Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Imene Imalimbikitsa Makhalidwe Abwino

Ntchito Imene Imalimbikitsa Makhalidwe Abwino

Ntchito Imene Imalimbikitsa Makhalidwe Abwino

Cha kumapeto kwa chaka cha 2001, amene anatsekula wailesi ku nyumba yaikulu youlutsira mawu ya ku Mozambique anamva chilengezo chotsatirachi:

“Pulezidenti wa dziko lino anakayendera maofesi a Mboni za Yehova ku Maputo. Walimbikitsa mpingo umenewu kuti ulimbikire ntchito yake yolimbikitsa makhalidwe abwino m’mabanja ndiponso pa maphunziro a anthu achikulire kudzera mu sukulu zophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga. Pafupifupi anthu 10,000 apindula kale ndi pulogalamu imeneyi. Malinga ndi zimene Pulezidenti Chissano wanena, mapulogalamu ngati ameneŵa ndi ofunika kuwayamikira chifukwa amathandiza kwambiri anthu kuthetsa mavuto a kusaphunzira amene ali m’dziko lino.”

Chilengezochi chinapitiriza ndi mawu awa amene pulezidentiyu ananena: “N’zolimbikitsa zedi kwa ife kuona kuti anthu ambiri ali ndi chidwi pa nkhani yothetsa umbuli. Zikutisonyeza kuti anthu adzatithandiza kuchepetsa chiŵerengero cha anthu osadziŵa kulemba ndi kuŵerenga. Motero, ndikulimbikitsa Mboni za Yehova kulimbikira pulogalamu yothandiza anthu kudziŵa kulemba ndi kuŵerenga, m’chilankhulo chilichonse. Chofunika kwambiri n’chakuti anthu azitha kulemba ndi kuŵerenga ndi kuti angathe kudziŵitsana zinthu mosavuta ndipo m’tsogolo angathandize nawo mokwanira pankhani ya maphunziro.”

M’dziko lonse la Mozambique Mboni za Yehova zimachititsa maphunziro othandiza kudziŵa kulemba ndi kuŵerenga m’madera okwana 850 kuti anthu athe kudziŵerengera Mawu a Mulungu. Kuwonjezera pamenepa, Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba aulere okwana 50,000 mlungu uliwonse. Zonsezi ndi mbali ya ntchito ya padziko lonse yophunzitsa Baibulo imene ikuchitika m’maiko okwana 235 tsopano. (Mateyu 24:14) Inunso mungapindule ndi pulogalamu imeneyi. Khalani omasuka kulankhula ndi Mboni za Yehova za m’dera lanulo.