Kodi Timafunikira Malo Olambiriramo?
Kodi Timafunikira Malo Olambiriramo?
‘Anthu mazana ambiri apaulendo wachipembedzo ovala zokongola ochokera mbali zosiyanasiyana zadziko, magulu a Amwenye ovina magule akale omwe ankavina motsatira ng’oma anthu a ku Spain asanadze, ndiponso anthu opembedza okhulupirika amene ankayenda ndi maondo awo movutikira podutsa khamu la anthu kuti afike kukachisi, anadzala pabwalo ndi m’misewu yozungulira tchalitchi.’
MMENEMU ndi mmene nyuzipepala ya El Economista inafotokozera namtindi wa anthu mu December 2001. Pa nthaŵi imeneyo anthu okwana pafupifupi mamiliyoni atatu anapita ku tchalitchi cha ku Mexico City kuti akasonyeze chikhulupiriro chawo kwa Namwali wa ku Guadalupe. Nyumba zina zachipembedzo, monga tchalitchi cha St. Peter ku Rome chimakopanso alendo ambiri.
Anthu ambiri amene amafuna kulambira Mulungu amaganiza kuti nyumba za chipembedzo ndi zopatulika ndiponso zofunika kuzilemekeza. Maria wa ku Brazil anati: “Kwa ine, ku tchalitchi n’kumene ndinkayandikira kwa Mulungu. Anali malo opatulika. Ndinkakhulupirira kuti kupita kutchalitchi kunkayeretsa moyo wanga ndiponso kuti ndi tchimo ngati osapita ku Misa kuti ndikalape Lamlungu lililonse.” Consuelo mwamuna wa ku Mexico anafotokoza kuti: “Tchalitchi chinkakhudza kwambiri mtima wanga; ndinkachilemekeza kwambiri. Ndikakhala kumeneko ndinkaona ngati ndili kumwamba.”
Ngakhale kuti anthu ena amaona tchalitchi kukhala malo ofunikira, ena amakaikira ngati malo olambiriramo ameneŵa alidi ofunika kwenikweni. Polankhulapo pankhani ya kutsika kwa chiŵerengero cha anthu opita ku tchalitchi, wansembe wa Chikatolika wa ku England dzina lake Peter Sibert anati: “[Anthu] amasankha mbali zina za chipembedzo zimene amakonda. Anthu ambiri achikulire ndi Akatolika ndipo amakhala mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo koma si mmene zili kwa achinyamata.” Nyuzipepala ya ku London ya Daily Telegraph ya pa November 20, 1998, inanena kuti: “Kuyambira m’chaka cha 1979 pafupifupi matchalitchi 1,500 atsekedwa ku England
pamene matchalitchi 495 ndi amene atsegulidwa ndipo 150 ndi amene amangidwanso.”M’chaka cha 1997, nyuzipepala ya Süddeutsche Zeitung ya ku Munich ku Germany inati: “Matchalitchi anasanduka malo oonetserako kanema ndi nyumba zogona: Okhulupirira sakupitanso kutchalitchi, malo olambiriramo akuwagwiritsa ntchito zina. . . . Zimene zakhala zikuchitika ku Netherland kapena ku England n’zimene zikuchitika ku Germany.” Nyuzipepalayi inapitiriza kunena kuti: “Munthu akhoza kupeza malo pafupifupi 30 kapena 40 odziŵika bwino amene ankagulitsa matchalitchi ku Germany zaka zingapo zapitazi.”
Kodi nyumba zolambiriramo n’zofunikadi polambira Mulungu? Kodi matchalitchi ochititsa kaso akutengera nyumba zolambiriramo zimene azifotokoza m’Malemba? Kodi ndi nyumba zotani zimene zakhala zikugwiritsidwa ntchito polambira Mulungu woona ndiponso wamoyo? Kodi tingaphunzirenji pa nyumba zimenezi pankhani ya kufunika kwa malo olambiriramo ndiponso zimene ziyenera kuchitika pa malo amenewo?