Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi munthu akawinda kwa Mulungu sangasinthe zivute zitani?

Malinga ndi Malemba, kuwinda ndiko kulonjeza kwa Mulungu ndi mtima wonse kuti munthu uchita chinachake, kupereka nsembe, kuchita utumiki kapena ntchito inayake, kapena kupeŵa kuchita zinthu zinazake zimene pazokha sizolakwika. M’Baibulo muli nkhani za kuwinda kumene kunadalira pa zimene Mulungu akanachita, m’ganizo lakuti munthu analonjeza kuchita chinachake akayamba Mulungu kuchita kenakake. Mwachitsanzo, Hana, mayi a mneneri Samueli “[a]nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera . . . ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.” (1 Samueli 1:11) Baibulo limafotokozanso kuti munthu amawinda mofuna yekha. Kodi munthu ukawinda kwa Mulungu sungasinthe?

Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inati: “Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita.” Inawonjezera kuti: “Chita chomwe unachiwindacho. Kusawinda kupambana kuwinda osachita.” (Mlaliki 5:4, 5) Chilamulo chimene Aisrayeli analandira kudzera mwa Mose chinati: “Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.” (Deuteronomo 23:21) Inde, kuwinda kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Munthu ayenera kuwinda pa zifukwa zomveka, ndipo powinda asakayikire zoti adzakwanitsa kuchita zimene wawindazo. Ngati sangatero, zingakhale bwino osawinda. Koma kodi munthu akawinda ndiye kuti ngakhale zitavuta sangasinthe?

Bwanji ngati zimene munthu anawinda zikum’pangitsa kuchita zinthu zimene kenako zikudziŵika kuti n’zosagwirizana ndi zimene Mulungu akufuna? Bwanji ngati mwina kunali kuwinda koti mwa njira ina kukugwirizanitsa makhalidwe oipa ndi kulambira koona? (Deuteronomo 23:18) Mwachionekere, munthu angasinthe kuwinda koteroko. Ndiponsotu, m’Chilamulo cha Mose, zimene mkazi anawinda zinkatha kuthetsedwa ndi bambo ake kapena mwamuna wake.​—Numeri 30:3-15.

Taganizaninso za munthu amene anawinda kwa Mulungu kuti adzakhala wosakwatira kapena wosakwatiwa koma tsopano akuona kuti wagwidwa njakata. Kuwinda kwakeko kwam’fikitsa poti akuona kuti kutsatirabe zimene anawindazo kukum’chititsa kutsala pang’ono kuswa miyezo ya Mulungu pankhani ya makhalidwe abwino. Kodi apitirizebe kutsatira zimene anawindazo? Kodi sikungakhale bwino kudziteteza kuti asakhale ndi mlandu wa kuchita chiwerewere mwa kusatsatira zimene anawindazo m’malo mwake n’kupempha Mulungu kuti amuchitire chifundo ndi kum’khululukira? Munthuyo ndi amene angasankhe zochita pankhaniyi. Palibe munthu wina amene angamusankhire zochita.

Bwanji ngati munthu wawinda ndipo kenako akuona kuti anachita zimenezo mopupuluma? Kodi ayenerabe kuumirira kuchita zimene anawindazo? Sizinali zophweka kuti Yefita achite zimene anawinda kwa Mulungu, koma chifukwa cha chikumbumtima anachitadi zimenezo. (Oweruza 11:30-40) Kulephera kuchita zimene munthu anawinda kungachititse Mulungu ‘kumukwiyira’ ndipo angawononge zimene munthuyo anachita. (Mlaliki 5:6) Kuona mopepuka nkhani ya kukwaniritsa zowinda kungachititse Mulungu kuleka kuyanja munthuyo.

Yesu Kristu anati: ‘Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi; ndipo chowonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.’ (Mateyu 5:37) Mkristu ayenera kudera nkhaŵa kuchita zimene anawinda kwa Mulungu ndiponso kukhala wokhulupirika m’mawu ake onse, kwa Mulungu ndiponso kwa anthu. Bwanji ngati akuona kuti wagwidwa njakata chifukwa choti anapanga pangano ndi munthu wina zimene poyamba zinaoneka ngati zabwino koma atapenda mosamalitsa akuona kuti sizinali zanzeru? Sayenera kuona nkhani zoterozo mopepuka. Koma mwa kukambirana mochokera pansi pa mtima, munthu winayo angaganize zom’masula ku panganolo.​—Salmo 15:4; Miyambo 6:2, 3.

Pankhani ya zowinda ndi nkhani zina, kodi chofunika kwambiri chimene tiyenera kuchiganizira n’chiyani? Ndicho chakuti nthaŵi zonse tiyenera kufunitsitsa kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu.

[Zithunzi pamasamba 30, 31]

Hana sanazengereze kuchita zimene anawinda

[Zithunzi pamasamba 30, 31]

Yefita anachita zimene anawinda ngakhale kuti kuchita zimenezo kunali kovuta