Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akristu Amafunika Kuthandizana

Akristu Amafunika Kuthandizana

Akristu Amafunika Kuthandizana

“Tili ziŵalo wina ndi mnzake.”​—AEFESO 4:25.

1. Kodi insaikulopediya ina inati chiyani za thupi la munthu?

THUPI la munthu linalengedwa modabwitsa. Insaikulopediya yakuti The World Book Encyclopedia inati: “Anthu nthaŵi zina amatchula thupi kuti ndi makina​—makina apamwamba kwambiri kuposa ena alionse amene anapangidwapo. Komabe sikuti thupi la munthu ndi makina enieni. Koma tingaliyerekezere ndi makina m’njira zambiri. Mofanana ndi makina, thupi lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Chiwalo chilichonse cha thupi chimagwira ntchito yapadera mofanana ndi mbali iliyonse ya makina. Koma ziwalo kapena mbali zonse zimagwirira ntchito limodzi ndipo motero zimachititsa thupi kapena makina kugwira bwino ntchito.”

2. Kodi thupi la munthu limafanana bwanji ndi mpingo wachikristu?

2 Inde, thupi la munthu lili ndi ziwalo zambiri ndipo chiwalo chilichonse chimagwira ntchito inayake yofunika. Palibe mtsempha, mnofu, kapena chiwalo chilichonse chomwe n’chopanda ntchito. N’chimodzimodzinso mumpingo wachikristu, munthu aliyense angathandize kuti mpingowo ukhale wathanzi ndiponso wabwino mwauzimu. (1 Akorinto 12:14-26) Ngakhale kuti munthu aliyense mumpingo sayenera kudziona ngati woposa ena, palibe amene ayenera kudziona ngati wosafunika.​—Aroma 12:3.

3. Kodi Aefeso 4:25 amasonyeza bwanji kuti Akristu amafunika kuthandizana?

3 Mofanana ndi ziwalo za thupi zimene zimadalirana, Akristu amafunika kuthandizana. Mtumwi Paulo anauza okhulupirira anzake odzozedwa kuti: “Mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziŵalo wina ndi mnzake.” (Aefeso 4:25) Popeza ‘ali ziwalo wina ndi mnzake,’ a Israyeli wauzimu, omwe ndi “thupi la Kristu,” amalankhulana zoona zokhazokha ndipo amagwirizana kwambiri. Inde, onse amadalirana. (Aefeso 4:11-13) Akristu enanso onena zoona, ogwirizana amene akuyembekezera kudzakhala pa dziko lapansi agwirizana nawo mosangalala.

4. Kodi anthu atsopano angathandizidwe m’njira zotani?

4 Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri oyembekezera kudzakhala m’paradaiso pa dziko lapansi akubatizidwa. Anthu ena mumpingo amawathandiza mosangalala “kutsata ukulu msinkhu.” (Ahebri 6:1-3) Thandizo limeneli lingaphatikizepo kuyankha mafunso okhudza nkhani za m’Malemba kapena kuwathandiza muutumiki. Tingathandize anthu atsopano popereka chitsanzo chabwino mwa kupezeka nthaŵi zonse pa misonkhano yachikristu. Pa nthaŵi ya mavuto, tingawalimbikitsenso kapena kuwatonthoza. (1 Atesalonika 5:14, 15) Tiyenera kupeza njira zothandizira ena kupitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’ (3 Yohane 4) Kaya ndife achichepere kapena achikulire, kaya tangoyamba kumene kuyenda m’choonadi kapena takhala m’choonadi kwa zaka zambiri, tingalimbikitse moyo wauzimu wa okhulupirira anzathu, ndipotu amafuna kuti tiwathandize.

Anapereka Thandizo Lofunika

5. Kodi Akula ndi Priska anathandiza bwanji Paulo?

5 Akristu okwatirana ndi ena mwa anthu amene amasangalala pothandiza okhulupirira anzawo. Mwachitsanzo, Akula ndi mkazi wake, Priska, anathandiza Paulo. Anamulandira m’nyumba yawo, anagwira naye ntchito yopanga mahema, ndiponso anamuthandiza kupanga mpingo watsopano mu Korinto. (Machitidwe 18:1-4) Mwa njira ina imene sanaifotokoze, iwo anaika ngakhale miyoyo yawo pachiswe m’malo mwa Paulo. Iwo ankakhala ku Roma pamene Paulo anauza Akristu kumeneko kuti: “Mulankhule Priska ndi Akula, antchito anzanga m’Kristu Yesu, amene anapereka khosi lawo chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, siine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.” (Aroma 16:3, 4) Mofanana ndi Akula ndi Priska, Akristu ena a masiku ano amalimbikitsa mipingo ndiponso amathandiza olambira anzawo m’njira zosiyanasiyana, nthaŵi zina ngakhale kuika miyoyo yawo pachiswe pofuna kuti atumiki ena a Mulungu asazunzidwe kapena kuphedwa ndi anthu ozunza.

6. Kodi Apolo analandira chithandizo chotani?

6 Akula ndi Priska anathandizanso Apolo, Mkristu wodziŵa kulankhula bwino, amene anali kuphunzitsa anthu a ku Efeso za Yesu Kristu. Panthaŵi imeneyo, Apolo ankangodziŵa za ubatizo umene ankachita Yohane basi, wosonyeza kulapa machimo ochimwira pangano la Chilamulo. Pozindikira kuti Apolo anafunika thandizo, Akula ndi Priska “[a]namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.” Iwo ayenera kuti anam’fotokozera kuti ubatizo wachikristu unkafuna kumizidwa m’madzi ndi kulandira mzimu woyera. Apolo anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira. Kenako ku Akaya, “iye anathangata ndithu iwo akukhulupira mwa chisomo; pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Kristu.” (Machitidwe 18:24-28) Ndemanga za okhulupirira anzathu nthaŵi zambiri zingatithandize kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Pambali imeneyinso, timafunika kuthandizana.

Kupereka Thandizo la Zinthu Zofunika pa Moyo

7. Kodi Afilipi anachita bwanji pamene Akristu anzawo anafunikira thandizo la zinthu zofunika pa moyo?

7 Anthu a mumpingo wachikristu wa ku Filipi anamukonda kwambiri Paulo ndipo anamutumizira zinthu zofunika pamoyo pamene anali ku Tesalonika. (Afilipi 4:15, 16) Pamene abale a ku Yerusalemu anafuna thandizo la zinthu zofunika pa moyo, Afilipi anapereka mwachangu ngakhale kuposa mmene ankapezera. Paulo anayamikira kwambiri mtima wa abale ndi alongo ake a ku Filipi moti ananena kuti anali chitsanzo kwa okhulupirira ena.​—2 Akorinto 8:1-6.

8. Kodi Epafrodito anasonyeza mtima wotani?

8 Pamene Paulo anali kundende, Afilipi sanangotumiza mphatso ya zinthu zofunika pa moyo zokha komanso anatumiza nthumwi yawo, Epafrodito. Paulo anati: “Chifukwa cha ntchito ya Kristu [Epafrodito] anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chipereŵero cha utumiki wanu wa kwa ine.” (Afilipi 2:25-30; 4:18) Sitikudziŵa ngati Epafrodito anali mkulu kapena mtumiki wotumikira. Komabe iye anali Mkristu wodzipereka ndiponso wothandiza, ndipo Paulo anamufunadi iye. Kodi mumpingo mwanu muli wina wake wofanana ndi Epafrodito?

Iwo Anali ‘Otonthoza Mtima’

9. Kodi Aristarko anapereka chitsanzo chotani?

9 Abale ndi alongo achikondi monga Akula, Priska, ndi Epafrodito, amayamikiridwa kwambiri mumpingo uliwonse. Ena mwa olambira anzathu angakhale ngati Aristarko, Mkristu wa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Iye pamodzi ndi ena anali ‘otonthoza mtima,’ mwina analimbikitsa kapena kuthandiza pa nkhani zofunika kwambiri. (Akolose 4:10, 11) Mwa kuthandiza Paulo, Aristarko anakhala bwenzi lenileni panthaŵi imene thandizo linafunika. Iye anali ngati munthu amene amufotokoza pa Miyambo 17:17 kuti: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Kodi tonsefe sitiyenera kukhala ‘otonthoza mtima’ kwa Akristu anzathu? Tifunika kuthandiza makamaka anthu amene akukumana ndi mavuto.

10. Kodi Petro anapereka chitsanzo chotani kwa akulu achikristu?

10 Makamaka akulu achikristu ayenera kukhala otonthoza mtima kwa abale ndi alongo awo auzimu. Kristu anauza mtumwi Petro kuti: “Ukhazikitse [“Ulimbikitse,” NW] abale ako.” (Luka 22:32) Petro anatha kuchita zimenezo chifukwa anasonyeza makhalidwe amphamvu, makamaka Yesu ataukitsidwa. Akulu, yesetsani mmene mungathere kuchita chimodzimodzi ndi mtima wonse ndiponso mwachifundo, chifukwa okhulupirira anzanu amafuna thandizo lanu.​—Machitidwe 20:28-30; 1 Petro 5:2, 3.

11. Kodi tingapindule bwanji mwa kupenda mtima wa Timoteo?

11 Timoteo, mnzake wa Paulo amene anali kuyenda naye anali mkulu amene anali kuganizira kwambiri Akristu ena. Ngakhale kuti ankavutika ndi matenda ena, Timoteo anasonyeza chikhulupiriro chosagwedera ndipo “anatumikira pamodzi ndi [Paulo] Uthenga Wabwino.” N’chifukwa chake mtumwiyo anauza Afilipi kuti: “Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.” (Afilipi 2:20, 22; 1 Timoteo 5:23; 2 Timoteo 1:5) Tingapindulitse olambira Yehova anzathu mwa kusonyeza mtima wonga wa Timoteo. N’zoona kuti tiyenera kulimbana ndi zofooka zathu monga anthu ndiponso mayesero osiyanasiyana, koma ifenso tingasonyeze ndipo tiyenera kusonyeza chikhulupiriro cholimba ndi kuwaganizira mwachikondi abale ndi alongo athu auzimu. Tiyenera kukumbukira nthaŵi zonse kuti amafuna thandizo lathu.

Akazi Amene Anasamala za Ena

12. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Dorika?

12 Mmodzi mwa akazi oopa Mulungu amene anasamala za ena anali Dorika. Iye atamwalira, ophunzira anakaitana Petro ndipo anam’pititsa ku chipinda chapamwamba. Kumeneko, “amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nawo pamodzi.” Dorika anaukitsidwa ndipo mosakayika anapitiriza ‘kudzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.’ Mumpingo wachikristu masiku ano, muli akazi onga Dorika amene angasoke zovala kapena kuchita zinthu zosonyeza chikondi kwa anthu amene akusoŵa thandizo. Komabe, ntchito zawo zabwino makamaka zimakhala zopititsa patsogolo zinthu za Ufumu ndi kugwira nawo ntchito yopanga ophunzira.​—Machitidwe 9:36-42; Mateyu 6:33; 28:19, 20.

13. Kodi Lidiya anasonyeza bwanji kuganizira Akristu anzake?

13 Mkazi wina woopa Mulungu dzina lake Lidiya anali kusamala za ena. Iye anali nzika ya ku Tiyatira ndipo anali kukhala ku Filipi pamene Paulo analalikira kumeneko cha m’ma 50 C.E. Lidiya ayenera kuti anali wotembenukira ku Chiyuda, koma ku Filipi kuyenera kuti kunali Ayuda ndi masunagoge ochepa chabe. Iye ndi akazi ena odzipereka anasonkhana kuti alambire m’mbali mwa mtsinje pamene mtumwiyo anawalalikira uthenga wabwino. Nkhaniyo imati: “Mtima [wa Lidiya] Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo. Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, muloŵe m’nyumba yanga, mugone mmenemo. Ndipo anatiumiriza ife.” (Machitidwe 16:12-15) Popeza Lidiya anafuna kuchitira ena zabwino, iye anakwanitsa kuumiriza Paulo ndi anzake kuti akhale m’nyumba mwake. Timayamikiratu kwambiri Akristu achifundo ndiponso achikondi a masiku ano akamasonyeza kuchereza alendo kotereku!​—Aroma 12:13; 1 Petro 4:9.

Ananu Timakufunaninso

14. Kodi Yesu Kristu anachita bwanji ndi ana?

14 Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu wachifundo ndiponso wachikondi, ndi amene anayambitsa mpingo wachikristu. Anthu anali omasuka akakhala naye limodzi chifukwa anali wachikondi ndiponso wachifundo. Nthaŵi ina pamene ena anayamba kubweretsa ana awo kwa Yesu, ophunzira ake anawaletsa. Koma Yesu anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzaloŵamo konse.” (Marko 10:13-15) Kuti tidzalandire madalitso a Ufumu, tiyenera kukhala odzichepetsa ndi ophunzitsika ngati ana aang’ono. Yesu anasonyeza kukonda ana aang’onowo mwa kuwayangata ndi kuwadalitsa. (Marko 10:16) Bwanji za ananu masiku ano? Dziŵani kuti timakukondani ndiponso timakufunani mumpingo.

15. Kodi ndi mfundo zotani zokhudza moyo wa Yesu zimene azilemba pa Luka 2:40-52, ndipo anapereka chitsanzo chotani kwa ana?

15 Yesu akadali wachichepere, anasonyeza kukonda Mulungu ndiponso Malemba. Ali ndi zaka 12, iye ndi makolo ake, Yosefe ndi Mariya, anachoka ku mudzi wa kwawo wa Nazareti kupita ku Yerusalemu kukakondwerera Paskha. Pobwerera, makolo a Yesu anapeza kuti iye sanali nawo limodzi pa gululo. Kenako anakam’peza atakhala m’bwalo lina la kachisi, akumvetsera aphunzitsi achiyuda ndi kuwafunsa mafunso. Podabwa kuti Yosefe ndi Mariya sanadziŵe kumene angamupeze, anawafunsa kuti: “Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?” Anabwerera kwawo ndi makolo ake, anali kuwamvera, ndipo anakulabe munzeru ndi usinkhu. (Luka 2:40-52) Yesu anaperekatu chitsanzo chabwino kwa ana athu. Iwo ayeneradi kumvera makolo awo ndi kukonda kuphunzira zinthu zauzimu.​—Deuteronomo 5:16; Aefeso 6:1-3.

16. (a) Kodi ana ena anafuula kuti chiyani pamene Yesu anali kulalikira pa kachisi? (b) Kodi achinyamata achikristu ali ndi mwayi wotani masiku ano?

16 Inu monga wachinyamata muyenera kuti mumalalikira za Yehova kusukulu ndiponso kunyumba ndi nyumba pamodzi ndi makolo anu. (Yesaya 43:10-12; Machitidwe 20:20, 21) Pamene Yesu anali kulalikira ndi kuchiritsa anthu pakachisi atatsala pang’ono kuphedwa, ana ena anafuula kuti: “Hosana kwa Mwana wa Davide.” Atakwiya ndi zimenezi, ansembe aakulu ndi alembi ananena kuti: “Mulinkumva kodi chimene alikunena aŵa?” Yesu anayankha kuti: “Inde: simunaŵerenga kodi, Mkamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?” (Mateyu 21:15-17) Mofanana ndi ana amenewo, achinyamatanu mumpingo muli ndi mwayi waukulu wotamanda Mulungu ndi Mwana wake. Tikufuna kuti mugwire nafe ntchito limodzi monga olengeza Ufumu.

Pakagwa Mavuto

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Paulo anakonza zosonkhetsa zopereka zothandizira Akristu a ku Yudeya? (b) Kodi zopereka zaufulu zothandizira okhulupirira a ku Yudeya zinakhudza bwanji Akristu achiyuda ndi Akristu omwe sanali achiyuda?

17 Kaya zinthu zili bwanji kwa ife, chikondi chimatilimbikitsa kuthandiza Akristu anzathu amene akusoŵa thandizo. (Yohane 13:34, 35; Yakobo 2:14-17) Kukonda abale ndi alongo ake a ku Yudeya kunachititsa Paulo kukonza zowasonkhetsera zopereka ku mipingo ya ku Akaya, Galatiya, Makedoniya, ndi madera ena a ku Asia. Chizunzo, zipolowe, ndi njala zimene ophunzira a ku Yerusalemu anakumana nazo ziyenera kuti zinachititsa zinthu zimene Paulo anazitcha kuti “zowawa,” “zisautso,” ndi “kulandidwa kwa chuma [chawo].” (Ahebri 10:32-34; Machitidwe 11:27–12:1) Motero, iye anayang’anira ndalama zimene zinaperekedwa zothandizira Akristu osauka a ku Yudeya.​—1 Akorinto 16:1-3; 2 Akorinto 8:1-4, 13-15; 9:1, 2, 7.

18 Zopereka zaufulu zothandizira oyera mtima a ku Yudeya zinasonyeza kuti panali ubale wolimba pakati pa olambira Yehova achiyuda ndi omwe sanali achiyuda. Kutumiza zoperekazo kunathandizanso Akristu omwe sanali achiyuda kusonyeza kuyamikira olambira anzawo a ku Yudeya chifukwa cha zinthu zauzimu zambiri zimene analandira kwa iwo. Motero panali kugawana zinthu zauzimu ndiponso zinthu zakuthupi. (Aroma 15:26, 27) Masiku anonso, anthu amapereka mwaufulu zopereka zothandiza okhulupirira anzawo osowa thandizo ndipo chikondi n’chimene chimawalimbikitsa kutero. (Marko 12:28-31) Pamenepanso timafuna thandizo la wina ndi mnzake kuti pakhale kufanana ndipo ‘iye wosonkhetsa pang’ono sichikum’sowa.’​—2 Akorinto 8:15.

19, 20. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene anthu a Yehova amathandizira pakagwa mavuto.

19 Pozindikira kuti Akristu amafunika kuthandizana, timafulumira kuthandiza abale ndi alongo athu auzimu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika zivomezi ndi zigumukire zitawononga ku El Salvador kuchiyambi kwa chaka cha 2001. Lipoti lina linati: “Abale a m’madera onse a El Salvador anapereka thandizo. Magulu a abale ochokera ku Guatemala, United States, ndi ku Canada anabwera kudzatithandiza. . . . Nyumba zoposa 500 ndi Nyumba za Ufumu zokongola zitatu zinamangidwa m’nthaŵi yochepa chabe. Kugwira ntchito mwakhama ndiponso kugwirizana kwa abale odzipereka ameneŵa zapereka umboni waukulu.”

20 Lipoti lochokera ku South Africa linati: “Madzi osefukira amene anawononga madera ambiri a ku Mozambique anakhudzanso abale athu ambiri achikristu. Nthambi ya ku Mozambique inakonza zowathandiza mbali yaikulu. Koma a ku nthambiyi anapempha kuti tiwatumizire zovala zogwiritsidwa ntchito kale koma zabwino kwa abale amene anali kusoŵa thandizowo. Tinasonkhanitsa zovala zambiri zimene zinadzala mu chikontena chachikulu cha mamita 12 n’kuwatumizira abale a ku Mozambique.” Inde, pa mbali zimenezinso timafunika kuthandizana.

21. Kodi nkhani yotsatira ifotokoza chiyani?

21 Monga taonera kale, ziwalo zonse za thupi n’zofunika. N’chimodzimodzinso mumpingo wachikristu. Anthu onse mumpingo amafunika kuthandizana. Afunikanso kupitiriza kutumikira mogwirizana. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zina mwa zinthu zimene zimathandiza kuti zimenezi zitheke.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi thupi la munthu limafanana bwanji ndi mpingo wachikristu?

• Kodi Akristu oyambirira anachita bwanji pamene okhulupirira anzawo anafuna thandizo?

• Kodi ndi zitsanzo zina za m’Malemba ziti zimene zikusonyeza kuti Akristu amafunika kuthandizana?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Akula ndi Priska anasamala za ena

[Zithunzi patsamba 12]

Anthu a Yehova amathandizana ndiponso kuthandiza ena pakagwa mavuto