Zimene Tingachite Kuti Tikhale ndi Maganizo Abwino pa Nkhani ya Ntchito
Zimene Tingachite Kuti Tikhale ndi Maganizo Abwino pa Nkhani ya Ntchito
M’DZIKO lino mmene nkhani ya zamalonda ikupanikiza kwambiri, mmene muli mpikisano wa wafawafa, ndiponso anthu akupanga zinthu zochuluka kwambiri, anthu ambiri sasangalala kupita kuntchito tsiku ndi tsiku. Komabe, tifunika kusangalala ndi ntchito yathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo Mulungu amasangalala ndi ntchito zake. Mwachitsanzo, poona zimene anachita pamapeto pa “masiku” asanu ndi limodzi, kapena kuti nyengo zazitali zisanu ndi imodzi zimene anali akulenga, Genesis 1:31 amati: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”
Mosakayika, kukonda ntchito kwa Yehova ndi chimodzi mwa zifukwa zimene iye amatchedwa “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Motero, kodi sizomveka kuti tikamutsanzira kwambiri ifenso tidzakhala achimwemwe? Pankhani imeneyi, Mfumu Solomo yakale ku Israyeli, imene inali yodziŵa bwino kumanga ndi kulinganiza zinthu, inalemba kuti: “Kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Mlaliki 3:13.
Masiku ano kukhala ndi maganizo abwino pankhani ya ntchito m’malo ogwirira ntchito amene zinthu sizichedwa kusinthasintha n’kovuta. Koma Yehova Mulungu amadalitsa anthu amene amamvera malangizo ake achikondi. (Salmo 119:99, 100) Anthu oterowo amakhala antchito ofunika ndiponso okhulupirika ndipo nthaŵi zambiri sachotsedwa ntchito. Iwo amaphunziranso kuona moyo wawo ndi ntchito yawo moganizira zinthu zauzimu osati mongoganizira chuma chokha. Zimenezi zimawathandiza kusankha zochita zanzeru pa moyo wawo ndi kuona kuti kukhala kwawo ndi chimwemwe ndiponso moyo wabwino sizingodalira ntchito yawo kapena misika ya ntchito yomwe nthaŵi zambiri ndi yosadalirika. (Mateyu 6:31-33; 1 Akorinto 2:14, 15) Zimawathandiza kukhala ndi maganizo abwino pankhani ya ntchito.
Onani Ntchito Monga Mmene Mulungu Amaionera
Anthu ambiri amagwira ntchito mopambanitsa, amaika ntchito patsogolo kuposa china chilichonse. Ena amangolakalaka kuti nthaŵi ithe aŵeruke azipita kunyumba. Kodi maganizo abwino a ntchito ndi ati? Baibulo limayankha kuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:6) Kugwira ntchito mopambanitsa kapena kwa nthaŵi yaitali kwambiri kungabwezere zinthu m’mbuyo, komwe ndi “kungosautsa mtima.” N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti tingawononge zinthu zimene zimathandiza kuti tisangalale kwambiri. Zimenezi ndizo kugwirizana ndi banja lathu ndiponso mabwenzi athu, moyo wathu wauzimu, thanzi lathu, ndiponso ngakhale utali wa moyo wathu. (1 Timoteo 6:9, 10) Maganizo abwino ndiwo kukhutira ndi zinthu zochepa koma tili ndi mtendere kusiyana ndi kugwira chintchito chachikulu koma tili ndi mavuto ndi chisoni.
Polimbikitsa maganizo amenewo, Baibulo silikunena kuti munthu akhale waulesi. (Miyambo 20:4) Ulesi umachititsa munthu kudziona kuti ndi wosafunika ndiponso anthu ena satilemekeza. Ndipo kuposa pamenepa, ulesi umawononga ubwenzi wathu ndi Mulungu. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti munthu amene safuna kugwira ntchito sayenera kudyera thukuta la ena. (2 Atesalonika 3:10) M’malo mwake, iye ayenera kusintha zochita zake ndi kugwira ntchito molimbika, ndipo motero angadzipezere zosoŵa m’njira yoyenera ndiponso kupezera zosoŵa anthu amene amadalira iye. Mwa kugwira ntchito molimbika, akhozanso kuthandiza anthu amene akufunikadi thandizo, ndipo zimenezi n’zimene Mawu a Mulungu amalimbikitsa.—Miyambo 21:25, 26; Aefeso 4:28.
Kuphunzira Kukonda Ntchito Kuyambira Paubwana
Kuzoloŵera kugwira bwino ntchito sikumangobwera kokha. Munthu amaphunzira ali mwana. N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa makolo kuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Kuwonjezera pa kupereka chitsanzo chabwino pogwira ntchito, makolo anzeru amayamba kuphunzitsa ana awo powapatsa ntchito zapakhomo zoyenerana ndi msinkhu wawo. Ngakhale kuti ana angaipidwe ndi ntchito zina, adzayamba kuona kuti ndi anthu ofunika m’banjalo, makamaka ngati mayi ndi bambo amayamikira anawo akagwira ntchito bwino. N’zomvetsa chisoni kuti makolo ena amachitira ana awo chilichonse, mwina chifukwa chowachitira chifundo molakwika. Makolo oterowo ayenera kuganizira lemba la Miyambo 29:21 limene limati: “Yemwe alera kapolo [kapena mwana] wake mwa ufulu [“mom’lekerera,” NW] kuyambira ubwana wake, pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala [“adzakhala mwana wosayamika,” NW].”
Makolo odziŵa bwino ntchito yawo amaganiziranso kwambiri maphunziro a ana awo, kuwalimbikitsa kuti azikaphunzira ndiponso kulimbikira kusukulu. Zimenezi zingapindulitse anawo m’tsogolo akadzayamba ntchito.
Sankhani Ntchito Mwanzeru
Ngakhale kuti Baibulo silitiuza ntchito imene tingasankhe, limatipatsa malangizo abwino kuti kupita kwathu patsogolo mwauzimu, kutumikira kwathu Mulungu, ndi maudindo ena ofunika zisadodometsedwe. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo . . . akuchita nalo dziko lapansi, [akhale] monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.” (1 Akorinto 7:29-31) Palibe chinthu chokhalitsa kapena chosasintha m’dongosolo la zinthu lino. Kuthera nthaŵi yathu yonse ndi mphamvu zathu zonse pa zimenezi kuli ngati kuika chuma cha moyo wathu wonse m’nyumba imene aimanga m’dera losefukira madzi. Kungakhaletu kuwononga chuma kopanda nzeru!
Mabaibulo ena amamasulira mawu akuti “osachititsa” kukhala “osatengeka nalo kwambiri.” (The Jerusalem Bible) Anthu anzeru saiwala mfundo yakuti nthaŵi ya dziko lino “yafupika” ndi kuti ‘kutengeka nalo kwambiri’ mosakayika kungagwiritse mwala ndi kuchititsa munthu kulilira kuutsi.—1 Yohane 2:15-17.
‘Mulungu Sadzakutayani Ndithu’
Yehova amadziŵa bwino zosoŵa zathu kuposanso mmene ifeyo tikudziŵira. Amadziŵanso nthaŵi imene tili m’kukwaniritsidwa kwa zolinga zake. Motero, amatikumbutsa kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye [Mulungu] anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Ndi mawu olimbikitsatu ameneŵa! Yesu potsanzira chikondi cha Mulungu ndi kudera kwake nkhaŵa anthu, anagwiritsa ntchito mbali yokulirapo ya Ulaliki wake wa pa Phiri kuphunzitsa ophunzira ake maganizo abwino pa nkhani ya ntchito ndiponso a zinthu zakuthupi.—Mateyu 6:19-33.
Mboni za Yehova zimayesetsa kumvera ziphunzitso zimenezo. Mwachitsanzo, pamene bwana anauza wantchito wina yemwe ndi Mboni amene amagwira ntchito ya zamagetsi kuti nthaŵi zonse azigwira ovataimu, wantchitoyo anakana. Chifukwa chiyani? Chifukwa sankafuna kuti ntchito yakeyo isokoneze nthaŵi imene ankaigwiritsa ntchito kukhala ndi banja lake kapena pa zinthu zauzimu. Popeza anali wantchito wabwino kwambiri ndiponso wokhulupirika, bwana wakeyo analemekeza maganizo ake. Inde, sikuti nthaŵi zonse zinthu zidzayenda choncho, ndipo mwina munthu angafunikire kufufuza ntchito kwina kuti azitha kuchita mbali zonse. Komabe, amene akhulupirira kwambiri Yehova nthaŵi zambiri amaona kuti makhalidwe awo abwino ndiponso maganizo awo pa nkhani ya ntchito amachititsa abwana awo kuwakonda.—Miyambo 3:5, 6.
Nthaŵi Imene Ntchito Zonse Zidzakhala Zopindulitsa
M’dongosolo la zinthu lino lopanda ungwiro, padzakhalabe mavuto ndiponso kusatsimikizirika
kwa ntchito ndi mwayi wopeza ntchito. Ndipotu, zinthu zingaipireipire pamene dziko likuwonjezeka kusakhazikika ndiponso chuma chikusinthasintha kapena kusokonezeka kumene. Koma zimenezi n’zanthaŵi yochepa chabe. Posachedwapa, palibe amene adzasoŵa ntchito. Ndiponso, ntchito zonse zidzakhala zogwira mtima ndi zopindulitsa. Kodi zidzatheka bwanji zimenezo? N’chiyani chidzasinthitsa zinthu motero?Yehova ananeneratu za nthaŵi imeneyo kudzera mwa mneneri wake Yesaya. Anati: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” (Yesaya 65:17) Iye anali kunena za boma lake latsopano, limene lidzakhaladi ndi anthu atsopano osiyana kwambiri ndi anthu amene alipo pakalipano.—Danieli 2:44.
Pofotokoza mmene anthu adzakhalira ndi kugwira ntchito nthaŵi imeneyo, ulosiwo unapitiriza kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.”—Yesaya 65:21-23.
Dziko latsopano la Mulungu limenelo lidzakhaladi losiyana kwambiri ndi limene lilipoli. Kodi simukufuna kudzakhala m’dziko limenelo, limene ‘simudzagwira ntchito mwachabe’ m’malo mwake mudzasangalala ndi “zipatso” za ntchito yanu? Komano, onani kuti amene adzasangalala ndi madalitso amenewo “ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova.” Inu mungakhale mmodzi mwa “odalitsidwa” amenewo mwa kuphunzira za Yehova ndi kuchita zimene iye amafuna. Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani kudziŵa zinthu zimenezi zimene zingakuthandizeni kupeza moyo. Zidzakuthandizani mwa kuphunzira nanu Mawu a Mulungu, Baibulo, mwadongosolo.
[Bokosi patsamba 6]
“ANTHU AMBIRI AMAZIFUNA”
Baibulo limati: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.” (Akolose 3:23) Mwachidziŵikire, munthu amene mfundo yabwino imeneyi imamutsogolera mmene amaonera ntchito, anthu ambiri adzafuna kumulemba ntchito. Chifukwa cha zimenezi, J. J. Luna m’buku lake lakuti How to be Invisible, analangiza anthu amene angafune kulemba ena ntchito kuti azifufuza anthu achangu a m’magulu ena ake a chipembedzo, koma anawonjezera kuti: “Kunena zoona, nthaŵi zambiri timaona kuti anthu amene tingawalembe ntchito ndi Mboni [za Yehova].” Zina mwa zifukwa zimene anapereka n’zakuti Mboni zimadziŵika bwino kuti n’zoona mtima, ndipo chifukwa cha zimenezi “anthu ambiri amazifuna” pa ntchito zosiyanasiyana.
[Zithunzi patsamba 5]
Kugwira ntchito komanso kukhala ndi nthaŵi yochita zinthu zauzimu ndiponso kusangalala zimabweretsa chimwemwe