Limbitsani Manja Anu
Limbitsani Manja Anu
M’BAIBULO, dzanja alitchula koposa ka 1,800. Zining’a zokhudza dzanja azigwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, dzanja loyera limaimira kupanda mlandu. (2 Samueli 22:21; Salmo 24:3, 4) Kutansa dzanja kapena kuoolowa dzanja kumatanthauza kukomera mtima anthu ena. (Deuteronomo 15:11; Salmo 145:16) Munthu amene wapulumutsidwa kwa adani amati wapulumutsidwa m’dzanja la adaniwo. (1 Samueli 4:3) Kulendeŵetsa dzanja kumatanthauza kukhumudwa. (2 Mbiri 15:7) Ndipo kulimbitsa dzanja kumatanthauza kukhala wokonzeka ndi kupeza mphamvu kuti munthu achite kanthu.—1 Samueli 23:16.
Masiku ano, tikufunika kwambiri kulimbitsa manja athu. Tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Anthufe tikakhumudwa, nthaŵi zambiri timakonda kutaya mtima, kulendeŵetsa manja athu. Sizachilendo kuona achinyamata akusiya sukulu, amuna akusiya mabanja awo, ndipo azimayi akusiya ana awo. Ife monga Akristu, tifunika kulimbitsa manja athu kuti tipilire mayesero amene timakumana nawo potumikira Mulungu. (Mateyu 24:13) Tikatero, timasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
Mmene Manja Amalimbitsidwira
Ayuda a nthaŵi ya Ezara anafunika kulimbitsa manja awo kuti amalize kumanganso kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Kodi manja awo analimbitsidwa bwanji? Nkhaniyo imati: “[A]nasunga madyerero a mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi aŵiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja awo mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.” (Ezara 6:22) Inde, Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu yake yogwira ntchito kulimbikitsa “mfumu ya Asuri” kuti ilole anthu a Mulungu kubwerera ndipo analimbikitsa anthu kuchitapo kanthu, moti anamaliza ntchito imene anaiyambayo.
Kenako, pamene malinga a Yerusalemu anafunikira kuwakonza, Nehemiya analimbitsa manja a abale ake kuti agwire ntchitoyo. Timaŵerenga kuti: “Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mawu anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.” Manja awo atalimbitsidwa, Nehemiya ndi Ayuda anzake anatha kumanganso malinga a Yerusalemu m’masiku 52 okha basi.—Nehemiya 2:18; 6:9, 15.
Mofananamo, Yehova amalimbitsa manja athu kuti tilalikire uthenga wabwino wa Ufumu. (Mateyu 24:14) Amachita zimenezo mwa ‘kutiyesa [“kutikonzekeretsa ndi,” NW] chinthu chilichonse chabwino kuti tichite chifuniro chake.’ (Ahebri 13:21) Iye watipatsa zida zapamwamba kwambiri. Tili ndi Baibulo ndi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, magazini, mabulosha, mathirakiti, ndi makaseti a wailesi ndi a vidiyo zoti tigwiritse ntchito polalikira kwa anthu padziko lonse lapansi. Ndipotu, zofalitsa zathu zikupezeka m’zinenero zoposa 380. Ndiponso, kudzera m’misonkhano ya mpingo ndi m’misonkhano yaikulu, Yehova amatiphunzitsa maphunziro auzimu ndi mmene tingagwiritsire ntchito chida chabwino chimenechi pokwaniritsa utumiki wathu.
Ngakhale kuti Yehova amalimbitsa manja athu m’njira zambiri, iye amafunanso kuti tichite khama. Takumbukirani zimene Elisa anauza Mfumu Yoasi, amene anapita kwa Elisa kukafuna thandizo kuti alimbane ndi Aaramu. Elisa anauza mfumuyo kuti itenge mivi ndi kukwapula nayo pansi. Nkhani ya m’Baibuloyo imati: “[A]nakwapula katatu, naleka. Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.” (2 Mafumu 13:18, 19) Chifukwa cholephera kuchita khama, Yoasi anagonjetsa Aaramu maulendo ochepa okha basi.
Mfundo imeneyi ikugwiranso ntchito kwa ife ngati tikufuna kukwaniritsa zimene Yehova watipatsa kuti tichite. M’malo modandaula ndi zopinga zimene timakumana nazo kapena kudandaula chifukwa cha kuvuta kwa ntchito imene tapatsidwa, tiyenera kuigwira mwakhama ndiponso ndi mtima wonse. Tifunika kulimbitsa manja athu ndi kudalira Yehova kuti atithandize.—Yesaya 35:3, 4.
Yehova Adzalimbitsa Manja Athu
Yehova sadzalephera kutithandiza ndi kulimbitsa manja athu kuti tichite chifuniro chake. Sikuti Mulungu adzachita zozizwitsa ndiponso kutichitira zinthu zonse ayi. Amafuna kuti nafenso tichite mbali yathu, kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse, kukonzekera ndi kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse, kuchita nawo utumiki nthaŵi zambiri malinga ndi mmene tingathere, ndi kupemphera kwa iye nthaŵi zonse. Ngati tichita mbali yathu mokhulupirika ndiponso mwakhama pamene tili ndi mpata wotero, Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tichite zimene iye akufuna.—Afilipi 4:13.
Taganizirani za Mkristu wina amene mkazi wake komanso mayi ake anamwalira chaka chimodzi. Chisoni chimenecho chisanathe, mpongozi wake anathawa mwana wake wamwamuna n’kusiya njira yamoyo yachikristu. Mbaleyu anati: “Ndinaphunzira kuti sitingasankhe kuti atigwere mayesero akutiakuti, ndiponso nthaŵi imene angatigwere. Sitingathenso kusankha kuti atigwere kangati.” Kodi akupeza bwanji mphamvu zoti apirirebe? Iye anati: “Pemphero ndi phunziro laumwini zandilimbikitsa kwambiri ndipo zandithandiza kukhalabe ndi moyo. Ndipo thandizo la abale ndi alongo anga auzimu landilimbikitsa kwambiri. Koposa zonse, ndazindikira kufunika kokhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova mavuto asanabuke.”
Kaya mukukumana ndi zotani m’moyo wanu, tsimikizani mtima kudalira kwambiri Yehova ndi kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene iye amapereka kuti mulimbitse manja anu. Mukatero mudzatha kum’tumikira bwino Yehova ndipo motero mudzatamanditsa ndi kulemekezetsa dzina lake.—Ahebri 13:15.
[Chithunzi patsamba 31]
Chifukwa cholephera kuchita khama, Yoasi anagonjetsa Aaramu maulendo ochepa okha basi