Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupereka Zoposa Zimene Munthu Angathe

Kupereka Zoposa Zimene Munthu Angathe

Kupereka Zoposa Zimene Munthu Angathe

“MUNGATHE kunditcha wopemphapempha; sindingadandaule. Ndikupemphetsera Yesu.” Mawu osapita m’mbali ameneŵa a mbusa wina wachipulotesitanti akusonyeza mkangano wokhudza mmene zipembedzo zimapezera ndalama. Zikuoneka kuti zipembedzo zomwe zili ndi ozitsatira ambiri zimayenda bwino pokhapokha ngati zapeza ndalama zambiri. Zifunika kupereka malipiro, akachisi ngofunika kumangidwa ndi kuwakonzetsanso, ndiponso m’pofunika ndalama za maulendo okalalikira. Kodi ndalama zofunika pa zinthu zimenezi zizipezedwa bwanji?

Kwa matchalitchi ambiri, yankho n’lakuti chakhumi. Mlaliki Norman Robertson anati: “Kupereka chakhumi ndiyo njira yomwe Mulungu akupezera ndalama zoyendetsera ufumu Wake pansi pano. Ndiyo njira Yake yopezera chuma chomwe chimathandiza kuti Uthenga Wabwino ulalikidwe.” Pokumbutsa om’tsatira ake za udindo wawo wopereka zinthu, iye ananena motsindika ndiponso mopanda manyazi, kuti: ‘Kupereka chakhumi si chinthu chomwe mumachita chifukwa choti mungathe kutero. Mumatero chifukwa cha kumvera. Kusapereka chakhumi n’kuswa malamulo a Mulungu mochita kuonekeratu. N’chimodzimodzi ndi kuba.’​—Tithing​—God’s Financial Plan.

Mosakayikira mukuvomereza inu kuti kupereka zinthu kuyenera kukhala mbali ya kulambira kwa Akristu. Komabe, kodi mumavutika chifukwa chokuumirirani kukupemphani ndalama, mwinanso kupsa nazo mtima kumene? Katswiri wina wamaphunziro a zaumulungu wa ku Brazil, Inácio Strieder anadzudzula matchalitchi chifukwa chogwiritsira ntchito kupereka chakhumi “pofuna kuthetsera mavuto awo” ndipo ananena kuti kuchita zimenezi “n’kosavomerezeka, ndi nkhanza, ndipo n’kuphonya mfundo zachipembedzo.” Iye anati chotsatira cha zimenezi n’chakuti “anthu omwe ali paulova, akazi amasiye, amphaŵi ndiponso anthu ongotsatira zinthu mwachimbulimbuli, amaganiza kuti Mulungu wawasiya ndipo akuyenera kupereka zinthu zambiri kwa ‘mlaliki’ moti mabanja awo amasoŵa chakudya.”

Mwina mungafunse kuti: ‘Kodi matchalitchi amene amakakamiza anthu kupereka chakhumi akugwiritsira ntchito Malemba moyenerera? Kapena kodi zipembedzo zina zikudyera anthu awo masuku pamutu powaopseza kuti Mulungu angadzawalange? Kunena zoona, kodi Mulungu amafuna kuti tizipereka zoposa zimene tingathe?’