponso yotiuza zochita. Cholinga chathu chinali chopitiriza kukhala m’Brazil, ndipo mothandizidwa ndi loya wina, mu 1945 tinapeza makalata otilola kukhazikika m’dzikomo.

Ntchito Yomwe Tinaigwira Nthaŵi Yaitali

Koma zimenezi zisanachitike, Jonathan, mwana wathu wamwamuna anabadwa mu 1941, Ruth anabadwa mu 1943, ndipo Esther anabadwa mu 1945. Kuti tithe kusamalira banja lathu lomwe linali kukula, ndinafunika kuloŵa ntchito. Margaritha anapitiriza ntchito yolalikira nthaŵi zonse mpaka pamene mwana wathu wachitatu anabadwa.

Kuyambira pachiyambi, tinkalalikirira pamodzi monga banja ndipo tinkalalikira m’mphambano za m’kati mwa mzinda, m’masiteshoni a sitima, m’misewu, ndiponso m’madera a zamalonda. Loŵeruka madzulo, tinkagaŵira limodzi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndipo tinkasangalala kwambiri ndi zimenezi.

Kunyumba, mwana aliyense anali ndi ntchito zake zoti azigwira tsiku ndi tsiku. Jonathan ankapukuta chitofu ndi kukonza m’khichini. Atsikana ankakonza m’firiji, kusesa pabwalo, ndi kupukuta nsapato zathu. Izi zinawathandiza kukhala anthu adongosolo ndiponso kuti azitha kuchita zinthu paokha. Panopo, ana athuŵa akugwira ntchito zolimba kusamalira bwino mabanja ndiponso katundu wawo, zinthu zimene ine ndi Margaritha timasangalala nazo kwambiri.

Tinkafunanso kuti anaŵa azisonyeza khalidwe labwino pamisonkhano. Msonkhano usanayambe, ankamweratu madzi ndi kupitiratu kokadzithandiza. Panthaŵi ya misonkhano, Jonathan ankakhala kumanzere kwanga, Ruth kumanja kwanga, kenako pankakhala Margaritha, ndipo kumanja kwake kunkakhala Esther. Zimenezi zinawathandiza kuti azikhala tcheru ndi kudya chakudya chauzimu kuyambira ali ang’onoang’ono.

Yehova wadalitsa khama lathu. Ana athu onse akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ndipo akulalikira nawo mosangalala kwambiri. Panopo Jonathan ndi mkulu mu mpingo wa Novo Méier, mu mzinda wa Rio de Janeiro.

Pofika chaka cha 1970, ana athu onse anali m’mabanja ndipo anali kukhala kwa okha, motero ine ndi Margaritha tinaganiza zopita kukatumikira kumene kunkafunikira olalikira ena. Poyambirira tinapita ku Poços de Caldas, m’chigawo cha Minas Gerais, kumene panthaŵiyo kunali kagulu kochepa ka ofalitsa Ufumu okwana 19. Ndinamva chisoni pamene ndinaona koyamba malo awo osonkhanira. Ankasonkhana m’chipinda chapansi chomwe chinalibe mawindo ndipo chinkafunika chitakonzedwa mofulumira. Mwamsangamsanga, tinayamba kufufuza Nyumba ya Ufumu yabwino ndipo patapita nthaŵi pang’ono tinapeza nyumba yomwe inali pamalo abwino kwambiri. Zimenezi zinapangitsa kuti pakhale kusintha kwakukulu. Zaka zinayi ndi theka pambuyo pake, chiŵerengero cha ofalitsa chinawonjezeka kufika pa 155. Mu 1989 tinapita ku Araruama, m’chigawo cha Rio de Janeiro, komwe tinatumikirako zaka zisanu ndi zinayi. M’kati mwa nthaŵi imeneyi, tinaona mipingo yatsopano iŵiri ikupangidwa.

Tafupidwa Chifukwa Chosasiya Ntchito Yomwe Tinapatsidwa

Mu 1998, tinasamukira ku São Gonçalo, m’chigawo cha Rio de Janeiro chifukwa cha mavuto a thanzi ndiponso kufuna kuyandikana ndi ana athu. Ndikutumikirabe kumeneko monga mkulu mu mpingo. Tikuyesetsa kuti nthaŵi ndi nthaŵi tizichita nawo ntchito yolalikira. Margaritha amakonda kulalikira kwa anthu pamsika wina wapafupi ndi komwe tikukhala, ndipo mpingo unatikomera mtima potisiyira gawo lina kufupi ndi nyumba yathu. Izi zapangitsa kuti tizitha kulalikira tikaona kuti tili bwinopo.

Ine ndi Margaritha takhala atumiki odzipatulira kwa Yehova kwa zaka zoposa 60 tsopano. Tadzionera tokha kuti ‘ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sizingatisiyanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’ (Aroma 8:38, 39) Ndipo tasangalala kwambiri kuona kusonkhanitsidwa kwa a “nkhosa zina,” amene ali ndi chiyembekezo chosangalatsa chodzakhala ndi moyo padziko lapansi langwiro, m’chilengedwe chokongola cha Mulungu! (Yohane 10:16) Pamene tinkafika kuno mu 1940, mu mzinda wa Rio de Janeiro munali mpingo umodzi wokha, wa ofalitsa 28. Lero muli mipingo pafupifupi 250 ndipo muli ofalitsa Ufumu oposa 20,000.

Panali nthaŵi zina pamene tikanatha kubwerera kumakakhala ndi mabanja athu ku Ulaya. Koma Yehova anatitumiza kuti titumikire kuno ku Brazil. Ndife okondwa kuti sitinasiye ntchito imene anatipatsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma sakusindikizidwanso.

^ ndime 12 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma sakusindikizidwanso.

^ ndime 33 Linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma silikusindikizidwanso.

[Chithunzi patsamba 21]

Ku Kingdom Farm, ku Steffisburg, Switzerland, chakumapeto kwa m’ma 1930 (ine ndili kumanzere kwenikweni)

[Chithunzi patsamba 23]

Titatsala pang’ono kuchita ukwati wathu, mu 1939

[Chithunzi patsamba 23]

Mzinda wa Casablanca m’ma 1940

[Chithunzi patsamba 23]

Kulalikira monga banja

[Chithunzi patsamba 24]

Kuchita nawo nthaŵi ndi nthaŵi utumiki masiku ano