Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mubale Chipatso Chambiri”

“Mubale Chipatso Chambiri”

“Mubale Chipatso Chambiri”

“Mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.”​—YOHANE 15:8.

1. (a) Kodi ndi mfundo iti yofunika kuti munthu akhale wophunzira imene Yesu anauza atumwi ake? (b) Kodi ndi funso lotani limene tiyenera kudzifunsa?

UNALI usiku woti imfa yake ichitika maŵa pamene Yesu anali atapeza nthaŵi yokwanira yolimbikitsa atumwi ake mwa kulankhula nawo mwachikondi ndiponso momasuka. Pofika nthaŵi imeneyi, pakati pausiku panali patadutsa, koma Yesu anapitirizabe kulankhula chifukwa chokonda mabwenzi ake apamtima. Ndiyeno, makambirano ali m’kati, iye anawakumbutsa mfundo inanso imene anafunika kukwaniritsa kuti akhalebe ophunzira ake. Iye anati: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.” (Yohane 15:8) Kodi ifeyo masiku ano timakwaniritsa mfundo imeneyi yofunika kuti tikhale ophunzira? Kodi ‘kubala chipatso chambiri’ kumatanthauzanji? Kuti tidziŵe yankho, tiyeni tipende makambirano a usiku umenewo.

2. Kodi ndi fanizo lotani lonena za chipatso limene Yesu anafotokoza usiku woti imfa yake ichitika maŵa?

2 Malangizo akuti tibale chipatso ali mbali ya fanizo limene Yesu anauza atumwi ake. Iye anati: “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam’munda. Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mawu amene ndalankhula ndi inu. Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: . . . Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga. Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m’chikondi changa. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa.”​—Yohane 15:1-10.

3. Kodi otsatira a Yesu ayenera kuchita chiyani kuti abale chipatso?

3 Mu fanizo ili Yehova ndiye Wam’munda, Yesu ndiye mpesa, ndipo atumwi omwe Yesu ankalankhula nawowo ndiwo nthambi. Malinga ngati atumwi akanalimbikira “kukhala mwa” Yesu, akanadzabala chipatso. Ndiyeno Yesu anafotokoza mmene atumwi akanathera kukhalabe mwa iye, kumene kuli kofunika kwambiri. Iye anati: “Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa.” Patapita nthaŵi, mtumwi Yohane analemba mawu ofanana ndi ameneŵa kwa Akristu anzake. Iye anati: “Munthu amene asunga malamulo [a Kristu] akhala mwa iye.” * (1 Yohane 2:24; 3:24) Chotero, mwa kusunga malamulo a Kristu, otsatira ake amakhala mwa iye, ndipo kukhala kwawo mwa iye kumeneku kumawachititsa kubala chipatso. Kodi chipatso chimene tifunika kubala chiyenera kukhala chotani?

Mwayi Wopita Patsogolo

4. Kodi tingaphunzire chiyani pamfundo yakuti Yehova ‘anachotsa’ nthambi iliyonse yosabala chipatso?

4 Mu fanizo la mpesa, Yehova ‘anachotsa’ kapena kuti anadula nthambi imene sinali kubala chipatso. Kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti ophunzira onse ayenera kubala chipatso komanso kuti onse angathe kubala chipatso, mosasamala kanthu za mmene moyo wawo ulili kapenanso zinthu zimene sangathe kuchita. Ndithudi, ‘kuchotsa’ kapena kuona wophunzira wa Kristu kuti sakuyenererera chifukwa cholephera kuchita chinthu chimene iye sangathe kungakhale kusemphana ndi njira za Yehova zachikondi.​—Salmo 103:14; Akolose 3:23; 1 Yohane 5:3.

5. (a) Kodi fanizo la Yesu likusonyeza bwanji kuti tingapite patsogolo pakukhala wobala chipatso? (b) Kodi ndi mitundu iwiri iti ya chipatso imene tikambirane?

5 Fanizo la mpesa la Yesu likusonyezanso kuti tiyenera kupeza mpata wopita patsogolo m’zochita zathu monga wophunzira malinga ndi mmene moyo wathu ulili. Taonani mmene Yesu ananenera. Iye anati: ‘Nthambi iliyonse ya mwa ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.’ (Yohane 15:2) Cha kumapeto kwa fanizolo, Yesu anauza otsatira ake kubala ‘chipatso chambiri.’ (Vesi 8) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Monga ophunzira, sitiyenera kukhala amphwayi. (Chivumbulutso 3:14, 15, 19) M’malo mwake, tiyenera kupeza njira zopitira patsogolo pobala chipatso. Kodi ndi chipatso cha mtundu wotani chimene tiyenera kuyesetsa kubala chochuluka kwambiri? Chipatso chimenechi chili m’mitundu iŵiri (1) “chipatso cha mzimu” ndi (2) chipatso cha Ufumu.​—Agalatiya 5:22, 23; Mateyu 24:14.

Chipatso cha Makhalidwe Achikristu

6. Kodi Yesu Kristu anagogomezera bwanji kufunika kwa chipatso cha mzimu choyamba kutchulidwa?

6 Chipatso choyamba pa “chipatso cha mzimu” ndi chikondi. Mzimu woyera wa Mulungu umabala chikondi mwa Akristu, chifukwa amamvera lamulo limene Yesu analipereka atatsala pang’ono kusimba fanizo la mpesa wobala chipatso. Iye anauza atumwi ake kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Ndipotu, pakukambirana nawo kwake konse usiku womaliza kukhala ndi moyo padziko lapansi, Yesu mobwerezabwereza anakumbutsa atumwi kufunika kwa kusonyeza khalidwe lachikondi.​—Yohane 14:15, 21, 23, 24; 15:12, 13, 17.

7. Kodi mtumwi Petro anasonyeza bwanji kuti kubala chipatso n’kogwirizana ndi kusonyeza makhalidwe ofanana ndi amene Kristu anali nawo?

7 Petro yemwe analipo usikuwo, anadziŵa kuti chikondi chofanana ndi cha Kristu ndiponso makhalidwe ena ofanana ndi ameneŵa ayenera kuonekera pa ophunzira oona a Kristu. Patapita zaka, Petro analimbikitsa Akristu kukhala ndi makhalidwe monga kudziletsa, chikondi cha pa abale ndiponso chikondi. Iye anawonjezera kuti kukhala ndi zimenezi kudzatichititsa ‘kusakhala aulesi kapena opanda zipatso.’ (2 Petro 1:5-8) Mulimonse mmene moyo wathu ungakhalire, kusonyeza chipatso cha mzimu n’kotheka. Chotero, tiyeni tiyesetse kusonyeza mochulukirako koposa chikondi, chifundo, chifatso, ndi makhalidwe ena amene Kristu anasonyeza chifukwa “palibe lamulo loletsa zimenezi” kapena malire. (Agalatiya 5:23, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Ndithudi, tiyeni tibale ‘chipatso chochuluka.’

Kubala Chipatso cha Ufumu

8. (a) Kodi chipatso cha mzimu ndi cha Ufumu zimagwirizana bwanji? (b) Kodi ndi funso lotani limene tifunika kuganizira?

8 Zipatso zooneka bwino ndi zokoma zimakongoletsa mpesa. Komabe, kufunika kwa zipatso zimenezi kumaposa pakukongoletsa chabe. Zipatso ndi zofunikanso pochulukitsa mpesa mwa mbewu zake. Mofananamo, chipatso cha mzimu chimachita zambiri kuposa pakukongoletsa chabe umunthu wathu wachikristu. Makhalidwe monga chikondi ndi chikhulupiriro zimatichititsanso kufalitsa uthenga wa Ufumu wofanana ndi mbewu umene ukupezeka m’Mawu a Mulungu. Taonani mmene mtumwi Paulo anagogomezera kugwirizana kofunika kumeneku. Iye anati: ‘Ifenso tili ndi chikhulupiriro, [mbali ya chipatso cha mzimu] chifukwa chake tilankhula.’ (2 Akorinto 4:13) Paulo anawonjezera kuti mwa njira imeneyi, ‘timapereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo,’ mtundu wachiŵiri wa chipatso chimene tiyenera kusonyeza. (Ahebri 13:15) Kodi tili ndi mipata yabwino pamoyo wathu yobala chipatso chochuluka, inde kubala “chipatso chambiri,” monga olengeza Ufumu wa Mulungu?

9. Kodi kubala chipatso n’kofanana ndi kupanga ophunzira? Fotokozani?

9 Kuti tiyankhe molondola, choyamba tifunika kudziŵa chimene chimapanga chipatso cha Ufumu. Kodi kungakhale kolondola kunena kuti kubala chipatso kumatanthauza kupanga ophunzira? (Mateyu 28:19) Kodi chipatso chimene tingabale, mokulira chimaimira anthu amene timathandiza kukhala olambira Yehova obatizidwa? Ayi. Zitakhala choncho, zingakhale zogwetsa ulesi kwambiri kwa Mboni zokondeka zimene zakhala zikulalikira uthenga wa Ufumu mokhulupirika kwa zaka zambiri m’magawo mmene anthu ambiri salabadira. Inde, ngati chipatso cha Ufumu chimene timabala chimaimiridwa kokha ndi ophunzira atsopano, Mboni zogwira ntchito molimbika zotero zingakhale monga nthambi zosabala za mu fanizo la Yesu. Komano, si mmene zilili. Chotero, kodi chipatso chofunika cha Ufumu cha utumiki wathu n’chiyani?

Kubala Zipatso mwa Kufalitsa Mbewu za Ufumu

10. Kodi fanizo la Yesu la wofesa ndiponso nthaka zosiyanasiyana, limasonyeza bwanji zimene chipatso cha Ufumu chili ndi zimene sichili?

10 Fanizo la Yesu la wofesa ndiponso nthaka zosiyanasiyana zimapereka yankho lolimbikitsa kwa anthu amene amalalikira m’magawo obala zipatso pang’ono. Yesu anati mbewu ndi uthenga wa Ufumu wopezeka m’Mawu a Mulungu ndiponso nthaka imaimira mtima wa munthu wophiphiritsa. Mbewu zina “zinagwa panthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso.” (Luka 8:8) Zipatso zotani? Chabwino, tirigu akamera ndi kukula, amabala zipatso, osati timapesi ta tirigu, koma mbewu zatsopano. Mofananamo, chipatso chimene Mkristu amabala ndicho mbewu zatsopano za Ufumu, osati kwenikweni ophunzira atsopano.

11. Kodi chipatso cha Ufumu chingatanthauziridwe bwanji?

11 Chotero, pamenepa chipatso sichili ophunzira atsopano kapena makhalidwe abwino achikristu. Popeza mbewu zofesedwa ndi mawu a Ufumu, chipatso chiyenera kukhala mbewu zambiri za mbewu yofesedwayo. Chotero, pamenepa kubala chipatso kukutanthauza kulankhula za Ufumu. (Mateyu 24:14) Kodi kubala chipatso cha Ufumu kumeneku, kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu, n’kotheka, mosasamala kanthu za mmene moyo wathu ulili? Inde, n’kotheka! Mu fanizo limeneli, Yesu anafotokoza chifukwa chake.

Kupereka Zimene Tingathe Kuti Mulungu Alemekezedwe

12. Kodi Akristu onse angathe kubala chipatso cha Ufumu? Fotokozani.

12 Yesu anati: ‘Amene afesedwa pa nthaka yabwino . . . azifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.’ (Mateyu 13:23) Mbewu zofesedwa m’munda zingabale mosiyanasiyana malinga ndi mmene zinthu zilili. Mofananamo, zimene tingachite polalikira uthenga wabwino zingakhale zosiyanasiyana malinga ndi mmene moyo wathu ulili, ndipo Yesu anasonyeza kuti amadziŵa zimenezi. Anthu ena angakhale ndi mipata yambiri; ena angakhale ndi thanzi labwino ndi nyonga zambiri. Chotero, zimene tingathe kuchita zingakhale zambiri kapena zochepa poyerekeza ndi zimene ena amachita, koma malinga ngati zimenezo ndi zimene ife tingathe kuchita, Yehova amasangalala. (Agalatiya 6:4) Ngakhale ngati ukalamba kapena kudwaladwala kumatilepheretsa kuchita zambiri potenga nawo mbali m’ntchito yolalikira, Atate wathu wachifundo, Yehova, mosakayikira amationa monga mmodzi wa anthu amene ‘akubala chipatso chambiri.’ Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti timam’patsa ‘zonse zimene tili nazo,’ utumiki wathu wa mtima wonse. *​—Marko 12:43, 44; Luka 10:27.

13. (a) N’chiyani chomwe chili chifukwa chachikulu choti ‘tipitirizebe’ kubala chipatso cha Ufumu? (b) Kodi n’chiyani chidzatithandiza kuti tibale chipatso m’magawo mmene anthu ambiri salabadira? (Onani bokosi patsamba 21.)

13 Kaya tingathe kubala chipatso cha Ufumu mpaka kufika pati, tidzalimbikitsika ‘[kupitirizabe] kubala chipatso,’ tikamakumbukira chifukwa chake tikuchita zimenezi. (Yohane 15:16) Yesu anatchula chifukwa chachikulu. Iye anati: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri.” (Yohane 15:8) Inde, ntchito yathu yolalikira imayeretsa dzina la Yehova pakati pa anthu onse. (Salmo 109:30) Honor, Mboni yokhulupirika yomwe ili ndi zaka pafupifupi 75, inati: “Ngakhale m’magawo mmene anthu ambiri salabadira, ndi mwayi kuimira Wam’mwambamwamba.” Atafunsidwa chifukwa chake amapitiriza kulalikira m’gawo lake ngakhale kuti anthu ambiri salabadira, Claudio, yemwe wakhala Mboni yachangu kuyambira mu 1974, anagwira mawu a pa Yohane 4:34, pamene timaŵerenga mawu a Yesu akuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” Claudio anawonjezera kuti: “Mofanana ndi Yesu, sindifuna chabe kuyamba ntchitoyi koma ndifunanso kumaliza ntchito yanga monga wolengeza Ufumu.” (Yohane 17:4) Mboni za Yehova padziko lonse zili ndi malingaliro ofanana ndi ameneŵa.​—Onani bokosi lakuti “Mmene ‘Tingabalire Zipatso Mopirira’” patsamba 21.

Kulalikira Ndiponso Kuphunzitsa

14. (a) Kodi ntchito ya Yohane Mbatizi ndi Yesu inali ndi zolinga ziŵiri ziti? (b) Kodi mungafotokoze bwanji ntchito ya Akristu masiku ano?

14 Wolengeza Ufumu woyamba kutchulidwa mu Mauthenga Abwino ndi Yohane Mbatizi. (Mateyu 3:1, 2; Luka 3:18) Cholinga chake chachikulu chinali ‘kuchita umboni,’ ndipo anachita zimenezi ndi chikhulupiriro chonse ndiponso ndi chiyembekezo chakuti “onse akakhulupirire.” (Yohane 1:6, 7) Ndithudi, anthu ena amene Yohane anawalalikira anakhala ophunzira a Kristu. (Yohane 1:35-37) Chotero, Yohane anali kulalikira komanso kupanga ophunzira. Yesu nayenso anali kulalikira ndi kuphunzitsa. (Mateyu 4:23; 11:1) N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti, Yesu analamula otsatira ake kulalikira uthenga wa Ufumu ndiponso kuthandiza anthu amene aulandira kukhala ophunzira ake. (Mateyu 28:19, 20) Chotero ntchito yathu ndi yambali ziŵiri, kulalikira ndi kuphunzitsa.

15. Kodi kulabadira ntchito yolalikira ya m’zaka zoyambirira za Nyengo Yathu Ino kumene ena anasonyeza kukufanana bwanji ndi masiku ano?

15 Anthu a m’zaka zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, amene anamvetsera Paulo akulalikira ndi kuphunzitsa, “ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvera.” (Machitidwe 28:24) Masiku ano, ndi mmenenso anthu amachitira. N’zomvetsa chisoni kuti mbewu za Ufumu zambiri zimagwera panthaka yosabala. Ngakhale zili chonchi, mbewu zina zimagwerabe panthaka yabwino, zimakhala ndi mizu ndipo zimamera, monga mmene Yesu ananeneratu. Ndipotu, padziko lonse, mlungu uliwonse pachaka avareji ya anthu oposa 5,000 amakhala ophunzira oona a Kristu. Ophunzira atsopano ameneŵa “amamvera zonenedwazo,” ngakhale kuti ena ambiri satero. Kodi chinathandiza n’chiyani kuti mtima wawo umvetsere uthenga wa Ufumu? Nthaŵi zambiri chidwi chimene Mboni zimakhala nawo, kuthirira mbewu imene yafesedwa kumene, kunena kwake titero, chimathandiza. (1 Akorinto 3:6) Taonani zitsanzo ziŵiri chabe mwa zitsanzo zambiri.

Kuwasonyeza Chidwi Kumathandiza

16, 17. N’chifukwa chiyani n’kofunika kukhala ndi chidwi kwa anthu amene timakumana nawo m’utumiki wathu?

16 Karolien, mtsikana wa Mboni wa ku Belgium, anafika panyumba ya mayi wina wachikulire amene analibe chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Popeza mkono wa mayiyo unali wokutidwa ndi bandeji, Karolien ndi bwenzi lake anapempha kum’thandiza, koma mayiyo anakana. Patatha masiku aŵiri, Mbonizo zinabwerera ku nyumba ya mayi uja ndipo zinam’funsa kuti akupeza bwanji. Karolien anati: “Zimenezi zinathandiza kwambiri. Mkaziyo anadabwa kwambiri kuona kuti tinachita chidwi kwambiri ndi iye. Anatiitanira kuloŵa m’nyumba yake, ndipo tinayamba kuphunzira naye Baibulo.”

17 Sandi, Mboni ya ku United States, amakhalanso ndi chidwi kwa anthu amene amawalalikira. Iye amaona zilengezo zakubadwa kwa ana m’nyuzipepala ya kudera la kwawo, ndiyeno amapita kwa anthu amene angobereka kumene ndi buku lakuti, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Popeza mayi amene wabereka kumene nthaŵi zambiri amangokhala panyumba ndipo amasangalala kusonyeza mwana wake kwa anthu obwera kudzamuona, nthaŵi zambiri pamakhala kukambirana. Sandi anati: “Ndimakambirana ndi makolo za kufunika kogwirizana kwambiri ndi mwana wobadwa kumeneyo mwa kuŵerenga. Kenako ndimafotokoza mavuto akulera mwana m’dzikoli masiku ano.” Chifukwa cha kufikira anthu mwa njira imeneyi, posachedwapa, mayi ndi ana asanu ndi mmodzi anayamba kutumikira Yehova. Kuyamba ifeyo kuchitapo kanthu ndi kusonyeza chidwi kungathandize kuti pakhale zotsatirapo zosangalatsa zofanana ndi zimenezi m’utumiki wathu.

18. (a) Kodi n’chifukwa chiyani n’kotheka kwa ife tonse kukwaniritsa mfundo ‘yobala chipatso chambiri’? (b) Kodi ndi mfundo zitatu ziti zofunika kuti munthu akhale wophunzira zomwe zatchulidwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane zimene mwatsimikiza mtima kuzikwaniritsa?

18 N’zolimbikitsatu kudziŵa kuti n’kotheka kukwaniritsa mfundo yakuti “mubale chipatso chambiri”! Kaya ndife achichepere kapena achikulire, kaya tili ndi thanzi labwino kapena timadwaladwala, kaya timalalikira m’magawo mmene anthu ambiri amalabadira kapena mmene ambiri satero, ife tonse tingathe kubala chipatso chambiri. Motani? Mwa kusonyeza chipatso cha mzimu mochulukirako koposa ndiponso mwa kufalitsa uthenga wa Ufumu wa Mulungu mmene ife tingathere. Ndiponso, tiyesetse ‘kukhalabe m’mawu a Yesu’ ndi ‘kukondana wina ndi mnzake.’ Inde, mwa kukwaniritsa mfundo zitatu zofunika kuti tikhale ophunzira zomwe zatchulidwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane, timatsimikiza kuti ‘tili akuphunzira [a Kristu] ndithu.’​—Yohane 8:31; 13:35.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Ngakhale kuti nthambi za mpesa mu fanizo zimaimira atumwi a Yesu ndi Akristu ena amene adzakhala ndi malo mu Ufumu wa Mulungu wakumwamba, fanizoli lili ndi choonadi chimene onse amene ali otsatira a Kristu masiku ano angapindule nacho.​—Yohane 3:16; 10:16.

^ ndime 12 Anthu amene amangokhala panyumba chifukwa cha kukalamba kapena kudwala angathe kulalikira mwakugwiritsira ntchito makalata kapena angalalikire pa telefoni ngati n’kololeka, kapenanso mwina angagaŵire uthenga anthu amene amabwera kudzawaona.

^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Mafunso Obwereramo

• Kodi ndi chipatso cha mtundu wotani chimene tiyenera kubala chochuluka kwambiri?

• N’chifukwa chiyani cholinga cha ‘kubala chipatso chambiri’ n’chotheka kuchikwaniritsa?

• Kodi ndi mfundo zitatu ziti zofunika kuti munthu akhale wophunzira zomwe zatchulidwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane zimene takambirana?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 21]

MMENE ‘TINGABALIRE ZIPATSO MOPIRIRA’

KODI n’chiyani chimakuthandizani kupitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu mokhulupirika m’magawo amene anthu ambiri salabadira? Nawa mayankho ena othandiza a funso limeneli.

“Kudziŵa kuti Yesu akutichirikiza kwambiri kumatilimbikitsa kukhala ndi maganizo oti zinthu zidzayenda bwino ndiponso kulimbikira, mulimonse mmene anthu angachitire m’gawo.”​—Anatero Harry, wa zaka 72; anabatizidwa mu 1946.

“Nthaŵi zonse lemba la 2 Akorinto 2:17 limandilimbikitsa. Limanena kuti timatenga nawo mbali mu utumiki ‘pamaso pa Mulungu, tili limodzi ndi Kristu.’ (NW) Nthaŵi imene ndili mu utumiki, ndimasangalala kukhala ndi mabwenzi anga apamtima.”​—Anatero Claudio, wa zaka 43; anabatizidwa mu 1974.

“Kunena zoona, ntchito yolalikira imandivuta. Komabe, ndimaona kuti mawu opezeka pa Salmo 18:29 akuti: ‘Mwa Mulungu wanga ndilumpha linga,’ ndi oona.”​—Anatero Gerard, wa zaka 79; anabatizidwa mu 1955.

“Ndikaŵerenga lemba limodzi chabe mu utumiki, ndimasangalala kuti munthu wina mtima wake wapendedwa ndi Baibulo.”​—Anatero Eleanor, wa zaka 26; anabatizidwa mu 1989.

“Ndimayesa njira zosiyanasiyana pokambirana ndi anthu. Zilipo zambiri moti sindidzatha kuzigwiritsira ntchito zonse pazaka zamoyo wanga zomwe zatsala.”​—Anatero Paul, wa zaka 79; anabatizidwa mu 1940.

“Sindimakhumudwa ngati anthu akana. Ndimayesetsa kuwafikira mwaubwenzi, kulankhula nawo ndi kumvetsera malingaliro awo.”​—Anatero Daniel, wa zaka 75; anabatizidwa mu 1946.

“Ndakumanapo ndi anthu omwe angobatizidwa kumene amene anandiuza kuti ntchito yanga yolalikira inawathandiza kuti akhale Mboni. Ine ndisakudziŵa munthu wina panthaŵi ina anaphunzira nawo Baibulo ndipo anawathandiza kupita patsogolo. Zimandisangalatsa kudziŵa kuti utumiki wathu ndi ntchito yothandizana.”​—Anatero Joan, wa zaka 66; anabatizidwa mu 1954.

Kodi n’chiyani chimakuthandizani ‘kubala zipatso mopirira’?​—Luka 8:15.

[Zithunzi patsamba 20]

Mwa kusonyeza chipatso cha mzimu ndiponso mwa kulengeza uthenga wa Ufumu, timabala chipatso chambiri

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anauza atumwi ake kuti: “Mubale chipatso chambiri”?