Mmene Kubadwa kwa Yesu Kunachitikira Ndiponso Chifukwa Chake Kunachitika
Mmene Kubadwa kwa Yesu Kunachitikira Ndiponso Chifukwa Chake Kunachitika
“N’ZOSATHEKA!” Anthu ambiri amene si Akristu anganene zimenezi atamva nkhani ya kubadwa kwa Yesu. Amaona kuti n’zosagwirizana ndi sayansi kukhulupirira kuti namwali angabereke mwana popanda kukhalira pamodzi ndi mwamuna. Kodi inu mumaganiza bwanji?
Mu chaka cha 1984, nyuzipepala ya The Times ya ku London inasindikiza kalata imene inanena zankhani imeneyi. Inati: “Si nzeru kugwiritsa ntchito sayansi kutsutsira zozizwitsa. Kukhulupirira kuti zozizwitsa sizingachitike kwangokhala chikhulupiriro monga mmene wina angakhulupirire kuti zingachitike.” Kalatayo inasainidwa ndi akatswiri a zasayansi okwana 14, a m’mayunivesite a ku Britain. Iwo anati: “Timakhulupirira ndi mtima wonse kuti namwali anabereka mwana komanso kuti zozizwitsa za m’Mauthenga Abwino ndiponso kuuka kwa Kristu zinachitikadi kalelo.”
Komabe, mpake munthu kudabwa nthaŵi yoyamba kumva nkhani yakuti Yesu anabadwa kwa namwali. Ngakhale namwaliyo, mayi wa Yesu, anadabwa mngelo wa Mulungu atamuuza kuti: “Taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.” Poyankha Mariya anafunsa kuti: “Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziŵa mwamuna?” Ndiyeno mngelo anafotokoza kuti Mulungu achita chozizwitsa chimenechi mwa mzimu Wake woyera. Komanso anati: “Palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.” (Luka 1:31, 34-37) Ndithudi, Iye amene anakonza njira yodabwitsa yakuti anthu azibereka, akanathanso kuchititsa kuti Yesu abadwe kwa namwali wodzisunga. Ngati Mulungu analenga zonse komanso kuziikira malamulo ogwira bwino ntchito, akanathanso kugwiritsa ntchito dzira la m’chiberekero cha Mariya kubereka Mwana wangwiro.
Chifukwa Chake Kunali Koyenera
Panthaŵi imene Mariya anali ndi mimba, n’kuti atatomeredwa ndi Yosefe, munthu woopa Mulungu. M’loto, mngelo wa Mulungu anafotokozera Yosefe chifukwa chenicheni chimene namwali amene anatomerayo anali ndi mimba. Mngelo anati: “Usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo awo.” (Mateyu 1:20, 21) M’Chihebri dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Limatikumbutsa kufunika kopulumuka ku uchimo ndi imfa ndiponso zimene Yehova Mulungu wakonza pa nkhani ya chipulumutso chimenechi kudzera mwa Yesu.
Chifukwa chakuti munthu woyambirira, Adamu, anachimwa, ana ake onse anabadwa opanda ungwiro, ndiponso okonda kusamvera malamulo a Mulungu. (Aroma 5:12) Kodi ana a adamu akanapulumutsidwa bwanji ku uchimo n’kukhala angwiro? Moyo wina wangwiro, wolingana ndi wa Adamu, unafunika kuperekedwa kuti pakhale chilungamo. N’chifukwa chake Mulungu anachititsa kuti munthu wangwiro Yesu, abadwe mozizwitsa ndiponso n’chifukwa chake Yesu analola adani ake kumupha. (Yohane 10:17, 18; 1 Timoteo 2:5, 6) Yesu ataukitsidwa ndiponso atapita kumwamba, ananena molimba mtima kuti: “Ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthaŵi za nthaŵi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi Hade [manda a anthu onse].”—Chivumbulutso 1:18.
Yesu anagwiritsa ntchito mfungulo zophiphiritsira za imfa ndi Hade, kutsegulira njira yakuti anthu ochimwa akapeze zimene Adamu, anataya. Yesu anafotokoza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.” (Yohane 11:25, 26) Ndi lonjezo labwino bwanji! Ndiponso, pali chifukwa china chachikulu chimene Yesu anabadwira.
Chifukwa Chachikulu Kwambiri
Moyo wa Yesu sunayambe pamene Mariya anatenga mimba yake. Iye ananena momveka bwino kuti: “Ndinatsika Kumwamba.” (Yohane 6:38) Yesu anakhala ku malo a mizimu ndi Atate ake akumwamba kuyambira pamene anayamba kulenga zinthu. Ndiponso, Baibulo limati iye ndi “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu ali kumwamba, anaona kupanduka kwa mngelo woipa. Mngelo ameneyu anapangitsa anthu oyambirira kuukira ulamuliro wa Mulungu. Izi zinachititsa Yesu kukhala ndi chifukwa chachikulu chofunira kubadwa monga Mwana wa Mulungu wangwiro. Kodi chifukwa chake chinali chotani?
Chinali chodzatsimikizira kuti Atate wake wakumwamba ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Yesu anasonyeza kufunitsitsa kwake kugonjera njira ya Yehova yolamulira zolengedwa Zake mwa kukhalabe wokhulupirika kuyambira pa kubadwa kwake mpaka pa imfa yake padziko lapansi. Yesu asanaphedwe ndi adani a Mulungu, ananena momveka bwino chifukwa chake anali wofunitsitsa kupereka moyo wake nsembe. Iye anati chifukwa chake chinali chakuti dziko lapansi lidziŵe kuti ankakonda Atate. (Yohane 14:31) Ngati anthu aŵiri oyamba aja, Adamu ndi Hava, akanakhala ndi chikondi chimenechi, bwenzi atakhulupirika pa chiyeso chawo chaching’ono chija.—Genesis 2:15-17.
Kukhulupirika kwa Yesu kunasonyezanso kuti mngelo woipa Satana ndi wabodza. Satana anasinjirira Mulungu ndiponso munthu mwa kunena pamaso pa angelo kumwamba kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo Yobu 2:1, 4) Satana ananena bodza lakuti anthu angasiye kumvera Mulungu kuti apulumutse moyo wawo.
wake.” (Nkhani zimenezi zinakayikitsa mfundo yoti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Kuti athetse nkhaniyi, Yesu anali wofunitsitsa kubadwa monga munthu komanso kukhala wokhulupirika mpaka imfa.
Choncho, chifukwa chenicheni chimene Yesu anabadwira padziko lapansi, chinali chakuti ‘achitire umboni choonadi,’ malinga ndi zimene mwiniwake ananena. (Yohane 18:37) Anachita zimenezi mwa mawu ndi zochita zake kuti ulamuliro wa Mulungu ndi woyenera kwambiri ndiponso kuti kugonjera ulamuliro umenewu kumabweretsa chimwemwe chosatha. Yesu ananenanso kuti anabwera padziko lapansi kudzapereka moyo wake “dipo la kwa anthu ambiri,” kutsegula njira yakuti anthu ochimwa akakhale angwiro ndiponso akapeze moyo wosatha. (Marko 10:45) Kuti anthu amvetse nkhani zofunika zimenezi, panafunika kulemba nkhani ya kubadwa kwa Yesu. Komanso, tingaphunzire zinthu zina zofunika kwambiri pa zimene zinachitika panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu, monga mmene nkhani yotsatirayi isonyezere.
[Zithunzi patsamba 4]
Kodi ana a Adamu akanapulumutsidwa bwanji ku uchimo?