Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?

Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?

Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?

“Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.”​—MARKO 1:15.

1, 2. Kodi mungalifotokoze bwanji lemba la Marko 1:14, 15?

MUNALI m’chaka cha 30 C.E. pamene Yesu Kristu anayamba utumiki wake waukulu ku Galileya. Anali kulalikira “uthenga wabwino wa Mulungu,” ndipo Agalileya ambiri analimbikitsidwa ndi mawu ake akuti: “Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.”​—Marko 1:14, 15.

2 “Nthaŵi” inakwana yoti Yesu ayambe utumiki wake ndiponso kuti anthu asankhe kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kuwayanja. (Luka 12:54-56) ‘Ufumu wa Mulungu unayandikira’ chifukwa Yesu anali pomwepo monga Mfumu Yosankhidwiratu. Ntchito yake yolalikira inachititsa anthu oongoka mtima kulapa. Koma kodi iwo anasonyeza bwanji ‘kukhulupirira uthenga wabwino,’ nanga ifeyo tingasonyeze bwanji?

3. Kodi anthu achita chiyani kusonyeza kuti akukhulupirira uthenga wabwino?

3 Mofanana ndi Yesu, mtumwi Petro analimbikitsa anthu kuti alape. Polankhula kwa Ayuda ku Yerusalemu pa Pentekoste mu 33 C.E., Petro anati: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.” Anthu zikwi zingapo analapa, anabatizidwa ndipo anakhala otsatira Yesu. (Machitidwe 2:38, 41; 4:4) Mu 36 C.E., anthu Akunja olapa anachitanso chimodzimodzi. (Machitidwe 10:1-48) Masiku ano, kukhulupirira uthenga wabwino kukuchititsa anthu ambirimbiri kulapa machimo awo, kudzipatulira kwa Mulungu, ndi kubatizidwa. Alandira uthenga wabwino wa chipulumutso ndipo akukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Ndiponso, akuchita chilungamo ndipo ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu.

4. Kodi chikhulupiriro n’chiyani?

4 Koma kodi chikhulupiriro n’chiyani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Chikhulupiriro chathu chimatichititsa kutsimikiza kuti zonse zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake zidzachitikadi ndipo zili ngati kuti zachitika kale. Zikufanana ndi kuti tili ndi chikalata chotsimikizira kuti malo ena ake ndi athuathu. Chikhulupiriro ndichonso “chiyesero,” kapena kuti umboni wotsimikizira zinthu zosaoneka. Kuzindikira kwathu zinthu ndiponso kukhala kwathu ndi mtima woyamikira kumatitsimikizira kuti zinthu zimenezo n’zenizeni, ngakhale kuti sitinazione.​—2 Akorinto 5:7; Aefeso 1:18.

Tifunika Chikhulupiriro!

5. N’chifukwa chiyani chikhulupiriro n’chofunika kwambiri?

5 Anthufe tinabadwa tikufuna zinthu zauzimu koma sitinabadwe tili ndi chikhulupiriro. Ndipotu, “si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Komabe, Akristu ayenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti adzalandire zimene Mulungu walonjeza. (Ahebri 6:12) Atatchula zitsanzo zambiri za anthu amene anali ndi chikhulupiriro, Paulo analemba kuti: “Popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” (Ahebri 12:1, 2) Kodi ‘tchimo limene limangotizinga’ n’chiyani? Ndilo kusoŵa chikhulupiriro, ngakhale kutaya kumene chikhulupiriro chimene tinali nacho. Kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba, tiyenera ‘kupenyerera Yesu’ ndi kutsatira chitsanzo chake. Tifunikanso kupeŵa makhalidwe oipa, kukana ntchito za thupi, ndi kupeŵa kukondetsa chuma, nzeru za dziko, ndi miyambo yosagwirizana ndi malemba. (Agalatiya 5:19-21; Akolose 2:8; 1 Timoteo 6:9, 10; Yuda 3, 4) Ndiponso, tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu ali nafe ndi kuti malangizo a m’Mawu ake amathandizadi kwambiri.

6, 7. N’chifukwa chiyani n’koyenera kupempherera chikhulupiriro?

6 Sitingathe kukhala ndi chikhulupiriro mwa mphamvu zathu. Chikhulupiriro ndi mbali ya chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito. (Agalatiya 5:22, 23) Nanga bwanji ngati chikhulupiriro chathu chikufunika kuchilimbitsa? Yesu anati: “Ngati inu . . . mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?” (Luka 11:13) Inde, tiyeni tipempherere mzimu woyera, chifukwa ungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro chimene chimafunika kuti tichite chifuniro cha Mulungu ngakhale panthaŵi ya mavuto aakulu.​—Aefeso 3:20.

7 N’koyenera kupempha kuti atiwonjezere chikhulupiriro. Yesu atatsala pang’ono kuti achotse chiwanda mwa mwana wina, bambo ake a mwanayo anapempha kuti: “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.” (Marko 9:24) Ophunzira a Yesu ananena kuti: “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” (Luka 17:5) Motero, tiyeni tizipempherera chikhulupiriro, tisakukayika kuti Mulungu amayankha mapemphero oterowo.​—1 Yohane 5:14.

Kukhulupirira Mawu a Mulungu N’kofunika

8. Kodi kukhulupirira Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji?

8 Atangotsala pang’ono kuti afe imfa ya nsembe, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.” (Yohane 14:1) Ife monga Akristu, timakhulupirira Mulungu ndi Mwana wake. Koma bwanji Mawu a Mulungu? Iwo angatilimbikitse kwambiri kuchita zabwino ngati tiwaphunzira ndi kuwagwiritsa ntchito tili ndi chikhulupiriro chonse kuti amatipatsa uphungu ndiponso malangizo abwino kwambiri.​—Ahebri 4:12.

9, 10. Kodi mungafotokoze bwanji zimene akunena pa Yakobo 1:5-8 zokhudza chikhulupiriro?

9 Moyo wathu monga anthu opanda ungwiro uli ndi mavuto ambiri. Komabe, kukhulupirira Mawu a Mulungu kungatithandizedi kwambiri. (Yobu 14:1) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti sitikudziŵa mmene tingachitire ndi vuto linalake. Mawu a Mulungu amatipatsa malangizo aŵa: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iŵiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse.”​—Yakobo 1:5-8.

10 Yehova Mulungu sadzatitonza chifukwa chosoŵa nzeru ndi kuipempherera. M’malo mwake, iye adzatithandiza kuti tione vutolo moyenera. Mwina okhulupirira anzathu angatchule malemba amene angatithandize kwambiri kapena tingaone malembawo pamene tikuphunzira Baibulo. Mwinanso, mzimu woyera wa Yehova ungatitsogolere mwa njira ina. Atate wathu wakumwamba adzatipatsa nzeru zoti tipirire mavuto ngati tipitiriza ‘kupempha ndi chikhulupiriro, osakayika konse.’ Tikakhala ngati funde la m’nyanja lotengeka ndi mphepo, sitingayembekezere kulandira chilichonse kwa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti zimenezi zingatanthauze kuti ndife a mitima iŵiri ndiponso osakhazikika m’pemphero kapena m’njira zina​—ee, ngakhalenso posonyeza chikhulupiriro. Motero tifunika kukhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu ndiponso malangizo amene amapereka. Tiyeni tione zina mwa zitsanzo za mmene amathandizira ndi kutipatsa malangizo.

Chikhulupiriro pa Nkhani ya Zofunika pa Moyo

11. Kodi kukhulupirira Mawu a Mulungu kumatitsimikizira chiyani pankhani ya zofunika zathu za tsiku ndi tsiku?

11 Bwanji ngati pakalipano tikuvutika ndi njala kapena umphaŵi? Kukhulupirira Mawu a Mulungu kumatithandiza kuyembekeza motsimikizira kuti Yehova adzasamalira zofunika pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndiponso kuti m’tsogolo adzapereka zinthu zambiri kwa anthu onse amene amamukonda. (Salmo 72:16; Luka 11:2, 3) Mwina zingatilimbikitse kusinkhasinkha mmene Yehova anaperekera chakudya kwa mneneri wake Eliya panthaŵi ya njala. Kenako, Yehova anapereka mozizwitsa ufa ndi mafuta zimene zinathandiza mkazi wina pamodzi ndi mwana wake komanso Eliya kuti akhale ndi moyo. (1 Mafumu 17:2-16) Mofanana ndi zimenezi, Yehova anapatsa mneneri wake Yeremiya zakudya panthaŵi imene Ababulo anazinga Yerusalemu. (Yeremiya 37:21) Ngakhale kuti Yeremiya ndi Eliya anali ndi chakudya chochepa, Yehova anawasamalira. Iye amachitanso chimodzimodzi kwa anthu amene amamukhulupirira masiku ano.​—Mateyu 6:11, 25-34.

12. Kodi chikhulupiriro chidzatithandiza bwanji kupeza zofunika kwambiri pamoyo?

12 Chikhulupiriro pamodzi ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo sikudzatilemeretsa, koma kudzatithandiza kupeza zofunika kwambiri pamoyo. Mwachitsanzo, Baibulo limatilangiza kuti tikhale anthu oona mtima, otha kuchita zinthu, ndiponso ogwira ntchito mwakhama. (Miyambo 22:29; Mlaliki 5:18, 19; 2 Akorinto 8:21) Sitifunika kuchepetsa kufunika kokhala ndi mbiri yabwino pamene tikugwira ntchito. Ngakhale kumadera amene ntchito n’zosoŵa, antchito oona mtima, aluso, ndiponso akhama pantchito zimawayendera bwino kuposa ena. Ngakhale kuti antchito oterowo sangakhale ndi chuma chambiri, nthaŵi zambiri amakhala ndi zofunika zazikulu ndipo amasangalala kudya chakudya chimene amachipeza mwa kugwira ntchito.​—2 Atesalonika 3:11, 12.

Chikhulupiriro Chimatithandiza Kupirira Chisoni

13, 14. Kodi chikhulupiriro chimatithandiza bwanji kupirira chisoni?

13 Mawu a Mulungu amasonyezeratu kuti n’chibadwa kumva chisoni munthu amene tinali kumukonda akamwalira. Kholo lakale lokhulupirika Abrahamu linalira mkazi wake wokondedwa Sara atamwalira. (Genesis 23:2) Davide anamva chisoni kwambiri atamva kuti mwana wake Abisalomu wamwalira. (2 Samueli 18:33) Ngakhale Yesu, yemwe anali wangwiro, analira pamene mnzake Lazaro anamwalira. (Yohane 11:35, 36) Munthu amene timamukonda akamwalira, tingakhale ndi chisoni chachikulu zedi, koma kukhulupirira malonjezo a m’Mawu a Mulungu kungatithandize kupirira chisoni choterocho.

14 Paulo ananena kuti: ‘Ndi[li] nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.’ (Machitidwe 24:15) Tiyenera kukhulupirira zimene Mulungu wakonza zodzaukitsa anthu ambirimbiri kuti akhale ndi moyo. (Yohane 5:28, 29) Ena mwa iwo adzakhala Abrahamu ndi Sara, Isake ndi Rebeka, Yakobo ndi Leya omwe pakalipano ali m’tulo ta imfa ndipo akuyembekezera kudzawaukitsa m’dziko latsopano la Mulungu. (Genesis 49:29-32) Inde, kudzakhala chimwemwe chachikulu anthu amene timawakonda akadzaukitsidwa ku tulo ta imfa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi lino. (Chivumbulutso 20:11-15) Pakadali pano, chikhulupiriro sichingachotse chisoni chonse, koma chidzatiyandikizitsa kwa Mulungu, amene amatithandiza kupirira chisoni.​—Salmo 121:1-3; 2 Akorinto 1:3.

Chikhulupiriro Chimalimbikitsa Ovutika Maganizo

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuvutika maganizo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro sikwachilendo? (b) Kodi tingatani kuti tithane ndi kuvutika maganizo?

15 Mawu a Mulungu amasonyezanso kuti ngakhale anthu amene ali ndi chikhulupiriro akhozanso kuvutika maganizo. Pamene Yobu anali pa mayeso owawa kwambiri, anaganiza kuti Mulungu anamusiya. (Yobu 29:2-5) Nehemiya anavutika maganizo chifukwa cha kupasuka kwa Yerusalemu ndi malinga ake. (Nehemiya 2:1-3) Petro anavutika maganizo kwambiri atakana Yesu moti “[a]nalira misozi ndi kuwawa mtima.” (Luka 22:62) Ndipo Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake mumpingo wa ku Tesalonika kuti ‘alimbikitse amantha mtima [“ovutika maganizo,” NW].’ (1 Atesalonika 5:14) Motero, kuvutika maganizo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro masiku ano sikwachilendo. Nangano, tingatani kuti tithane ndi kuvutika maganizo?

16 Tingavutike maganizo chifukwa chakuti tikukumana ndi mavuto aakulu angapo. M’malo mowaona ngati chivuto chimodzi chachikulu, tingathe kumathetsa vuto limodzilimodzi pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zingachepetse kuvutika kwathu maganizo. Kugwira ntchito zosiyanasiyana mosapitirira malire ndiponso kupuma mokwanira kungathandizenso. Mfundo yotsimikizika ndi yakuti: Kukhulupirira Mulungu ndi Mawu ake kumalimbikitsa moyo wabwino wauzimu chifukwa kumalimbitsa chidaliro chathu chakuti iye amatisamalira.

17. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amatisamalira?

17 Petro akutilimbikitsa ndi kutitsimikizira kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:6, 7) Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova agwiriziza onse akugwa, nawongoletsa onse owerama.” (Salmo 145:14) Tiyenera kukhulupirira zimene akutitsimikizirazi, chifukwa zikupezeka m’Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti kuvutika maganizo kungapitirire, n’zolimbikitsa kwambiri chikhulupiriro kudziŵa kuti tingatule nkhaŵa zathu zonse kwa Atate wathu wachikondi wakumwamba.

Chikhulupiriro Pamene Tikukumana ndi Mavuto Ena

18, 19. Kodi chikhulupiriro chimatithandiza bwanji kupirira matenda ndi kulimbikitsa okhulupirira anzathu amene akudwala?

18 Chikhulupiriro chathu chingayesedwe kwambiri ngati ife kapena anthu amene timawakonda akudwala kwambiri. Ngakhale kuti Baibulo silinena kuti Akristu monga Epafrodito, Timoteo, ndi Trofimo anachira mozizwitsa, mosakayika Yehova anawathandiza kupirira. (Afilipi 2:25-30; 1 Timoteo 5:23; 2 Timoteo 4:20) Ndiponso pankhani ya munthu “amene asamalira wosauka,” wamasalmo anaimba kuti: “Yehova adzam’gwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.” (Salmo 41:1-3) Kodi mawu a wamasalmoŵa angatithandize bwanji polimbikitsa okhulupirira anzathu amene akudwala?

19 Njira imodzi yolimbikitsira mwauzimu anthu amene akudwala ndiyo kupemphera nawo ndi kuwapempherera. Ngakhale kuti sitiyenera kupempherera kuchiritsidwa mozizwitsa masiku ano, tingapemphe kuti Mulungu awapatse mphamvu zoti apirire matenda awo ndiponso mphamvu zauzimu zofunika kuti apirire nthaŵi za kufooka zimenezo. Yehova adzawathandiza ndipo chikhulupiriro chawo chidzalimbikitsidwa mwa kuyembekezera nthaŵi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) N’zolimbikitsatu kudziŵa kuti kudzera mwa Yesu Kristu amene anaukitsidwa ndiponso mwa Ufumu wa Mulungu, anthu omvera adzamasuka ku uchimo, matenda, ndiponso imfa mpaka kalekale! Tikuthokoza Yehova amene ‘adzachiritsa nthenda zathu zonse’ chifukwa cha chiyembekezo chachikulu chimenechi.​—Salmo 103:1-3; Chivumbulutso 21:1-5.

20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikhulupiriro chingatithandize kupirira “masiku oipa” a ukalamba?

20 Chikhulupiriro chingatithandizenso kupirira “masiku oipa” a ukalamba, pamene thanzi ndi mphamvu zimachepa. (Mlaliki 12:1-7) Motero, anthu okalamba amene tili nawo angapemphere monga mmene anachitira wamasalmo wokalamba amene anaimba kuti: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova . . . Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salmo 71:5, 9) Wamasalmoyo anaona kuti akufunikira kuti Yehova amuthandize, monga mmene amachitira Akristu anzathu ambiri amene akhala akutumikira Mulungu kwa zaka zambiri ndipo akalamba. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo, iwo angatsimikize kuti manja osatha a Yehova adzawathandiza mpaka kalekale.​—Deuteronomo 33:27.

Khulupiriranibe Mawu a Mulungu

21, 22. Kodi kukhulupirira kungakhudze bwanji ubwenzi wathu ndi Mulungu?

21 Kukhulupirira uthenga wabwino ndi Mawu onse a Mulungu kumatithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova. (Yakobo 4:8) N’zoona kuti iye ndi Ambuye Mfumu yathu, komanso ndi Mlengi ndi Atate wathu. (Yesaya 64:8; Mateyu 6:9; Machitidwe 4:24) Wamasalmo anaimba kuti: “Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.” (Salmo 89:26) Ngati tikhulupirira Yehova ndi Mawu ake ouziridwa, ifenso tingamuone monga ‘thanthwe la chipulumutso chathu.’ Ndi mwayi wosangalatsatu kwambiri umenewo!

22 Yehova ndi Atate wa Akristu odzozedwa ndi mzimu ndiponso ndi Atate wa anzawo amene akuyembekezera kudzakhala pa dziko lapansi. (Aroma 8:15) Ndipo kukhulupirira Atate wathu wakumwamba sikugwiritsa mwala. Davide anati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Ndiponso tili ndi chitsimikizo chakuti: “Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu.”​—1 Samueli 12:22.

23. Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tikhale pa ubwenzi wokhalitsa ndi Yehova?

23 Inde, kuti tikhale paubwenzi wokhalitsa ndi Yehova, tiyenera kukhulupirira uthenga wabwino ndi kulandira Malemba monga momwe alilidi Mawu a Mulungu. (1 Atesalonika 2:13) Tiyenera kumukhulupirira kwambiri Yehova ndi kulola kuti Mawu ake aunikire njira yathu. (Salmo 119:105; Miyambo 3:5, 6) Chikhulupiriro chathu chidzakula pamene tikupemphera kwa iye ndi chidaliro chonse kuti adzatichitira chifundo ndi kutithandiza.

24. Kodi ndi mfundo yolimbikitsa iti imene tikuipeza pa Aroma 14:8?

24 Chikhulupiriro chinatichititsa kudzipatulira kwa Mulungu mpaka kalekale. Tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba, ngakhale timwalire, ndifebe atumiki ake odzipatulira oyembekezera kudzaukitsidwa. Inde, “tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.” (Aroma 14:8) Tiyeni tikhalebe ndi mfundo yolimbikitsa imeneyi mumtima mwathu pamene tikupitirizabe kukhulupirira Mawu a Mulungu ndiponso uthenga wabwino.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi chikhulupiriro n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani timafunikira khalidwe limeneli?

• N’chifukwa chiyani tifunika kukhulupirira uthenga wabwino ndiponso Mawu onse a Mulungu?

• Kodi chikhulupiriro chimatithandiza bwanji kupirira mavuto osiyanasiyana?

• N’chiyani chidzatithandiza kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 12]

Yehova anapereka zakudya kwa Yeremiya ndi Eliya chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro

[Zithunzi patsamba 13]

Yobu, Petro, ndi Nehemiya anali ndi chikhulupiriro cholimba

[Zithunzi patsamba 15]

Kuti tikhale paubwenzi wokhalitsa ndi Yehova, tifunika kukhulupirira uthenga wabwino