‘Kondanani Wina ndi Mnzake’
‘Kondanani Wina ndi Mnzake’
“Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—YOHANE 13:35.
1. Kodi ndi khalidwe liti limene Yesu anagogomezera imfa yake itatsala pang’ono kuchitika?
“TIANA.” (Yohane 13:33) Yesu anagwiritsira ntchito mawu osonyeza chikondi amenewo polankhula kwa atumwi ake usiku woti imfa yake ichitika maŵa. Palibe paliponse m’Mauthenga Abwino pamene Yesu anagwiritsirapo ntchito mawu osonyeza chikondi ameneŵa polankhula nawo. Komabe, usiku wapadera umenewu iye analimbikitsidwa kugwiritsira ntchito mawu achikondi ameneŵa kusonyeza chikondi chachikulu chimene anali nacho kwa otsatira ake. Ndipotu, usiku umenewu Yesu analankhula za chikondi pafupifupi ka 30. N’chifukwa chiyani anagogomezera khalidwe limeneli motere?
2. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti Akristu asonyeze chikondi?
2 Yesu anafotokoza chifukwa chake chikondi n’chofunika kwambiri. Iye anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35; 15:12, 17) Kukhala wotsatira wa Kristu kumayendera limodzi ndi kusonyeza chikondi kwa abale. Akristu oona amadziŵika, osati ndi kuvala mwapadera kapena kuchita miyambo ina yapadera, koma ndi chikondi chochokera pansi pamtima chimene amasonyeza kwa wina ndi mnzake. Kukhala ndi chikondi chapadera chimenechi ndi mfundo yachiŵiri mwa mfundo zofunika kwambiri zitatu zimene wophunzira wa Kristu afunika kukwaniritsa zomwe zinatchulidwa pachiyambi m’nkhani yoyamba. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupitirizabe kukwaniritsa mfundo yofunika imeneyi?
“Muchulukireko Koposa”
3. Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani okhudza chikondi?
3 Monga mmene zinalili ndi otsatira Kristu m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, 1 Atesalonika 3:12; 4:9, 10) Ifenso tifunika kumvera malangizo a Paulo ndipo tifunika kuyesetsa kusonyeza chikondi kwa wina ndi mnzake ‘mochulukirako koposa.’
chikondi chapadera chimenechi chimaonekeranso masiku ano pa ophunzira oona a Kristu. Kwa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake; pakutinso munawachitira ichi abale onse.” Ngakhale zinali choncho, Paulo anawonjezera kunena kuti: “Muchulukireko koposa.” (4. Kodi ndani amene tiyenera kuwaganizira mwapadera, malinga ndi kunena kwa Paulo ndi Yesu?
4 M’kalata youziridwa yomweyi, Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake ‘kulimbikitsa amantha mtima’ ndi ‘kuchirikiza ofooka.’ (1 Atesalonika 5:14) Panthaŵi ina, anakumbutsa Akristu kuti ‘amene ali olimba ayenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu.’ (Aroma 15:1) Yesu nayenso anapereka malangizo okhudza kuthandiza anthu ofooka. Ataneneratu kuti pausiku umene adzamangidwe, Petro adzam’kana, Yesu anauza Petro kuti: “Pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwonso adzam’kana Yesu ndipo chotero adzafunika thandizo. (Luka 22:32; Yohane 21:15-17) Chotero, Mawu a Mulungu amatiuza kusonyeza chikondi chathu kwa amene ali ofooka mwauzimu ndiponso amene angakhale kuti sakugwirizananso ndi mpingo wachikristu. (Ahebri 12:12) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Mafanizo aŵiri omveka bwino amene Yesu anasimba akupereka yankho.
Nkhosa ndi Ndalama Zotayika
5, 6. (a) Kodi ndi mafanizo aŵiri ati achidule amene Yesu anasimba? (b) Kodi mafanizo ameneŵa akutiuza chiyani za Yehova?
5 Kuti aphunzitse omvera ake mmene Yehova amaonera amene asochera, Yesu anafotokoza mafanizo aŵiri achidule. Lina limanena za mbusa. Yesu anati: “Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yotayikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera. Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo. Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.”—Luka 15:4-7.
6 Fanizo lachiŵiri limanena za mkazi. Yesu anati: “Mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo mmene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”—Luka 15:8-10.
7. Kodi zinthu ziŵiri ziti zimene mafanizo a nkhosa ndi ndalama zotayika akutiphunzitsa?
7 Kodi tingaphunzire chiyani pa mafanizo achidule ameneŵa? Akutisonyeza (1) mmene tiyenera kuonera amene afooka ndipo (2) chimene tiyenera kuchita kuti tiwathandize. Tiyeni tikambirane mfundo zimenezi?
Yotayika Komabe Yofunika
8. (a) Kodi mbusa ndi mkazi anachita bwanji zinthu zawo zitatayika? (b) Kodi zimene anachita zikutiuza chiyani za mmene ankaonera chinthu chotayikacho?
8 M’mafanizo aŵiriwa zinthu zinatayika, koma taonani mmene eni ake zinthuzo anachitira. Mbusayo sananene kuti: ‘Nkhosa imodzi ndi ya ntchito yanji popeza ndikadali nazo nkhosa 99? Ndi yosafunika nkhosayo.’ Ndipo mkaziyo sananene kuti: ‘N’kuvutikiranji chifukwa cha ndalama imodzi? Ndalama nayini zomwe ndili nazo n’zondikwanira.’ M’malo mwake, mbusa anafunafuna nkhosa yake yotayika ngati kuti anali ndi nkhosa imodzi yokhayo. Ndipo mkazi anakhudzidwa kwambiri ndi kutayika kwa ndalama yakeyo ngati kuti analibe ndalama zina. Pa zochitika ziŵirizi zinthu zotayikazo zinali za mtengo
wapatali kwa eni ake. Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?9. Kodi nkhaŵa imene mbusa ndi mkaziyo anali nayo ikusonyeza chiyani?
9 Taonani mawu omaliza a Yesu m’mafanizo aŵiriwa. Iye anati: “Kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima,” ndiponso “chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.” Chotero, nkhaŵa imene mbusa ndi mkazi anali nayo ikusonyeza pang’ono chabe, nkhaŵa imene Yehova ndi zolengedwa zake zakumwamba amakhala nayo. Monga mmene zotayika zinakhalirabe zamtengo wapatali kwa mbusa ndi mkaziyo, anthunso amene apatuka ndipo sakugwirizana ndi anthu a Mulungu amakhalabe amtengo wapatali pamaso pa Yehova. (Yeremiya 31:3) Anthu otero angakhale ofooka mwauzimu, koma sikuti apanduka. Ngakhale kuti ndi ofooka, mwina angakhale akutsatirabe zimene Yehova amafuna. (Salmo 119:176; Machitidwe 15:29) Chotero, mofanana ndi m’nthaŵi zakale, Yehova safulumira ‘kuwatayiratu pankhope pake.’—2 Mafumu 13:23.
10, 11. (a) Kodi tifunika kuwaona bwanji amene apatuka kuchoka mu mpingo? (b) Kodi tingawasonyeze bwanji kuti timawadera nkhaŵa, malinga ndi mafanizo aŵiri a Yesu?
10 Mofanana ndi Yehova ndiponso Yesu, ifenso timadera nkhaŵa kwambiri amene ali ofooka ndipo sakupezeka pampingo wachikristu. (Ezekieli 34:16; Luka 19:10) Timaona munthu wofooka monga nkhosa yotayika osati yosatheka kubwerera. Sitimanena kuti: ‘Nkuderanji nkhaŵa za munthu wofooka? Mpingo ukuyenda bwino kwambiri popanda iye.’ M’malo mwake, mofanana ndi Yehova , timaona anthu amene apatuka koma akufuna kubwerera kukhala ofunika.
11 Komano, tingasonyeze bwanji nkhaŵa yathu? Mafanizo aŵiri a Yesu akusonyeza kuti tingachite zimenezi (1) mwa kuyamba ife kuchitapo kanthu, (2) mwa kukhala okoma mtima, ndipo (3) mwa kuchita khama. Tiyeni tikambirane mbali zimenezi imodzi ndi imodzi.
Kuyamba Ife Kuchitapo Kanthu
12. Kodi mawu akuti ‘analondola yotayikayo’ akutiuza chiyani za maganizo a mbusayo?
12 M’fanizo loyamba mwa mafanizo aŵiri aja, Yesu akunena kuti mbusa ‘analondola yotayikayo.’ Mbusa akuyamba kuchitapo kanthu ndipo akuyesetsa mwakhama kuti apeza nkhosa yotayikayo. Mavuto, ngozi, ndiponso mtunda sizikum’lepheretsa. M’malo mwake, mbusa akulimbikira “kufikira aipeza.”—Luka 15:4.
13. Kodi amuna akale okhulupirika anachita bwanji ataona kuti ofooka afunika thandizo, ndipo tingatsanzire bwanji zitsanzo za m’Baibulo zimenezi?
13 Mofananamo, kuthandiza munthu amene afunika kum’limbikitsa nthaŵi zambiri kumafuna kuti yemwe ali wamphamvu ayambe kuchitapo kanthu. Anthu akale okhulupirika anadziŵa zimenezi. Mwachitsanzo, pamene Jonatani, mwana wa Mfumu Sauli, anaona kuti Davide bwenzi lake lapamtima anafunika kum’limbikitsa, iye “ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, nam’limbitsa dzanja lake mwa Mulungu.” (1 Samueli 23:15, 16) Patapita zaka mazana ambiri, Kazembe Nehemiya ataona kuti abale ake ena achiyuda anafooka, iyenso ‘ananyamuka’ ndipo anawalimbikitsa ‘kukumbukira Yehova.’ (Nehemiya 4:14) Ifenso masiku ano tidzafunika ‘kunyamuka,’ kuyamba ife kuchitapo kanthu, kuwalimbikitsa amene ali ofooka. Kodi ndani m’mpingo ayenera kuchita zimenezi?
14. Kodi ndani m’mpingo wachikristu ayenera kuthandiza ofooka?
Yesaya 35:3, 4; 1 Petro 5:1, 2) Komabe, taonani kuti malangizo a Paulo akuti “limbikitsani amantha mtima” ndiponso “chirikizani ofooka” sananene kwa akulu okha. M’malo mwake, Paulo ananena mawu ameneŵa ku ‘mpingo wonse wa Atesalonika.’ (1 Atesalonika 1:1; 5:14) Chotero kuthandiza anthu ofooka ndi udindo wa Akristu onse. Mofanana ndi mbusa wa mu fanizo lija, Mkristu aliyense ayenera kulimbikitsika ‘kulondola yotayikayo.’ Mwachionekere, zimenezi zimachitidwa bwino kwambiri mwa kugwirizana ndi akulu. Kodi mungachite china chake kuthandiza amene ali wofooka m’mpingo wanu?
14 Makamaka, akulu achikristu ali ndi udindo ‘wolimbitsa manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa mawondo a gwedegwede’ ndiponso ‘kunena kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musawope.’ (Khalani Okoma Mtima
15. N’chifukwa chiti chimene chiyenera kuti chinachititsa mbusayo kuchita zinthu mmene anachitiramo?
15 Kodi mbusa anachita chiyani pamene pamapeto pake anapeza nkhosa yotayikayo? “A[na]isenza pa mapewa ake.” (Luka 15:5) Ndi mfundotu yokhudza mtima komanso yosonyeza mmene anamvera! Nkhosayo iyenera kuti inali itayendayenda usana ndi usiku kwa masiku angapo m’madera osadziŵika ndiponso mwina inali pangozi yoti ikanagwidwa ndi mikango. (Yobu 38:39, 40) Mosakayikira nkhosayo inali yofooka kwambiri chifukwa chosadya moti sikanagonjetsa zopinga zimene ikanakumana nazo pobwerera ku khola. N’chifukwa chake, mbusa anaŵerama, ndipo mokoma mtima ananyamula nkhosayo, ndipo anabwerera nayo ku gulu la nkhosa kudutsa zopinga zonse. Kodi tingasonyeze bwanji kukoma mtima kumene mbusayu anali nako?
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kukoma mtima kumene mbusa anasonyeza kwa nkhosa yosochera?
16 Munthu amene sakugwirizana ndi mpingo angakhale wotopa kwambiri mwauzimu. Monga nkhosa imene yasiyana ndi mbusa, munthu wotero angakhale atayendayenda mopanda cholinga m’madera oipa a dzikoli. Popanda chitetezo cha gulu, mpingo wachikristu, amakhala pangozi yaikulu kwambiri yogwidwa ndi Mdyerekezi, amene “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Ndiponso, amakhala wofooka kwambiri chifukwa chosapeza chakudya chauzimu. Chotero, popanda wom’thandiza amakhala wofooka kwambiri moti sangagonjetse zopinga zomwe angakumane nazo paulendo wake wobwerera ku mpingo. N’chifukwa chake, tifunika kuŵerama, kunena kwake titero, ndipo mokoma mtima kunyamula wofookayo ndi kubwerera naye. (Agalatiya 6:2) Kodi tingachite bwanji zimenezi?
17. Kodi tingatsanzire bwanji mtumwi Paulo pokaona munthu wofooka?
17 Mtumwi Paulo anati: “Afooka ndani wosafooka inenso?” (2 Akorinto 11:29; 1 Akorinto 9:22) Paulo anali kuchitira anthu chifundo, ngakhalenso ofooka. Tifunika kukhala ndi chifundo chofananacho kwa anthu ofooka. Pokaona Mkristu wofooka mwauzimu, m’limbikitseni kuti ndi wofunika pamaso pa Yehova ndipo Mboni zinzake zimam’soŵa kwambiri. (1 Atesalonika 2:17) Muuzeni kuti zili zokonzeka kum’limbikitsa ndipo n’zofunitsitsa kukhala ‘mbale wobadwira kuti athandize pooneka tsoka.’ (Miyambo 17:17; Salmo 34:18) Mawu athu ochokera pansi pamtima, pang’onon’pang’ono ndiponso mokoma mtima adzam’limbikitsa munthuyo, mwina kufika pobwerera ku gulu la nkhosa. Kodi ndiyeno kenako tichite chiyani? Fanizo la mkazi ndi ndalama yotayika likutiuza chochita.
Khalani Akhama
18. (a) N’chifukwa chiyani mkazi wa m’fanizolo sanataye mtima? (b) Kodi n’kuyesetsa mwakhama kotani kumene mkaziyo anachita, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
18 Mkazi yemwe ndalama inam’tayika anadziŵa kuti n’zovuta kuipeza koma sanataye mtima. Ngati ndalamayo ikanagwera m’munda waukulu, woŵirira kapena m’nyanja yakuya ya matope, iye mwina akanataya mtima kuti ndalamayo siipezekanso. Komabe, podziŵa kuti ndalamayo inali penapake m’nyumba mwake, poti n’kuipeza, iye anayamba kuifunafuna bwinobwino komanso mwakhama. (Luka 15:8) Choyamba, iye anayatsa nyali kuti aunikire m’nyumba mwake mmene munali mdima. Ndiyeno anasesa ndi tsache lake, akuyembekezera kumva kulira kwa ndalama. Pomaliza, anafunafuna mosamalitsa malo onse m’nyumbamo mpaka nyaliyo inaunika ndalamayo. Mkaziyo anapindula ndi kuyesetsa kwake mwakhama.
19. Kodi tikuphunzira chiyani pankhani yothandiza anthu ofooka poona zimene mkazi wa m’fanizo la ndalama yotayika anachita?
19 Monga mmene mfundo imeneyi ya fanizolo ikutikumbutsira, sikuti sitingathe kusenza udindo wathu wa m’Malemba wa kuthandiza Akristu ofooka. Ndiponso, tikudziŵa kuti m’pofunika khama. Inde, mtumwi Paulo anati kwa akulu a ku Efeso: “Pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka.” (Machitidwe 20:35a) Kumbukirani kuti mkaziyo sanapeze ndalama mwa kuyang’ana mwachisawawa, patalipatali m’nyumba yake, kapena kungoyang’ana apa ndi apo. Ayi, anaipeza chifukwa chakuti anafunafuna mosamalitsa ‘kufikira anaipeza.’ Mofananamo, ngati tifuna kubweza munthu wofooka mwauzimu, tiyenera kuchita zimenezi mwakhama ndiponso mokhala ndi cholinga. Kodi tingachite chiyani?
20. N’chiyani chimene tingachite kuti tithandize ofooka?
20 Kodi tingathandize bwanji wofooka kuti akhale ndi chikhulupiriro ndiponso kuyamikira? Kum’phunzitsa Baibulo mwa kugwiritsira ntchito buku loyenera lachikristu kungakhale kuti n’kumene kukufunika. Ndithudi, kuphunzira Baibulo ndi munthu wofooka kumatichititsa kum’thandiza mokhazikika ndiponso mwa njira yosamalitsa. Woyang’anira utumiki ndi amene angaone bwino kuti ndani amene angapereke thandizo loyenerera. Iye anganene nkhani zimene akuona kuti zingaphunziridwe ndiponso buku limene lingakhale lothandiza *
kwambiri. Monga mmene mkazi wa m’fanizolo anagwiritsira ntchito zida zothandiza kuchita ntchito yake, chotero masiku ano tili ndi zida zotithandiza kuchita ntchito imene Mulungu watipatsa yothandiza ofooka. Zida zathu ziŵiri zatsopano kapena kuti mabuku, zidzatithandiza makamaka poyesa kuchita zimenezi. Mabukuwa ndiwo akuti, Worship the Only True God ndiponso Yandikirani kwa Yehova.21. Kodi kuthandiza ofooka kumapindulitsa bwanji onse?
21 Kuthandiza ofooka kumapindulitsa onse. Munthu amene akuthandizidwa amakhala wosangalala chifukwa choyanjananso ndi mabwenzi ake enieni. Timakhala ndi chimwemwe chochokera pansi pamtima chimene chimakhalapo kokha chifukwa cha kupatsa. (Luka 15:6, 9; Machitidwe 20:35b) Mpingo wonse umakhala ndi chikondi pamene aliyense m’mpingowo amasonyeza chikondi ndi chidwi kwa ena. Ndipo chofunika kwambiri, ulemu umapita kwa Abusa athu achikondi, Yehova ndi Yesu, pamene kufuna kwawo kuthandiza ofooka kukuonekera mwa atumiki awo padziko lapansi. (Salmo 72:12-14; Mateyu 11:28-30; 1 Akorinto 11:1; Aefeso 5:1) Chotero, tili ndi zifukwa zabwino zopitiriza ‘kukondana wina ndi mnzake.’
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungafotokoze?
• N’chifukwa chiyani ife tonse tifunika kusonyeza chikondi?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza chikondi kwa ofooka?
• Kodi mafanizo a nkhosa ndi ndalama zotayika akutiphunzitsa chiyani?
• Kodi tingachite chiyani kuti tithandize munthu wofooka?
[Mafunso]
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Pothandiza ofooka, timayamba ndife kuchitapo kanthu ndipo timakhala okoma mtima komanso akhama
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kuthandiza ofooka kumapindulitsa onse