Zimene Yoswa Anakumbukira
Zimene Yoswa Anakumbukira
“MOSE mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuwoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kuloŵa m’dzikomo ndilikuwapatsa,” anatero Yehova. (Yoswa 1:2) Inalitu ntchito yovuta kwambiri imene Yoswa amafunika kuigwira! Anali atakhala mtumiki wa Mose zaka pafupifupi 40. Tsopano akuuzidwa kuti atenge malo a mbuye wake ndi kuloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa ana a Israyeli omwe ankavuta nthaŵi zambiri.
Pamene Yoswa ankalingalira zomwe zinali m’tsogolo, mwina ziyeso zomwe anali atakumana nazo kale ndi kuzigonjetsa zinangoti pwirikiti m’maganizo mwake. Mosakayikira, zimene Yoswa anakumbukira zinam’thandiza kwambiri nthaŵi imeneyo, ndipo zingathandize Akristu masiku ano.
Kuchoka pa Kapolo N’kukhala Mkulu wa Asilikali
Yoswa anakumbukira zaka zambirimbiri za ukapolo. (Eksodo 1:13, 14; 2:23) Zimene Yoswa anakumana nazo m’zaka za ukapolozo sitingathe kuzifotokoza mwatchutchutchu chifukwa chakuti Baibulo silifotokoza tsatanetsatane wa mmene moyo wake unalili panthaŵi imeneyi. Koma Yoswa ayenera kuti anaphunzira luso lolinganiza bwino zinthu panthaŵi yomwe ankagwira ntchito ku Igupto, ndipo n’kutheka kuti anathandiza nawo kulinganiza za ulendo wa Ahebri pamodzi ndi ‘anthu ambiri osakanizika,’ wotuluka m’dzikolo.—Eksodo 12:38.
Yoswa ankachokera m’banja la fuko la Efraimu. Agogo ake a Elisama anali kalonga wa fukolo ndipo zikuoneka kuti ankayang’anira amuna okhala ndi zida okwana 108,100 a limodzi la magulu a mafuko atatuatatu a Israyeli. (Numeri 1:4, 10, 16; 2:18-24; 1 Mbiri 7:20, 26, 27) Komabe Aamaleki ataputa Israyeli, panthaŵi yomwe Israyeliyo anali atangotuluka kumene mu Igupto, Mose anauza Yoswa kuti akonzekeretse asilikali. (Eksodo 17:8, 9a) N’chifukwa chiyani anauza Yoswa osauza,mwachitsanzo, agogo wake kapena bambo wake? Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti: “Monga mkulu wa fuko lofunika kwambiri la Efraimu, ndiponso monga munthu woti ankadziŵika kale ndi luso lake lolinganiza bwino zinthu, komanso munthu woti anthu ankam’khulupirira kwambiri, Mose anaona kuti [Yoswa] ndiye mtsogoleri woyenerera kusankha ndi kukonzekeretsa asilikali.”
Kaya panali chifukwa chotani, koma Yoswa atasankhidwa anachita ndendende zinthu zomwe Mose anamulamula kuti achite. Ngakhale kuti Israyeli sankadziŵa nkhondo m’pang’ono pomwe, Yoswa anali wotsimikiza kuti Mulungu awathandiza. Chotero Mose atamuuza kuti, “maŵa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m’dzanja langa,” zinali zokwana kwa Yoswa. Yoswa ayenera kuti anakumbukira kuti Yehova anali atangowononga kumene gulu la asilikali lamphamvu kwambiri panthaŵiyo. Tsiku lotsatira, Mose atakweza manja mpaka dzuŵa kukaloŵa, panalibe mdani aliyense akanatha kulimbana ndi Israyeli, ndipo Aamaleki anagonjetsedwa kotheratu. Kenako Yehova analamula Mose kuti alembe m’buku ndi ‘kumveketsa kwa Yoswa’ mawu a Yehova akuti: “Ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleki pansi pa thambo.” (Eksodo 17:9b-14) Inde, Yehova sadzalephera kupereka chilango chimenecho.
Monga Mtumiki wa Mose
Zomwe zinachitika ndi Aamaleki ziyenera kuti zinalimbitsa kwambiri ubale wa Yoswa ndi Mose. Yoswa anali ndi mwayi wokhala “mtumiki,” “kuyambira ubwana wake” mpaka kufika pa imfa ya Mose, nyengo ya zaka ngati 40.—Numeri 11:28.
Udindo umenewu unam’patsa mwayi wochita nawo zinthu zina zapadera ndiponso mwayi wokhala ndi maudindo akuluakulu. Mwachitsanzo, pamene Mose, Aroni, ana a Aroni, ndi akulu 70 a Israyeli anakwera phiri la Sinai ndi kuona masomphenya a ulemerero wa Yehova, n’zachidziŵikire kuti Yoswa anali nawo. Pantchito yake monga mtumiki, iye anaperekeza Mose kupita pamwamba pa phiri ndipo mwachionekere iye anaima pataliko ndithu pamene Mose analoŵa mu mtambo wosonyeza kuti pamalopo pali Yehova. Chochititsa chidwi n’chakuti zikuoneka kuti Yoswa anakhala pa phiripo masiku 40 usana ndi usiku. Anayembekezera mokhulupirika kuti mbuye wake abwere, chifukwa chakuti pamene Mose anayamba kutsika atanyamula magome a mboni, Yoswa anali kum’chingamira.—Eksodo 24:1, 2, 9-18; 32:15-17.
Nkhani ya kulambira fano la mwana wang’ombe kwa Israyeli itatha, Yoswa anapitiriza kutumikira Mose pa chihema chokomanako kunja kwa chigono. Kumeneko Yehova analankhula ndi Mose maso ndi maso. Koma Mose atabwerera ku chigono, Yoswa “sanachoka m’chihemamo.” Mwina ankafunika kukhala kumeneko kuti Aisrayeli asamaloŵe m’chihema Eksodo 33:7, 11.
ali odetsedwa. Yoswa sanauone mopepuka udindo umenewu.—Kuchitira zinthu pamodzi ndi Mose kuyenera kuti kunalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Yoswa. Malinga n’kunena kwa Josephus yemwe anali katswiri wa mbiri yakale, Mose anali wamkulu kwa Yoswa ndi zaka 35. Anthu amati ubwenzi wawo unali “mgwirizano wa munthu wachikulire ndi munthu wachinyamata, wa mphunzitsi ndi wophunzira,” zomwe zinachititsa Yoswa kukhala “munthu wolimba mtima ndi wodalirika.” Tilibe aneneri monga Mose masiku ano, koma m’mipingo ya anthu a Yehova muli anthu achikulire amene chifukwa cha zokumana nazo pa moyo wawo ndiponso khalidwe lawo lauzimu amalimbikitsa kwambiri. Kodi mumaona anthu ameneŵa kukhala ofunika? Kodi mukupindula kukhalira nawo pamodzi?
Mzondi ku Kanani
Nthaŵi yovuta kwambiri pamoyo wa Yoswa inali pamene Israyeli anali atangolandira kumene Chilamulo. Anasankhidwa kuti aimire fuko lake pokazonda Dziko Lolonjezedwa. Nkhani yake ndi yodziŵika kwambiri. Azondi onse 12 anavomereza kuti linali dziko ‘loyendadi mkaka ndi uchi,’ mongadi mmene Yehova anawalonjezera. Koma, azondi khumi chifukwa chosoŵa chikhulupiriro anaopa kuti Israyeli sadzatha kuthamangitsa nzika za dzikolo. Yoswa ndi Kalebe ndi okhawa omwe analimbikitsa anthu kuti asapanduke chifukwa cha mantha, popeza kuti Yehova adzakhala nawo ndithu. Atanena zimenezi, khamu lonse linawatsutsa ndi kumanena zoti liwaponye miyala anthu aŵiriwo. Mwina likanaterodi ngati Yehova akanapanda kuloŵererapo mwa kusonyeza ulemerero wake. Chifukwa choti mtunduwo unalibe chikhulupiriro, Mulungu analamula kuti palibe amene analembetsa m’kaundula mu Israyeli wa zaka zakubadwa zoyambira pa 20 kupita m’tsogolo amene adzaloŵe Kanani. Yoswa, Kalebe, ndi Alevi okha ndiwo anapulumuka.—Numeri 13:1-16, 25-29; 14:6-10, 26-30.
Kodi si anthu onse amene anaona ntchito zikuluzikulu za Yehova ku Igupto? Nangano, n’chiyani chinathandiza Yoswa kukhulupirira thandizo la Mulungu pamene anthu ambiri ankakayikira? Yoswa ayenera kuti ankakumbukira bwino zinthu zonse zimene Yehova analonjeza ndi kuchita, ndipo ankasinkhasinkha zinthu zimenezo. Patatha zaka zambiri iye ananena kuti ‘pa mawu okoma onse Yehova ananena kwa Israyeli sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitika.’ (Yoswa 23:14) Motero Yoswa anali ndi chikhulupiriro chakuti malonjezo onse onena za m’tsogolo amene Yehova anapanga, nawonso adzakwaniritsidwa ndithu. (Ahebri 11:6) Izi ziyenera kupangitsa munthu kudzifunsa kuti: ‘Bwanji za ineyo? Kodi khama langa lophunzira ndi kusinkhasinkha malonjezo a Yehova landipangitsa kutsimikiza mtima kuti malonjozowo ndi oona? Kodi ndimakhulupirira kuti Mulungu angathe kunditeteza pamodzi ndi anthu ake pa chisautso chachikulu chimene chikubwera?’
Yoswa sanangosonyeza chikhulupiriro chokha koma anasonyezanso kulimba mtima pakuchita chabwino. Iye ndi Kalebe anali okhaokha, ndipo khamu lonse linkanena kuti liwaponye miyala. Kodi inu mukanamva bwanji? Mukanachita mantha? Yoswa sanatero. Iye ndi Kalebe ananena molimba zinthu zimene ankakhulupirira. Kukhala okhulupirika kwa Yehova kungafune kuti nafenso tidzachite zofananazi tsiku lina.
Nkhani ya azondi imatiuzanso kuti dzina la Yoswa linasinthidwa. Pa dzina lake loyambirira, lakuti Hoseya, kutanthauza “Chipulumutso,” Mose anawonjezapo zilembo za pa dzina la Mulungu ndi kumutcha Yehosuwa kapena kuti Yoswa kutanthauza kuti “Yehova ndi Chipulumutso.” Septuagint imamutcha kuti “Yesu.” (Numeri 13:8, 16) Mogwirizana ndi dzina lalikululi, Yoswa analengeza molimba mtima kuti Yehova ndi chipulumutso. Dzina la Yoswa sikuti linangosinthidwa mwachisawawa. Izi zinasonyeza kuti Mose anali kulemekeza khalidwe la Yoswa ndipo zinagwirizana ndi ntchito yaikulu kwambiri imene Yoswa anaigwira yotsogolera mtundu watsopano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.
Pamene makolo awo anali kumwalira mmodzi ndi mmodzi, Aisrayeli ankangoyendayenda m’chipululu kwa zaka 40 zotopetsa. Sitikudziŵa chilichonse chokhudza Yoswa panthaŵi imeneyi. Koma ziyenera kuti zinam’phunzitsa zambiri. Mosakayikira anaona ndi maso Mulungu akuweruza Kora, Datani, ndi Abiramu amene Numeri 16:1-50; 20:9-13; 25:1-9.
anapandukira pamodzi ndi owatsatira awo ndiponso anthu amene anachita nawo kulambira konyansa, kolambira Baala Peori. Mosakayikira Yoswa anamva chisoni kwambiri atadziŵa kuti Mose nayenso sadzaloŵa m’dziko lalonjezano chifukwa chakuti analephera kulemekeza Yehova pa za madzi a pa Meriba.—Aikidwa Kukhala Woloŵa M’malo wa Mose
Imfa ya Mose itayandikira, iye anapempha Mulungu kuti asankhe munthu wodzaloŵa m’malo mwake kotero kuti Israyeli asadzakhale ngati “nkhosa zopanda mbusa.” Kodi Yehova anayankha motani? Yoswa, “munthu [amene] mwa iye muli mzimu,” anasankhidwa pamaso pa khamu lonse. Anafunika kumumvera. Inalitu nkhani yabwino! Yehova anali ataona chikhulupiriro ndi luso la Yoswa. Udindo wotsogolera Israyeli sukanaperekedwanso m’manja mwa munthu wina kuposa Yoswa. (Numeri 27:15-20) Komabe, Mose ankadziŵa kuti Yoswa anakumana ndi mikwingwirima. Motero Mose analimbikitsa woloŵa m’malo wakeyu kuti akhale ‘wamphamvu, wolimba mtima,’ chifukwa chakuti Yehova adzakhalabe naye.—Deuteronomo 31:7, 8.
Mulungu mwiniyo anabwereza mawu olimbikitsaŵa kwa Yoswa ndi kuwonjezera kuti: “Usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhaŵa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.”—Yoswa 1:7-9.
Iye akamaganizira mawu a Yehovaŵa komanso ndi zinthu zimene zinali zitachitika kale pa moyo wake, kodi Yoswa akanakayikiranso bwanji? Zinali zotsimikizika kuti adzalanda dziko. Inde padzakhala mavuto ena ndi ena, ndipo limodzi mwa mavuto akuluakulu ndi lomwe linali loyambirira, kuwoloka mtsinje wa Yordano utasefukira. Komabe Yehova mwiniwakeyo analamula kuti: “Tauka . . . nuwoloke Yordano uyu.” Nangano pakanakhalanso vuto losagonjetseka?—Yoswa 1:2.
Zinthu zimene zinachitika motsatizanatsatizana pa moyo wa Yoswa, kugonjetsa Yeriko, kugonjetsa adani awo kotheratu, ndiponso kugaŵa dziko, zikusonyeza kuti iye sanaiŵale m’pang’ono pomwe malonjezo a Mulungu. Imfa ya Yoswa itayandikira ndipo Yehova atapumulitsa Israyeli ku adani ake, Yoswa anasonkhanitsa anthu kuti aonenso zimene Mulungu anawachitira ndi kuwalimbikitsa kuti apitirize kumutumikira Mulungu ndi mtima wonse. Zotsatira zake zinali zakuti Israyeli anachitanso pangano lake ndi Yehova, ndipo n’zosakayikitsa kuti atakhudzidwa mtima ndi chitsanzo cha mtsogoleri wake, “Israyeli anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa.”—Yoswa 24:16, 31.
Yoswa ndi chitsanzo chathu chabwino kwambiri. Akristu masiku ano amakumana ndi zinthu zosiyanasiyana zoyesa chikhulupiriro. Kugonjetsa zinthu zimenezi n’kofunika kwambiri kuti Yehova apitirize kuwayanja ndi kuti potsiriza pake adzalandire malonjezo ake. Chikhulupiriro cholimba ndi chimene chinathandiza kuti Yoswa apambane. Ndi zoona kuti sitinaone ntchito zikuluzikulu za Mulungu ngati zimene Yoswa anaona, koma ngati wina angakayikire, buku la m’Baibulo la dzina la Yoswa ndilo umboni woona ndi maso wakuti mawu a Yehova ngodalirika. Ife, monga Yoswa, tingapeze nzeru ndiponso tingakhale opambana ngati tiŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndi kuyesetsa kuwagwiritsira ntchito.
Kodi nthaŵi zina mumakhumudwa ndi khalidwe la Akristu anzanu? Ganizirani za kupirira kwa Yoswa pa zaka 40 zimene anafunika kuyendayenda m’chipululu ndi anzake osakhulupirika, ndipo izi zinachitika ngakhale kuti analakwa si iye. Kodi zimakuvutani kukhalira kumbuyo zinthu zimene mumakhulupirira? Kumbukirani zimene Yoswa ndi Kalebe anachita. Chifukwa cha kukhulupirika ndi kumvera kwawo, analandira mphoto yaikulu kwambiri. Inde, Yoswa ankakhulupiriradi kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake onse. Tiyeni nafenso titero.—Yoswa 23:14.
[Chithunzi patsamba 10]
Yoswa ndi Kalebe ankadalira mphamvu za Yehova
[Chithunzi patsamba 10]
Kuchitira zinthu pamodzi ndi Mose kunalimbitsa chikhulupiriro cha Yoswa
[Chithunzi patsamba 10]
Utsogoleri wa Yoswa unalimbikitsa anthu kumamatira kwa Yehova