Pa Tebulo la Mmalinyero Wamkulu
Pa Tebulo la Mmalinyero Wamkulu
ANTHU ochititsa kaso, chakudya chokoma, ndi nkhani zosangalatsa zimapangitsa kuti nthaŵi ya chakudya pa tebulo la mmalinyero wamkulu m’sitima ikhale yosangalatsa. Koma kukambirana komwe kunachitika pa tebulo la Captain Robert G. Smith, wa kampani ya maulendo a panyanja ya White Star Line, kunam’tsegula maso pa chakudya chauzimu.—Yesaya 25:6.
Mu 1894, pamsinkhu wa zaka 24, Robert anatsogolera ulendo wa sitima yapanyanja ya Kinclune of Dundee ndipo unali ulendo wake woyamba wozungulira dziko lonse. Kenako anatsogoleranso maulendo a sitima zina za kampani ya White Star monga Cedric, Cevic, ndi Runic. * Pamene ankadutsa nyanja ya Atlantic pochoka ku New York kupita ku Liverpool, ku England, pa imodzi mwa sitimazi, Robert anachereza Charles Taze Russell pa tebulo lake. Nkhani yomwe anakambirana ndi Russell inachititsa Robert kuyamba kukhala ndi chidwi ndi uthenga wa Baibulo, ndipo pofuna kuti akaphunzire zambiri, iye analandira mabuku a Studies in the Scriptures kuchokera kwa Russell.
Russell ankamulembera Robert makalata, ndipo izi zinachititsa kuti chidwi chake pa uthenga wa Baibulo chikule. Robert anafotokozera mkazi wake zinthu zomwe anali atangodziŵa kumenezo. Sipanapite nthaŵi yaitali, onse aŵiri anakhala achangu monga Ophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo nthaŵi imeneyo. Pambuyo pake, Robert anali ndi mwayi wokamba nkhani za Baibulo. Mwachitsanzo, ku Brisbane, m’dziko la Australia, anakamba nkhani yakuti “Mvunguti wa Gileadi” ndipo anasonyeza mmene Mawu a Mulungu alili ndi uthenga womwe ndi “mankhwala othetsera mavuto onse a dzikoli.” Ku England, mkazi wake ndi ana ake ang’onoang’ono anathandiza kuonetsa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” ndi kumaika makaseti a mawu a Russell pamene amaonetsa kanemayo.
Robert anapatsa ana ake choloŵa cha choonadi cha Baibulo chimene iye analandira. Lero, patapita mibadwo isanu, anthu 18 mwa mbumba yake ali kalikiliki kuuza ena uthenga wabwino, kusangalala ndi chakudya chomwe chinali pa tebulo la mmalinyero wamkulu.
Kudzera m’mabuku awo ndiponso ntchito yawo yophunzitsa Baibulo, Mboni za Yehova zikuthandiza anthu padziko lonse kuphunzira uthenga wa Baibulo womwe Captain Smith anasangalala nawo kwambiri. Nanunso mungapeze chomwe chinali chosangalatsa kwambiri pa tebulo la mmalinyero wamkulu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Sitima yofanana ndi imeneyi inali Titanic, yomwe inaphwasuka paulendo wake woyamba ndipo panthaŵi ya ngoziyo inkatsogoleredwa ndi Captain E. J. Smith (panalibe ubale uliwonse ndi Robert).
[Chithunzi patsamba 8]
Robert G. Smith
[Chithunzi patsamba 8]
Charles T. Russell