Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wina Aliyense Ndi Wolandiridwa pa Nyumba ya Ufumu

Wina Aliyense Ndi Wolandiridwa pa Nyumba ya Ufumu

Olengeza Ufumu Akusimba

Wina Aliyense Ndi Wolandiridwa pa Nyumba ya Ufumu

PAMENE ankaphunzitsa ophunzira ake ntchito yotumikira anthu onse, Yesu Kristu anawalimbikitsa ‘kulalikira pa machindwi a nyumba.’ (Mateyu 10:27) Inde, anali kudzachita utumiki wawo wachikristu poyera, anthu onse akuona. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo ya m’malangizo ameneŵa, nayonso ntchito ya Mboni za Yehova imachitika mosabisa. Kusabisa zinthu kumeneku kwathandiza Mboni kugonjetsa chitsutso ndiponso kuti anthu azidziŵe bwino kwambiri.

Ngakhale kuti munthu aliyense ndi wololedwa kufika pa misonkhano ya mpingo ya Mboni za Yehova, anthu ena amalephera kuloŵa m’Nyumba ya Ufumu chifukwa chokhala ndi malingaliro olakwika. Zimenezi ndi zomwe zikuchitika ku Finland. Anthu ena amalephera kuloŵamo chifukwa choti sakonda kupita ku malo achilendo basi. Nyumba ya Ufumu ikamangidwa kapena ina yakale ikakonzedwanso, nthaŵi zambiri amakonza zoti wina aliyense wofuna apite kukaiona. Mwina angathe kukonza zoitana anthu a m’deralo kuti abwere ku Nyumba ya Ufumuyo ndi kudzaona zimene Mboni za Yehova zimachita.

M’dera lina, Mboni zinakonza zogaŵira magazini patsiku lomwe anakonza zoti aliyense wofuna akaone Nyumba yawo ya Ufumu yatsopano. Mboni ziŵiri zinakumana ndi mwamuna wina wachikulire yemwe ananena kuti amakonda kuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Abalewo anam’fotokozera za makonzedwe opita ku Nyumba ya Ufumuyo ndipo anamuuza kuti angathe kumutenga kupita naye ku nyumbayo. Mwamunayo anawauza kuti akufuna kupita nawo. Mkazi wake, atamva zomwe amakambiranazo, anafuula kuti, “Ine musandisiye!”

Ataloŵa m’Nyumba ya Ufumuyo, mwamunayo anamwazamwaza maso n’kunena kuti: “Muno si mwakuda ngakhale pang’ono. Ndi mokongola ndiponso mowala kwambiri. Ndinauzidwa kuti Nyumba ya Ufumu imakhala yakuda!” Banjalo linakhala kanthaŵi ndithu pa Nyumba ya Ufumupo ndipo linapempha mabuku omwe anali pakauntala ya mabuku.

Mpingo wina unafuna kulengeza m’nyuzipepala ya m’dera lake zakuti aliyense angathe kufika ndi kudzaona Nyumba yake ya Ufumu pa mwambo woipatulira. Atauzidwa za mwambowo, mkonzi wamkulu wa nyuzipepalayo anapempha kuti alembe nkhani yokhudza mwambowo. Abalewo anavomera, ndipo patapita nthaŵi pang’ono, nyuzipepalayo inasindikiza nkhani yabwino kwambiri yomwe inadzala theka la tsamba. Nkhaniyo inanena za mwambowo ndiponso inafotokoza ntchito imene mpingo wa Mboni za Yehova wa m’deralo ukugwira.

Nkhaniyo itasindikizidwa, Mboni ina yachikulire inakumana ndi mayi wina wa m’deralo yemwe anauza Mboniyo kuti: “Lero m’nyuzipepala muli nkhani yosangalatsa kwambiri yonena za Mboni za Yehova!” Mlongoyo analalikira kwa mayiyo ndipo kenako anam’gaŵira bulosha lakuti Mboni za Yehova m’Zaka za Zana la Makumi Aŵiri.

Kuwonjezera pa kuthetsa malingaliro ena olakwika okhudza Mboni za Yehova, makonzedwe ameneŵa kuphatikizapo kulola wina aliyense kudzaona Nyumba ya Ufumu ndiponso mwambo wopatulira Nyumba za Ufumu zathandiza ofalitsa powalimbikitsa kuitanira anthu ambiri kubwera ku misonkhano. Inde, m’mayiko ambiri, kuphatikizapo ku Finland, anthu adziŵa kuti wina aliyense ndi wolandiridwa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.