Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Poona mmene lemba la Chivumbulutso 20:8 limafotokozera, kodi tinene kuti padzakhala anthu ambirimbiri amene Satana adzawasokeretsa pa chiyeso chomaliza?

Lemba la Chivumbulutso 20:8 limafotokoza kuukira komaliza kwa Satana pa anthu amene adzakhala pa dziko lapansi pamapeto pa ulamuliro wa zaka 1000 wa Mfumu ya Umesiya. Pofotokoza za Satana, vesilo limati: “[A]dzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinayi za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiŵerengero chawo cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.”

Ngakhale kuti njira ndi zipangizo za sayansi zapita patsogolo kwambiri, sizikudziŵikabe kuti “mchenga wa ku kunyanja” ndi nambala yaikulu bwanji. Motero, tinganene kuti mawu ameneŵa akuimira nambala yosadziŵika. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti imeneyi ndi nambala yaikulu zedi, kapena yangokhala nambala yosadziŵika komabe yokulirapo ndithu?

M’Baibulo, mawu akuti “ngati mchenga wa kunyanja” amawagwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, pa Genesis 41:49 timaŵerenga kuti: “Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuŵerenga; chifukwa anali wosaŵerengeka.” Apa nkhani yagona pakuti tiriguyo anali wosaŵerengeka. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anati: “Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbewu za Davide mtumiki wanga.” Monga mmene zilili zotsimikizika kuti nyenyezi za kumwamba ndi mchenga wa kunyanja sizingaŵerengedwe, n’zotsimikizikanso kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake kwa Davide.​—Yeremiya 33:22.

Nthaŵi zambiri, mawu akuti “mchenga wa kunyanja” amatanthauza zinthu zochulukirapo kapena zochuluka ndithu. Aisrayeli ali ku Giligala anasauka mtima ndi ankhondo a Afilisti amene anasonkhana ku Mikimasi, omwe anali ‘ochuluka monga mchenga wa pa doko la nyanja.’ (1 Samueli 13:5, 6; Oweruza 7:12) Ndiponso “Mulungu anam’patsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziŵa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m’mbali mwa nyanja.” (1 Mafumu 4:29) Ngakhale kuti chilichonse chimene anachitchula m’mavesi ameneŵa chinali chochuluka ndithu, chiŵerengero chake chinali ndi polekezera.

Mawu akuti “mchenga wa kunyanja” angaimirenso nambala yosadziŵika, popanda kusonyeza kuti ndi yaikulu kwambiri. Yehova anauza Abrahamu kuti: “Kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Genesis 22:17) Pobwereza lonjezo limeneli kwa Yakobo, mdzukulu wa Abrahamu, Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti “fumbi lapansi,” amene Yakobo pobwereza kutchula mawuŵa anati “mchenga wa pa nyanja yaikulu.” (Genesis 28:14; 32:12) Monga mmene zinakhalira, kupatulapo Yesu Kristu, “mbewu” ya Abrahamu ndi yokwana 144,000, imene Yesu anaitcha “kagulu ka nkhosa.”​—Luka 12:32; Agalatiya 3:16, 29; Chivumbulutso 7:4; 14:1, 3.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zimenezi? Tikuphunzira kuti mawu akuti “ngati mchenga wa kunyanja” sikuti nthaŵi zonse amatanthauza nambala yaikulu zedi, yopanda mapeto, ayi. Ndiponso tikuphunzira kuti sikuti nthaŵi zonse imagwiritsidwa ntchito pofotokoza zinthu zochuluka zedi, ayi. Nthaŵi zambiri mawuŵa amatanthauza nambala yosadziŵika koma yaikulu ndithu. Motero, m’pake kukhulupirira kuti anthu opanduka amene adzakhala kumbali ya Satana poukira komaliza anthu a Mulungu sadzakhala ochulukitsitsa, komabe adzakhala ochuluka ndithu moti n’kuopseza ena. Koma pakalipano sizikudziŵika kuti ndi ochuluka bwanji.