Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Umanena Zoona, Moyo Ndi Wokoma!”

“Umanena Zoona, Moyo Ndi Wokoma!”

“Umanena Zoona, Moyo Ndi Wokoma!”

KODI ungakonde kudziŵa cholinga chenicheni cha moyo? Mtsikana wina wa Mboni za Yehova wa zaka 18, dzina lake Magdalena, amene amakhala mu mzinda wa Szczecin ku Poland, anathandiza Katarzyna, mnzake wa m’kalasi pasukulu ya sekondale kuchita zimenezi. Katarzyna anali wolimba kwambiri pa kusakhulupirira kwake Mulungu, koma Magdalena atakamba naye za m’Baibulo, anasonyeza chidwi kwambiri.

Ngakhale kuti Katarzyna anasangalala kwambiri ndi zinthu za m’Baibulo zimene Magdalena anamuuza, iye sanazikhulupirire kwenikweni. Nthaŵi ina Katarzyna akukambirana ndi Magdalena za mabwenzi enieni, anati: “Iwe uli ndi Baibulo; umadziŵa mfundo zofunika kuzitsatira ndiponso umadziŵa kumene ungapeze anthu ocheza nawo. Koma bwanji nanga amene mwina pakalipano sangakhulupirire mfundo zimenezo?”

Zinthu zinasintha Katarzyna atapita ku London, dziko la England. Kumeneko anakafika ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ndipo anakopeka mtima ndi chikondi chimene anamuonetsera. Zinthu zazing’ono monga kumutsegulira chitseko ndiponso kumvetsera zimene anali kunena zinam’sangalatsa kwambiri.

Atatsegulira sukulu chaka chatsopano mu September 2001, Katarzyna anaganiza zovomera kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse. Akupitiriza kukonda mfundo za m’Baibulo ndipo wayamba kuzigwiritsira ntchito pa moyo wake watsiku ndi tsiku. Posachedwapa, anamuuza Magdalena mawu a kukhosi kwake. Anati: “Ndikuona ngati ndayamba moyo watsopano.” Ndiponso anamutumizira uthenga wapatelefoni ya m’manja wonena kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha phunziro la lero! Umanena zoona, moyo ndi wokoma! N’zosangalatsa kudziŵa amene tiyenera kumuthokoza chifukwa cha zimenezi.”