Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kutumikira ndi Mtima Umodzi

Pitirizani Kutumikira ndi Mtima Umodzi

Pitirizani Kutumikira ndi Mtima Umodzi

“Ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW], kuti onseŵa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.”​—Zefaniya 3:9.

1. Kodi n’chiyani chikuchitika pokwaniritsa ulosi wa pa Zefaniya 3:9?

ANTHU padziko lonse lerolino amalankhula zinenero pafupifupi 6,000. Kuwonjezera pa zinenero zimenezi palinso zinenero zina zing’onozing’ono zodalira madera amene anthuwo ali. Ngakhale kuti anthu amalankhula zinenero zosiyana kwambiri monga Chiarabu ndi Chizulu, Mulungu wachita chinachake chosangalatsa kwambiri. Wachititsa anthu kulikonse kuphunzira ndi kulankhula chinenero chimodzi chokha choyera. Zimenezi zikuchitika pokwaniritsa ulosi umene anapereka kudzera mwa mneneri Zefaniya kuti: “[Ine Yehova Mulungu] ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW], kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.”​—Zefaniya 3:9.

2. Kodi “chinenero choyera” n’chiyani ndipo chathandiza kuti pachitike chiyani?

2 “Chinenero choyera” ndicho choonadi cha Mulungu chimene chimapezeka m’Mawu ake, Baibulo. Chimenechi makamaka ndi choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu, umene udzayeretsa dzina la Yehova, kutsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse, ndiponso kubweretsa madalitso kwa anthu. (Mateyu 6:9, 10) Anthu a mitundu yonse ndiponso a mafuko onse amalankhula chinenero choyera popeza icho n’chinenero chokhacho chomwe chili choyera mwauzimu. Chimawathandiza kutumikira Yehova mogwirizana, kapena kuti “ndi mtima umodzi.”

Palibe Tsankho

3. Kodi n’chiyani chimatithandiza kutumikira Yehova mogwirizana?

3 Monga Akristu, ndife okondwa chifukwa cha kugwirizana kwa anthu a zinenero zosiyanasiyana kumene tili nako. Ngakhale kuti timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’zinenero zosiyanasiyana, tikutumikira Mulungu mogwirizana. (Salmo 133:1) Zimenezi n’zotheka chifukwa kulikonse kumene tikukhala m’dzikoli, timalankhula chinenero chimodzi chokha choyera chimene timatamanda nacho Yehova.

4. N’chifukwa chiyani sipayenera kukhala kusankhana pakati pa anthu a Mulungu?

4 Pakati pa anthu a Mulungu sipayenera kukhala tsankho. Mtumwi Petro anasonyeza bwino zimenezo pamene analalikira kunyumba ya mkulu wa asilikali wachikunja, Korneliyo, mu 36 C.E. ndipo zinamulimbikitsa kunena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Popeza zimenezo n’zoona, mumpingo wachikristu sitiyenera kusankhana, kupanga timagulu, kapena kukondera.

5. N’chifukwa chiyani n’kulakwa kuyambitsa timagulu mumpingo?

5 Pofotokoza za ulendo umene anapita ku Nyumba ya Ufumu, wophunzira wina wa pakoleji anati: “Nthaŵi zambiri matchalitchi amakhala a mtundu kapena fuko linalake. . . . Koma Mboni za Yehova zonse zinakhalira limodzi ndipo sizinakhale m’timagulu.” Komabe, anthu ena mumpingo wakale ku Korinto ankapanga timagulu. Popeza zimenezi zinayambitsa magaŵano, iwo anali kulepheretsa mzimu woyera wa Mulungu kugwira ntchito yake, chifukwa mzimuwo umalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere. (Agalatiya 5:22) Ngati titayambitsa timagulu mumpingo, ndiye kuti tikhala tikulimbana ndi mzimu. Motero, tiyeni tizikumbukira mawu a mtumwi Paulo kwa Akorinto akuti: “Ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.” (1 Akorinto 1:10) Paulo anatsindikanso za mgwirizano m’kalata imene analembera Aefeso.​—Aefeso 4:1-6, 16.

6, 7. Kodi ndi langizo lotani limene Yakobo anapereka pankhani ya kukondera, ndipo kodi mawu akewo amagwira ntchito bwanji?

6 Kuyambira kale, Akristu safunika kusankhana. (Aroma 2:11) Popeza ena mumpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anali kusonyeza kukondera anthu olemera, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Abale anga, musakhale nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Kristu, Ambuye wa ulemerero, ndi kusamala maonekedwe. Pakuti akaloŵa m’sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolidi, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akaloŵanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?”​—Yakobo 2:1-4.

7 Ngati osakhulupirira olemera ovala mphete zagolidi ndi zovala zapamwamba anafika pa msonkhano wachikristu pamodzinso ndi osakhulupirira osauka ovala zovala zosaoneka bwino, wolemerayo anali kum’samala bwino kwambiri. Anali kum’patsa pokhala “pabwino,” pamene wosaukayo ankamuuza kuti angoimirira kapena kukhala pansi kumapazi a munthu wina. Koma Mulungu mopanda tsankho anapereka nsembe ya dipo ya Yesu Kristu kwa anthu olemera ndi osauka mofanana. (Yobu 34:19; 2 Akorinto 5:14) Motero ngati tikufuna kusangalatsa Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima umodzi sitiyenera kukondera kapena ‘kutama anthu chifukwa choti tipindule.’​—Yuda 4, 16.

Peŵani Kudandaula

8. N’chiyani chinachitika chifukwa cha kudandaula kwa Aisrayeli?

8 Kuti tikhalebe ogwirizana ndiponso kuti Mulungu apitirize kutiyanja, tiyenera kumvera langizo la Paulo lakuti: “Chitani zonse kopanda madandaulo.” (Afilipi 2:14, 15) Aisrayeli osakhulupirika amene anawamasula ku ukapolo wa ku Igupto anam’dandaula Mose ndi Aroni ndipo motero anam’dandaula ngakhalenso Yehova Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, amuna onse a zaka zoyambira 20 kupita m’tsogolo, kupatulapo Yoswa ndi Kalebi ndi Alevi, sanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa m’malo mwake anamwalira m’kati mwa ulendo wa Israyeli wa zaka 40 m’chipululu. (Numeri 14:2, 3, 26-30; 1 Akorinto 10:10) Analangidwatu kwambiri chifukwa chodandaula!

9. Kodi n’chiyani chinachitikira Miriamu chifukwa cha kudandaula kwake?

9 Zimenezi zikusonyeza zimene zingachitikire mtundu wonse wa anthu odandaula. Bwanji nanga anthu odandaula paokha? Chabwino, mlongo wake wa Mose, Miriamu, pamodzi ndi mbale wake Aroni anadandaula kuti: “Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga?” Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Yehova anamva.” (Numeri 12:1, 2) Ndiyeno chinachitika n’chiyani? Miriamu amene ayenera kuti ndi amene anatsogolera kudandaulako, anachititsidwa manyazi ndi Mulungu. Motani? Anatero mwa kum’kantha ndi khate ndipo anabindikiritsidwa kunja kwa chigono kwa masiku asanu ndi aŵiri mpaka pamene anayeretsedwa.​—Numeri 12:9-15.

10, 11. N’chiyani chingachitike ngati kudandaula sikuthetsedwa? Perekani chitsanzo.

10 Kudandaula sikungokhudza zinthu zolakwika zokha. Anthu odandaula mosalekeza amaona kuti maganizo awo kapena udindo wawo ndizo zofunika kwambiri, amadziganizira kwambiri okha osati Mulungu. Ngati zimenezi sizithetsedwa, zimayambitsa kugawikana pakati pa abale auzimu ndipo zimawalepheretsa kutumikira Yehova ndi mtima umodzi. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti odandaulawo saleka kufotokoza madandaulo awo, mosakayika amayembekezera kuti apeza ena amene adzagwirizana nawo pa madandaulo awowo.

11 Mwachitsanzo, munthu wina angasulize mmene mkulu wina amasamalirira mbali zake mumpingo kapena mmene amagwirira ntchito zake. Ngati timvetsera wodandaulayo, tingayambe kuganiza mmene iye akuganizira. Mbewu za kusakhutirazo zisanadzalidwe m’maganizo mwathu, zimene mkuluyo ankachita sitinkaipidwa nazo, koma tsopano tayamba kuipidwa nazo. Kenako, palibe chilichonse chimene mkuluyo angachite chimene tingachione ngati n’chabwino, ndiyeno ifenso tingayambe kudandaula za iye. Khalidwe limeneli siloyenera mumpingo wa anthu a Yehova.

12. Kodi kudandaula kungakhudze bwanji ubwenzi wathu ndi Mulungu?

12 Kudandaula za amuna amene ntchito yawo ndi yoweta gulu la Mulungu kungachititse kuwanyoza. Kudandaula koteroko kapena kusawafunira zabwino kungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (Eksodo 22:28) Anthu onyoza osalapa sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 5:11; 6:10) Wophunzira Yakobo analemba za odandaula amene “[a]napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero,” kapena kuti amuna audindo mumpingo. (Yuda 8) Anthu odandaulawo Mulungu sanawayanje, ndipo ife tiyenera kupeŵa kutsatira khalidwe lawo loipalo.

13. N’chifukwa chiyani si madandaulo onse amene ali oipa?

13 Komabe, sikuti madandaulo onse ndi olakwika kwa Mulungu. Iye sananyalanyaze “kulira” kwa Sodomu ndi Gomora, m’malo mwake anawononga mizinda yoipa imeneyo. (Genesis 18:20, 21; 19:24, 25) Ku Yerusalemu, Pentekoste wa 33 C.E. atangochitika kumene, “kunauka chidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.” Chifukwa cha zimenezi, “khumi ndi aŵiriwo” anathetsa vutolo mwa kusankha “amuna asanu ndi aŵiri a mbiri yabwino” kuti agwire “ntchito” yogaŵa chakudya. (Machitidwe 6:1-6) Akulu masiku ano sayenera ‘kutseka makutu awo’ pakakhala madandaulo omveka. (Miyambo 21:13) Ndipo m’malo mosuliza okhulupirira anzawo, akulu ayenera kukhala olimbikitsa.​—1 Akorinto 8:1.

14. Kuti tipeŵe kudandaula, kodi ndi khalidwe liti limene likufunika kwambiri?

14 Tonsefe tifunika kupeŵa kudandaula chifukwa mtima wodandaula ndi wowononga mwauzimu. Mtima umenewo ungasokoneze mgwirizano wathu. M’malo mwake, tiyeni nthaŵi zonse tilole mzimu woyera utithandize kukhala achikondi. (Agalatiya 5:22) Kutsatira ‘lamulo lachifumu la chikondi’ kudzatithandiza kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima umodzi.​—Yakobo 2:8; 1 Akorinto 13:4-8; 1 Petro 4:8.

Peŵani Kusinjirira

15. Kodi mungasiyanitse bwanji miseche ndi kusinjirira?

15 Popeza kudandaula kungayambitse miseche, tiyenera kusamala zimene timanena. Miseche ndiyo kulankhula zopanda pake za anthu ena ndiponso zochita zawo. Koma kusinjirira ndiko kunena za bodza zokhudza munthu wina n’cholinga chomuipitsira mbiri yake. Kulankhula kotereku n’kwa njiru ndipo n’kosagwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. N’chifukwa chake Mulungu anauza Aisrayeli kuti: “Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako.”​—Levitiko 19:16.

16. Kodi Paulo ananena chiyani za anthu ena a miseche, ndipo kodi langizo lake liyenera kutikhudza bwanji?

16 Popeza kulankhula zopanda pake kungayambitse kusinjirira, Paulo anadzudzula anthu ena a miseche. Atafotokoza za amasiye amene anayenerera kulandira thandizo la mpingo, iye anadzanena za amasiye amene anaphunzira “kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.” (1 Timoteo 5:11-15) Ngati mkazi wachikristu aona kuti ndi wofooka pambali yolankhula nkhani zimene zingayambitse kusinjirira, ayenera kumvera langizo la Paulo lakuti akhale ‘wolemekezeka, wosadyerekeza.’ (1 Timoteo 3:11) Amuna achikristu ayeneranso kupeŵa miseche.​—Miyambo 10:19.

Musaweruze!

17, 18. (a) Kodi Yesu anati chiyani za kuweruza mbale wathu? (b) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mawu a Yesu onena za kuweruza?

17 Ngakhale ngati sitikusinjirira wina aliyense, tiyenera kuyesetsa ndi mtima wonse kupeŵa kuweruza. Yesu anatsutsa mtima woterowo pamene anati: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, kudzayesedwa kwa inunso. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwemwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m’diso lakoli. Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.”​—Mateyu 7:1-5.

18 Tisamati tikufuna kuchotsa “kachitsotso” chabe kamene kali m’diso la mbale wathu kuti timuthandize, pamene luso lathu loweruza moyenera laphimbika ndi “mtanda” wophiphiritsa. Ndipotu, ngati timamvetsetsa chifundo chimene Mulungu ali nacho, sitingakhale okonda kuweruza abale ndi alongo athu auzimu. Kodi tingathe bwanji kuwadziŵa monga mmene amawadziŵira Atate wathu wakumwamba? N’zosadabwitsa kuti Yesu anatichenjeza ‘kusaweruza kuti tingaweruzidwe.’ Kupenda moona mtima zofooka zathu kuyenera kutithandiza kupeŵa kuweruza kumene Mulungu angakuone kuti n’kosalungama.

Ofooka Koma Olemekezeka

19. Kodi okhulupirira anzathu tiziwaona bwanji?

19 Ngati tili otsimikiza mtima kutumikira Mulungu ndi mtima umodzi pamodzi ndi abale athu, sitidzangopeŵa chabe kuweruza. Tidzakhala patsogolo kuwalemekeza. (Aroma 12:10) Ndipotu, tidzawafunira zabwino osati kudzifunira zabwino ife tokha, ndipo mosangalala tidzagwira ntchito modzichepetsa m’malo mwawo. (Yohane 13:12-17; 1 Akorinto 10:24) Kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima woterowo? Tingakhale ndi mtima umenewu ngati tikumbukira kuti wokhulupirira aliyense ndi wamtengo wapatali kwa Yehova ndi kuti timafunika kuthandizana, monganso mmene chiwalo chilichonse cha thupi chimadalira ziwalo zinzake.​—1 Akorinto 12:14-27.

20, 21. Kodi mawu a pa 2 Timoteo 2:20, 21 amatanthauza chiyani kwa ife?

20 N’zoona kuti Akristu ndiwo zotengera zadothi zofooka zimene zapatsidwa chuma chamtengo wapatali cha utumiki. (2 Akorinto 4:7) Kuti tigwire ntchito yopatulika imeneyi ndi kutamanda Yehova, tiyenera kukhalabe olemekezeka kwa iye ndi Mwana wake. Tingakhale zotengera zaulemu zoti Mulungu azigwiritse ntchito ngati tikhalabe oyera mwauzimu ndiponso mwamakhalidwe. Pankhani imeneyi Paulo analemba kuti: “M’nyumba yaikulu simuli zotengera za golidi ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu. Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.”​—2 Timoteo 2:20, 21.

21 Anthu amene makhalidwe awo sakugwirizana ndi zimene Mulungu amafuna ndiwo ‘zotengera zopanda ulemu.’ Komabe, mwa kutsatira njira ya Mulungu, tidzakhala ‘zotengera za kuulemu zopatulidwa, zoyenera kuchita nazo Mbuye, zokonzera ntchito yonse yabwino.’ Ndiyeno tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndine “chotengera cha ulemu”? Kodi ndimalimbikitsa okhulupirira anzanga? Kodi mumpingo ndimagwira ntchito ndi mtima umodzi ndi okhulupirira anzanga?’

Pitirizani Kutumikira ndi Mtima Umodzi

22. Kodi mpingo wachikristu ungayerekezeredwe ndi chiyani?

22 Mpingo wachikristu ndi wofanana ndi banja. M’banja mumakhala chikondi, kuthandizana, ndi chisangalalo ngati onse m’banjamo amalambira Yehova. M’banja mungakhale anthu angapo a mitima yosiyana, koma aliyense amafunika ulemu. N’chimodzimodzinso mu mpingo. Ngakhale kuti tonsefe ndife osiyana ndiponso opanda ungwiro, Mulungu watikokera kwa iye kudzera mwa Kristu. (Yohane 6:44; 14:6) Yehova ndi Yesu amatikonda, ndipo mofanana ndi banja logwirizana, tifunikadi kukondana.​—1 Yohane 4:7-11.

23. Kodi tiyenera kukumbukira ndi kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

23 Mumpingo wachikristu wonga banja moyenera timayembekezera kupezamo anthu okhulupirika. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera [“okhulupirika,” NW], opanda mkwiyo ndi makani.” (1 Timoteo 2:8) Motero, Paulo anagwirizanitsa kukhulupirika ndi pemphero la onse “pamalo ponse” pamene Akristu amasonkhana pamodzi. Amuna okhulupirika okha ndi amene ayenera kuimira mpingo m’pemphero la onse. Inde, Mulungu amafuna kuti tonsefe tikhale okhulupirika kwa iye ndi kwa wina ndi mnzake. (Mlaliki 12:13, 14) Ndiyetu tiyeni titsimikize mtima kugwira ntchito pamodzi mogwirizana, mofanana ndi ziwalo za thupi. Tiyeninso titumikire mogwirizana monga mbali ya banja la olambira Yehova. Koposa zonse, tiyeni tizikumbukira kuti tifunika kuthandizana ndipo Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa ngati tipitiriza kutumikira Yehova ndi mtima umodzi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chiyani chimathandiza anthu a Yehova kuti amutumikire ndi mtima umodzi?

• N’chifukwa chiyani Akristu amapeŵa tsankho?

• Kodi mungati kudandaula n’koipa chifukwa chiyani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza okhulupirira anzathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Petro anazindikira kuti “Mulungu alibe tsankho”

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi mukudziŵa chifukwa chake Mulungu anachititsa manyazi Miriamu?

[Chithunzi patsamba 18]

Akristu okhulupirika amatumikira Yehova mosangalala ndi mtima umodzi