“Olengeza Ufumu Achangu” Anasonkhana Mosangalala
“Olengeza Ufumu Achangu” Anasonkhana Mosangalala
MAVUTO achikhalidwe, achuma, ndi andale akusokoneza dziko lapansi. Komabe ngakhale izi zili choncho, Mboni za Yehova zinasonkhana bwinobwino masiku atatu pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Olengeza Ufumu Achangu.” Kuyambira mu May 2002, misonkhano imeneyi inachitika padziko lonse.
Nthaŵi ya misonkhano imeneyi inalidi yosangalatsa kwambiri. Tiyeni tibwereze mwachidule pulogalamu yolimbikitsa ya m’Baibulo imeneyi.
Tsiku Loyamba Linagogomezera Changu cha Yesu
Mutu wa tsiku loyamba la msonkhano unali wakuti “Tsanzirani Changu cha Ambuye Wathu Yesu.” (Yohane 2:17) Nkhani yakuti “Kondwerani Posonkhana Pamodzi Monga Olengeza Ufumu” inapempha mwachikondi opezekapo kutenga mbali mu chisangalalo chomwe chimapezeka nthaŵi zonse pamisonkhano ya anthu a Mulungu. (Deuteronomo 16:15) Nkhaniyi itatha panali kufunsa olengeza achangu a uthenga wabwino.
Nkhani yakuti “Kondwerani ndi Yehova” inafotokoza vesi lililonse la Salmo 37:1-11. M’nkhaniyi tinauzidwa kuti ‘tisamavutike mtima’ ngati ochita zoipa akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Ngakhale kuti ochita zoipa angatinamizire, Yehova panthaŵi yake adzaonetsa omwe ali anthu ake okhulupirika. Nkhani yakuti “Khalani Oyamikira” inafotokoza mmene tingayamikirire Mulungu. Akristu onse ayenera kupereka “nsembe yakuyamika” kwa Yehova. (Ahebri 13:15) Mwachionekere, nthaŵi imene timathera mu utumiki wa Yehova imadalira kuyamikira kwathu ndiponso mmene zinthu zilili kwa ife.
Nkhani yaikulu inali ndi mutu wakuti “Changu cha Olengeza Ufumu Chinakolezeka.” Nkhaniyi inasonyeza kuti Yesu Kristu ndiye chitsanzo chathu chabwino koposa cha changu. Ufumu wakumwamba utakhazikitsidwa mu 1914, Akristu oona anafunikira changu kuti alengeze uthenga wabwino umenewu. Wokamba nkhaniyi anafotokoza za msonkhano wa ku Cedar Point, Ohio, ku United States, mu 1922 ndipo anatikumbutsa za chilengezo chosaiwalika chakuti: “Lengezani Mfumu ndi Ufumu wake”! M’kupita kwanthaŵi, changu cha atumiki a Mulungu okhulupirika chinawachititsa kulengeza choonadi chosangalatsa cha Ufumu kwa mitundu yonse.
Nkhani yakuti “Musaope Podziŵa Kuti Yehova Ali Nafe” yomwe inakambidwa masana patsiku loyamba, inasonyeza kuti Satana amafuna kwambiri anthu a Mulungu. Komabe ngakhale kuti anthu amatitsutsa, kupenda kwathu zitsanzo zambiri za m’Baibulo ndi za masiku ano za chikhulupiriro zimatilimbitsa mtima kupirira ziyeso mopanda mantha.—Yesaya 41:10.
Nkhani yotsatira papulogalamu inali yosiyirana ya mbali zitatu ya mutu wakuti “Ulosi wa Mika Umatilimbikitsa Kuti Tiyende M’dzina la Yehova.” Wokamba nkhani woyamba anayerekeza 2 Petro 3:11, 12.
kupanda khalidwe, mpatuko wazipembedzo, ndi kukonda chuma zomwe zinali m’tsiku la Mika ndi nthaŵi zathu zino. Iye anati: “Kuyembekeza kwathu zinthu zabwino m’tsogolo kungakhale kotsimikizika ngati tikhala ndi mtima womvera ndi kuonetsetsa kuti khalidwe lathu n’loyera ndiponso mwa kudzipereka ndi mtima wonse kuchita zimene Mulungu akufuna. Sitiyenera kuiwala kuti tsiku la Yehova lidzafika.”—Wokamba nkhani wachiŵiri pankhani yosiyiranayi anafotokoza kutsutsa atsogoleri achiyuda kumene Mika anachita. Iwo anapondereza anthu osauka ndi opanda chitetezo. Koma Mika analoseranso za kupambana kwa kulambira koona. (Mika 4:1-5) Ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova, tatsimikiza kulengeza uthenga wotsitsimula wachiyembekezo. Bwanji ngati tikulephera chifukwa cha matenda kapena ndife opereŵera m’njira zina? Wokamba nkhani wachitatu anati: “Zimene Yehova amafuna kwa ife si zopambanitsa ndipo tingathe kuzichita.” Ndiyeno anafotokoza mbali zosiyanasiyana za Mika 6:8, pamene timaŵerenga kuti: “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”
Popeza kuti makhalidwe onyansa angakhudze Akristu, ife tonse tinapindula ndi nkhani yakuti “Khalanibe Oyera mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu.” Mwachitsanzo, kukhala kwathu oyera kudzatithandiza kuti tikhale ndi ukwati wachimwemwe. Monga Akristu, sitifunika kuganizira ngakhale zochita chiwerewere.—1 Akorinto 6:18.
Nkhani yakuti “Peŵani Chinyengo” inasonyeza kuti tingachite bwino kuona ngati poizoni nkhani zopotoka, nkhani zoti kwinaku n’zoona kwinaku zabodza ndiponso bodza lenileni zimene ampatuko amafalitsa. (Akolose 2:8) Ndiponso, sitiyenera kudzinyenga tokha poganiza kuti tingachite machimo popanda kukumana ndi zotsatira zake zopweteka.
“Lambirani Mulungu Woona Yekha” unali mutu wa nkhani yomaliza patsiku loyamba. Pamene zinthu m’dziko zikukhala zovuta kwambiri, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova posachedwapa
adzabweretsa dziko lake latsopano lolungama. Kodi ndani adzakhalamo? Ndi okhawo amene amalambira Yehova. Wokamba nkhaniyi anatulutsa buku lophunzira latsopano lakuti Worship the Only True God, lotithandiza ifeyo, ana athu, ndi omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti tichite zimenezi. Tinasangalala kwambiri kulandira buku limeneli!Tsiku Lachiŵiri Linatsindika Kukhala Achangu pa Zinthu Zabwino
Mutu wa tsiku lachiŵiri la msonkhano unali wakuti “Khalani Achangu pa Zinthu Zabwino.” (1 Petro 3:13) Wokamba nkhani woyamba anafotokoza lemba la Baibulo latsikulo. Iye anagogomezera kuti kuŵerenga lemba latsiku nthaŵi zonse ndiponso moikirapo mtima kumawonjezera changu chathu.
Ndiyeno panali nkhani yosiyirana yakuti “Olengeza Ufumu Amene Amalemekeza Utumiki Wawo.” Mbali yoyamba inagogomezera kufunika kolunjika nawo bwino Mawu a Mulungu. (2 Timoteo 2:15) Kugwiritsira ntchito bwino Baibulo kumapereka mpata woti mawuwo akhale “ochitachita, [“amphamvu,” NW]” pa moyo wa anthu. (Ahebri 4:12) Tiyenera kugwiritsira ntchito Baibulo ndi kulifotokoza mogwira mtima. Mbali yachiŵiri ya nkhani yosiyiranayi inatiuza kuti tizipanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi mobwerezabwereza. (1 Akorinto 3:6) Kuti tibwerere mwamsanga kwa anthu onse achidwi m’pofunika kukonzekera ndi kulimba mtima. Mbali yachitatu inatiuza kuti tiyenera kuona munthu aliyense amene tikumana naye monga munthu woti angadzakhale wophunzira. Ndipo mbaliyi inasonyezanso kuti kupempha anthu kuphunzira nawo paulendo woyamba kungapangitse kuti tikhale achimwemwe powathandiza kukhala ophunzira.
Nkhani yotsatira inali ndi mutu wakuti “Chifukwa Chomwe Tiyenera ‘Kupempherera Kosaleka.’” Baibulo limalangiza Akristu kuyang’ana kwa Mulungu kuti awatsogolere mbali zonse za moyo wawo. Tifunika kukhala ndi nthaŵi yopemphera. Ndipotu, tiyenera kupemphera kosaleka, chifukwa Yehova angatilole kupitirizabe kupemphera kwakanthaŵi asanayankhe mapemphero athu.—Yakobo 4:8.
Nkhani yakuti “Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa” inatiuza kuti tiyenera kugwiritsira ntchito mphatso yakulankhula kuti ifeyo ndi anthu ena tipindule. (Afilipi 4:8) Anthu okwatirana ndiponso ana afunika kukambirana zinthu zauzimu tsiku lililonse. Kuti athe kuchita zimenezi, mabanja ayenera kuyesetsa kudyera pamodzi mwina kamodzi patsiku kuti akhale ndi makambirano olimbikitsa.
Chigawo cha m’maŵa chinatha ndi nkhani yakuti “Mmene Kudzipatulira ndi Kubatizidwa Kumatsogolerera ku Chipulumutso.” Obatizidwa anapeza chidziŵitso, anasonyeza chikhulupiriro, analapa, anasiya kuchita zoipa ndipo anadzipatulira kwa Mulungu. Wokamba nkhaniyi anati, akabatizidwa ayenera kupitirizabe kukula mwauzimu ndi kukhalabe achangu ndiponso akhalidwe labwino.—Afilipi 2:15, 16.
Panthaŵi ya masana, nkhani yakuti “Khalani Odzichepetsa Ndiponso a Diso la Kumodzi” inagogomezera mfundo ziŵiri zazikulu. Kukhala odzichepetsa kumatanthauza kuzindikira zomwe munthuwe sungakwanitse kuchita ndi kudziona moyenera pamaso pa Mulungu. Kudzichepetsa kumatithandiza kukhala ndi diso “la kumodzi,” kuika maganizo pa Ufumu wa Mulungu, osati pa zinthu zakuthupi. Tikachita zimenezi, sitifunika kuda nkhaŵa chifukwa Yehova adzatipatsa zofuna zathu.—Mateyu 6:22-24, 33, 34.
Wokamba nkhani yotsatira ya mutu wakuti “Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wonse Panthaŵi za Mavuto,” anasonyeza chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezi. Kodi tingathane bwanji ndi zinthu monga kufooka kwathu ndi mavuto azachuma kapena matenda? Tiyeni tipemphe Yehova nzeru ndi kupempha ena kuti atithandize. M’malo mothedwa nzeru kapena kutaya mtima, tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu mwa kuŵerenga Mawu ake.—Aroma 8:35-39.
Nkhani yosiyirana yomaliza pamsonkhanowu inali ndi mutu wakuti “Chikhulupiriro Chathu Chimayesedwa ndi Mayesero Osiyanasiyana.” Mbali yoyamba inatikumbutsa kuti Akristu oona onse amakumana ndi chizunzo. Chili ngati umboni, chimalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndipo chimatipatsa mwayi woti tisonyeze kukhulupirika kwathu kwa Mulungu. Ngakhale kuti sitimaika moyo wathu pangozi mwadala, 1 Petro 3:16.
sitingagwiritsire ntchito njira zosemphana ndi Malemba kupeŵa chizunzo.—Wokamba nkhani wachiŵiri pankhani yosiyiranayi anayankha mafunso okhudza kusatenga mbali m’zochitika zadzikoli. Akristu oyambirira sanali otsutsa nkhondo, koma anadziŵa kuti amafunika kukhala okhulupirika choyamba kwa Mulungu. Mofananamo masiku ano, Mboni za Yehova zimatsatirabe mfundo yakuti: “Simuli a dziko lapansi.” (Yohane 15:19) Popeza mayeso akusatenga mbali m’zochitika zadzikoli angabuke mwamsanga, mabanja afunika kupeza nthaŵi kubwereramo m’malangizo a m’Baibulo pankhani imeneyi. Monga mmene nkhani yachitatu pankhani yosiyiranayi inafotokozera, cholinga cha Satana si ndicho kutipha basi, koma kutiumiriza kuti tikhale osakhulupirika. Pamene tipirira mokhulupirika kunyozedwa, zinthu zimene zingatipangitse kuchita choipa, kuvutika maganizo, ndi matenda, timatamanda Yehova.
Mawu olimbikitsa akuti “Yandikirani kwa Yehova” anali mutu wankhani yomaliza patsikuli. Kumvetsa makhalidwe ofunika kwambiri a Yehova kumatiyandikizitsa kwa iye. Iye amagwiritsira ntchito mphamvu zake zopanda malire kuteteza anthu ake, makamaka mwauzimu. Chilungamo chake si cha nkhanza koma chimam’pangitsa kupereka moyo wosatha kwa aliyense amene amachita chilungamo. Nzeru ya Mulungu imaonekera m’njira imene anagwiritsira ntchito anthu opanda ungwiro kulemba Baibulo. Chosangalatsa kwambiri ndi chikondi chake, chimene chinam’pangitsa kupanga makonzedwe oti anthu apulumuke kudzera mwa Yesu Kristu. (Yohane 3:16) Wokamba nkhaniyi anamaliza mwa kutulutsa buku latsopano lolimbikitsa lakuti Yandikirani kwa Yehova.
Tsiku Lachitatu Linatsindika Kukhala Achangu pa Ntchito Zokoma
Mutu watsiku lachitatu la msonkhano unali wakuti “Anthu Achangu Pa Ntchito Zokoma.” (Tito 2:14) Pulogalamu ya m’maŵa inayamba ndi banja limene linakambirana lemba latsiku. Ndiyeno panatsatira nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mumakhulupirira Yehova?” Mitundu imakhulupirira zinthu zolakwika chifukwa cha kudalira nzeru ndi mphamvu zawo. Komabe, mosiyana ndi zimenezi, atumiki a Yehova molimba mtima ndi mosangalala amadalira Yehova ngakhale kuti amakumana ndi mavuto.—Salmo 46:1-3, 7-11.
Nkhani ya mutu wakuti “Achinyamata—Konzani Tsogolo Lanu ndi gulu la Yehova” inayankha funso lakuti: Kodi wachinyamata angakhale bwanji ndi moyo wopindulitsa kwambiri? Zimenezi sizingatheke mwa kufunafuna ndalama, katundu ndi kukhala wotchuka. Mlengi wathu mwachikondi amauza achinyamata kum’kumbukira pamene akadali achinyamata. Wokamba nkhaniyi anafunsa ena amene analimbikira utumiki wachikristu ali achinyamata, ndipo tinatha kuona chimwemwe chawo. Ndipo zinali zosangalatsa kulandira thirakiti latsopano lakuti, Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?, limene lakonzedwa kuthandiza Mboni zachinyamata kuyala maziko a tsogolo losatha ndi gulu la Yehova.
Ndiyeno panachitika seŵero la m’Baibulo lochititsa chidwi lakuti “Chirimikani M’nthaŵi Zovuta.” Seŵeroli linafotokoza mwachidule ntchito yomwe Yeremiya anachita kwanthaŵi yaitali kuyambira ali wachinyamata mpaka nthaŵi imene Yerusalemu anali kuwonongedwa. Ndipo ndi iye amene analosera zimenezi mwachangu. Yeremiya ankadziona ngati wosayenerera kuchita ntchito imeneyi, koma anaichita ngakhale kuti ankatsutsidwa, ndipo Yehova anam’landitsa.—Yeremiya 1:8, 18, 19.
Seŵero litatha panali nkhani yakuti “Lengezani Mawu a Mulungu Mopanda Mantha Monga Yeremiya.” Olengeza Ufumu amakono nthaŵi zambiri amawanamizira ndiponso anthu amafalitsa nkhani zabodza zofuna kuipitsa mbiri yawo. (Salmo 109:1-3) Komabe, monga Yeremiya tingalimbane ndi zinthu zofooketsa mwa kukondwera ndi Mawu a Yehova. Ndipo tili otsimikiza kuti amene amalimbana nafe sadzapambana.
Nkhani ya onse ya mutu wakuti “Maonekedwe a Dzikoli Akusintha” inalidi ya panthaŵi yake. M’nthaŵi yathu ino zinthu zasintha kwambiri. Baibulo linalosera kuti zinthu zimenezi, kuphatikizapo chilengezo cha “mtendere ndi mosatekeseka” zidzatsogolera ku tsiku la Mulungu lochititsa mantha la chiweruzo. (1 Atesalonika 5:3) Lidzabweretsa kusintha kosangalatsa, kutha kwa nkhondo, upandu, chiwawa, ngakhalenso matenda. M’malo mokhulupirira dongosolo ili la zinthu, ino ndiyo nthaŵi yokhala wodzipereka kwa Mulungu ndiponso kukhala ndi makhalidwe abwino.
Chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo chitatha panali nkhani yomaliza ya msonkhano ya mutu wakuti “Chitani Ntchito Zabwino Zochuluka Monga Olengeza Ufumu Achangu.” Wokamba nkhaniyi anafotokoza mmene pulogalamuyi inatitsitsimulira mwauzimu ndiponso kutilimbikitsa kudalira Yehova. Pomaliza anatilimbikitsa kukhala oyera, achikondi komanso olengeza achangu a Ufumu wa Mulungu.—1 Petro 2:12.
Pobwerera ku nyumba tinali ndi maganizo ofanana ndi a atumiki a Yehova a m’nthaŵi ya Nehemiya. Tinasangalala kwambiri chifukwa cha madalitso auzimu amene tinawalandira pa Msonkhano Wachigawo wa “Olengeza Ufumu Achangu.” (Nehemiya 8:12) Kodi msonkhano wolimbikitsawu sunakupatseni chimwemwe ndiponso kukuthandizani kukhala wotsimikiza kupirira monga wolengeza Ufumu wachangu?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]
Buku Latsopano Lothandiza Pophunzitsa!
Pomaliza tsiku loyamba la msonkhano, opezekapo anasangalala ndi kutulutsidwa kwa buku latsopano lakuti Worship the Only True God. Bukuli lakonzedwa kuti ochititsa maphunziro a Baibulo aziphunzira ndi anthu amene amaliza kuphunzira buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha ndipo mosakayikira lidzalimbitsa chikhulupiriro cha anthu “ofuna moyo wosatha.”—Machitidwe 13:48, NW.
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi pachikuto cha buku: U.S. Navy photo
[Bokosi/Zithunzi patsamba 24]
Buku Lothandiza Kuyandikira kwa Mulungu
Wokamba nkhani womaliza patsiku lachiŵiri la msonkhano analengeza kuti patuluka buku latsopano lakuti Yandikirani kwa Yehova. Bukuli lili ndi zigawo zinayi zazikulu ndipo chilichonse chimalongosola khalidwe limodzi mwa makhalidwe aakulu a Yehova, omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru ndi chikondi. Chigawo chilichonse cha bukuli chili ndi mutu wosonyeza mmene Yesu Kristu anasonyezera zitsanzo zooneka bwino za mmene Mulungu amasonyezera makhalidwe ake. Cholinga chachikulu cha buku latsopanoli ndi kutithandiza ife ndi amene timaphunzira nawo Baibulo kukhala ndi ubwenzi wapamtima ndiponso wolimba kwambiri ndi Yehova Mulungu.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 26]
Malangizo Auzimu kwa Achinyamata
Tsiku lachitatu la msonkhano linali lapadera chifukwa cha kutuluka kwa thirakiti lapadera la mutu wakuti, Achinyamata—Kodi Moyo wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji? Thirakitili lakonzedwa kuthandiza Mboni zachinyamata kusankha zochita zabwino zokhudza tsogolo lawo. Thirakiti latsopano limeneli likupereka malangizo a m’Malemba a mmene angakhalire ndi ntchito yosatha m’utumiki wa Yehova.