Kuona Mtima N’kwabwino, Koma Kodi N’kokwanira?
Kuona Mtima N’kwabwino, Koma Kodi N’kokwanira?
KODI kuona mtima n’kwabwinodi pamoyo wathu watsiku ndi tsiku? Mawu akuti “kuona mtima” amatanthauza kusachita chinyengo; kunena zoona; kulunjika; kuchita zenizeni. Mwachionekere, khalidwe limeneli n’lothandiza polimbikitsa kukhala bwino ndi anthu ena. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Mverani m’zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi [“moona mtima,” NW], akuopa Ambuye.” (Akolose 3:22) Kodi ndani amene sangasangalale kukhala ndi wantchito woona mtima chonchi? Masiku ano, anthu oona mtima amakhala ndi mwayi waukulu wopeza ntchito ndiponso wokhalitsa pantchito.
Komabe, chimene chimapangitsa kuona mtima kukhala kwabwino kwambiri, ndi mmene kumakhudzira unansi wathu ndi Mulungu. Mulungu anali kudalitsa Aisrayeli akale akatsatira malamulo ndiponso kuchita maphwando mosamalitsa. Pamene Paulo anali kukamba zoti mpingo uyenera kukhala woyera, anapempha Akristu kuti: “Tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.” (1 Akorinto 5:8) Kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu, kuona mtima n’kwabwino komanso n’kofunika. Komabe, dziŵani kuti kuona mtima kokha sikokwanira. Kuyenera kuyendera limodzi ndi choonadi.
Anthu amene anapanga ndiponso amene anakwera sitima yapamadzi ya Titanic, ayenera kuti anakhulupirira moona mtima kuti sitimayi singamire. Koma, paulendo wake woyamba mu chaka cha 1912, inawomba madzi oundana olimba ngati mwala ndipo anthu 1,517 anafa. Ayuda ena a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ayenera kuti ankakhulupirira moona mtima njira yawo yolambirira Mulungu, koma changu chawo sichinali ‘monga mwa chidziŵitso.’ (Aroma 10:2) Kuti Mulungu ativomereze, zimene timazikhulupirira ndi mtima wonse ziyenera kuchokera pa mfundo zolondola. Mboni za Yehova za m’dera lanu zidzasangalala kukuthandizani kupenda zimene zimafunika potumikira Mulungu moona mtima ndi m’choonadi.