Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingaphunzire pa Nkhani ya Kubadwa kwa Yesu

Zimene Tingaphunzire pa Nkhani ya Kubadwa kwa Yesu

Zimene Tingaphunzire pa Nkhani ya Kubadwa kwa Yesu

ANTHU ambiri amachita chidwi ndi zimene zinachitika panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu. Timaona zimenezi panyengo ya Khirisimasi m’zithunzi ndiponso maseŵero a kubadwa kwa Yesu amene amachitika padziko lonse. Ngakhale kuti zimene zinachitika panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu n’zochititsadi chidwi, sizinalembedwe m’Baibulo kuti zisangalatse anthu. Komano, ndi mbali ya Malemba onse amene Mulungu anauzira kuti aphunzitse ndi kuwongola zinthu.​—2 Timoteo 3:16.

Mulungu akanafuna kuti Akristu azikumbukira kubadwa kwa Yesu, ndiye kuti Baibulo likanatchula tsiku lenileni limene Yesu anabadwa. Kodi limatchula? Albert Barnes yemwe anali katswiri wamaphunziro a Baibulo m’ma 1800, atatchula kuti Yesu anabadwa panthaŵi imene abusa anali kunja usiku kudyetsa ziŵeto zawo, anati: “Pamenepa n’zoonekeratu kuti Mpulumutsi wathu anabadwa pasanafike pa 25 December . . . Panthaŵi imeneyi kumakhala kozizira, makamaka ku malo okwera ndi amapiri cha ku Betelehemu. Mulungu sanaulule tsiku limene [Yesu] anabadwa. . . . Komanso sikunali kofunika kudziŵa nthaŵi imene anabadwa; ikanakhala yofunika, Mulungu akanasunga nkhani imene imatchula tsiku la kubadwalo.”

Komano, amene analemba Mauthenga Abwino anayi amatiuza momveka za tsiku limene Yesu anafa. Linali tsiku la Paskha, amene ankachitika pa 14 pa mwezi wachiyuda wa Nisani, pa nyengo ya masika. Komanso, Yesu analamula om’tsatira ake mosapita m’mbali kuti azim’kumbukira pa tsiku limeneli. (Luka 22:19) M’Baibulo mulibiretu lamulo la ngati limeneli pa nkhani yokumbukira kubadwa kwa Yesu, ngakhalenso kwa munthu wina aliyense. Chomvetsa chisoni n’chakuti kukangana pa nkhani ya tsiku limene Yesu anabadwa kungaphimbe zinthu zofunika kwambiri zimene zinachitika panthaŵiyo.

Makolo Amene Mulungu Anasankha

Pa mabanja ambirimbiri a mu Israyeli, kodi ndi makolo otani amene Mulungu anasankha kuti alere Mwana wake? Kodi Iye anayang’ana zinthu monga kutchuka ndi kulemera kukhala zofunika? Ayi ndithu. Koma Yehova anaona makhalidwe auzimu a makolowo. Taonani nyimbo yotamanda imene Mariya anaimba atauzidwa za mwayi wake wapadera wokhala mayi wa Mesiya. Nyimboyi ikupezeka pa Luka 1:46-55. Mwa zina, anati: “Moyo wanga ulemekeza Ambuye . . . . Chifukwa Iye anayang’anira umphaŵi wa mdzakazi wake.” Modzichepetsa anadziona kuti anali mmodzi wa ‘amphaŵi,’ mdzakazi wa Yehova. Chofunika kwambiri n’chakuti, mawu abwino otamanda a m’nyimbo ya Mariya amasonyeza kuti anali munthu wokonda zinthu zauzimu amene ankadziŵa bwino Malemba. Ngakhale kuti anali mwana wochimwa wa Adamu, anali munthu wabwino kukhala mayi wa Mwana wa Mulungu padziko lapansi.

Bwanji mwamuna wa Mariya, amene anali bambo wa Yesu wom’lera? Yosefe anali mwamuna wodziŵa bwino ukalipentala. Chifukwa cha mtima wake wofuna kugwira ntchito zolimba ndi manja ake, ankatha kupezera banja lake zinthu zofunika, limene m’kupita kwanthaŵi linali ndi ana aamuna asanu ndi ana aakazi osachepera aŵiri. (Mateyu 13:55, 56) Yosefe sanali wolemera. Nthaŵi itakwana yoti Mariya apite ndi mwana wake woyamba ku kachisi wa Mulungu, Yosefe ayenera kuti anakhumudwa poona kuti satha kupereka nsembe ya nkhosa imene inali kufunika. M’malo mwake, anagwiritsa ntchito mwayi umene osauka anali nawo. Lamulo la Mulungu kwa mayi amene anali ndi mwana wakhanda linali lakuti: “Chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziŵiri kapena maunda aŵiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe am’chitire chom’tetezera, ndipo adzakhala woyera.”​—Levitiko 12:8; Luka 2:22-24.

Baibulo limati Yosefe “anali wolungama.” (Mateyu 1:19) Mwachitsanzo, sanagone ndi mkazi wake namwaliyo mpaka Yesu anabadwa. Izi zinathandiza kuti pasakhale kukayikira za amene anali Atate weniweni wa Yesu. Kwa anthu amene angokwatirana kumene ndiponso oti akukhala m’nyumba imodzi, kusagonana sinali nkhani yophweka, koma kunasonyeza mmene aŵiriwo anayamikirira mwayi wosankhidwa kulera Mwana wa Mulungu.​—Mateyu 1:24, 25.

Mofanana ndi Mariya, Yosefe anali munthu wokonda zinthu zauzimu. Chaka chilichonse ankaimikira ntchito n’kupita ndi banja lake paulendo wa masiku atatu kuchokera ku Nazareti kupita ku Yerusalemu kukakhala nawo pa madyerero apachaka a Paskha. (Luka 2:41) Komanso, Yosefe ayenera kuti anaphunzitsa Yesu wachichepereyo kuzoloŵera kupita mlungu uliwonse ku sunagoge kukalambira. Ndipo kumeneku kunkaŵerengedwa Mawu a Mulungu ndi kuwafotokozera. (Luka 2:51; 4:16) Choncho, n’zosakayikitsa kuti Mulungu anasankha amayi ndiponso abambo a Mwana wake omulera oyenera padziko lapansi.

Abusa Wamba Adalitsidwa Kwabasi

Ngakhale kuti mkazi wake anali akuvutika, amene tsopano anali ndi mimba ya miyezi nayini, Yosefe anapita ku mzinda wa makolo ake kukalembetsa kalembera, potsatira lamulo la Kaisara. Banjalo litafika ku Betelehemu, silinapeze malo ogona m’mzindawo chifukwa munadzaza anthu. Choncho chifukwa cha momwe zinthu zinalili sakanachitira mwina koma kugwiritsa ntchito khola, mmene Yesu anabadwira ndipo anam’goneka modyera ng’ombe. Pofuna kulimbitsa chikhulupiriro cha makolo osaukawo, Yehova anawatsimikizira kuti kubadwaku kunalidi chifuno cha Mulungu. Kodi anatumiza nthumwi za akulu otchuka a ku Betelehemu kuti akatsimikizire banjalo? Ayi ndithu. Koma Yehova Mulungu anaulula nkhaniyi kwa abusa olimbikira ntchito amene anachezera usiku wonse kunja kuyang’anira zoŵeta zawo.

Mngelo wa Mulungu anawaonekera ndi kuwauza kupita ku Betelehemu, kumene akapeze Mesiya wobadwa kumeneyo “atagona modyera.” Kodi amuna wamba ameneŵa anadabwa kapena kuchita manyazi kumva kuti Mesiya wobadwa kumeneyo ali m’khola? Ayi ndithu. Mofulumira, anasiya zoŵeta zawo ulendo ku Betelehemu. Atam’peza Yesu, anauza Yosefe ndi Mariya zimene mngelo wa Mulungu ananena. Izi mosakayikira zinalimbitsa chikhulupiriro cha banjalo kuti zonse zinali kuchitika mmene Mulungu ankafunira. Ndiyeno “abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona.” (Luka 2:8-20) Inde, Yehova anasankha bwino poululira zinthu abusa oopa Mulungu amenewo.

Pa zimenezi, tikuphunzira kuti tiyenera kukhala anthu otani kuti Yehova atiyanje.” Sikuti tiyenera kukhala otchuka kapena olemera kuti iye atiyanje. Komano monga Yosefe, Mariya, ndiponso abusa, tifunika kumvera Mulungu ndi kusonyeza kuti timam’konda mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo pa zinthu zakuthupi. Ndithudi pali zinthu zabwino zimene tikuphunzira mwa kusinkhasinkha zimene zinachitika panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi kupereka kwa Mariya maunda aŵiri kumasonyezanji?

[Chithunzi patsamba 7]

Mulungu anasankha kuululira abusa wamba ndiponso oŵerengeka za kubadwa kwa Yesu