Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika

Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika

Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika

KWA zaka zambiri, anthu ambiri anzeru ndiponso a maphunziro azaumulungu avutika maganizo ndi funso lakuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuvutika. Ena anena kuti popeza Mulungu ndi wamphamvuyonse, ndiye kuti ndi amene amachititsa mavuto. Wolemba buku la nthano la m’zaka za m’ma 100 lakuti The Clementine Homilies, anati, Mulungu amalamulira dziko lapansi ndi manja aŵiri. Ku “dzanja lamanzere,” kuli Mdyerekezi, amene amachititsa kuvutika ndipo ku “dzanja lamanja,” kuli Yesu, amene amapulumutsa ndi kudalitsa.

Anthu ena, chifukwa chosakhulupirira kuti Mulungu angalole kuvutika ngakhale kuti sindiye amakuchititsa, amanena kuti palibe mavuto. “Timangoganizira kuti mavuto alipo, koma zilibe maziko enieni,” analemba motero Mary Baker Eddy. “Zikanakhala kuti anthu akuona kuti uchimo, matenda, ndi imfa si zenizeni, bwenzi kulibe.”​— Science and Health With Key to the Scriptures.

Chifukwa cha zochitika zomvetsa chisoni m’mbiri, makamaka kuyambira nkhondo yoyamba ya padziko lonse mpaka nthaŵi yathu ino, anthu ambiri amati Mulungu wangolephera kuletsa kuvutika. Katswiri wamaphunziro wachiyuda David Wolf Silverman analemba kuti: “Ndikuganiza kuti, kuphedwa kwa Ayuda a ku Ulaya ndiponso anthu ena ndi a Nazi pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, kwachotseratu maganizo oti Mulungu ndi wamphamvuyonse.” Anawonjezera kuti: “Ngati Mulungu angamvetsetseke mwanjira ina, ndiye kuti ubwino Wake uyenera kuyendera limodzi ndi kuipa ndipo zimenezi zingakhale choncho ngati iyeyo si wamphamvuyonse.”

Komabe, kunena kuti Mulungu amachititsako kuvutika, ndi kuti kulibe mavuto, kapena kuti walephera kukuletsa sikumalimbikitsa kwenikweni amene akuvutika. Ndiponso kuposa pamenepo, maganizo ameneŵa sagwirizana ndi mfundo yakuti Mulungu ndi wachilungamo, wamphamvu ndi wachikondi monga mmene Baibulo limafotokozera. (Yobu 34:10, 12; Yeremiya 32:17; 1 Yohane 4:8) Ndiyeno, kodi Baibulo limati n’chifukwa n’chiyani Mulungu walola kuvutika?

Kodi Kuvutika Kunayamba Bwanji?

Mulungu sanalenge anthu kuti azivutika. M’malo mwake, analenga mwamuna ndi mkazi oyambirira, Adamu ndi Hava, ali ndi maganizo ndi matupi angwiro. Anawakonzera munda wosangalatsa kuti azikhalamo ndipo anawapatsa ntchito yabwino ndi yosangalatsa. (Genesis 1:27, 28, 31; 2:8) Komabe, kuti apitirizebe kusangalala, zinadalira kuzindikira kwawo kuti Mulungu ndiye wolamulira ndiponso kuti ndi woyenera kusankha chabwino ndi choipa. “Mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa” ndi umene unaimira ulamuliro wa Mulungu umenewu. (Genesis 2:17) Adamu ndi Hava akanasonyeza kugonjera kwawo Mulungu ngati akanamvera lamulo lake loti asadye za m’mtengowo. *

Zomvetsa chisoni n’zoti Adamu ndi Hava analephera kumvera Mulungu. Cholengedwa chauzimu chopanduka, chomwe chinadzatchedwa Satana Mdyerekezi, chinamuchititsa Hava kukhulupirira kuti kumvera Mulungu sikukanamupindulitsa. Ndiponso kuti Mulungu ankam’bisira kanthu kena kofunika kwambiri: ufulu, kudzisankhira yekha chomwe chinali chabwino ndi choipa. Satana ananena kuti akadya za m’mtengowo ‘adzatseguka maso ake, ndipo adzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.’ (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Atanyengeka ndi zoti azadzilamulira okha, Hava anadya chipatso choletsedwa, ndipo posapita nthaŵi Adamu anachitanso chimodzimodzi.

Tsiku lomwelo, Adamu ndi Hava anayamba kuona zotsatira za kupanduka kwawo. Chifukwa cha kukana ulamuliro wa Mulungu, sanakhalenso ndi chitetezo ndiponso madalitso zimene anali nazo chifukwa chomvera Mulungu. Mulungu anawathamangitsa m’Paradaiso ndipo anauza Adamu kuti: “Nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka.” (Genesis 3:17, 19) Adamu ndi Hava anafunika kudwala, kuvutika, kukalamba ndi kufa. Kuvutika kunakhala mbali ya moyo wa munthu.​—Genesis 5:29.

Kuthetsa Nkhaniyo

Munthu wina angafunse kuti, ‘Kodi Mulungu sakanangonyalanyaza tchimo la Adamu ndi Hava?’ Ayi. Chifukwa choti zimenezo zikanachepetsa kwambiri kulemekeza ulamuliro wake, mwinamwake kuchititsa kupanduka kwina m’tsogolo kumene kukanapangitsa mavuto aakulu. (Mlaliki 8:11) Ndiponso, kunyalanyaza kusamvera kwawo kukanasonyeza kuti Mulungu akugwirizana nalo tchimolo. Wolemba Baibulo Mose akutikumbutsa kuti: “Ntchito yake [Mulungu] ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Kuti atsimikiziredi kuti ali ndi makhalidwe ameneŵa, Mulungu analola Adamu ndi Hava kuona zotsatira za kusamvera kwawo.

N’chifukwa chiyani Mulungu sanawononge nthaŵi yomweyo mwamuna ndi mkazi oyambirira limodzi ndi Satana, munthu wosaoneka amene anawachititsa kuti apanduke? Iye anali ndi mphamvu yochita zimenezi. Adamu ndi Hava sakanakhala ndi ana omwe ali ndi choloŵa cha kuvutika ndi kufa. Komabe, kusonyeza mphamvu zake mwanjira imeneyo sikukanatsimikizira kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira zolengedwa zanzeru. Ndiponso, Adamu ndi Hava akanakhala kuti amwalira opanda ana, zimenezo zikanatanthauza kuti chifuno cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi ndi mbadwa zawo zangwiro chalephera. (Genesis 1:28) Ndipo “Mulungu sali ngati anthu . . . Zilizonse zimene walonjeza, amazikwaniritsa; zimene wanena, zimachitika.”​—Numeri 23:19, Today’s English Version.

Ndi nzeru zake zangwiro, Yehova Mulungu analola kuti kupandukako kukhalepo kwakanthaŵi. Opandukawo anakhala ndi nthaŵi yokwanira yoti aone zotsatirapo za kusadalira Mulungu. Zochitika m’mbiri ya anthu zasonyezeratu kufunika koti Mulungu atsogolere anthu ndiponso kuti ulamuliro wake ndi wabwino kuposa wa anthu kapena wa Satana. Panthaŵi imodzimodzi, Mulungu anachitapo kanthu kuonetsetsa kuti chifuno chake choyamba polenga dziko lapansi chikwaniritsidwe. Iye analonjeza kuti “mbewu” idzafika yomwe ‘idzalalira mutu wa Satana,’ kuchotseratu kupanduka kwake ndi zotsatira zake zopweteka.​—Genesis 3:15.

Yesu Kristu anali Mbewu yolonjezedwayo. Pa 1 Yohane 3:8, timaŵerenga kuti “Mwana wa Mulungu adaonekera, . . . kuti akawononge ntchito za Mdyerekezi.” Anachita zimenezi mwa kupereka nsembe moyo wake wangwiro ndi kupereka mtengo wa dipo kuti awombole ana a Adamu ku cholowa cha uchimo ndi imfa. (Yohane 1:29; 1 Timoteo 2:5, 6) Amene amasonyezadi chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu akulonjezedwa kuti adzamasuka kotheratu ku mavuto. (Yohane 3:16; Chivumbulutso 7:17) Kodi zimenezi zidzachitika liti?

Kutha kwa Mavuto

Kukana ulamuliro wa Mulungu kwachititsa mavuto osaneneka. N’chifukwa chake n’koyenera kuti Mulungu agwiritsire ntchito ulamuliro wake mwanjira yapadera kuti athetse mavuto a anthu ndi kukwaniritsa chifuno chake choyambirira polenga dziko lapansi. Yesu anatchula makonzedwe a Mulungu ameneŵa pamene anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: ‘Atate wathu wa Kumwamba, . . . Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.’​—Mateyo 6:9, 10.

Nthaŵi imene Mulungu walola anthu kuti ayese kudzilamulira okha ili pafupi kutha. Pokwaniritsa ulosi wa Baibulo, Ufumu wake unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, ndipo Yesu Kristu anakhala Mfumu ya ufumuwo. * Posachedwapa, udzaphwanya ndi kutha maboma onse a anthu.​—Danieli 2:44.

Panthaŵi yochepa ya utumiki wake padziko lapansi, Yesu anasonyeza pang’ono madalitso amene anthu adzakhala nawo Mulungu akadzayambiranso kulamulira. Mauthenga Abwino amasonyeza kuti Yesu anali wachifundo kwa anthu amene anali osauka ndi amene anali kusankhidwa. Anachiritsa odwala, kudyetsa anjala, ndi kuukitsa akufa. Ngakhale mphamvu zachilengedwe zinam’mvera. (Mateyu 11:5; Marko 4:37-39; Luka 9:11-16) Taganizani zimene Yesu adzachita nthaŵi imene adzagwiritsira ntchito mphamvu yoyeretsa ya nsembe yake ya dipo kupindulitsa anthu onse omvera! Baibulo limalonjeza kuti kupyolera m’ulamuliro wa Kristu, Mulungu “adzawapukutira [anthu] misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”​—Chivumbulutso 21:4.

Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika

N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova, Mulungu wathu wachikondi ndi wamphamvuyonse amatisamalira ndi kuti posachedwapa adzabweretsa mpumulo kwa anthu. Nthaŵi zambiri, munthu wodwala kwambiri amalandira chithandizo cha kuchipatala chimene chingam’chiritse ngakhale chitakhala choŵaŵa kwambiri. Mofananamo, ngati tikudziŵa kuti njira imene Mulungu akuchitira zinthu idzabweretsa madalitso osatha, zimenezo zingatithandize kupirira ngakhale tikumane ndi mavuto akanthaŵi amtundu wanji.

Ricardo, amene watchulidwa m’nkhani yoyamba ija, ndi mmodzi mwa anthu amene aphunzira kupeza chilimbikitso m’malonjezo a m’Baibulo. Iye anati: “Mkazi wanga atamwalira, ndinkafunitsitsa kudzipatula kwa anthu, koma posapita nthaŵi ndinazindikira kuti zimenezi sizikanabweretsa mkazi wanga ndipo zikanangowonjezera kuvutika kwanga maganizo.” M’malo mwake, Ricardo ankapitabe ku misonkhano yachikristu ndi kuuza ena uthenga wa m’Baibulo. Ricardo anati: “Pamene ndinkaona kuti Yehova akundichirikiza mwachikondi ndi mmene ankayankhira mapemphero anga pa zinthu zimene zinkaoneka zazing’ono, ndinayandikira kwambiri kwa iye. Ndipo kudziŵa za chikondi cha Mulungu kumeneku n’kumene kunandithandiza kupirira chiyeso chachikulu chomwe ndinali ndisanakumanepo nacho.” Iye akuti: “Ndimam’soŵabe kwambiri mkazi wanga, koma tsopano ndikukhulupiriradi kuti palibe chimene Yehova angalole kutichitikira chimene chingativulaziretu.”

Kodi inuyo, mofanana ndi Ricardo ndi anthu ena ambiri, mumalakalaka nthaŵi imene kuvutika kwa anthu kumene kulipo ‘sikudzakumbukika, pena kulowa mumtima’? (Yesaya 65:17) Dziŵani kuti mungalandire madalitso a Ufumu wa Mulungu ngati mutsatira malangizo a Baibulo akuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi.”​—Yesaya 55:6.

Kuti muthe kuchita zimenezi, kuŵerenga ndi kuphunzira mosamalitsa Mawu a Mulungu kuyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu. Mudziŵeni Mulungu ndi iye amene anam’tuma, Yesu Kristu. Yesetsani kugwiritsira ntchito miyezo ya Mulungu ndipo motero sonyezani kuti muli wofunitsitsa kugonjera ulamuliro wake. Kuchita zimenezo kudzakupangitsani kukhala ndi chimwemwe chochuluka tsopano ngakhale mukumane ndi mayeso. Ndipo m’tsogolomu, mudzasangalala ndi moyo m’dziko lopanda mavuto.​—Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 M’Baibulo la The Jerusalem Bible, mawu a m’munsi pa Genesis 2:17, amati “kudziŵa zabwino ndi zoipa” ndiko “kutha kusankha . . . zabwino ndi zoipa ndi kuchita malinga ndi zomwe wasankhazo, kunena kuti ndi wodziimira payekha zimene zimachititsa munthu kusavomereza kuti anachita kulengedwa.” Mawuwo akupitiriza kuti: “Tchimo loyambali linaukira ulamuliro wa Mulungu.”

^ ndime 17 Kuti mumve tsatanetsane wa ulosi wa m’Baibulo wokhudza 1914, onani mutu 10 ndi 11 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi pamasamba 6, 7]

KODI TINGAPIRIRE BWANJI MAVUTO?

‘Tayani pa [Mulungu] nkhaŵa yanu yonse.’ (1 Petro 5:7) Tikamavutika kapena tikaona amene timam’konda akuvutika sikwachilendo kusokonezeka maganizo, kukwiya, ndi kuona ngati anthu onse sakutikonda. Ngakhale zili choncho, dziŵani kuti Yehova akudziŵa mmene timamvera. (Eksodo 3:7; Yesaya 63:9) Monga mmene anachitira amuna okhulupirika akale, tingamuuze zakukhosi ndi kufotokoza nkhaŵa zathu. (Eksodo 5:22; Yobu 10:1-3; Yeremiya 14:19; Habakuku 1:13) Iye mwina sangachotse mozizwitsa ziyeso zathu, koma poyankha mapemphero athu apansi pamtima, angatipatse nzeru ndi nyonga yakuti tipirire.​—Yakobo 1:5, 6.

“Musadabwe ndi chiyeso choŵaŵa chimene mukuvutika nacho, ngati kuti n’chinthu chachilendo chimene chikukuchitikirani.” (1 Petro 4:12, New International Version) Pano Petro akunena za chizunzo, koma mawu ake amagwiranso ntchito pa mavuto alionse amene wokhulupirira angakumane nawo. Anthu amavutika ndi umphaŵi, matenda ndi imfa. Baibulo limanena kuti “yense angoona zomgwera m’nthaŵi mwake.” (Mlaliki 9:11) Zinthu zimenezi zangokhala mbali ya moyo wa munthu masiku ano. Kudziŵa zimenezi kudzatithandiza kupirira mavuto akachitika. (1 Petro 5:9) Chofunika kwambiri, kukumbukira lonjezo lakuti “maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake achereza kulira kwawo” kudzatilimbikitsa kwambiri.​—Salmo 34:15; Miyambo 15:3; 1 Petro 3:12.

“Kondwerani m’chiyembekezo.” (Aroma 12:12) M’malo mongoganiza za nthaŵi yomwe tinkasangalala, tingasinkhesinkhe za lonjezo la Mulungu la kuthetsa mavuto onseŵa. (Mlaliki 7:10) Chiyembekezo chosakayikitsa chimenechi chidzatiteteza monga momwe chisoti chimatetezera mutu. Chiyembekezo chimapangitsa mavuto amene timakumana nawo pa moyo kukhala osapweteka kwambiri ndipo chimatithandiza kuti mavuto ameneŵa asawonongere

[Chithunzi patsamba 5]

Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Mulungu akulonjeza dziko lopanda mavuto