Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene anati: “Nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho”?

Pofotokoza za kukhazikitsidwa kwa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, Paulo analemba kuti: “Nthaŵi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.” (1 Akorinto 11:25, 26) Ena amaganiza kuti mawu akuti “nthaŵi zonse” pano amasonyeza kuti imfa ya Kristu iyenera kukumbukiridwa pafupipafupi, kapena kuti nthaŵi zambiri. Motero, iwo amachita chikumbutsochi nthaŵi zambiri osati kamodzi pachaka. Kodi ndi zimene Paulo ankatanthauza?

Tsopano papita zaka pafupifupi 2,000 kuyambira pamene Yesu anakhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake. Motero, kuchita Chikumbutsochi ngakhale kamodzi pachaka kukutanthauza kuti chachitika nthaŵi zonse kuyambira mu 33 C.E. Komabe, m’nkhani ya pa 1 Akorinto 11:25, 26, Paulo anali kufotokoza mmene Chikumbutsocho chiyenera kuchitikira osati chizichitika kangati. M’Chigiriki choyambirira, iye sanagwiritse ntchito liwu lakuti pol·laʹkis, limene limatanthauza “nthaŵi zambiri” kapena “pafupipafupi.” M’malo mwake, iye anagwiritsira ntchito liwu lakuti ho·saʹkis, limene limatanthauza “nthaŵi zonse,” mawu okuluwika amene amatanthauza kuti “nthaŵi ina iliyonse,” “nthaŵi iliyonse imene.” Paulo anali kunena kuti: ‘Nthaŵi iliyonse imene mukuchita zimenezi, mukulengeza imfa ya Ambuye.’

Nangano, kodi Chikumbutso cha imfa ya Yesu chizichitika kangati? N’koyenera kuchita chikumbutsochi kamodzi kokha pachaka. Chimenechi ndi chikumbutso ndithu, ndipo zikumbutso nthaŵi zambiri zimachitika kamodzi pachaka. Ndiponso, Yesu anafa patsiku la Paskha wa Ayuda, amene ankachitika kamodzi pachaka. Moyenerera, Paulo anatcha Yesu kuti ‘Paskha wathu Kristu,’ chifukwa imfa ya nsembe ya Yesu inatsegula njira ya kumoyo ya Israyeli wauzimu monga mmene nsembe ya Paskha woyambirira inapulumutsa ana oyamba kubadwa a Aisrayeli enieni ku Igupto ndipo inatsegula njira yoti mtunduwo umasuke ku ukapolo. (1 Akorinto 5:7; Agalatiya 6:16) Kugwirizana kumeneku ndi Paskha wa Ayuda amene ankachitika kamodzi pachaka ndi umboni winanso wakuti Chikumbutso cha imfa ya Yesu chiyenera kuchitika kamodzi kokha pachaka.

Ndiponso, Paulo anagwirizanitsa imfa ya Yesu ndi Tsiku la Chitetezo, lomwe linali phwando linanso la Ayuda limene linkachitika kamodzi pachaka. Pa Ahebri 9:25, 26, timaŵerenga kuti: “Kosati kuti [Yesu] adzipereke yekha kaŵirikaŵiri; monga mkulu wa ansembe alowa m’malo opatulika chaka ndi chaka [pa Tsiku la Chitetezo] ndi mwazi wosati wake; . . . koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthaŵizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.” Popeza nsembe ya Yesu inaloŵa m’malo mwa nsembe ya Tsiku la Chitetezo yochitika kamodzi pachaka, n’koyenera kuchita Chikumbutso cha imfa yake kamodzi pachaka. Palibe zifukwa za m’Malemba zochitira Chikumbutso nthaŵi zambiri kuposa pamenepo.

Mogwirizana ndi zimenezi, wolemba mbiri wina, John Laurence von Mosheim ananena kuti Akristu a m’zaka za m’ma 100 a ku Asia Minor anazoloŵera kuchita Chikumbutso cha imfa ya Yesu “pa tsiku la 14 la mwezi woyamba wachiyuda [Nisan].” Patapita zaka m’pamene Matchalitchi Achikristu anayamba kumachita chikumbutso nthaŵi zambiri osati kamodzi pachaka.