Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi “Anzeru a Kum’maŵa” Anali Ndani?

Kodi “Anzeru a Kum’maŵa” Anali Ndani?

Kodi “Anzeru a Kum’maŵa” Anali Ndani?

Nthaŵi zambiri zithunzi za kubadwa kwa Yesu zimasonyeza amuna atatu ovala mikanjo ali pa akavalo awo, atafika mu khola limene Yesu wakhandayo anali gone m’chodyera cha ng’ombe. Alendo ovala bwinowo amatchuka ndi dzina loti anzeru a kum’maŵa. Kodi Baibulo limati chiyani za amuna ameneŵa?

Malinga ndi Baibulo, amuna ameneŵa anachokera “kum’maŵa,” ndipo n’kumene anamvera za kubadwa kwa Yesu. (Mateyu 2:1, 2, 9) Ulendo wa ku Yudeya uyenera kuti unawatengera nthaŵi yaitali amuna ameneŵa. Pamene amam’peza Yesu, n’kuti asalinso m’khola monga kakhanda. Koma anapeza Mariya ndi “kamwanako” akukhala m’nyumba.​—Mateyu 2:11.

Baibulo limatcha amuna ameneŵa “akatswiri a nyenyezi,” (Chipangano Chatsopano Cholembedwa M’Chicheŵa Chamakono) ndipo silinena kuti anali angati. Buku la The Oxford Companion to the Bible limafotokoza kuti: “Zikuoneka kuti chidwi chimene alendowo anachita ndi nyenyezi imene inawalondolera ku Betelehemu, chikusonyeza kuti matsenga ndi kukhulupirira nyenyezi n’zogwirizana.” Baibulo mosabisa limadana ndi mtundu wina uliwonse wa matsenga ndiponso chizoloŵezi cha Ababulo cha kumva mauthenga mwa kupenda nyenyezi.​—Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 47:13.

Uthenga umene amuna ameneŵa anamva sunabweretse zabwino. Unachititsa Mfumu yoipa Herode kuchita nsanje ndiponso kukwiya. Ndipo zimenezi zinachititsa Yosefe, Mariya ndi Yesu kuthaŵira ku Igupto ndiponso zinaphetsa ana aamuna onse m’Betelehemu ‘ofikira zaka ziŵiri ndi tating’ono tonse.’ Herode anadziŵa bwinobwino nthaŵi imene Yesu anabadwa pa zimene anamva kwa okhulupirira nyenyezi. (Mateyu 2:16) Poona mavuto onse amene ulendo wawo unabweretsa, n’kwanzeru kunena kuti nyenyezi imene anaonayo ndiponso uthenga wonena za “amene anabadwa Mfumu ya Ayuda” unachokera kwa mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, amene ankafuna kupha Yesu.​—Mateyu 2:1, 2.