Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kakalata Kamene Kanasintha Moyo Wanga

Kakalata Kamene Kanasintha Moyo Wanga

Mbiri ya Moyo Wanga

Kakalata Kamene Kanasintha Moyo Wanga

YOSIMBIDWA NDI IRENE HOCHSTENBACH

Zinachitika Lachiŵiri usiku m’chaka cha 1972. Ndinali ndi zaka 16 ndipo ndinapita ndi makolo anga ku msonkhano wa chipembedzo ku Eindhoven, mzinda wa m’chigawo cha Brabant, ku Netherlands. Sunandisangalatse ndipo ndinkangofuna ndili kwina kwake osati pamaloŵa. Kenako atsikana aŵiri anandipatsa kakalata ka uthenga wakuti: “Wokondeka Irene, tikufunitsitsa kuti tikuthandize.” Sindinkadziŵa momwe kakalata kameneka kasinthire moyo wanga. Ndisananene zimene zinachitika, ndiloleni ndikuuzeni za moyo wanga m’mbuyomo.

NDINABADWIRA pa chilumba cha Belitung, ku Indonesia. Ndimakumbukira zina zimene ndinkamva pa chilumbapo​—kaphokoso ka mitengo ya kanjedza mphepo ikamawomba, kaphokoso kamadzi a mumtsinje womwe tinali nawo pafupi, kuseka kwa ana omwe ankaseŵera pafupi ndi nyumba yathu komanso mawu a nyimbo zimene tinali kumvetsera kunyumba kwathu. Mu 1960, ndili ndi zaka zinayi, banja lathu linasamukira ku Netherlands kuchoka ku Indonesia. Tinayenda ulendo wautali wa pa sitima ya m’madzi, ndipo kaphokoso kamene ndimakakumbukira kwambiri ndi ka chidole chimene ndinkachikonda kwambiri chimene ndinatenga paulendowu​—chidole chimenechi chinali ndi zoliralira. Ndili ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, ndinasiya kumva chifukwa cha matenda, ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo ndakhala ndisakumva mawu a chinthu china chilichonse. Ndimangokumbukira zimene ndinamva m’mbuyomo.

Kukula Ndili Wosamva

Chifukwa chakuti makolo anga ankandisamalira ndiponso ankandikonda, poyamba sindinkadziŵa kwenikweni mmene kukhala wosamva kumapwetekera. Monga mwana, ndinkaganiza kuti chinthu chachikulu chothandizira kumva chimene ndinali nacho chinali chosekesa ngakhale kuti sichinkandithandiza kwenikweni. Ana anzanga polankhula nane, ankalemba ndi choko nkhani yonse pansi ndiyeno ndinkawayankha, ngakhale kuti sindinkamva ndi mawu anga omwe.

Ndikukula, ndinazindikira kuti ndinali wosiyana ndi anthu ena. Ndinayambanso kuona kuti anthu ena ankandiseka chifukwa cha kusamva, ndipo ena ankandisankha akamacheza. Ndinayamba kusungulumwa ndiponso kuzindikira mmene kusamva kumapwetekera. Ndikukula, mpamene ndimaopanso kwambiri anthu amene amamva.

Kuti ndikaphunzire sukulu ya anthu osamva, makolo anga anasamutsa banja lonse ku chigawo cha Limburg kupita ku mzinda wa Eindhoven. Kumeneko, bambo anga anapeza ntchito, ndipo mchimwene wanga ndi azichemwali anga anayamba sukulu. Ndimathokoza kwambiri zonse zimene anachita n’cholinga chofuna kundithandiza. Kusukulu, ndinaphunzira momwe ndingamasinthire kukwera kwa mawu ndiponso kulankhula zomveka bwino. Ndipo ngakhale kuti aphunzitsi sankaphunzitsa m’chinenero cholankhula ndi manja, anzanga a mkalasi anandiphunzitsa kalankhulidwe kameneka.

Kusadziŵa Zimene Zikuchitika

Ndikukula, makolo anga anayesetsa kulankhula nane, koma panali zinthu zambiri zimene sindinkadziŵa. Mwachitsanzo, sindinkadziŵa kuti makolo anga anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma ndimakumbukira kuti tsiku lina banja lathu linapita ku malo ena kumene anthu ambiri anakhala m’mipando. Onse anayang’ana kutsogolo, pena ankawomba m’manja ndipo pena ankaima ndiyeno n’kukhala pansi, koma sindinkadziŵa chifukwa chake anali kuchita zimenezi. Patapita nthaŵi yaitali, ndinadziŵa kuti panali pamsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova. Makolo anganso ankakonda kupita nane ku holo yaing’ono ya mu mzinda wa Eindhoven. Kumeneko ndinkamasuka chifukwa onse anali okoma mtima ndipo makolo ndi achibale anga ankaoneka kuti akusangalala, koma sindinkadziŵa chifukwa chake tinkapita kumeneko nthaŵi zonse. Tsopano ndikudziŵa kuti holo yaing’onoyo inali Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.

Zachisoni kuti, pamisonkhano imeneyi panalibe wondimasulira mapulogalamuwo. Tsopano ndikuzindikira kuti amene ankapezeka pa misonkhanoyo ankafuna kundithandiza koma kungoti sankadziŵa mmene angachitire ndi kusamva kwangako. Pamisonkhano imeneyi, ndinkasungulumwa ndipo ndinkaganiza kuti, ‘N’kanakhala kusukulu bwenzi zili bwino kulekana n’kuno.’ Koma pamene ndinali kuganiza zimenezi, atsikana aŵiri analemba kakalata n’kundipatsa. Aka n’kakalata kamene ndakatchula kumayambiriro kwa nkhani ino. Sindinkadziŵa mpang’ono pomwe kuti kakalata kameneka n’chiyambi cha ubwenzi wamtengo wapatali umene uthetse kusungulumwa kwanga.

Kuyamba Ubwenzi Wamtengo Wapatali

Colette ndi Hermine, amene anandipatsa kakalatako, anali m’zaka za m’ma 20. Kenako, ndinamva kuti anabwera ku mpingo wa Mboni za Yehova kumene ndinkasonkhana, kukatumikira monga apainiya okhazikika, kapena kuti atumiki a nthaŵi zonse. Ngakhale kuti Colette ndi Hermine sankadziŵa kwenikweni chinenero cholankhula ndi manja, ndinkatha kumva zonena zawo mwakuona mmene akugwedezera milomo akamalankhula, ndipo mwanjira imeneyi tinkalankhulana bwinobwino.

Makolo anga anasangalala Colette ndi Hermine atapempha zoti aziphunzira nane Baibulo, koma atsikana ameneŵa sikuti anangochita zokhazi ayi. Anayesetsa kwambiri kundimasulira misonkhano pa Nyumba ya Ufumu komanso kusandisankha akamacheza ndi anthu ena pampingopo. Ankayeserera ndi ine zitsanzo za ulaliki wa Baibulo umene akagwiritse ntchito mu ntchito yolalikira ndiponso anandithandiza kukonzekera nkhani za ophunzira za mu Sukulu ya Utumiki wa Teokalase. Tangolingalirani, ndinafika polimba mtima kukamba nkhani pamaso pa gulu la anthu amene amamva.

Komanso Colette ndi Hermine anandithandiza kuti ndiziwadalira. Anali oleza mtima ndipo ankamvetsera zonena zanga. Ngakhale kuti nthaŵi zambiri tinkaseka ndikalakwitsa; iwo sankandiseka; komanso sankachita manyazi kucheza nane. Ankayesetsa kumvetsa mmene ndimamvera mumtima ndipo anali kukhala nane monga munthu wofanana nawo. Atsikana achifundo ameneŵa anandipatsa mphatso yabwino kwambiri​—kundikonda komanso kucheza nane.

Chofunika kwambiri Colette ndi Hermine anandiphunzitsa kudziŵa Mulungu wathu, Yehova, monga bwenzi lodalirika. Anafotokoza kuti Yehova anandiona nditakhala mu Nyumba ya Ufumu ndiponso kuti amamvetsa mavuto a munthu wosamva. Ndikusangalala kwambiri kuti kukonda kwathu Yehova kwatigwirizanitsa atatufe kukhala mabwenzi. Nditaona mmene Yehova amandisamalirira ndiponso chifukwa chakuti ndimamukonda, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa iye mwa kubatizidwa mu July 1975.

Kuyenda ndi Mnzanga Wapamtima

M’zaka zotsatira, ndinadziŵana ndi abale ndi alongo ambiri achikristu. Mbale wina anakhala mnzanga wapamtima zedi, ndipo tinakwatirana mu 1980. Patapita kanthaŵi, ndinayamba upainiya, ndipo mu 1994, ine ndi mwamuna wanga, Harry, tinatumizidwa kukatumikira monga apainiya apadera ku gawo la Adatchi olankhula ndi manja. Chaka chotsatira, ndinali ndi ntchito yovuta kwambiri. Ndinayenera kuyenda ndi mwamuna wanga, amene amamva, pamene akuyendera mipingo yosiyanasiyana monga woyang’anira dera wogwirizira.

Nazi zimene ndimachita. Tikapita pampingo paulendo wathu woyamba, ndimafulumira kuzidziŵikitsa kwa abale ndi alongo ambiri. Ndimawauza kuti sindimamva ndipo ndimawapempha kuti akamandilankhula azindiyang’ana ndiponso azilankhula pang’onopang’ono. Ndimayesetsanso kuyankha pamisonkhano ya mpingo penipenipo. Ndipo ndimafunsa ngati wina akufuna kuti azindimasulira pa misonkhano ndiponso mu utumiki wakumunda mlungu umenewo.

Njira imeneyi imayenda bwino kwambiri, moti nthaŵi zina abale ndi alongo anga amaiŵala kuti sindimva, zimene zimaseketsa kwambiri. Mwachitsanzo, amandiuza kuti akandiona m’tauni, amandiimbira hutala kuti andipatse moni, koma sindichita kalikonse. Inenso nthaŵi zina ndimaiŵala kuti sindimamva, mwachitsanzo ndikamanong’oneza mwamuna wanga kanthu kenakake kachinsinsi. Ndikamuona kuti wasintha nkhope, ndimadziŵa kuti “kunong’onako” kunali kokwera mawu kwambiri.

Ana amathandiza njira zimene sitiziganizira. Paulendo wathu woyamba kupita pa mpingo wina, mnyamata wa zaka naini anaona kuti anthu ena pa Nyumba ya Ufumu amaopa kundilankhula, ndipo anafuna kuthandiza. Anabwera pamene panali ine n’kundigwira mkono, kupita nane pakati pa Nyumba ya Ufumu, ndipo anafuula kwambiri kuti, “Ndikufuna mumudziŵe Irene​—ndi wosamva!” Anthu amene analipo anabwera kwa ine kumandiuza mayina awo.

Ndikamayenda ndi mwamuna wanga mu ntchito yadera, mabwenzi anga amachulukirachulukira. Moyo wanga wasintha kwambiri masiku ano kusiyananiratu ndi zaka zimene ndinkaona kuti amandisankha komanso kuti ndinkasungulumwa. Kuyambira usiku umene Colette ndi Hermine anandipatsa kakalata kameneko, ndaona kufunika kwa mayanjano ndipo ndadziŵana ndi anthu amene tsopano ndi anthu ofunika kwambiri kwa ine. Koposa zonse, ndadziŵa Yehova, Bwenzi lapamtima loposa onse. (Aroma 8:38, 39) Kakalata kameneko kanasintha moyo wanga bwanji!

[Chithunzi patsamba 24]

Ndimakumbukira kaphokoso ka chidole changa chimene ndinkachikonda kwambiri

[Zithunzi patsamba 25]

Ndili mu utumiki ndiponso ndili ndi mwamuna wanga, Harry