Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunziro Laumwini Limene Limatikonzekeretsa Monga Aphunzitsi

Phunziro Laumwini Limene Limatikonzekeretsa Monga Aphunzitsi

Phunziro Laumwini Limene Limatikonzekeretsa Monga Aphunzitsi

“Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo,” NW] kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho.”​—1 Timoteo 4:15, 16.

1. Kodi nthaŵi ndi phunziro laumwini zimagwirizana bwanji?

“KANTHU kali konse kali ndi nthaŵi yake,” limatero Baibulo pa Mlaliki 3:1. Zimenezi zilinso choncho pankhani ya phunziro laumwini. Ambiri zimawavuta kusinkhasinkha zinthu zauzimu ngati ili nthaŵi yolakwika ndiponso akakhala pamalo olakwika. Mwachitsanzo, kodi mungakonde kuphunzira mutagwira ntchito yolemetsa pa tsikulo ndi kudya kwambiri chakudya chamadzulo, ndiponso makamaka ngati mwakhala pa mpando wanu wawofuwofu umene mumaukonda uku mukuonera TV? Zokayikitsa. Nanga tingathetse bwanji vutoli? Mwachionekere, pokhala n’cholinga choti tipindule kwambiri ndi phunziro lathu, tiyenera kusankha kuti ndi nthaŵi yanji imene tingaphunzire ndiponso kuti tikaphunzirira kuti.

2. Kodi kaŵirikaŵiri nthaŵi yabwino yochita phunziro laumwini ndi iti?

2 Ambiri amaona kuti nthaŵi yabwino kuphunzira ndiyo kum’maŵa pamene maganizo awo ali ogalamuka. Ena amaphunzira masana panthaŵi yopuma. Taonani za nthaŵi imene anachitira zinthu zofunika kwambiri zauzimu m’zitsanzo zotsatirazi. Mfumu Davide ya Israyeli wakale inalemba kuti: “Mundimvetse chifundo chanu mamaŵa; popeza ndikhulupirira Inu: mundidziŵitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.” (Salmo 143:8) Mneneri Yesaya anasonyezanso kuti ankaona kuphunzira kukhala kofunika pamene analemba kuti: “Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m’maŵa ndi m’maŵa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.” Mfundo ndi yakuti tifunika kuphunzira ndi kulankhula ndi Yehova pa nthaŵi imene tingathe kuika maganizo athu pa zimene tikuphunzirazo, zilibe kanthu kuti ndi nthaŵi yanji.​—Yesaya 50:4, 5; Salmo 5:3; 88:13.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimafunika kuti phunziro likhale lopindulitsa?

3 Chinthu chinanso chofunika kuti tithe kuphunzira bwino n’chakuti sitiyenera kukhala pa mpando wa ndakhuta ndalema kapena pa sofa. Sitingathe kuika maganizo pa phunzirolo ngati tikhala pa malo otero. Tikamaphunzira, maganizo athu amafunika kuti azigalamuka, pamene kukhala pampando wawofuwofu sikugalamutsa maganizo athu. Ndiponso malo abwino oŵerengera ndi kusinkhasinkha ayenera kukhala opanda phokoso ndiponso opanda zododometsa. Simungapindule ngati muyesa kuphunzira mukumvetsera wailesi, kuonera TV, kapena pali ana oti muwalabadire. Pamene Yesu anafuna kusinkhasinkha, anapita pamalo oduka mphepo. Iye ananenanso kuti n’kofunika kupeza malo amseri pofuna kupemphera.​—Mateyu 6:6; 14:13; Marko 6:30-32.

Phunziro Laumwini Limene Limatikonzekeretsa Kuyankha

4, 5. Kodi bulosha la Mulungu Amafunanji n’lothandiza bwanji?

4 Phunziro laumwini limasangalatsa tikamagwiritsira ntchito zothandizira kumvetsa Baibulo kuti timvetse kwambiri nkhaniyo, makamaka tikamatero pofuna kukayankha mafunso ochokera pansi pa mtima amene munthu wina wafunsa. (1 Timoteo 1:4; 2 Timoteo 2:23) Monga poyambira, atsopano ambiri akuphunzira bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, * limene tsopano likupezeka m’zinenero 261. Buloshali limafotokoza zinthu mosavuta kumva koma molunjika ndipo zonse zili mmenemo n’zochokera m’Baibulo. Limathandiza oŵerenga kudziŵa mofulumira zimene Mulungu amafuna kwa olambira oona. Komabe popeza ndi bulosha, n’zosatheka kufotokoza nkhani iliyonse mwatsatanetsatane. Ngati wophunzira wanu wafunsa mafunso ochokera pansi pa mtima okhudza nkhani zina za m’Baibulo zimene mukukambirana, kodi mungapeze bwanji mfundo zina za m’Baibulo zimene zingamuthandize kuyankha mafunso amenewo?

5 Amene ali ndi Watchtower Library yomwe ndi ya pakompyuta m’chinenero chawo, n’kosavuta kupeza magwero ambiri a nkhani pa kompyutapo. Nanga bwanji amene alibe kompyuta? Tiyeni tione nkhani ziŵiri zimene azifotokoza m’bulosha la Mulungu Amafunanji kuti tione mmene tingawonjezere kumvetsa kwathu ndi kutha kuyankha mwatsatanetsatane, makamaka munthu akafunsa mafunso onga akuti, Kodi Mulungu ndani, ndiponso kodi Yesu anali wotani makamaka?​—Eksodo 5:2; Luka 9:18-20; 1 Petro 3:15.

Kodi Mulungu Ndani?

6, 7. (a) Kodi pali funso lotani lokhudza Mulungu? (b) Kodi mtsogoleri wina wachipembedzo anaphonya mfundo yofunika kwambiri iti pamene anali kukamba nkhani?

6 Phunziro 2 m’bulosha la Mulungu Amafunanji limayankha funso lofunika kwambiri lakuti, Kodi Mulungu Ndani? Limeneli ndi funso lofunika kwambiri chifukwa munthu sangalambire Mulungu woona pamene sakumudziŵa kapena amakayikira ngati aliko. (Aroma 1:19, 20; Ahebri 11:6) Komabe, anthu padziko lonse ali ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana za amene Mulungu ali. (1 Akorinto 8:4-6) Gulu lililonse la chipembedzo lili ndi mayankho akeake okhudza funso lakuti Mulungu ndani. Mipingo yambiri ya Matchalitchi Achikristu imakhulupirira kuti Mulungu ndi wa Utatu. Mtsogoleri wina wachipembedzo wotchuka ku United States anakamba nkhani yakuti “Kodi Mumam’dziŵa Mulungu?” koma m’nkhani yake yonse sanatchule n’kamodzi komwe dzina la Mulungu, ngakhale kuti anagwira mawu kangapo Malemba Achihebri. Iye anali kuŵerenga m’Baibulo limene linagwiritsira ntchito mawu osokoneza ndiponso osatchula dzina akuti “Ambuye” m’malo mwa Yehova kapena Yahweh.

7 Mtsogoleri wachipembedzo ameneyu anaphonyatu mfundo yofunika kwambiri pamene anagwira mawu pa Yeremiya 31:33, 34 pamene pamati: “Sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziŵe Ambuye [Chihebri, Mudziŵe Yehova]; pakuti iwo onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Ambuye [Chihebri, Yehova].” Baibulo limene anagwiritsira ntchito linalibe dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova.​—Salmo 103:1, 2.

8. Kodi n’chiyani chikusonyeza kufunika kogwiritsira ntchito dzina la Mulungu?

8 Lemba la Salmo 8:9 limasonyeza chifukwa chake kugwiritsira ntchito dzina la Yehova n’kofunika kwambiri. Lembalo limati: “Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!” Tayerekezerani zimenezo ndi mmene vesili lilili m’mabaibulo ena omwe amati: “AMBUYE, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!” (King James Version; mungaonenso mu The New American Bible, The Holy Bible​—New International Version, Tanakh​—The Holy Scriptures) Inde, monga tinafotokozera m’nkhani yapitayo, ‘tingam’dziŵedi Mulungu’ ngati tilola Mawu ake kutiunikira. Koma kodi ndi chothandizira kuphunzira Baibulo chiti chimene chingatiyankhe mosavuta mafunso okhudza kufunika kwa dzina la Mulungu?​—Miyambo 2:1-6.

9. (a) Kodi ndi bulosha liti limene lingatithandize kufotokoza kufunika kogwiritsira ntchito dzina la Mulungu? (b) Kodi omasulira ambiri alephera bwanji kulemekeza dzina la Mulungu?

9 Tingagwiritsire ntchito bulosha lakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, limene alimasulira m’zinenero 69. * Chigawo chakuti “Dzina la Mulungu​—Tanthauzo ndi Matchulidwe Ake” (masamba 6 mpaka 11) chimasonyeza kuti zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu m’Chihebri zimapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’malemba akale a Chihebri. Komabe, atsogoleri achipembedzo ndi omasulira a Chiyuda ndiponso a Matchalitchi Achikristu achotsa dala dzinalo m’mabaibulo awo ambiri. * Kodi anganene bwanji kuti amam’dziŵa Mulungu ndi kukhala naye pa ubwenzi wovomerezeka ngati akukana kumuitanira dzina lake? Dzina lake lenileni limathandiza kumvetsa zolinga zake ndi kum’dziŵa kuti iyeyo ndani. Ndiponso kodi mbali ya pemphero lachitsanzo la Yesu yakuti “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe,” ingakhale ndi phindu lanji ngati dzina la Mulungu silikugwiritsidwa ntchito?​—Mateyu 6:9; Yohane 5:43; 17:6.

Kodi Yesu Kristu Ndani?

10. Kodi ndi njira ziti zimene zingatithandize kumvetsa bwino moyo wa Yesu ndi utumiki wake?

10 Phunziro 3 m’bulosha la Mulungu Amafunanji lili ndi mutu wakuti “Kodi Yesu Kristu Ndani?” M’ndime zisanu ndi imodzi zokha, phunziroli likufotokoza mwachidule za Yesu, chiyambi chake, ndi cholinga chake pobwera padziko lapansili. Komabe, ngati mukufuna nkhani yatsatanetsatane ya moyo wake, buku labwino kwambiri limene mungagwiritsire ntchito, kupatulapo Mauthenga Abwino enieniwo, ndilo Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, limene likupezeka m’zinenero 111. * Buku limeneli limafotokoza za moyo wa Kristu ndi zimene anaphunzitsa, malinga ndi mmene Mauthenga Abwino amafotokozera, ndipo lafotokoza zochitika motsatizana malinga ndi nthaŵi imene zinachitikira. Muli mitu 133 ndipo ikufotokoza zimene zinachitika m’moyo wa Yesu ndi muutumiki wake. Ngati mukufuna kuona kufotokoza kwina kwatsatanetsatane, mungaone m’buku la Insight, Voliyumu 2, pa mutu wakuti “Jesus Christ.”

11. (a) Kodi Mboni za Yehova zimasiyana bwanji ndi ena pa chikhulupiriro chawo pankhani ya Yesu? (b) Kodi malemba ena a m’Baibulo amene amatsutsa momveka chiphunzitso cha Utatu ndi ati, ndipo ndi bulosha liti limene lingathandize pa mbali imeneyi?

11 M’Matchalitchi Achikristu, kutsutsana pa nkhani ya Yesu kwagona pakuti kaya iye ndi “Mwana wa Mulungu” komanso “Mulungu Mwana.” M’mawu ena, amalimbana pa zimene katekisima wa Akatolika (Catechism of the Catholic Church) amatcha ‘chinsinsi chachikulu cha chikhulupiriro chachikristu,’ chomwe ndi Utatu. Mosiyana ndi Matchalitchi Achikristu, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Yesu analengedwa ndi Mulungu koma iye si Mulungu. Bulosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? limene alimasulira m’zinenero 95 limafotokoza bwino nkhani imeneyi. * Ena mwa malemba ambiri amene lagwiritsira ntchito potsutsa chiphunzitso cha Utatu ndiwo Marko 13:32 ndi 1 Akorinto 15:24, 28.

12. Kodi ndi funso lina liti limene tifunika kuliganizira?

12 Zimene takambirana pamwambapa zokhudza Mulungu ndi Yesu Kristu zikutithandiza kuona mmene tingachitire phunziro laumwini n’cholinga choti tithandize anthu omwe sakudziŵa choonadi cha Baibulo kuti adziŵe zolondola. (Yohane 17:3) Nanga bwanji amene akhala akusonkhana ndi mpingo wachikristu kwa zaka zambiri? Popeza adziŵa zambiri za m’Baibulo, kodi akufunikanso kuonetsetsa kuti akuchita phunziro laumwini la Mawu a Yehova?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kudzipenyerera’?

13. Kodi ena angakhale ndi maganizo olakwika ati pankhani ya phunziro laumwini?

13 Ena amene akhala mumpingo wachikristu kwa zaka zambiri angakhale ndi chizoloŵezi chongodalira zinthu za m’Baibulo zimene anazidziŵa m’zaka zawo zoyamba atakhala Mboni za Yehova. N’zosavuta kuganiza kuti: “Sindifunika kuphunzira kwambiri monga mmene angachitire anthu atsopano. Ndipotu tangoonani nthaŵi zimene ndaŵerenga Baibulo lonse ndi mabuku othandizira kuphunzira Baibulo m’zaka zonsezi.” Zimenezi zingafanane ndi kunena kuti: “Sindiyenera kudera nkhaŵa kwambiri ndi mmene ndikudyera masiku ano, chifukwa tangoganizani zakudya zimene ndadya m’zaka zapitazi.” Tikudziŵa kuti thupi nthaŵi zonse limafuna kudya chakudya chabwino ndiponso chokonzedwa bwino kuti likhale lathanzi ndi kuti lizitha kugwira bwino ntchito. Ngati zili choncho ndi thanzi lakuthupi, kuli bwanji nanga thanzi lauzimu! Inde, tiyenera kuyesetsa kuti likhalebe labwino ndiponso lamphamvu.​—Ahebri 5:12-14.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzipenyerera nthaŵi zonse?

14 Choncho, tonsefe, kaya takhala tikuphunzira Baibulo kwa nthaŵi yaitali kapena ayi, tifunika kumvera zimene Paulo analangiza Timoteo, yemwe panthaŵiyo anali woyang’anira wokhwima mwauzimu. Iye anati: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:15, 16) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a Paulo ameneŵa? Kumbukirani kuti Paulo anafotokozanso kuti tikulimbana ndi “machenjerero a Mdyerekezi” ndiponso ‘mizimu yoipa yakumwamba.’ Ndipo mtumwi Petro anachenjeza kuti Mdyerekezi “[a]kufunafuna wina akamlikwire,” ndipo “wina” ameneyo angakhale aliyense wa ife. Kudziona ngati ndife achikwanekwane kungangopereka mpata umene iye amaufunafuna.​—Aefeso 6:11, 12; 1 Petro 5:8.

15. Kodi tili ndi chitetezo chauzimu chotani, ndipo tingachilimbitse bwanji?

15 Ndiyeno kodi tili ndi chitetezo chotani? Mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti: “Mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachirimika.” (Aefeso 6:13) Kugwira bwino ntchito kwa zida zauzimu zimenezo kumadalira osati kokha mmene zidazo zinalili poyamba koma kumadaliranso mmene tikuzisamalirira nthaŵi ndi nthaŵi. Motero, zida za Mulungu zonse zimenezo ziyenera kuphatikizapo chidziŵitso cha Mawu a Mulungu chamakono. Zimenezi zikusonyeza kufunika koti tisamatsalire m’mbuyo pakamvedwe kathu ka choonadi chimene Yehova akuvumbula kudzera m’Mawu ake ndi mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Phunziro laumwini la nthaŵi zonse la Baibulo ndi la mabuku othandiza kuphunzira Baibulo n’lofunika kwambiri kuti zida zathu zauzimu zikhalebe zamphamvu.​—Mateyu 24:45-47; Aefeso 6:14, 15.

16. Kodi tingachite chiyani kuti tionetsetse kuti “chikopa [chathu] cha chikhulupiriro” chili bwinobwino?

16 Paulo anasonyeza chida chachikulu mwa zida zathu chomwe ndi “chikopa cha chikhulupiriro,” chimene tingadzibise nacho ndi kuzima nacho mivi yoyaka moto ya Satana ya kutineneza kwabodza ndi ziphunzitso za anthu a mpatuko. (Aefeso 6:16) Motero, n’kofunika kwambiri kutsimikizira ngati chikopa chathu cha chikhulupiriro chili cholimba ndiponso kuona njira zimene tingatsatire kuti chikhalebe chabwino ndi kuchilimbitsa. Mwachitsanzo, mungafunse kuti: ‘Kodi ndimakonzekera bwanji phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu logwiritsira ntchito Nsanja ya Olonda? Kodi ndaphunzira mokwanira moti ndingathe “kufulumiza ena ku chikondano ndi ntchito zabwino” mwa kupereka mayankho abwino pa misonkhano? Kodi ndimatsegula Baibulo ndi kuŵerenga malemba amene awasonyeza koma osawagwira mawu? Kodi ndimalimbikitsa ena mwakutenga nawo mbali mwachangu pa misonkhano?’ Chakudya chathu chauzimu n’cholimba ndipo chimafunika kuchigaya mokwanira kuti tipindule nacho.​—Ahebri 5:14; 10:24.

17. (a) Kodi ndi zinthu zoipa ziti zimene Satana akugwiritsira ntchito kuti awononge moyo wathu wauzimu? (b) Kodi tingadziteteze bwanji ku zinthu zowononga za Satana?

17 Satana amadziŵa zofooka za thupi lopanda ungwiro, ndipo machenjera ake ndi obisika. Imodzi mwa njira zimene amawonongera anthu ndiyo kuchititsa kuti zinthu zolaula zizionetsedwa pa TV, pa Intaneti, m’mavidiyo, ndi m’mabuku. Akristu ena alola zinthu zoipa zimenezi kuloŵerera chitetezo chawo chofooka, ndipo zawachititsa kuti asakhalenso ndi mwayi wa utumiki umene anali nawo mumpingo ngakhalenso kukumana ndi mavuto ena aakulu kwambiri. (Aefeso 4:17-19) Kodi tingadziteteze bwanji ku zinthu zowononga za Satana zimenezi? Sitiyenera kunyalanyaza phunziro lathu laumwini la Baibulo la nthaŵi zonse, misonkhano yathu yachikristu, ndiponso kuvala zida zonse za Mulungu. Zonsezi pamodzi zimatithandiza kutha kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndi kudana ndi zimene Mulungu amadana nazo.​—Salmo 97:10; Aroma 12:9.

18. Kodi “lupanga la mzimu” lingatithandize bwanji pa nkhondo yathu yauzimu?

18 Tikakhalabe ndi chizoloŵezi chophunzira Baibulo nthaŵi zonse, tidzakhala ndi chitetezo cholimba chimene timachipeza mwa kudziŵa zolondola za m’Mawu a Mulungu ndiponso kulimbana ndi Satana pogwiritsira ntchito “lupanga la Mzimu, ndilo Mawu a Mulungu.” Mawu a Mulungu ndi “akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Aefeso 6:17; Ahebri 4:12) Ngati tikhala ndi luso pogwiritsira ntchito “lupanga” limeneli, ndiye kuti tikakumana ndi mayesero, sitidzapusitsidwa ndi zinthu zimene zingaoneke ngati zosavulaza kapenanso zosangalatsa, ndipo tidzavumbula msampha wakupha wa woipayo. Nkhokwe yathu ya chidziŵitso cha Baibulo idzatithandiza kupeŵa zoipa ndi kuchita zabwino. Motero tonsefe tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi lupanga langa n’lakuthwa kapena n’lobuntha? Kodi ndimavutika kukumbukira malemba a m’Baibulo amene angandilimbitse kuti ndilimbane ndi zinthu zoipa?’ Tiyeni tikhalebe ndi chizoloŵezi chabwino chochita phunziro laumwini la Baibulo ndipo tikatero tidzatha kutsutsa Mdyerekezi.​—Aefeso 4:22-24.

19. Kodi tingapindule chiyani ngati tichita phunziro laumwini ndi mtima wonse?

19 Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Ngati titsatira zimene Paulo anamuuza Timoteo, tingalimbitse moyo wathu wauzimu ndipo utumiki wathu ungakhale wogwira mtima kwambiri. Akulu ndi atumiki otumikira auzimu angapindulitse kwambiri mpingo, ndipo tonsefe tingakhalebe olimba m’chikhulupiriro.​—2 Timoteo 3:16, 17; Mateyu 7:24-27.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nthaŵi zambiri, munthu wachidwi amene akuphunzira bulosha la Mulungu Amafunanji, akamaliza amayamba kuphunzira buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mabuku onseŵa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Malingaliro amene aperekedwa apa adzathandiza kuthetsa zopinga zimene zingabwezere m’mbuyo kupita patsogolo kwauzimu.

^ ndime 9 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Amene amamva Chingelezi ndipo ali ndi buku la Insight on the Scriptures angaone mu Voluyumu 2, pa kamutu kakuti “Jehovah.”

^ ndime 9 Mabaibulo angapo a Chispanya ndi a Chikataloniya ndi osiyana kwambiri ndi mabaibulo ena chifukwa amamasulira zilembo zinayi zoimira dzina la Yehova m’Chihebri, pogwiritsira ntchito mawu akuti “Yavé,” “Yahveh,” “Jahvè,” ndi “Jehová.”

^ ndime 10 Zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 11 Zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi nthaŵi yanji ndiponso malo otani amene angathandize kuti phunziro lanu laumwini likhale lopindulitsa?

• Kodi omasulira Baibulo ambiri amalakwitsa bwanji pankhani ya dzina la Mulungu?

• Kodi mungagwiritsire ntchito malemba a m’Baibulo ati potsutsa chiphunzitso cha Utatu?

• Kodi tiyenera kutani kuti tidziteteze ku machenjera a Satana, ngakhale titakhala Akristu oona kwa zaka zambiri?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 19]

Kuti mupindule ndi phunziro lanu laumwini, mufunika kukhala pa malo abwino opanda zododometsa

[Zithunzi patsamba 23]

Kodi “lupanga” lanu n’lakuthwa kapena n’lobuntha?