Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Anthu Amakhalira pa Msasa wa Anthu Othaŵa Kwawo

Mmene Anthu Amakhalira pa Msasa wa Anthu Othaŵa Kwawo

Mmene Anthu Amakhalira pa Msasa wa Anthu Othaŵa Kwawo

KODI n’chiyani chimabwera m’maganizo anu mukamva mawu akuti “msasa wa anthu othaŵa kwawo”? Kodi munayamba mwafika pamsasa wa anthu othaŵa kwawo? Kodi umaoneka bwanji kwenikweni?

Pamene nkhaniyi inkalembedwa, misasa ya anthu othaŵa kwawo yokwana 13 inali itakhazikitsidwa ku madzulo kwa Tanzania. Anthu pafupifupi 500,000 othaŵa kwawo chifukwa cha nkhondo ya pachiŵeniŵeni ochokera kumayiko ena a m’Africa anali kuthandizidwa ndi boma la Tanzania mogwirizana ndi bungwe la United Nations loona za anthu othaŵa kwawo la UNHCR. Kodi anthu amakhala bwanji pamsasapo?

Kufika pa Msasawo

Mtsikana wotchedwa Kandida anafotokoza zimene zinachitika pamene iye ndi achibale ake anafika pamsasa zaka zingapo zapitazi. Iye anati: “Anatipatsa khadi loonetsa polandira chakudya lomwe linali ndi nambala yotidziŵira. Ndipo banja lathu linauzidwa kukhala pamsasa wa othaŵa kwawo wa Nyarugusu. Kumeneko anatipatsa nambala ya malo ndiponso ya msewu. Anatisonyeza kodula mitengo ndiponso komweta udzu wogwiritsira ntchito pomanga nyumba yathu yaing’ono. Tinaumba zidina. A bungwe la UNHCR anatipatsa pepala la pulasitiki limene tinaika padenga. Inali ntchito yolemetsa kwambiri, koma tinasangalala pamene nyumba yathu yosalira zambiriyo inatha kumangidwa.”

Timagwiritsira ntchito khadi loonetsa polandira chakudya Lachitatu lililonse pakapita milungu iŵiri. Kandida anapitiriza kuti: “Inde, timakhala pamzera ku kantini kuti tilandire chakudya chimene a bungwe la UNHCR amatipatsa.”

Kodi chakudya cha munthu mmodzi patsiku lililonse chimakhala chotani?

“Aliyense amalandira makapu atatu a ufa, kapu imodzi ya nsawawa, ufa wa soya wolemera magalamu 20, masupuni aŵiri a mafuta ophikira ndiponso mchere wolemera magalamu 10. Nthaŵi zina timalandiranso mtanda umodzi wa sopo, umene timafunika kuugwiritsira ntchito mwezi wonse.”

Bwanji za madzi abwino? Kodi amapezeka? Mtsikana wina dzina lake Riziki anati: “Inde, madzi amawapopa kuchokera ku mitsinje yapafupi kudutsa m’mapaipi mpaka ku mathanki aakulu. Madzi amawathira mankhwala asanapopere ku malo ambiri otungirako madzi pamsasa uliwonse. Timayesetsabe kuphitsa madzi tisanawamwe kuti tisadwale. Nthaŵi zambiri timakhala otanganidwa kuyambira m’maŵa mpaka usiku kutunga madzi ndi kutchapa zovala zathu pamalo otungira madziwa. Patsiku timatunga madzi ongokwana ndowa imodzi ndi theka basi.”

Ngati mungadutse pamsasa umodzi muli pa galimoto, mungaone sukulu zamkaka, sukulu zapulaimale ndiponso sukulu zasekondale. Pamsasa pamakhalanso maphunziro a anthu akulu. Polisi ndiponso ofesi ya boma zomwe zili pafupi ndi msasa zimathandiza kuti pamsasa pakhale posungika ndi potetezeka. Mungaonenso msika waukulu wokhala ndi timasitolo tating’ono tambiri kumene anthuwo amakagula ndiwo zamasamba, zipatso, nsomba, nkhuku ndi zakudya zina. Anthu ena am’deralo amafika pamsikawo kudzachita malonda. Komano kodi othaŵa kwawowa amapeza kuti ndalama zogulira zinthu? Ena amalima kadimba ka ndiwo zamasamba ndipo amagulitsa masambawo kumsika. Ena amagulitsa ufa wawo wina kapena nsawawa zimene alandira, kuti apeze ndalama zogulira nyama kapena zipatso. Ndithudi, msasa ungaoneke monga mudzi waukulu osati msasa chabe. Sidzachilendo kuona anthu ena pamsika akuseka ndi kusangalala monga mmene akanachitira ku mayiko akwawo.

Ngati mwafika pachipatala, mmodzi mwa madokotala angakuuzeni kuti pamsasawo pali zipatala zazing’ono zingapo kumene matenda aang’ono amachiritsidwa; zogwa mwadzidzidzi ndiponso matenda aakulu amawapititsa kuchipatala. Mwachionekere, dipatimenti yosamalira amayi apathupi ndiponso kochirira n’zofunika kwambiri pachipatalapo, chifukwa choti pamsasa wa anthu othaŵa kwawo okwana 48,000, pangakhale ana obadwa 250 pamwezi umodzi.

Kudya Bwino Mwauzimu

Padziko lonse, Mboni za Yehova zingafune kudziŵa za abale awo auzimu omwe akukhala m’misasa ya ku Tanzania. Onse pamodzi alipo pafupifupi 1,200, omwe ali m’mipingo 14 ndi magulu akutali atatu. Kodi zikuwayendera bwanji?

Akristu odzipereka ameneŵa atafika pamisasa, chimodzi mwa zinthu zoyamba kuchita chinali kupempha malo oti amangepo Nyumba ya Ufumu. Zimenezi zikanathandiza anthu othaŵa kwawowo kudziŵa kumene angapeze Mboni ndiponso kumene angachitire misonkhano yawo ya mlungu ndi mlungu. Pamsasa wa Lugufu, pali mipingo isanu ndi iŵiri imene ili ndi Akristu achangu okwana 659. Kuphatikiza pamodzi anthu onse opezeka pa misonkhano ya Lamlungu, m’mipingo yonse isanu ndi iŵiriyi, nthaŵi zambiri amakwana 1,700.

Mboni m’misasa yonseyi zimapindulanso ndi misonkhano yachikristu yaikulu. Nthaŵi imene msonkhano wachigawo woyamba unachitika ku msasa wa Lugufu, anthu 2,363 anapezekapo. Kunja kwa malo a msonkhano Mboni zinapanga malo obatiziramo. Malowo anali dzenje lomwe anakumba ndipo m’kati mwake anayalamo pepala la pulasitiki kuti madzi akhalemo. Mwakugwiritsira ntchito njinga, abale ankatunga madzi m’mtsinje womwe unali pafupifupi makilomita aŵiri kuchoka pamalowo. Popeza amangotha kunyamula malita 20 ulendo uliwonse, zimenezi zinatanthauza kuyenda maulendo ambiri. Anthu ofuna kubatizidwa anavala zovala zoyenera ndipo anaima pamzera kuti abatizidwe. Onse omwe anabatizidwa mwa kumizidwa m’madzi anali 56. Mtumiki wina wanthaŵi zonse yemwe anafunsidwa pamsonkhanowo anafotokoza kuti ankachititsa maphunziro a Baibulo 40. Ndipo anayi mwa anthu omwe ankaphunzira nawo anabatizidwa pamsonkhanowo.

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova inakonza zoti oyang’anira oyendayenda aziwayendera nthaŵi zonse. Woyang’anira wina anati: “Abale athu ndi achangu mu utumiki. Ali ndi gawo lalikulu lolalikiramo, ndipo m’mpingo wina Mboni iliyonse imathera pafupifupi maola 34 pamwezi mu utumiki. Ambiri amachititsa maphunziro a Baibulo asanu kapena kuposapo ndi anthu achidwi. Mpainiya wina [mtumiki wanthaŵi zonse] anati kulibe kwina kumene akanakhala ndi gawo labwino koposa limeneli. Anthu m’misasa amasangalala kwambiri ndi mabuku athu.”

Kodi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amafika bwanji kumisasa? Nthambi imawatumiza pa sitima kupita ku Kigoma, tauni yomwe ili ku gombe la kum’maŵa kwa nyanja ya Tanganyika. Kumeneko abale amalandira mabuku ndipo amalinganiza kuwatumiza ku mipingo. Nthaŵi zina amachita hayala galimoto ndipo amakasiya okha mabukuwo kumisasa yonse. Zimenezi zimatenga masiku atatu kapena anayi m’misewu yokumbika kwambiri.

Thandizo la Zinthu Zofunika Pamoyo

Mboni za Yehova ku France, Belgium ndi Switzerland zathandiza kwambiri othaŵa kwawo m’misasa imeneyi. Atavomerezedwa ndi Unduna woona nkhani za m’dziko ndiponso a bungwe la UNHCR, anthu ena apita kukaona anthu kumisasa ya ku Tanzania. Mboni za ku Ulaya zinasonkha mkaka wambiri wa soya, zovala, nsapato, mabuku a kusukulu ndiponso sopo. Zinthu zimenezi anazipereka kuti zipatsidwe kwa anthu onse othaŵa kwawo, mogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”​—Agalatiya 6:10.

Ntchito zothandiza anthu zimenezi zakhala ndi zotsatira zabwino kwambiri, othaŵa kwawo ambiri athandizidwa. Komiti yoyang’anira othaŵa kwawo mu msasa wina inayamikira mwa kunena kuti: “Moimira anthu onse a pamsasa wathu, tapatsidwa mwayi kulankhula nanu kuti tikuyamikireni pantchito zanu zothandiza anthu zimene bungwe lanu latipatsa katatu konse . . . Zovala zathandiza anthu osoŵa okwana 12,654 omwe ndi amuna, akazi ndi ana komanso ana ongobadwa kumene . . . Anthu othaŵa kwawo pamsasa wa Muyovozi tsopano alipo 37,000. Anthu onse pamodzi, 12,654 anathandizidwa, kapena kuti anthu 34 pa anthu 100 alionse pa chiŵerengero chonsecho.”

Pamsasa wina, anthu othaŵa kwawo 12,382 aliyense anapatsidwa zovala zitatu, ndipo pamsasa wina analandira mabuku zikwi zambiri ogwiritsira ntchito kusukulu zasekondale ndi zapulaimale ndiponso m’malo osamalirako ana masana. Mkulu woyang’anira anthu wa bungwe la UNHCR m’dera lina anati: “Ndife oyamikira kwambiri chifukwa cha zinthu zimene tinalandira [zimene zathandiza] anthu osoŵa kwambiri omwe ali m’misasa ya othaŵa kwawo. Katundu amene tinalandira posachedwapa anali zimakontena zikuzikulu zisanu za mabuku, amene oyang’anira pamsasa anagaŵira anthu othaŵa kwawo. . . . Zikomo kwambiri.”

Ngakhale olemba nyuzipepala a kuderali ananena za thandizo limene linaperekedwali. Mutu wa nkhani m’nyuzipepala ya Sunday News ya May 20, 2001, unati: “Zovala za Anthu Othaŵa Kwawo Amene Ali ku Tanzania Zikubwera.” Nkhani ya nyuzipepalayi ya pa February 10, 2002, inati: “Anthu othaŵa kwawo amayamikira katundu amene anapatsidwa chifukwa ana ena amene anali atasiya sukulu chifukwa analibe zovala, tsopano akupezeka nawo kumakalasi nthaŵi zonse.”

Osautsika Koma Osakhala Kakasi

Kwa anthu othaŵa kwawo ambiri zimawatengera pafupifupi chaka kuti azoloŵere moyo wa pamsasa. Iwo amakhala moyo wosafuna zambiri. Mboni za Yehova zomwe zili m’misasa imeneyi zikugwiritsira ntchito nthaŵi yawo yambiri kuuza othaŵa kwawo anzawo uthenga wabwino wolimbikitsa wochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Izo zimafotokoza za dziko latsopano, mmene anthu onse “adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.” Ndiyeno anthu onse “adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.” Mwachionekere, mwa dalitso la Mulungu, limeneli lidzakhala dziko lopanda misasa ya anthu othaŵa kwawo.​—Mika 4:3, 4; Salmo 46:9.

[Chithunzi patsamba 8]

Nyumba za pamsasa wa Nduta

[Zithunzi patsamba 10]

Nyumba ya Ufumu ya Lukole (kumanja) Ubatizo ku Lugufu (m’munsi)

[Chithunzi patsamba 10]

Msonkhano wachigawo pamsasa wa Lugufu