Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Malemba amavomereza Mkristu kuika dzanja lake pa Baibulo ndi kulumbira pofuna kunena zoona zokhazokha m’khoti?

Munthu aliyense ayenera kusankha yekha chochita pankhani imeneyi. (Agalatiya 6:5) Komabe, Baibulo sililetsa kulumbira pofuna kunena zoona m’khoti.

Kuyambira kalekale, kulumbira n’kotchuka. Mwachitsanzo, kalelo Agiriki ankatukula mkono n’kuloza kumwamba kapena kugwira guwa la nsembe akamalumbira. Mroma ankati akamalumbira, ankanyamula mwala ndi kulumbira kuti: “Ngati ndinama mwadala, pamene [mulungu] Jupiter adzapulumutsa mzinda ndi linga lolimba, andichotsere zabwino zonse, monga mmene ndikutayira mwalawu.”​—Inatero Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yolembedwa ndi John McClintock ndi James Strong, Voliyumu VII, tsamba 260.

Zimenezi zinasonyeza kuti anthu amazindikira kuti kuli mulungu amene angathe kuona anthu ndiponso kuti anthu adzadziŵerengera mlandu kwa iye. Kuyambira kale, olambira Yehova oona ankazindikira kuti iye ankadziŵa zimene iwo anali kunena ndi kuchita. (Miyambo 5:21; 15:3) Tingati ankalumbira pamaso pa Mulungu kapena iye ankakhala mboni pa kulumbira kwawoko. Mwachitsanzo, Boazi, Davide, Solomo, ndi Zedekiya anachita zimenezo. (Rute 3:13; 2 Samueli 3:35; 1 Mafumu 2:23, 24; Yeremiya 38:16) Olambira Mulungu woona ankalolanso kuti ena awalumbiritse. Zimenezi n’zimene zinachitika kwa Abrahamu ndiponso kwa Yesu Kristu.​—Genesis 21:22-24; Mateyu 26:63, 64.

Munthu amene anali kulumbira pamaso pa Yehova nthaŵi zina ankasonyeza chizindikiro chinachake. Abramu (Abrahamu) anauza mfumu ya Sodomu kuti: “Dzanja langa ndam’tukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 14:22) Mngelo amene anali kulankhula ndi mneneri Danieli “[a]nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha.” (Danieli 12:7) Ngakhale Mulungu, amam’fotokoza mwafanizo kuti anakweza dzanja lake polumbira.​—Deuteronomo 32:40; Yesaya 62:8.

Malemba saletsa kulumbira. Komabe, Mkristu safunika kulumbira kuti atsimikizire mfundo iliyonse imene akulankhula. Yesu anati: ‘Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi.’ (Mateyu 5:33-37) Wophunzira Yakobo anatchulanso mfundo imeneyi. Pamene ananena kuti “musalumbire,” iye ankachenjeza za kulumbira pankhani zilizonse. (Yakobo 5:12) Yesu ndiponso Yakobo sananene kuti n’kulakwa kulumbira pofuna kunena zoona m’khoti.

Nanga bwanji ngati Mkristu am’pempha kulumbira m’khoti posonyeza kuti umboni wake ndi woona? Iye angaone kuti akhoza kulumbira. Kapena, angamulole kuti afotokoze motsimikiza kuti sakunama.​—Agalatiya 1:20.

Ngati malamulo a m’khoti amafuna kutukula mkono kapena kuika dzanja pa Baibulo polumbira, Mkristu angasankhe kugwirizana nazo. Mwina angakumbukire zitsanzo za m’Malemba zosonyeza kuti munthu ankasonyeza chizindikiro chinachake polumbira. Kwa Mkristu, chinthu chofunika kwambiri kuposa kuchita chizindikiro chinachake polumbira ndicho kukumbukira kuti akulumbira pamaso pa Mulungu kuti anena zoona. Kulumbira koteroko ndi nkhani yaikulu. Ngati Mkristu akuona kuti angayankhe ndipo ayenera kuyankha funso limene wafunsidwa m’zochitika zimenezi, ndiye kuti ayenera kukumbukira kuti iye walumbira kuti anena zoona, zomwe n’zimenedi Mkristu afunika kulankhula nthaŵi zonse.