Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthaŵi Yabwino Yokhala ndi Moyo

Nthaŵi Yabwino Yokhala ndi Moyo

Nthaŵi Yabwino Yokhala ndi Moyo

MUKAKHALA pamavuto, kodi mumalakalaka kale litabwerera? Ndiye taganizirani mawu a Mfumu yanzeru Solomo, akuti: “Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.”​—Mlaliki 7:10.

N’chifukwa chiyani Solomo anapereka malangizo ameneŵa? Chifukwa chakuti ankadziŵa kuti kuliganizira bwino kale n’kothandiza kwambiri polimbana ndi mavuto a makono. N’kutheka kuti anthu amene amalakalaka kale litabwerera amaiŵala kuti kalelo nalonso linali ndi mikwingwirima komanso kuti moyo sunkakoma nthaŵi zonse. Mwina zinthu zina kalelo zinkayenda bwino, koma n’zodziŵikiratu kuti si zonse. Monga momwe Solomo ananenera, n’kupanda nzeru kuganizira za kale mosayenera, popeza n’zodziŵikiratu kuti kalelo silingabwerere.

Kodi pali vuto lililonse kulakalaka zinthu zitakhala monga kale? Inde, ngati kuchita zimenezo kutilepheretsa kuti tisinthe ndi kugwirizana ndi makono kapena ngati kutilepheretsa kusangalala ndi nthaŵi imene tikukhalamo ino komanso ndi zinthu zomwe tikuyembekezera m’tsogolo.

Kunena zoona, ino ndiyo nthaŵi yabwino yokhala ndi moyo, ngakhale kuti mavuto akuwonjezeka m’dzikoli. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti tikuyandikira nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi ndiponso madalitso a ulamuliro wamtendere wa Ufumu wake. Baibulo limalonjeza kuti: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Ndiyeno, zinthu zikadzakhala bwino choncho, palibe amene adzakhale ndi chifukwa chofunira kale litabwerera.