Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Dikirani”!

“Dikirani”!

“Dikirani”!

“Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.”​—Marko 13:37.

1, 2. (a) Kodi mwamuna wina anaphunzira mfundo yotani pankhani ya kuteteza katundu wake? (b) Kodi tikuphunzira chiyani m’chitsanzo cha Yesu cha mbala pankhani ya kudikira?

JUAN ankasunga chuma chake m’nyumba. Ankachisunga pansi pa bedi lake, malo amene iye ankaona ngati ndi otetezeka kwambiri kuposa ena alionse m’nyumbamo. Komabe tsiku lina usiku, iye ndi mkazi wake ali mtulo, wakuba analowa kuchipinda chogonacho. Mwachionekere, wakubayo anadziŵa malo enieni oti apeze chumacho. Iye anatenga mwakachetechete chuma chonse pamodzinso ndi ndalama zimene Juan anaziika m’dirowa ya tebulo imene inali pafupi ndi bedi. M’mawa mwake, Juan anazindikira kuti waberedwa. Sadzaiwala mfundo yopweteka imene anaiphunzira yakuti: Munthu yemwe ali mtulo sangateteze chuma chake.

2 Zimenezi zilinso chimodzimodzi ndi moyo wauzimu. Sitingateteze chiyembekezo chathu ndi chikhulupiriro chathu ngati tigona. N’chifukwa chake Paulo analangiza kuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:6) Posonyeza mmene kudikira kulili kofunika kwambiri, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la mbala. Atafotokoza zinthu zimene zidzachitika atatsala pang’ono kubwera monga Woweruza, anachenjeza kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Koma dziŵani ichi, kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi iti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:42-44) Mbala silengezeratu nthaŵi imene idzafika. Imafuna kufika panthaŵi imene anthu sakuiyembekezera kuti ingafike. N’chimodzimodzinso, monga Yesu ananenera, mapeto a dongosolo lino adzafika ‘munthaŵi imene sitiganizira.’

“Dikirani, Chirimikani M’chikhulupiriro”

3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kufunika kodikira pogwiritsa ntchito fanizo la akapolo amene anali kudikira kubwera kwa mbuye wawo kuchokera ku ukwati?

3 M’mawu amene ali mu Uthenga Wabwino wa Luka, Yesu anayerekezera Akristu ndi akapolo amene anali kuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera ku ukwati. Iwo anafunika kukhala tcheru kuti pofika mbuye wawoyo adzakhale akudikira, okonzeka kumulandira. Mofanana ndi zimenezi, Yesu anati: “Nthaŵi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.” (Luka 12:40) Anthu ambiri amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri angaleke kuona kuti nthaŵi imene tikukhala ino ndi yofunika kukhala tcheru. Iwo mwina angafike poganiza kuti mapeto ayenera kuti akadali kutali. Koma maganizo oterowo angatichititse kusasamala zinthu zauzimu ndi kumakonda kwambiri zinthu zakuthupi, zinthu zododometsa zimene zingatichititse kugona mwauzimu.​—Luka 8:14; 21:34, 35.

4. Kodi ndi kukhulupirira chiyani kumene kudzatilimbikitsa kudikira, ndipo Yesu anasonyeza bwanji zimenezi?

4 Tingaphunzirenso mfundo ina m’fanizo la Yesu. Ngakhale kuti akapolowo sankadziŵa nthaŵi imene mbuye wawoyo adzafika, iwo ayenera kuti ankadziŵa usiku umene anali kudzafika. Zikanakhala zovuta kudikira usiku wonsewo ngati akanaganiza kuti mbuye wawo angadzabwere usiku wina osati umene ankadikirawo. Koma ayi, ankadziŵa kuti ndi usiku uti umene anali kubwera, ndipo zimenezo zinawalimbikitsa kudikirabe. Mofananako ndi zimenezi, maulosi a Baibulo akuvumbula momveka bwino kuti tikukhala m’nthaŵi ya mapeto, koma satiuza tsiku ndi nthaŵi yeniyeni ya mapetowo. (Mateyu 24:36) Kukhulupirira kwathu kuti mapeto akubwera kumatithandiza kudikira, koma kukukhulupirira kuti tsiku la Yehova lilidi pafupi, kudzatilimbikitsa kwambiri kudikira kuposa pamenepo.​—Zefaniya 1:14.

5. Kodi tingamvere bwanji langizo la Paulo lakuti ‘tidikire’?

5 Paulo polembera Akorinto analimbikitsa kuti: “Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro.” (1 Akorinto 16:13) Inde, kudikira akukugwirizanitsa ndi kukhala kwathu ochirimika m’chikhulupiriro chachikristu. Kodi tingatani kuti tidikire? Tingadikire mwa kudziŵa zakuya za m’Mawu a Mulungu. (2 Timoteo 3:14, 15) Kuzoloŵera kuchita phunziro laumwini labwino ndi kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse zimathandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Ndiponso kuganizira tsiku la Yehova ndi mbali yofunika kwambiri ya chikhulupiriro chathu. Motero, kupenda kwathu nthaŵi ndi nthaŵi umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti tayandikira mapeto a dongosolo lino, kudzatithandiza kusaiwala choonadi chofunika kwambiri chokhudza mapeto amene akubwerawa. * N’kopindulitsanso kuganizira zochitika zimene tikuziona m’dzikoli zimene zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo. Mbale wina ku Germany analemba kuti: “Nthaŵi iliyonse pamene ndimvetsera nkhani ndi kuona pa TV nkhondo, zivomezi, chiwawa kuipitsidwa kwa dziko lapansili, zimanditsimikizira kuti mapeto alidi pafupi.”

6. Kodi Yesu anachitira fanizo bwanji maganizo oleka kukhala tcheru mwauzimu pamene nthaŵi ikupita?

6 Pa Marko chaputala 13, timapezapo nkhani inanso yofotokoza langizo la Yesu kwa ophunzira ake loti adikire. Malinga ndi chaputala chimenechi, Yesu akufanizira mmene zinthu zinalili kwa ophunzirawo ndi mmene zinalili kwa wapakhomo amene anali kudikira kubwera kwa mbuye wake kuchokera ku ulendo wautali. Wapakhomoyo sankadziŵa nthaŵi imene mbuyeyo adzabwera. Anangofunika kudikira. Yesu anatchula maulonda anayi amene mbuyeyo akanatha kufika. Ulonda wachinayi unkayambira fili koloko m’maŵa mpaka kutuluka kwa dzuŵa. Pa ulonda womalizawu, wapakhomoyo akanatha kugona mosavuta. Anthu amati asilikali amaona nthaŵi yoyandikira mbanda kucha kukhala yabwino kwambiri kugwira adani awo adaniwo asakudziŵa. Mofananamo, m’nthaŵi ya mapeto ino pamene dzikoli mwauzimu lili m’tulo tofa nato, tingafunike kuyesetsa kwambiri kuti tidikire. (Aroma 13:11, 12) Motero, m’fanizo lake, Yesu analimbikitsa mobwerezabwereza kuti: “Yang’anirani, dikirani . . . Chifukwa chake dikirani . . . Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.”​—Marko 13:32-37.

7. Kodi pali ngozi yeniyeni iti, ndipo poganizira zimenezi, ndi malangizo otani amene timawaŵerenga kaŵirikaŵiri m’Baibulo?

7 Yesu nthaŵi zambiri pamene anali kutumikira ndiponso ataukitsidwa, analimbikitsa kukhala tcheru. Ndipotu, pafupifupi nthaŵi iliyonse pamene Malemba anena za kutha kwa dongosolo lino la zinthu, timapeza chenjezo lakuti tidikire. * (Luka 12:38, 40; Chivumbulutso 3:2; 16:14-16) Inde, kugona mwauzimu ndi ngozidi yeniyeni. Tonsefe tifunikira machenjezo ameneŵa.​—1 Akorinto 10:12; 1 Atesalonika 5:2, 6.

Atumwi Atatu Amene Analephera Kudikira

8. Kodi m’munda wa Getsemane, atumwi atatu a Yesu anatani iye atawapempha kuti achezere?

8 Kudikira kumafuna zambiri osati kungokhala ndi zolinga zabwino chabe, monga mmene tikuonera m’chitsanzo cha Petro, Yakobo, ndi Yohane. Anthu atatu ameneŵa anali amuna okonda zauzimu omwe anatsatira Yesu mokhulupirika ndipo anamukonda kwambiri. Komabe, pa usiku wa pa Nisan 14, mu 33 C.E., iwo analephera kudikira. Atachoka m’chipinda chapamwamba kumene anachita phwando la Paskha, atumwi atatuŵa anatsagana ndi Yesu ku munda wa Getsemane. Kumeneko Yesu anawauza kuti: “Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.” (Mateyu 26:38) Yesu anapemphera ndi mtima wonse katatu kwa Atate wake wakumwamba, ndipo maulendo onse atatu ankati akabwerera kwa anzakewo ankangowapeza akugona.​—Mateyu 26:40, 43, 45.

9. Kodi n’chiyani chiyenera kuti chinachititsa atumwiwo kugona?

9 N’chifukwa chiyani amuna okhulupirika ameneŵa anakhumudwitsa Yesu usiku umenewo? Kutopa kwa thupi n’kumene kunawapangitsa kutero. Inali nthaŵi yotayika, mwina kupitirira pakati pausiku, ndipo “zikope zawo zinalemera ndi tulo.” (Mateyu 26:43) Komabe, Yesu anawauza kuti: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.”​—Mateyu 26:41.

10, 11. (a) Ngakhale kuti anali atatopa, kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuchezera m’munda wa Getsemane? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira atumwi atatuwo pamene Yesu anawauza kuti achezere?

10 Mosakayika, Yesu analinso wotopa pa usiku wapadera umenewo. Komabe, m’malo mogona, iye anagwiritsa ntchito nthaŵi yofunika kwambiri imeneyi yomaliza kukhala waufulu mwa kupemphera kuchokera pansi pa mtima. Masiku angapo zimenezi zisanachitike, iye analimbikitsa otsatira ake kupemphera. Anati: “Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:36; Aefeso 6:18) Ngati timvera malangizo a Yesu ndi kutsatira chitsanzo chake chabwino pankhani ya pemphero, kupemphera kwathu kwa Yehova kochokera pansi pa mtima kudzatithandiza kukhala maso mwauzimu.

11 Komabe, Yesu ankadziŵa kuti posachedwa adzamangidwa ndi kuweruzidwa kuti aphedwe, zimene ophunzira ake sankadziŵa panthaŵiyo. Mayesero ake anali oti adzafika popweteka kwambiri pa mtengo wozunzirapo. Yesu anali atachenjeza atumwi ake zimenezi, koma iwo sanamvetse zimene iye anali kunena. Motero, iwo anagona iye akuchezera kupemphera. (Marko 14:27-31; Luka 22:15-18) Monga mmene zinalili kwa atumwiwo, thupi lathunso n’lofooka ndipo pali zinthu zimene sitinazidziŵebe. Komabe, ngati tiiwala kuti nthaŵi imene tikukhala ino ndi yofunika kukhala tcheru, tingagone mwauzimu. Tidzatha kudikira ngati tikhala tcheru.

Makhalidwe Atatu Ofunika

12. Kodi ndi makhalidwe atatu ati amene Paulo akuwagwirizanitsa ndi kukhala kwathu maso?

12 Kodi tingatani kuti tikhalebe tcheru? Taona kale kufunika kwa pemphero ndi kufunika kokumbukira tsiku la Yehova. Ndiponso, Paulo anatchula makhalidwe ofunika kwambiri atatu amene tifunika kukhala nawo. Iye anati: “Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8) Tiyeni tikambirane mwachidule kufunika kwa chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi pa kukhala kwathu maso mwauzimu.

13. Kodi chikhulupiriro chimatithandiza bwanji kukhala tcheru?

13 Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chosagwedera chakuti Yehova alipo ndi kuti “ali wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wa Yesu wonena za mapeto m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino kumalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti udzakwaniritsidwa kwambiri m’nthaŵi yathu ino. Ndipo chikhulupiriro chathu chimatithandiza kuyembekezera mwatcheru tsiku la Yehova, tikutsimikiza kuti “[masomphenya aulosi] afika ndithu, osazengereza.”​—Habakuku 2:3.

14. Kodi chiyembekezo n’chofunika motani kuti tidikire?

14 Chikhulupiriro chathu chotsimikizika chili ngati “nangula wa moyo” amene amatithandiza kupirira mavuto ngakhale ngati tingafunike kuyembekezera kukwaniritsidwa kwinakwake kwa malonjezo a Mulungu. (Ahebri 6:18, 19) Mlongo wina wodzozedwa ndi mzimu wa zaka za m’ma 90 dzina lake Margaret, amene anabatizidwa zaka zoposa 70 zapitazo, anavomereza kuti: “Pamene mwamuna wanga anali kumwalira ndi kansa mu 1963, ndinaganiza kuti zikanakhala bwino ngati mapeto akanafika mofulumira. Koma tsopano ndikuzindikira kuti ndinkangoganizira makamaka ubwino wa ine basi. Sitinkadziŵa nthaŵi imeneyo kuti ntchitoyi idzafutukuka padziko lonse mpaka kufika pati. Ngakhale pakalipano, pakadali madera ambiri kumene ntchito yangotseguka kumene. Motero, ndikusangalala kuti Yehova waleza mtima.” Mtumwi Paulo akutitsimikizira kuti: “Chipiriro chichita chizoloŵezi; ndi chizoloŵezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi.”​—Aroma 5:3-5.

15. Kodi chikondi chidzatilimbikitsa bwanji ngakhale zitaoneka kuti tadikira kwa nthaŵi yaitali?

15 Chikondi chachikristu ndi khalidwe lapadera chifukwa ndi limene limatilimbikitsa kwambiri pa chilichonse chimene timachita. Timatumikira Yehova chifukwa chakuti timamukonda, mosaganizira za ndandanda yake yochitira zinthu. Kukonda anzathu kumatichititsa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mosaganizira kuti ndi nthaŵi yaitali bwanji imene Mulungu akufuna kuti titero ndiponso mosaganizira kuti ndi nthaŵi zambiri bwanji zimene tapita ku nyumba zimodzimodzi. Monga mmene Paulo analembera, “zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.” (1 Akorinto 13:13) Chikondi chimatithandiza kupirira ndiponso chimatithandiza kudikirabe. “[Chikondi] chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.”​—1 Akorinto 13:7, 8.

‘Gwirani Chimene Muli Nacho’

16. M’malo mochita ulesi, kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani?

16 Tikukhala m’nthaŵi yapadera kwambiri pamene zochitika m’dzikoli nthaŵi zonse zikutikumbutsa kuti tili kumapeto kwa masiku otsiriza. (2 Timoteo 3:1-5) Ino si nthaŵi yochita ulesi, m’malo mwake ndi nthaŵi ‘yogwira chimene tili nacho.’ (Chivumbulutso 3:11) Mwa kukhala ‘odikira m’mapemphero’ ndi kukhala ndi chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi, tidzakhala okonzeka panthaŵi ya mayeso. (1 Petro 4:7) Tili ndi zambiri zoti tichite m’ntchito ya Ambuye. Kukhala otanganidwa m’ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu kudzatithandiza kudikira.​—2 Petro 3:11.

17. (a) N’chifukwa chiyani zokhumudwitsa za nthaŵi zina siziyenera kutifooketsa? (Onani bokosi pa tsamba 21.) (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova, ndipo ndi madalitso otani omwe anthu amene akuchita zimenezo adzalandira?

17 Yeremiya analemba kuti: “Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira. Yehova akhalira wabwino om’lindirira, ndi moyo wom’funafuna. N’kokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” (Maliro 3:24-26) Enafe tadikira kwa nthaŵi yochepa chabe. Ena adikira kwa zaka zambiri kuti aone chipulumutso cha Yehova. Komatu nthaŵi imene tikudikira ndi yochepa poyerekezera ndi nthaŵi yopanda mapeto imene ili m’tsogolo! (2 Akorinto 4:16-18) Ndipo pamene tikudikira nthaŵi yoikika ya Yehova, tingakulitse makhalidwe ofunika kwambiri achikristu ndiponso kuthandiza ena kutengerapo mwayi pa kuleza mtima kwa Yehova ndi kuphunzira choonadi. Ndiyetu tiyeni tonsefe tidikire. Tiyeni titsanzire Yehova ndi kukhala oleza mtima, kuyamikira chiyembekezo chimene watipatsa. Ndipo pamene tikukhalabe tcheru mokhulupirika, tiyeni tigwiritsitse chiyembekezo cha moyo wosatha. Tikatero, malonjezo aulosi aŵa adzagwira ntchito kwa ife: “[Yehova] adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya.”​—Salmo 37:34.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kupenda maumboni asanu ndi umodzi osonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ amene tinawandandalika mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2000, masamba 12 mpaka 13, kungakuthandizeni.​—2 Timoteo 3:1.

^ ndime 7 Pofotokoza za liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “dikirani,” wolemba mabuku otanthauzira mawu, W. E. Vine anafotokoza kuti liwulo kwenikweni limatanthauza ‘kuthamangitsa tulo,’ ndipo “silimangosonyeza kukhala maso chabe, koma kukhala tcheru, makamaka anthu amene ali ndi cholinga pa chinthu chinachake.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu chakuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi?

• Kodi tingaphunzire chiyani pa zitsanzo za Petro, Yakobo, ndi Yohane?

• Kodi ndi makhalidwe atatu ati amene angatithandize kukhalabe tcheru mwauzimu?

• N’chifukwa chiyani ino ndi

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 21]

“Wodala Iye Amene Ayembekeza.”​—Danieli 12:12

Tayerekezani kuti mlonda akuyembekezera kuti wakuba akukonza zoti adzabe pa malo amene iye akulondera. Pamene kukuda, mlondayo akumvetsera mwatcheru mtswatswa uliwonse umene ungasonyeze kuti wakubayo wafika. Nthaŵi iliyonse amakhala akumvetsera ndipo sagona. N’zosavuta kuona mmene anganyengedwere ndi zizindikiro zonama monga kaphokoso kamphepo ikamagwedeza mitengo kapena mphaka akagubuduza chinachake.​—Luka 12:39, 40.

Zinthu ngati zimenezi zikhozanso kuchitika kwa anthu amene ‘akulindira vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu.’ (1 Akorinto 1:7) Atumwi anaganiza kuti Yesu anali ‘kudzabwezeretsa ufumu kwa Israyeli’ atangoukitsidwa kumene. (Machitidwe 1:6) Patapita zaka, Akristu a ku Tesalonika anafunika kukumbutsidwa kuti kukhalapo kwa Yesu kunali kudzachitika m’tsogolo. (2 Atesalonika 2:3, 8) Komabe, zizindikiro zonama zokhudza tsiku la Yehova sizinachititse otsatira Yesu oyambirirawo kusiya njira ya ku moyo.​—Mateyu 7:13.

M’masiku athu ano, kukhumudwa chifukwa choona ngati mapeto a dongosolo lino akuchedwa sikuyenera kutigwetsa ulesi. Mlonda watcheru akhoza kunyengedwa ndi zizindikiro zonama, komabe ayenera kukhala maso. Imeneyo ndi ntchito yake. N’chimodzimodzinso ndi Akristu.

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mukukhulupirira kuti tsiku la Yehova layandikira?

[Zithunzi patsamba 19]

Misonkhano, pemphero, zizoloŵezi zabwino zophunzira zimatithandiza kudikira

[Chithunzi patsamba 22]

Mofanana ndi Margaret, tiyeni tidikire moleza mtima ndiponso kukhala achangu