Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani pa Yesaya 30:21 pamati mawu a Yehova achokera “kumbuyo kwa iwe,” popeza vesi lam’mbuyo limamuika Yehova patsogolo ponena kuti,“Maso ako adzaona aphunzitsi ako [“Mlangizi wako Wamkulu,” NW]”?

Pa Yesaya 30:20, 21 pamati: “Aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako [“Mlangizi wako Wamkulu,”]; ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.”

Munthu woŵerenga akalitenga lembali momwe lilili, amaona Yehova, Mlangizi Wamkulu, kutsogolo kwake koma amamva mawu Ake kuchokera kumbuyo. Koma, mawu ameneŵa ndi ophiphiritsira ndipo ndi mmene afunika kuwatengera.

Zimene zimabwera m’maganizo pa mawu ophiphiritsira a mu vesi 20 ndi a mnyamata amene akusamalira mbuye wake, amene ali wokonzeka nthaŵi zonse kuchita zimene mbuye wake akunena. Mofanana ndi mnyamata amene akuyang’ana mwatcheru dzanja la mbuye wake kuti azindikire ngati akufuna chinachake, anthu a Yehova masiku ano amaika maganizo awo pa malangizo a m’Baibulo amene Yehova amapereka pang’onopang’ono kudzera mu gulu lake la padziko lapansi. (Salmo 123:1, 2) Inde, amachita zimene amawalangiza, amakhala tcheru ndi chilichonse chimene Yehova amawasonyeza mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mateyu 24:45-47.

Ndiyeno, kodi tingati mawu amene atumiki ake amawamva kumbuyo ndi chiyani? N’koyenera kunena kuti mawu ochokera kumbuyo ndi mawu a Mulungu akale amene analankhula kudzera m’Mawu ake olembedwa amene amamveketsedwa bwino kudzera mwa “mdindo [wake] wokhulupirika.” (Luka 12:42) Atumiki a Mulungu a masiku ano amamva mawu ake mwa kuphunzira mwakhama Baibulo ndiponso mwa kutsatira mfundo zake pa moyo wawo mothandizidwa ndi mabuku amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” “mdindo wokhulupirika,” amapanga. Mwa kudalira ndiponso kumvetsera kwambiri malangizo a panthaŵi yake amene Mlangizi Wamkulu amapereka ndiponso mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, amene analembedwa zaka zambiri zapitazo, atumiki ake mophiphiritsa amamuona kutsogolo kwawo ndipo amamva mawu ake kumbuyo kwawo.​—Aroma 15:4.